-
2 Petulo 3:11, 12Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
11 Popeza zinthu zonsezi zidzasungunuka chonchi, ganizirani za mtundu wa anthu amene muyenera kukhala. Muyenera kukhala anthu akhalidwe loyera ndipo muzichita ntchito zosonyeza kuti ndinu odzipereka kwa Mulungu. 12 Muzichita zimenezi pamene mukuyembekezera komanso kukumbukira nthawi zonse* kubwera kwa tsiku la Yehova.*+ Pa tsikuli kumwamba kudzapsa ndi moto nʼkuwonongekeratu+ ndipo zinthu zimene zimapanga kumwamba ndi dziko lapansi zidzatentha kwambiri nʼkusungunuka.
-