Maliko 6:56 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 56 Ndipo akangolowa mʼmidzi kapena mʼmizinda komanso mʼmadera ozungulira, anthu ankakhazika odwala mʼmisika. Iwo ankamuchonderera kuti angogwira ulusi wopota wamʼmphepete mwa malaya ake akunja,+ ndipo anthu onse amene anaugwira anachira. Machitidwe 5:15 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 15 Anthuwo ankabweretsa odwala mʼmisewu nʼkuwagoneka pamabedi angʼonoangʼono ndi pamphasa kuti Petulo akamadutsa, chithunzithunzi chake chokha chifike pa ena mwa odwalawo.+
56 Ndipo akangolowa mʼmidzi kapena mʼmizinda komanso mʼmadera ozungulira, anthu ankakhazika odwala mʼmisika. Iwo ankamuchonderera kuti angogwira ulusi wopota wamʼmphepete mwa malaya ake akunja,+ ndipo anthu onse amene anaugwira anachira.
15 Anthuwo ankabweretsa odwala mʼmisewu nʼkuwagoneka pamabedi angʼonoangʼono ndi pamphasa kuti Petulo akamadutsa, chithunzithunzi chake chokha chifike pa ena mwa odwalawo.+