-
Yesaya 35:5, 6Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
5 Pa nthawi imeneyo, maso a anthu amene ali ndi vuto losaona adzatsegulidwa,+
Ndipo makutu a anthu amene ali ndi vuto losamva adzayamba kumva.+
6 Pa nthawi imeneyo, munthu wolumala adzadumpha ngati mmene imachitira mbawala,+
Ndipo lilime la munthu wosalankhula lidzafuula mosangalala.+
Mʼchipululu mudzatumphuka madzi,
Ndipo mʼdera lachipululu mudzayenda mitsinje.
-