25 Pa chifukwa chimenechi, ndikukuuzani kuti: Siyani kudera nkhawa za moyo wanu,+ kuti mudzadya chiyani kapena kuti mudzamwa chiyani kapenanso kudera nkhawa za matupi anu kuti mudzavala chiyani.+ Kodi moyo si wofunika kwambiri kuposa chakudya ndipo kodi thupi si lofunika kwambiri kuposa chovala?+