8 Koma mukadzalandira mzimu woyera, mudzakhala ndi mphamvu.+ Ndipo mudzakhala mboni+ zanga mu Yerusalemu,+ ku Yudeya konse ndi ku Samariya,+ mpaka kumalekezero* a dziko lapansi.”+
9 Ine Yohane mʼbale wanu, amene mofanana ndi inu ndikupirira,+ ndikukumana ndi masautso+ ndipo tidzalamulira limodzi mu ufumu+ monga otsatira a Yesu,+ ndinali pachilumba cha Patimo chifukwa cholankhula za Mulungu ndi kuchitira umboni za Yesu.
9 Atamatula chidindo cha 5, ndinaona pansi pa guwa lansembe+ pali miyoyo*+ ya anthu amene anaphedwa chifukwa cha mawu a Mulungu ndiponso chifukwa cha ntchito yochitira umboni.+