Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • bi12 Genesis 1:1-50:26
  • Genesis

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Genesis
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Genesis

Genesis

1 Pa chiyambi,+ Mulungu+ analenga+ kumwamba ndi dziko lapansi.+

2 Dziko lapansi linali lopanda maonekedwe enieni ndiponso lopanda kanthu. Panali madzi akuya+ kwambiri ndipo pamwamba pake panali mdima wokhawokha. Ndipo mphamvu* ya Mulungu inali kuyendayenda+ pamwamba pa madzi akuyawo.+

3 Ndiyeno Mulungu anati:+ “Pakhale kuwala.” Ndipo kuwala kunakhalapo.+ 4 Zitatero, Mulungu anaona kuti kuwalako kunali kwabwino. Kenako Mulungu analekanitsa kuwala ndi mdima.+ 5 Ndiyeno Mulungu anatcha kuwalako Usana,+ koma mdimawo anautcha Usiku.+ Panali madzulo ndiponso panali m’mawa, tsiku loyamba.

6 Mulungu tsopano anati: “Pakhale mlengalenga+ pakati pa madzi, ndiponso pakhale cholekanitsa pakati pa madzi ndi madzi.”+ 7 Motero Mulungu anapanga mlengalenga. Anapanganso cholekanitsa madzi, kuti ena akhale pansi pa mlengalenga, ena akhale pamwamba pa mlengalenga.+ Ndipo zinaterodi. 8 Mulungu atatero, anatcha mlengalengawo Kumwamba.+ Panali madzulo ndiponso panali m’mawa, tsiku lachiwiri.

9 Kenako Mulungu anati: “Madzi apansi pa thambo asonkhane malo amodzi, mtundanso uonekere.”+ Ndipo zinaterodi. 10 Tsopano Mulungu anatcha mtundawo Dziko,+ koma madzi osonkhanawo anawatcha Nyanja.+ Ndipo Mulungu anaona kuti zili bwino.+ 11 Ndiyeno Mulungu anati: “Dziko lapansi limere udzu, limere zomera zobala mbewu,+ limere mitengo yobala zipatso zokhala ndi mbewu yake, monga mwa mtundu wake.”+ Ndipo zinaterodi. 12 Motero dziko lapansi linamera udzu, zomera zobala mbewu monga mwa mtundu wake,+ mitengo yobala zipatso zokhala ndi mbewu zake monga mwa mtundu wake.+ Zitatero, Mulungu anaona kuti zili bwino. 13 Panali madzulo ndiponso panali m’mawa, tsiku lachitatu.

14 Kenako Mulungu anati: “Kukhale zounikira kuthambo kuti zilekanitse usana ndi usiku+ ndipo zikhale zizindikiro, komanso kuti zisonyeze nyengo ndi masiku ndi zaka.+ 15 Zikhale zounikira zakuthambo zowalitsa dziko lapansi.”+ Ndipo zinaterodi. 16 Motero Mulungu anapanga zounikira zikuluzikulu ziwiri. Chounikira chokulirapo anachipanga kuti chilamulire usana, ndi chocheperapo kuti chilamulire usiku, komanso nyenyezi.+ 17 Mulungu atatero, anaziika kuthambo kuti ziunikire dziko lapansi,+ 18 ndi kuti zilamulire usana ndi usiku, komanso zilekanitse kuwala ndi mdima.+ Zitatero, Mulungu anaona kuti zili bwino.+ 19 Panali madzulo ndiponso panali m’mawa, tsiku lachinayi.

20 Kenako Mulungu anati: “M’madzi mukhale zamoyo zambirimbiri,+ ndiponso zolengedwa zouluka ziuluke m’mlengalenga mwa dziko lapansi.”+ 21 Motero Mulungu analenga zilombo zikuluzikulu za m’nyanja+ ndi chamoyo chilichonse chokhala mmenemo.+ Nyanja inatulutsa zimenezi zambirimbiri monga mwa mitundu yake.+ Analenganso chamoyo chilichonse chouluka monga mwa mtundu wake. Ndipo Mulungu anaona kuti zili bwino. 22 Mulungu atatero, anazidalitsa kuti: “Muswane, muchuluke, mudzaze nyanja zonse.+ Ndipo zolengedwa zouluka zichuluke padziko lapansi.” 23 Panali madzulo ndiponso panali m’mawa, tsiku lachisanu.

24 Tsopano Mulungu anati: “Dziko lapansi+ likhale ndi zamoyo monga mwa mitundu yake, nyama zoweta,+ nyama zokwawa,*+ komanso nyama zakutchire+ monga mwa mitundu yake.” Ndipo zinaterodi. 25 Motero Mulungu anapanga nyama zakutchire monga mwa mitundu yake. Anapanganso nyama zoweta monga mwa mitundu yake, komanso nyama iliyonse yokwawa panthaka monga mwa mtundu wake.+ Ndipo Mulungu anaona kuti zili bwino.

