-
Genesis 19:15, 16Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
15 Kutatsala pangʼono kucha, angelowo anayamba kumuuza Loti kuti afulumire. Iwo anamuuza kuti: “Fulumira! Tenga mkazi wako ndi ana ako aakazi awiriwa, kuti musawonongedwe limodzi ndi mzindawu chifukwa cha kulakwa kwake.”+ 16 Iye ankazengereza koma popeza Yehova anamuchitira chifundo,+ alendowo anagwira dzanja la iyeyo, mkazi wake ndi ana ake aakazi awiriwo nʼkuwatulutsa kukawasiya kunja kwa mzinda.+
-