4 Koma iwo asanagone, chigulu cha amuna a mumzinda wa Sodomu, chinafika nʼkuzungulira nyumba ya Loti. Pachigulupo panali anyamata komanso achikulire. 5 Iwo ankauza Loti mofuula kuti: “Kwanu kuno kwabwera amuna enaake usiku uno. Ali kuti amuna amenewo? Atulutse kuti tigone nawo.”+