26 Kenako Mulungu anati: “Tiyeni+ tipange munthu m’chifaniziro chathu,+ kuti akhale wofanana nafe.+ Ayang’anire nsomba zam’nyanja ndi zolengedwa zouluka m’mlengalenga, komanso nyama zoweta. Ayang’anirenso dziko lonse lapansi ndi nyama zonse zokwawa padziko lapansi.”+ 27 Motero Mulungu analenga munthu m’chifaniziro chake,+ m’chifaniziro cha Mulungu anam’lenga iye. Anawalenga mwamuna ndi mkazi.+ 28 Komanso, Mulungu anawadalitsa+ n’kuwauza kuti: “Muberekane,+ muchuluke, mudzaze dziko lapansi, ndipo muliyang’anire.+ Muyang’anirenso+ nsomba zam’nyanja ndi zolengedwa zouluka m’mlengalenga, komanso cholengedwa chilichonse chokwawa padziko lapansi.”

29 Tsopano Mulungu anati: “Taonani, ndakupatsani zomera zonse zobala mbewu zapadziko lonse lapansi, ndi mitengo yonse yobala zipatso za mbewu+ kuti zikhale chakudya chanu.+ 30 Kwa nyama iliyonse yam’tchire ya padziko lapansi, ndi kwa cholengedwa chilichonse chouluka m’mlengalenga, komanso kwa chokwawa chilichonse cha padziko lapansi chimene chili ndi moyo, ndapereka zomera zonse kuti zikhale chakudya chawo.”+ Ndipo zinaterodi.

31 Ndiyeno Mulungu anaona kuti zonse zimene anapanga zinali zabwino kwambiri.+ Panali madzulo ndiponso panali m’mawa, tsiku la 6.

2 Motero, kumwamba ndi dziko lapansi ndi zonse za mmenemo zinamalizidwa kulengedwa.+ 2 Pofika tsiku la 7, Mulungu anali atamaliza ntchito yake imene anali kuchita. Pa tsiku la 7 limenelo, iye anayamba kupuma pa ntchito yake yonse imene anali kuchita.+ 3 Kenako Mulungu anadalitsa tsiku la 7. Analipatula kuti likhale lopatulika, chifukwa kuyambira pa tsikuli, iye wakhala akupuma pa ntchito yake yonse yolenga ndi yopanga zimene anafuna.+

4 Iyi ndi nkhani yofotokoza mmene kumwamba ndi dziko lapansi zinalengedwera, m’tsiku limene Yehova Mulungu anapanga dziko lapansi ndi kumwamba.+

5 Nthaka ya padziko lapansi inali isanayambe kumera zitsamba ndi zomera zina, chifukwa Yehova Mulungu anali asanagwetse mvula+ padziko lapansi. Panalibenso munthu woti n’kulima nthakayo. 6 Koma nkhungu+ inali kukwera m’mwamba kuchokera padziko lapansi, ndipo inali kunyowetsa nthaka yonse.+

7 Kenako, Yehova Mulungu anaumba munthu kuchokera kufumbi lapansi,+ ndipo anauzira mpweya wa moyo+ m’mphuno mwake, munthuyo n’kukhala wamoyo.+ 8 Yehova Mulungu atatero, anakonza munda ku Edeni,+ chakum’mawa, ndipo m’mundamo anaikamo munthu amene anamuumbayo.+ 9 Motero Yehova Mulungu anameretsa m’nthaka mtengo wamtundu uliwonse wooneka bwino ndi wa zipatso zabwino kudya. Anameretsanso mtengo wa moyo+ pakati pa mundawo, komanso mtengo wodziwitsa chabwino ndi choipa.+

10 Panalinso mtsinje wochokera mu Edeni umene unali kuthirira mundawo. Potuluka mmenemo, mtsinjewo unayamba kugawikana n’kukhala mitsinje inayi. 11 Mtsinje woyamba dzina lake ndi Pisoni, umene umazungulira dziko lonse la Havila+ kumene kuli golide. 12 Golide wa dziko limenelo ndi wabwino.+ Kulinso mafuta onunkhira a bedola+ ndi miyala yamtengo wapatali ya onekisi.+ 13 Dzina la mtsinje wachiwiri ndi Gihoni, umene umazungulira dziko lonse la Kusi. 14 Dzina la mtsinje wachitatu ndi Hidekeli,+ umene umalowera kum’mawa kwa Asuri.+ Ndipo mtsinje wachinayi ndi Firate.+

15 Tsopano Yehova Mulungu anatenga munthu uja n’kumuika m’munda wa Edeni+ kuti aziulima ndi kuusamalira.+ 16 Ndiyeno Yehova Mulungu anapatsa munthuyo lamulo lakuti: “Zipatso za mtengo uliwonse wa m’mundamu uzidya ndithu.+ 17 Koma usadye zipatso za mtengo wodziwitsa chabwino ndi choipa. Chifukwa tsiku limene udzadya, udzafa ndithu.”+

