-
Maliko 12:43, 44Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
43 Ndiyeno Yesu anaitana ophunzira ake nʼkuwauza kuti: “Ndithu ndikukuuzani kuti mkazi wamasiye wosaukayu waponya zochuluka kuposa ena onse amene aponya ndalama moponyera zoperekamo.+ 44 Zili choncho chifukwa onsewo aponya zimene atapa pa zochuluka zimene ali nazo, koma mayiyu, mu umphawi wake, waponya zonse zimene anali nazo, inde zonse zimene zikanamuthandiza pa moyo wake.”+
-