-
Mateyu 28:5-7Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
5 Koma mngeloyo anauza azimayiwo kuti: “Inu musachite mantha, chifukwa ndikudziwa kuti mukufuna Yesu amene anaphedwa popachikidwa pamtengo.+ 6 Muno mulibe chifukwa waukitsidwa mogwirizana ndi zimene ananena.+ Bwerani muone pamene anagona. 7 Ndipo pitani mwamsanga mukauze ophunzira ake kuti waukitsidwa kwa akufa, moti panopa watsogola kupita ku Galileya.+ Kumeneko mukamuona. Umenewutu ndi uthenga wanga kwa inu.”+
-
-
Maliko 16:5-7Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
5 Atalowa mʼmandamo, anaona mnyamata atakhala pansi mbali yakumanja, atavala mkanjo woyera ndipo iwo anadabwa kwambiri. 6 Iye anawauza kuti: “Musadabwe choncho.+ Ndikudziwa kuti mukufuna Yesu Mnazareti, amene anaphedwa popachikidwa pamtengo. Iyetu waukitsidwa kwa akufa,+ muno mulibe. Taonani, pamene anamugoneka paja si apa!+ 7 Inuyo pitani mukauze ophunzira ake komanso Petulo kuti, ‘Watsogola kupita ku Galileya.+ Kumeneko mukamuona, mogwirizana ndi zimene anakuuzani.’”+
-