18 Kenako Yehova Mulungu anati: “Si bwino kuti munthu akhale yekha. Ndimupangira womuthandiza, monga mnzake womuyenerera.”+ 19 Yehova Mulungu anali kuumba ndi dothi nyama iliyonse yakutchire, ndi cholengedwa chilichonse chouluka m’mlengalenga. Ndipo anayamba kuzibweretsa kwa munthuyo, kuti chilichonse achitche dzina. Dzina lililonse limene munthuyo anatchula chamoyo chilichonse,+ limenelo linakhaladi dzina lake.+ 20 Choncho munthuyo anali kutcha mayina nyama zonse zoweta, ndiponso zolengedwa zonse zouluka m’mlengalenga, komanso nyama iliyonse yakutchire. Koma munthuyo analibe womuthandiza, monga mnzake womuyenerera. 21 Motero Yehova Mulungu anagoneka munthuyo tulo tofa nato.+ Munthuyo ali chigonere choncho, Mulungu anamuchotsa nthiti imodzi n’kutseka pamalopo ndi mnofu. 22 Ndiyeno Yehova Mulungu anapanga mkazi kuchokera kunthiti imene anaichotsa kwa mwamunayo. Atatero, anamubweretsa kwa iye.+

23 Ndiyeno mwamunayo anati:

“Uyu tsopano ndiye fupa la mafupa anga

Ndi mnofu wa mnofu wanga.+

Ameneyutu adzatchedwa Mkazi,

Chifukwa iyeyu watengedwa kwa mwamuna.”+

24 Pa chifukwa chimenechi, mwamuna adzasiya bambo ake ndi mayi ake,+ n’kudziphatika kwa mkazi wake, ndipo iwo adzakhala thupi limodzi.+ 25 Ndipo onsewo, mwamuna ndi mkazi wakeyo, anali kukhala maliseche.+ Koma sankachita manyazi.+

3 Tsopano njoka+ inali yochenjera kwambiri+ kuposa nyama zonse zakutchire zimene Yehova Mulungu anapanga.+ Ndipo njokayo inafunsa mkaziyo+ kuti: “Eti n’zoona kuti Mulungu anati musadye zipatso za mtengo uliwonse wa m’mundamu?”+ 2 Pamenepo mkaziyo anayankha njokayo kuti: “Zipatso za mitengo yonse ya m’mundamu anatiuza kuti tizidya.+ 3 Koma zipatso za mtengo umene uli pakati pa munda,+ Mulungu anati, ‘Musadye zipatso zake ayi, musaukhudze kuti mungafe.’”+ 4 Pamenepo njokayo inauza mkaziyo kuti: “Kufa simudzafa ayi.+ 5 Mulungutu akudziwa kuti tsiku limene mudzadye chipatso cha mtengo umenewu, maso anu adzatseguka ndithu, ndipo mudzafanana ndi Mulungu. Mudzadziwa zabwino ndi zoipa.”+

6 Mkaziyo atamva zimenezo, anayamba kuona kuti zipatso za mtengowo n’zokoma kudya, zokhumbirika ndi zosiririka.+ Choncho anathyola chipatso cha mtengowo n’kudya. Pambuyo pake, anapatsako mwamuna wake pamene anali limodzi, ndipo nayenso anadya.+ 7 Atatero maso awo anatseguka, ndipo anazindikira kuti ali maliseche.+ Choncho anadzisokera masamba a mkuyu n’kupanga zovala zomangira m’chiuno.+

8 Pambuyo pake, iwo anamva mawu a Yehova Mulungu pamene iye anali kuyendayenda m’mundamo pa nthawi ya kamphepo kayeziyezi.+ Mwamuna ndi mkaziyo atamva, anathawa n’kukabisala pakati pa mitengo ya m’mundamo kuti Yehova Mulungu asawaone.+ 9 Koma Yehova Mulungu anapitiriza kuitana mwamunayo, ndipo anati: “Kodi uli kuti?”+ 10 Potsirizira pake, mwamunayo anayankha kuti: “Ndinamva kuitana kwanu m’munda muno, koma ndinachita mantha poona kuti ndili maliseche. Choncho ndinabisala.”+ 11 Pamenepo Mulungu anati: “Wakuuza ndani kuti uli maliseche?+ Kodi wadya chipatso cha mtengo umene ndinakulamula kuti usadzadye?”+ 12 Mwamunayo anayankha kuti: “Mkazi amene munandipatsayu ndi amene wandipatsa chipatso cha mtengowo, ndipo ine ndadya.”+ 13 Yehova Mulungu atamva zimenezi, anafunsa mkaziyo kuti: “Ndiye chiyani wachitachi?” Mkaziyo anayankha kuti: “Njoka ndi imene inandinyenga, ndipo ine ndadya.”+

14 Tsopano Yehova Mulungu anauza njokayo+ kuti: “Chifukwa cha zimene wachitazi, ukhala wotembereredwa pa nyama zonse zoweta ndi zakutchire. Udzakwawa ndi mimba yako ndipo udzadya fumbi masiku onse a moyo wako.+ 15 Ndidzaika+ chidani+ pakati pa iwe+ ndi mkaziyo,+ ndi pakati pa mbewu yako+ ndi mbewu yake.+ Mbewu ya mkaziyo+ idzaphwanya mutu wako,+ ndipo iwe+ udzaivulaza chidendene.”+

