28 Kenako Yesu anati: “Mukadzamukweza Mwana wa munthu,+ pamenepo mudzadziwa kuti amene munkamuyembekezera uja ndi ine+ komanso kuti sindichita chilichonse mongoganiza ndekha.+ Koma zimene ndimalankhula zimakhala zogwirizana ndendende ndi zimene Atate anandiphunzitsa.