-
Yohane 19:10, 11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
10 Ndiyeno Pilato anamuuza kuti: “Kodi sukufuna kulankhula nane? Kodi sukudziwa kuti ndili ndi mphamvu zokumasula komanso zokupachika?”* 11 Yesu anamuyankha kuti: “Simukanakhala ndi mphamvu iliyonse pa ine mukanapanda kupatsidwa kuchokera kumwamba. Nʼchifukwa chake munthu amene wandipereka kwa inu ali ndi tchimo lalikulu kwambiri.”
-
-
Machitidwe 4:27, 28Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
27 Zimenezi zinachitikadi pamene Herode, Pontiyo Pilato,+ anthu a mitundu ina komanso anthu a mu Isiraeli, anasonkhana mumzindawu nʼkuukira Yesu, mtumiki wanu woyera, amene inu munamudzoza.+ 28 Anasonkhana kuti achite zimene munaneneratu. Zimenezi zinachitika chifukwa inu muli ndi mphamvu komanso chifukwa zinali zogwirizana ndi chifuniro chanu.+
-