Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 2 Samueli 22:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  3 Mulungu wanga ndi thanthwe langa,+ ine ndimathawira kwa iye,

      Iye ndi chishango changa,+ nyanga* yanga ya chipulumutso* ndi malo anga achitetezo.*+

      Komanso ndi malo anga othawirako,+ mpulumutsi wanga+ amene amandipulumutsa kwa anthu achiwawa.

  • Yesaya 43:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  3 Chifukwa ine ndine Yehova Mulungu wako,

      Woyera wa Isiraeli, Mpulumutsi wako.

      Ndapereka Iguputo kuti akhale dipo* lako.

      Ndaperekanso Itiyopiya ndi Seba mʼmalo mwa iwe.

  • Habakuku 3:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Ine ndidzakhalabe wosangalala chifukwa cha Yehova,

      Ndipo ndidzasangalala chifukwa cha Mulungu wachipulumutso changa.+

  • Tito 1:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Koma pa nthawi yake, anachititsa kuti mawu ake adziwike kudzera mu ntchito yolalikira imene ndinapatsidwa+ mogwirizana ndi lamulo la Mpulumutsi wathu, Mulungu.

  • Yuda 25
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 25 Iye yekha ndi Mulungu komanso Mpulumutsi wathu mwa Yesu Khristu Ambuye wathu, ndipo ndi woyenera ulemerero, ufumu, mphamvu ndi ulamuliro kuchokera kalekale kufika panopa komanso mpaka muyaya. Ame.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena