-
Agalatiya 5:19-21Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
19 Tsopano ntchito za thupi lochimwali zimaonekera mosavuta. Ntchito zimenezi ndi chiwerewere,*+ khalidwe limene limadetsa munthu, khalidwe lopanda manyazi,*+ 20 kulambira mafano, kukhulupirira mizimu,*+ chidani, ndewu, nsanje, kupsa mtima, mikangano, kugawikana, magulu ampatuko, 21 kaduka, kumwa mwauchidakwa,*+ maphwando oipa,* ndi zina zotero.+ Abale, mogwirizana ndi zimene ndinakuchenjezani kale, ndikukuchenjezaninso kuti anthu amene amachita zimenezi sadzalowa mu Ufumu wa Mulungu.+
-