17 Yesu atalankhula zinthu zimenezi, anakweza maso ake kumwamba nʼkunena kuti: “Atate, nthawi yafika. Lemekezani mwana wanu, kuti mwana wanu akulemekezeni.+ 2 Inu mwapatsa mwana wanu ulamuliro pa anthu onse+ kuti onse amene inu mwamupatsa,+ awapatse moyo wosatha.+