16 Kwa mkaziyo, Mulungu ananena kuti: “Ndidzawonjezera kuvutika kwako pamene uli ndi pakati.+ Pobereka ana udzamva zowawa.+ Udzakhumba mwamuna wako, ndipo iye adzakulamulira.”+

17 Kwa Adamu, Mulungu ananena kuti: “Chifukwa wamvera mawu a mkazi wako, ndipo wadya chipatso cha mtengo umene ndinakulamula+ kuti, ‘Usadzadye zipatso zake,’ nthaka ikhale yotembereredwa kwa iwe.+ Udzadya zotuluka m’nthakayo movutikira masiku onse a moyo wako.+ 18 Minga ndi zitsamba zobaya* zidzamera panthaka,+ ndipo udzadya zomera za m’nthaka. 19 Udzadya chakudya kuchokera m’thukuta la nkhope yako mpaka utabwerera kunthaka, pakuti n’kumene unatengedwa.+ Popeza ndiwe fumbi, kufumbiko udzabwerera.”+

20 Pambuyo pa izi, Adamu anatcha mkazi wake dzina lakuti Hava,*+ chifukwa anali kudzakhala mayi wa munthu aliyense wamoyo.+ 21 Kenako Yehova Mulungu anapangira Adamu ndi mkazi wake zovala zazitali zachikopa, n’kuwaveka.+ 22 Ndiyeno Yehova Mulungu anati: “Tsopano munthu wakhala wodziwa zabwino ndi zoipa ngati ife.+ Choncho, kuti asathyolenso ndi kudya chipatso cha mtengo wa moyo,+ n’kukhala ndi moyo mpaka kalekale,* . . .” 23 Yehova Mulungu atatero, anatulutsa munthuyo kunja kwa munda wa Edeni,+ kuti akalime nthaka imene anatengedwako.+ 24 Chotero anam’pitikitsa munthuyo. Ndiyeno anaika akerubi+ kum’mawa kwa munda wa Edeniwo.+ Anaikanso lupanga loyaka moto, limene linali kuzungulira mosalekeza, kutchinga njira yopita ku mtengo wa moyo.

4 Kenako Adamu anagona ndi Hava mkazi wake, ndipo mkaziyo anatenga pakati.+ M’kupita kwa nthawi, mkaziyo anabereka Kaini*+ n’kunena kuti: “Ndabereka mwana wamwamuna ndi thandizo la Yehova.”+ 2 Pambuyo pake, Hava anabereka Abele+ m’bale wake wa Kaini.

Abele anakhala woweta nkhosa,+ koma Kaini anali mlimi.+ 3 Patapita nthawi, Kaini anabweretsa zina mwa zokolola zake zakumunda,+ n’kuzipereka nsembe kwa Yehova.+ 4 Abele nayenso anabweretsa ana oyamba+ a nkhosa zake n’kuwapereka nsembe, ndipo anaperekanso nsembe mafuta a nkhosazo.+ Yehova anakondwera ndi Abele ndipo analandira nsembe yake,+ 5 koma sanakondwere naye Kaini ndi nsembe yake+ m’pang’ono pomwe. Chotero Kaini anapsa mtima kwambiri+ ndipo nkhope yake inagwa. 6 Pamenepo Yehova anafunsa Kaini kuti: “N’chifukwa chiyani wapsa mtima choncho, ndipo nkhope yako yagweranji? 7 Ukasintha n’kuchita chabwino, sindikuyanja kodi?+ Koma ngati susintha kuti uchite chabwino, uchimo wamyata pakhomo kukudikirira, ndipo ukulakalaka kukudya.+ Kodi iweyo suugonjetsa?”+

8 Zitatero, Kaini anauza Abele m’bale wake kuti: “Tiye tipite kumunda.” Ali kumeneko, Kaini anam’kantha Abele m’bale wake n’kumupha.+ 9 Pambuyo pake, Yehova anafunsa Kaini kuti: “Kodi m’bale wako Abele ali kuti?”+ Iye anayankha kuti: “Sindikudziwa. Kodi ndine mlonda wa m’bale wangayo?”+ 10 Pamenepo Mulungu anati: “N’chiyani chimene wachitachi? Tamvera tsono. Magazi a m’bale wako akundilirira munthaka.+ 11 Tsopano ndiwe wotembereredwa, ndipo ndikukupitikitsa m’dera limene nthaka+ yake yatsegula pakamwa ndi kulandira magazi a m’bale wako, amene iwe wakhetsa ndi manja ako.+ 12 Uziti ukalima, nthaka sizikubalira mokwanira.+ Udzakhala moyo woyendayenda ndi wothawathawa padziko lapansi.”+ 13 Kaini atamva zimenezi anadandaulira Yehova kuti: “Chilango cha kulakwa kwanga n’chachikulu kwambiri moti sindingathe kuchipirira. 14 Lero ndiye mukundipitikitsa pamalo ano ndi pamaso panu.+ Ndidzakhala woyendayenda+ ndi wothawathawa padziko lapansi, ndipo n’zoonekeratu kuti aliyense wondipeza, adzandipha ndithu.”+ 15 Yehova atamva zimenezi anauza Kaini kuti: “Pa chifukwa chimenechi, aliyense amene adzaphe Kaini adzalangidwa maulendo 7.”+

