-
Yohane 18:25-27Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
25 Pa nthawiyi Simoni Petulo anali ataima pomwepo nʼkumawotha moto. Ndiyeno iwo anamufunsa kuti: “Kodi iwenso si mmodzi wa ophunzira ake?” Iye anakana nʼkunena kuti: “Ayi si ine.”+ 26 Mmodzi wa akapolo a mkulu wa ansembe, amenenso anali wachibale wa munthu amene Petulo anamudula khutu uja,+ anati: “Ndinakuona mʼmunda muja uli naye limodzi, ndikunama kapena?” 27 Koma Petulo anakananso ndipo nthawi yomweyo tambala analira.+
-