-
1 Timoteyo 3:2-7Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
2 Choncho woyangʼanira ayenera kukhala wopanda chifukwa chomunenezera, mwamuna wa mkazi mmodzi, wosachita zinthu mopitirira malire, woganiza bwino,+ wochita zinthu mwadongosolo, wochereza alendo+ ndiponso wodziwa kuphunzitsa.+ 3 Asakhale munthu womwa mowa mwauchidakwa,+ kapena wankhanza,* koma wololera.+ Asakhalenso wokonda kukangana+ kapena wokonda ndalama.+ 4 Akhale mwamuna woyangʼanira bwino banja lake ndiponso woti ana ake amamumvera ndi mtima wonse.+ 5 (Ngati munthu sadziwa kuyangʼanira banja lake, ndiye mpingo wa Mulungu angausamalire bwanji?) 6 Asakhale woti wangobatizidwa kumene,*+ kuopera kuti angayambe kudzitukumula chifukwa cha kunyada nʼkulandira chiweruzo chofanana ndi chimene Mdyerekezi analandira. 7 Akhalenso ndi mbiri yabwino kwa osakhulupirira*+ kuti asanyozedwe ndi anthu komanso kukodwa mumsampha wa Mdyerekezi.
-