Choncho Yehova anaikira Kaini chizindikiro kuti aliyense womupeza asamuphe.+ 16 Pamenepo Kaini anachoka pamaso pa Yehova+ n’kupita kukakhala kudera la kum’mawa kwa Edeni monga wothawa.

17 Patapita nthawi, Kaini anagona ndi mkazi wake+ ndipo mkaziyo anatenga pakati n’kubereka Inoki. Ndiyeno Kaini anayamba kumanga mzinda umene anautcha dzina la mwana wake lakuti Inoki.+ 18 Kenako Inoki anabereka Irade, Irade anabereka Mehuyaeli, Mehuyaeli anabereka Metusaeli, ndipo Metusaeli anabereka Lameki.

19 Lameki anakwatira akazi awiri. Woyamba anali Ada ndipo wachiwiri anali Zila. 20 M’kupita kwa nthawi Ada anabereka Yabala, amene anakhala tate wa anthu okhala m’mahema+ ndi oweta ziweto.+ 21 M’bale wake wa Yabala anali Yubala. Ameneyu ndiye anali tate wa onse oimba zeze+ ndi chitoliro.+ 22 Koma Zila anabereka Tubala-kaini, amene anali mmisiri wosula zipangizo zamtundu uliwonse, zamkuwa ndi zachitsulo.+ Ndipo mlongo wake wa Tubala-kaini anali Naama. 23 Kenako Lameki anakonzera akazi ake, Ada ndi Zila ndakatulo iyi:

“Tamverani mawu anga inu akazi a Lameki.

Tcherani khutu ku zonena zanga:

Ndapha munthu chifukwa chondipweteka,

Ndaphadi, mnyamata chifukwa chondimenya.

24 Ngati wopha Kaini ati adzalangidwe maulendo 7,+

Ndiyetu wopha ine Lameki, adzalangidwa maulendo 77.”

25 Adamu anagonanso ndi mkazi wake Hava, ndipo mkaziyo anabereka mwana wamwamuna yemwe anamupatsa dzina lakuti Seti.*+ Hava anapereka dzina limeneli chifukwa chakuti Seti atabadwa, Havayo ananena kuti: “Mulungu wandipatsa* mbewu ina m’malo mwa Abele, popeza iye anaphedwa ndi Kaini.”+ 26 Nayenso Seti anabereka mwana wamwamuna n’kumutcha dzina lakuti Enosi.+ Pa nthawi imeneyi, anthu anayamba kuitanira pa dzina la Yehova.+

5 Tsopano nayi mbiri ya Adamu. M’tsiku limene Mulungu analenga Adamu, anam’panga iye m’chifaniziro cha Mulungu.+ 2 Anawalenga iwo mwamuna ndi mkazi.+ Kenako, anawadalitsa ndi kuwatchula dzina lakuti Anthu,+ m’tsiku limene anawalenga.+

3 Adamu atakhala ndi moyo zaka 130, anabereka mwana wamwamuna m’chifaniziro chake, wofanana naye. Anamutcha dzina lake Seti.+ 4 Adamu atabereka Seti, anakhalabe ndi moyo zaka zina 800. Pa zaka zimenezi, anaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi.+ 5 Chotero, masiku onse amene Adamu anakhala ndi moyo anakwana zaka 930, kenako anamwalira.+

6 Seti atakhala ndi moyo zaka 105, anabereka Enosi.+ 7 Atabereka Enosi, Seti anakhalabe ndi moyo zaka zina 807. Pa zaka zimenezi, anaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi. 8 Chotero, masiku onse a Seti anakwana zaka 912, kenako anamwalira.

9 Enosi atakhala ndi moyo zaka 90, anabereka Kenani.+ 10 Atabereka Kenani, Enosi anakhalabe ndi moyo zaka zina 815. Pa zaka zimenezi, anaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi. 11 Chotero, masiku onse a Enosi anakwana zaka 905, kenako anamwalira.

12 Kenani atakhala ndi moyo zaka 70, anabereka Mahalalele.+ 13 Atabereka Mahalalele, Kenani anakhalabe ndi moyo zaka zina 840. Pa zaka zimenezi, anaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi. 14 Chotero, masiku onse a Kenani anakwana zaka 910, kenako anamwalira.

