-
Oweruza 14:5, 6Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
5 Choncho Samisoni anapita ku Timuna pamodzi ndi bambo ndi mayi ake. Atafika mʼminda ya mpesa ya ku Timuna, anakumana ndi mkango ndipo unayamba kubangula. 6 Ndiyeno mzimu wa Yehova unamupatsa mphamvu,+ moti anakhadzula mkangowo pakati ngati mmene munthu angakhadzulire kamwana ka mbuzi ndi manja. Koma sanauze bambo kapena mayi ake zimene anachitazi.
-
-
1 Samueli 17:34-36Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
34 Davide anauza Sauli kuti: “Ine mtumiki wanu ndinakhala mʼbusa wa nkhosa za bambo anga. Ndiyeno kunabwera mkango+ komanso chimbalangondo ndipo chilombo chilichonse chinagwira nkhosa. 35 Zitatero, ndinatsatira chilombocho nʼkuchimenya, ndipo ndinapulumutsa nkhosa mʼkamwa mwake. Chitayamba kundilusira ndinachikoka ubweya* nʼkuchipha. 36 Ine mtumiki wanu ndinapha zilombo ziwiri zonsezi, mkango komanso chimbalangondo. Mfilisiti wosadulidwayu akhalanso ngati chimodzi mwa zilombo zimenezi, chifukwa wanyoza asilikali a Mulungu wamoyo.”+
-