26 Ngati tikuchita machimo mwadala pambuyo podziwa choonadi molondola,+ palibenso nsembe ina imene ingaperekedwe chifukwa cha machimo athuwo.+ 27 Koma pali chiyembekezo china choopsa cha chiweruzo, ndiponso mkwiyo woyaka moto umene udzawononge otsutsawo.+