-
Yohane 19:40-42Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
40 Choncho iwo anatenga mtembo wa Yesu nʼkuukulunga ndi nsalu zamaliro zonunkhira,+ mogwirizana ndi mwambo umene Ayuda ankatsatira poika maliro. 41 Tsopano kumalo kumene anamupachikirako kunali munda mmene munali manda* atsopano,+ ndipo anali asanaikemo munthu chiyambire. 42 Popeza linali Tsiku Lokonzekera+ Chikondwerero cha Ayuda, ndipo mandawo anali pafupi, iwo anaika Yesu mmenemo.
-