-
Afilipi 2:1, 2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
2 Muzichita zonse zimene mungathe kuti muzilimbikitsana mwa Khristu, muzitonthozana mwachikondi, muzisonyeza mzimu wokonda kuchitira zinthu limodzi,* muzisonyezana chikondi chachikulu komanso chifundo. 2 Mukamachita zimenezi, mudzachititsa kuti chimwemwe changa chisefukire. Muzisonyeza kuti mumaganiza mofanana, muli ndi chikondi chofanana komanso kuti ndinu ogwirizana kwambiri ndipo maganizo anu ndi amodzi.+
-