Mawu Oyamba
BAIBULO Lopatulika ndi uthenga wochokera kwa Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, umene unalembedwa kuti anthu onse padziko lapansi audziwe. Buku louziridwa limeneli limakhudza mitima ya anthu padziko lonse lapansi chifukwa lili ndi uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu, umene udzabweretse mtendere ndi chilungamo. Dziko lapansi lidzakhala paradaiso wa anthu onse. Baibulo limasonyeza kuti Mulungu mwachikondi anapereka kwa anthu ochimwa mwayi wopulumuka ku imfa, kudzera mu nsembe ya dipo ya Mwana wake Yesu Khristu.—Yohane 3:16.
Poyambirira penipeni, Baibulo linalembedwa m’Chiheberi, m’Chiaramu (chinenero chofanana ndi Chiheberi), ndi m’Chigiriki. Popeza masiku ano ndi anthu ochepa okha amene amamva zinenero zimenezi, m’pofunika kumasulira Baibulo Lopatulika m’zinenero za masiku ano kuti anthu a mitundu yonse amve uthenga wopatsa moyo umene uli m’Baibulo.
Baibulo lachichewa latsopanoli talimasulira kuchokera ku Baibulo lachingelezi la New World Translation of the Holy Scriptures la 1984. Lili ndi mabuku 39 a Malemba Achiheberi ndi Chiaramu. Lilinso ndi mabuku 27 a Malemba Achigiriki amene anatuluka m’Chichewa mu 2006, omwe tawakonzanso. Komiti Yomasulira Baibulo la Dziko Latsopano inaganiza zotchula zigawo ziwiri zimenezi za Malemba Opatulika potsatira zinenero zake zoyambirira. Sinafune kutsatira katchulidwe kofala kakuti “Chipangano Chakale” ndi “Chipangano Chatsopano,” chifukwa Baibulo ndi buku limodzi. Palibe mbali ina imene ili yotha ntchito kapena “yakale.” Uthenga wake ndi wogwirizana kuyambira buku loyambirira m’chigawo chachiheberi mpaka buku lomalizira m’chigawo chachigiriki. Pofuna kuthandiza owerenga kuti athe kuphunzira bwinobwino Baibulo lonse, taikamo malifalensi olozera ku mavesi ena oposa 125,000. Taikamonso kalozera wa mawu a m’Baibulo ndi mndandanda wa Matanthauzo a Mawu Ena.
Baibulo limafotokoza cholinga chopatulika cha Ambuye Wamkulu Koposa wa chilengedwe chonse. Chotero kuchotsamo dzina la Mulungu kapena kulibisa, kungakhale kupanda ulemu kwambiri komanso kunyoza mphamvu ndi ulamuliro wake, chifukwa dzinali limapezeka nthawi pafupifupi 7,000 m’Malemba Achiheberi. Choncho chinthu chapadera kwambiri m’Baibulo lino n’chakuti tabwezeretsa dzina la Mulungu m’malo ake oyenerera. Tachita zimenezi pogwiritsa ntchito dzina la Mulungu limene pa Chichewa limadziwika bwino kwambiri kuti “Yehova.” M’Baibulo lino, dzinali likupezeka maulendo 6,973 m’Malemba Achiheberi ndiponso maulendo 237 m’Malemba Achigiriki. Kuti mumve zambiri pa nkhani imeneyi, onani Zakumapeto.
Chifukwa chakuti Baibuloli tamasulira anthu olankhula Chichewa a m’mayiko osiyanasiyana, tayesetsa kugwiritsa ntchito mawu odziwika kwa anthu ambiri a m’mayikowa. Pamene sizinatheke kupeza mawu odziwika m’mayiko onsewa, mawu enawo tawaika m’mawu a m’munsi kuti tithandize anthu amene sangadziwe mawu amene tagwiritsa ntchitowo.
Omasulira Baibulo lino amakonda Mulungu yemwe ndiye Mlembi Wamkulu wa Malemba Opatulika. Choncho iwo amaona kuti ali ndi udindo wapadera kwambiri womasulira maganizo ake ndi mawu ake molondola kwambiri. Amaonanso kuti ali ndi udindo wapadera kwa owerenga ofuna kumvetsetsa mawu a Mulungu. Kuti anthu amenewa adzapulumuke n’kupeza moyo wosatha, amadalira Baibulo lomasulira bwino Mawu ouziridwa a Mulungu Wam’mwambamwamba. Tikufunitsitsa kuti anthu akawerenga Baibulo lino, apeze njira yopita ku moyo wosatha m’dziko latsopano la Wamphamvuyonse, mmene mudzakhale chilungamo.—Yesaya 65:17; 2 Petulo 3:13.
—Ofalitsa