-
Afilipi 3:13, 14Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
13 Abale, ine sindikudziona ngati ndalandira kale mphotoyo ayi. Koma pali chinthu chimodzi chimene ndikuchita: Ndikuiwala zinthu zakumbuyo+ ndipo ndikuyesetsa kuti ndikapeze zakutsogolo.+ 14 Ndikuyesetsa kuti ndikwaniritse cholinga changa chokalandira mphoto.+ Mphoto imeneyi ndi kukakhala ndi moyo kumwamba+ ndipo Mulungu adzaipereka kwa anthu amene anawaitana kudzera mwa Khristu Yesu.
-