-
3 Yohane 9, 10Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
9 Mpingo wanu ndinaulembera kalata, koma Diotirefe amene amakonda kukhala woyamba pakati panu,+ salemekeza chilichonse chimene tanena.+ 10 Nʼchifukwa chake ndikadzabwera, ndidzaulula zimene akuchita pofalitsa mabodza onena za ife.+ Ndipo chifukwa chosakhutira ndi zimenezi, amakana kulandira abale+ mwaulemu. Komanso anthu amene amafuna kuwalandira, amayesa kuwatsekereza ndiponso kuwachotsa mumpingo.
-