-
1 Samueli 17:34, 35Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
34 Davide anauza Sauli kuti: “Ine mtumiki wanu ndinakhala mʼbusa wa nkhosa za bambo anga. Ndiyeno kunabwera mkango+ komanso chimbalangondo ndipo chilombo chilichonse chinagwira nkhosa. 35 Zitatero, ndinatsatira chilombocho nʼkuchimenya, ndipo ndinapulumutsa nkhosa mʼkamwa mwake. Chitayamba kundilusira ndinachikoka ubweya* nʼkuchipha.
-