-
Luka 24:9-11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
9 ndipo anachoka kumandako* nʼkubwerera kukanena zonsezi kwa ophunzira 11 aja ndi kwa ena onse.+ 10 Azimayiwa anali Mariya wa ku Magadala, Jowana ndi Mariya amayi ake a Yakobo. Komanso azimayi ena onse amene anali nawo limodzi ankauza atumwi zinthu zimenezi. 11 Koma kwa iwo, zimene ankawauzazo zinkaoneka ngati zopanda pake ndipo sanawakhulupirire azimayiwo.
-