-
Akolose 1:15-17Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
15 Iye ndi chifaniziro cha Mulungu wosaonekayo,+ woyamba kubadwa wa chilengedwe chonse.+ 16 Kudzera mwa iye, Mulungu analenga zinthu zina zonse kumwamba ndi padziko lapansi. Analenga zinthu zooneka ndi zinthu zosaoneka,+ kaya ndi mipando yachifumu, ambuye, maboma komanso maulamuliro. Inde, analenga zinthu zina zonse kudzera mwa iye+ ndiponso chifukwa cha iye. 17 Ndiponso iye analipo kale zinthu zina zonse zisanakhaleko+ ndipo zinthu zina zonse zinakhalapo kudzera mwa iye.
-