15 Mahalalele atakhala ndi moyo zaka 65, anabereka Yaredi.+ 16 Atabereka Yaredi, Mahalalele anakhalabe ndi moyo zaka zina 830. Pa zaka zimenezi, anaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi. 17 Chotero, masiku onse a Mahalalele anakwana zaka 895, kenako anamwalira.

18 Yaredi atakhala ndi moyo zaka 162, anabereka Inoki.+ 19 Atabereka Inoki, Yaredi anakhalabe ndi moyo zaka zina 800. Pazaka zimenezi, anaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi. 20 Chotero, masiku onse a Yaredi anakwana zaka 962, kenako anamwalira.

21 Inoki atakhala ndi moyo zaka 65, anabereka Metusela.+ 22 Atabereka Metusela, Inoki anayendabe ndi Mulungu woona kwa zaka 300. Pa zaka zimenezi, anaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi. 23 Chotero, masiku onse a Inoki anakwana zaka 365. 24 Inoki anayendabe+ ndi Mulungu woona.+ Kenako iye sanaonekenso, chifukwa Mulungu anam’tenga.+

25 Metusela atakhala ndi moyo zaka 187, anabereka Lameki.+ 26 Atabereka Lameki, Metusela anakhalabe ndi moyo zaka zina 782. Pa zaka zimenezi, anaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi. 27 Chotero, masiku onse a Metusela anakwana zaka 969, kenako anamwalira.

28 Lameki atakhala ndi moyo zaka 182, anabereka mwana wamwamuna. 29 Mwanayo anamutcha dzina lakuti Nowa,+ ndipo anati: “Uyu ndi amene adzatibweretsere mpumulo ku ntchito yathu yopweteketsa manja, chifukwa cholima nthaka imene Yehova anaitemberera.”+ 30 Atabereka Nowa, Lameki anakhalabe ndi moyo zaka zina 595. Pa zaka zimenezi, anaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi. 31 Chotero masiku onse a Lameki anakwana zaka 777, kenako anamwalira.

32 Nowa anakwanitsa zaka 500. Pambuyo pake iye anabereka Semu,+ Hamu+ ndi Yafeti.+

6 Pamene anthu anayamba kuchuluka padziko lapansi, kunabadwa ana aakazi.+ 2 Ndiyeno ana a Mulungu+ woona anayamba kuona+ kuti ana aakazi a anthu anali okongola. Chotero, anayamba kudzitengera okha akazi alionse amene anawasankha. 3 Pambuyo pake, Yehova anati: “Mzimu wanga+ supitiriza mpaka kalekale kulezera mtima anthu,+ popeza alinso athupi.+ Choncho, masiku a moyo wawo adzangokhala zaka 120.”+

4 M’masiku amenewo ndiponso kupita m’tsogolo, padziko lapansi panali Anefili.* Pa nthawiyo, ana a Mulungu woona anali kugona ndi ana aakazi a anthu ndipo anawaberekera ana. Anawo anali ziphona zakalelo, amuna otchuka.

5 Pamenepo, Yehova anaona kuti kuipa kwa anthu kwachuluka padziko lapansi, ndipo malingaliro+ onse a m’mitima ya anthu anali oipa okhaokha nthawi zonse.+ 6 Chotero, Yehova anamva chisoni+ kuti anapanga anthu padziko lapansi, ndipo zinam’pweteka kwambiri mumtima.+ 7 Choncho Yehova anati: “Ndidzaseseratu padziko lapansi anthu amene ndinawalenga.+ Kuyambira munthu, nyama yoweta, nyama yokwawa, mpaka cholengedwa chouluka m’mlengalenga,+ chifukwa ndikumva chisoni kuti ndinazipanga.”+ 8 Koma Nowa anayanjidwa ndi Yehova.

9 Tsopano nayi mbiri ya Nowa.

Nowa anali munthu wolungama.+ Iye anali wopanda cholakwa pakati pa anthu a m’nthawi yake. Nowa anayenda ndi Mulungu woona.+ 10 M’kupita kwa nthawi, Nowa anabereka ana aamuna atatu, Semu, Hamu ndi Yafeti.+ 11 Koma dziko lapansi linali litaipa pamaso pa Mulungu woona,+ ndipo linadzaza ndi chiwawa.+ 12 Chotero, Mulungu poyang’ana dziko lapansi anaona kuti laipa,+ chifukwa njira za anthu onse zinali zitaipa.+

13 Pambuyo pake, Mulungu anauza Nowa kuti: “Nthawi yafika yakuti ndiwononge anthu onse,+ popeza dziko lapansi ladzaza ndi chiwawa chifukwa cha iwo. Choncho ndiwawonongera limodzi ndi dziko lapansi.+ 14 Udzipangire chingalawa cha mtengo wa mnjale.+ Uchigawe zipindazipinda, ndipo uchimate ndi phula+ mkati ndi kunja komwe. 15 Uchipange motere: M’litali chikhale mikono*+ 300, m’lifupi mikono 50, ndipo kutalika kwake kuyambira pansi mpaka pamwamba chikhale mikono 30. 16 Chingalawacho uchiike windo.* Windolo likhale la mpata wa mkono umodzi kuchokera kudenga* lake. Khomo la chingalawacho uliike m’mbali mwake.+ Chikhale cha nyumba zosanjikiza zitatu, yapansi, yapakati, ndi yapamwamba.

