16 Ine ndidzapempha Atate ndipo adzakupatsani mthandizi wina kuti adzakhale nanu mpaka kalekale.+ 17 Mthandizi ameneyo ndi mzimu wa choonadi+ umene dziko silingaulandire, chifukwa siliuona kapena kuudziwa.+ Inu mumaudziwa chifukwa umakhala mwa inu ndipo uli mwa inu.