22 Pilato anafunsanso kuti: “Nanga Yesu, amene mumati ndi Khristu uja, ndichite naye chiyani?” Onse anayankha kuti: “Apachikidwe ameneyo!”+ 23 Iye anati: “Chifukwa chiyani? Kodi iyeyu walakwa chiyani?” Koma anthuwo anapitiriza kufuula mwamphamvu kuti: “Ameneyo apachikidwe basi!”+