17 “Koma ine ndidzabweretsa chigumula+ chamadzi padziko lapansi, kuti chiwononge chamoyo+ chilichonse cha pansi pa thambo, chimene chili ndi mphamvu ya moyo* m’thupi mwake. Chilichonse cha m’dziko lapansi chidzafa.+ 18 Ndipo ndikupanga pangano ndi iwe. Iweyo udzalowe m’chingalawacho limodzi ndi ana ako, mkazi wako, ndi akazi a ana ako.+ 19 Udzalowetsenso m’chingalawacho chamoyo chilichonse cha mtundu uliwonse.+ Udzazilowetse ziwiriziwiri, champhongo ndi chachikazi, kuti zidzasungike zamoyo limodzi nawe.+ 20 Udzalowe nazo ziwiriziwiri za mtundu uliwonse. Zolengedwa zouluka monga mwa mitundu yawo, nyama zoweta monga mwa mitundu yawo,+ nyama zonse zokwawa panthaka monga mwa mitundu yawo, kuti zidzasungike zamoyo.+ 21 Koma iweyo udzatenge chakudya cha mtundu uliwonse chodyedwa.+ Udzachisonkhanitse kuti chidzakhale chakudya chanu ndi cha zamoyo zinazo.”+

22 Ndipo Nowa anachita zonse motsatira zimene Mulungu anamulamula. Anachitadi momwemo.+

7 Pambuyo pake Yehova anauza Nowa kuti: “Lowa m’chingalawacho, iwe ndi banja lako,+ chifukwa iwe ndi amene ndakuona kuti ndiwe wolungama pakati pa m’badwo uwu.+ 2 Pa nyama zilizonse zosadetsedwa utengepo zokwanira 7, yamphongo ndi yaikazi yake.+ Koma pa nyama zilizonse zodetsedwa utengepo ziwiri zokha, yamphongo ndi yaikazi yake. 3 Pa zolengedwa zilizonse zouluka m’mlengalenga, utengeponso zokwanira 7, chachimuna ndi chachikazi,+ kuti zisungike padziko lonse lapansi.+ 4 Kwangotsala masiku 7 okha kuti ndigwetse chimvula+ padziko lapansi kwa masiku 40, usana ndi usiku.+ Ndipo ndidzaseseratu chamoyo chilichonse padziko lapansi chimene ndinachipanga.”+ 5 Choncho, Nowa anachita zonse motsatira zimene Yehova anamulamula.

6 Pamene chigumula chamadzi chinachitika padziko lapansi, Nowa anali ndi zaka 600.+ 7 Pamenepo Nowa analowa m’chingalawacho, limodzi ndi ana ake aamuna, mkazi wake, ndi akazi a ana ake. Iwo analowamo madzi achigumula asanayambe.+ 8 Nyama zilizonse zosadetsedwa, nyama zilizonse zodetsedwa, zolengedwa zilizonse zouluka, komanso zilizonse zokwawa pansi,+ 9 zinalowa ziwiriziwiri m’chingalawa mmene munali Nowa, yamphongo ndi yaikazi, monga mmene Yehova analamulira Nowa. 10 Ndipo patapita masiku 7, madzi a chigumula anafika padziko lapansi.

11 M’chaka cha 600 cha moyo wa Nowa, m’mwezi wachiwiri,* pa tsiku la 17 la mweziwo, pa tsiku limeneli akasupe onse amadzi akuya* anaphulika ndipo zotsekera madzi akumwamba zinatseguka.+ 12 Ndiyeno chimvula chinakhuthuka padziko lapansi kwa masiku 40 usana ndi usiku.+ 13 Pa tsiku limeneli Nowa analowa m’chingalawacho. Analowa limodzi ndi ana ake, Semu, Hamu ndi Yafeti,+ ndiponso mkazi wake, ndi akazi atatu a ana akewo.+ 14 Iwo analowa pamodzi ndi nyama zakutchire zamtundu uliwonse,+ nyama zoweta zamtundu uliwonse, nyama zokwawa* pansi zamtundu uliwonse,+ zolengedwa zouluka zamtundu uliwonse,+ ndiponso mbalame zilizonse ndi zolengedwa zilizonse zamapiko.+ 15 Zamoyo zamtundu uliwonse, zokhala ndi mphamvu ya moyo+ m’thupi mwawo, zinali kupita ziwiriziwiri m’chingalawa mmene munali Nowa. 16 Zimene zinali kulowazo, zazimuna ndi zazikazi zamtundu uliwonse, zinalowa monga mmene Yehova anamulamulira Nowa. Kenako Yehova anatseka chitseko.+

