-
Ekisodo 12:14Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
14 Tsiku limeneli lidzakhala chikumbutso kwa inu, ndipo muzichitira Yehova chikondwerero mʼmibadwo yanu yonse. Limeneli ndi lamulo mpaka kalekale, kuti muzichita chikondwerero chimenechi.
-
-
Deuteronomo 16:1, 2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
16 “Muzikumbukira kuti mwezi wa Abibu* ndi wofunika ndipo muzichita chikondwerero cha Pasika kwa Yehova Mulungu wanu,+ chifukwa mʼmwezi wa Abibu Yehova Mulungu wanu anakutulutsani mu Iguputo usiku.+ 2 Ndipo muzipereka nsembe ya Pasika kwa Yehova Mulungu wanu.+ Muzipereka nkhosa ndi ngʼombe+ pamalo amene Yehova adzasankhe kuikapo dzina lake.+
-