-
1 Akorinto 11:23-25Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
23 Zimene ndinamva kwa Ambuye nʼzimene inenso ndinakuphunzitsani, kuti Ambuye Yesu, usiku+ umene anaperekedwa anatenga mkate, 24 ndipo atayamika anaugawagawa* nʼkunena kuti: “Mkate uwu ukuimira thupi langa+ limene likuperekedwa chifukwa cha inu. Muzichita zimenezi pondikumbukira.”+ 25 Anachitanso chimodzimodzi ndi kapu+ atadya chakudya chamadzulo, ndipo anati: “Kapu iyi ikuimira pangano latsopano+ limene linakhazikitsidwa pogwiritsa ntchito magazi anga.+ Muzichita zimenezi mukamamwa zamʼkapu imeneyi pondikumbukira.”+
-