19 Ndiyeno wansembe wamkulu anafunsa Yesu za ophunzira ake komanso zimene ankaphunzitsa. 20 Yesu anamuyankha kuti: “Ndalankhula poyera ku dzikoli. Nthawi zonse ndinkaphunzitsa mʼmasunagoge ndi mʼkachisi,+ kumene Ayuda onse ankasonkhana, ndipo sindinalankhule chilichonse kumbali.