Miyambo 15:1 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 15 Kuyankha modekha* kumabweza mkwiyo,+Koma mawu opweteka amayambitsa mkwiyo.+ Agalatiya 6:1 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Abale, ngati munthu wapatuka nʼkuyamba kulowera njira yolakwika mosazindikira, inu amene ndi oyenerera mwauzimu, yesani kuthandiza munthu woteroyo ndi mzimu wofatsa.+ Koma pamene mukuchita zimenezi musamale,+ kuopera kuti inunso mungayesedwe.+ Tito 3:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 Asamanenere zoipa munthu aliyense ndiponso asamakonde kukangana. Koma akhale ololera+ ndipo azikhala ofatsa kwa anthu onse.+ 1 Petulo 3:15 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 15 Koma muvomereze mumtima mwanu kuti Khristu ndi Ambuye ndiponso kuti ndi woyera. Nthawi zonse muzikhala okonzeka kuyankha aliyense amene wakufunsani za chiyembekezo chanu, koma muziwayankha mofatsa+ ndiponso mwaulemu kwambiri.+
6 Abale, ngati munthu wapatuka nʼkuyamba kulowera njira yolakwika mosazindikira, inu amene ndi oyenerera mwauzimu, yesani kuthandiza munthu woteroyo ndi mzimu wofatsa.+ Koma pamene mukuchita zimenezi musamale,+ kuopera kuti inunso mungayesedwe.+
2 Asamanenere zoipa munthu aliyense ndiponso asamakonde kukangana. Koma akhale ololera+ ndipo azikhala ofatsa kwa anthu onse.+
15 Koma muvomereze mumtima mwanu kuti Khristu ndi Ambuye ndiponso kuti ndi woyera. Nthawi zonse muzikhala okonzeka kuyankha aliyense amene wakufunsani za chiyembekezo chanu, koma muziwayankha mofatsa+ ndiponso mwaulemu kwambiri.+