17 Chigumulacho chinapitirira padziko lapansi kwa masiku 40. Ndipo madzi anachulukirachulukira, moti anayamba kunyamula chingalawacho, mpaka chinali kuyandama pamwamba kwambiri kuchokera padziko lapansi. 18 Madziwo anapitirizabe kuwonjezeka koopsa padziko lapansi, ndipo chingalawachonso chinapitirizabe kuyandama pamwamba pa madzi.+ 19 Madziwo anawonjezeka kwambiri padziko lapansi moti anamiza mapiri onse ataliatali amene anali pansi pa thambo lonse.+ 20 Madziwo anakwera kwambiri kupitirira mapiri ataliataliwo ndi mikono 15.+

21 Chotero zamoyo zonse zoyenda padziko lapansi, monga zolengedwa zouluka, nyama zoweta, nyama zakutchire, ndiponso tizilombo tonse tambirimbiri toyenda padziko lapansi, zinafa+ pamodzi ndi anthu onse.+ 22 Chilichonse chokhala ndi mpweya wa moyo* m’mphuno mwake, kutanthauza zonse zimene zinali pamtunda, zinafa.+ 23 Chotero, Mulungu anaseseratu chamoyo chilichonse chimene chinali padziko lapansi, kuyambira munthu mpaka nyama, zokwawa pansi mpaka zolengedwa zouluka m’mlengalenga, anazisesa zonse padziko lapansi.+ Koma Nowa yekha, pamodzi ndi amene anali naye limodzi m’chingalawacho, anapulumuka.+ 24 Ndipo madzi anamizabe dziko lapansi kwa masiku 150.

8 Pambuyo pake, Mulungu anakumbukira+ Nowa ndi nyama zonse zakutchire, ndiponso nyama zonse zoweta zimene anali nazo m’chingalawa.+ Ndiyeno Mulungu anachititsa chimphepo kuwomba padziko lapansi, ndipo madzi anayamba kuchepa.+ 2 Pamenepo, akasupe a madzi akuya+ ndi zotsekera madzi+ akumwamba zinatsekeka, choncho madzi omwe anali kukhuthuka kuchokera kumwamba anasiya. 3 Komanso madzi anali kuchepa pang’onopang’ono padziko lapansi. Pakutha pa masiku 150, madziwo anali atachepa ndithu.+ 4 M’mwezi wa 7,* pa tsiku la 17 la mweziwo, chingalawacho+ chinaima pamapiri a Ararati.+ 5 Madzi anapitirizabe kuchepa mpaka mwezi wa 10. M’mwezi wa 10 umenewo, pa tsiku loyamba la mweziwo, nsonga za mapiri zinaonekera.+

6 Ndiyeno patatha masiku 40, Nowa anatsegula windo+ la chingalawa limene anaika. 7 Atatero, anatumiza khwangwala,+ koma iye anali kumangouluka kunjako, kupita ndi kubwera kufikira pamene madzi anaphwa padziko lapansi.

8 Kenako, Nowa anatumiza njiwa+ kuti aone ngati madzi anaphwa padziko lapansi. 9 Koma njiwayo sinapeze malo alionse oti n’kuterapo. Chotero, inabwerera kwa iye m’chingalawamo chifukwa madzi anali asanaphwe padziko lonse lapansi.+ Itabwerera, iye anatulutsa dzanja lake, n’kuitenga kuilowetsa m’chingalawamo. 10 Anapitirizabe kudikira masiku ena 7. Kenako, anatumizanso njiwa ija kuchokera m’chingalawamo. 11 Njiwayo inabwerera kwa iye nthawi yamadzulo. Inabwerako ndi tsamba laliwisi kukamwa kwake, longothyoledwa kumene pamtengo wa maolivi.+ Nowa ataona, anadziwa kuti madzi anali ataphwa padziko lapansi.+ 12 Anadikirabe masiku enanso 7. Kenako anaitumizanso njiwa ija, koma sinabwererenso kwa iye.+

13 Tsopano m’chaka+ cha 601 cha Nowa, mwezi woyamba, pa tsiku loyamba la mweziwo, madzi anali ataphwa padziko lapansi. Ndipo Nowa anayang’ana kunja kudzera pachibowo chimene chinali padenga la chingalawacho. Atatero, anaona kuti madzi aphwa panthaka.+ 14 M’mwezi wachiwiri, pa tsiku la 27 la mweziwo, madzi anaphweratu padziko lapansi.+

15 Ndiyeno Mulungu analankhula ndi Nowa, kuti: 16 “Tsopano tulukani m’chingalawamo, iweyo, mkazi wako, ana ako, ndi akazi a ana ako.+ 17 Utuluke limodzi ndi zamoyo zamtundu uliwonse+ zimene uli nazo: Zolengedwa zouluka,+ zinyama+ ndi zonse zokwawa padziko lapansi,+ kuti zibalalike padziko lapansi, ziswane ndi kuchulukana.”+

18 Pamenepo, Nowa anatuluka limodzi ndi ana ake,+ mkazi wake, ndi akazi a ana ake. 19 Komanso, zamoyo zilizonse, nyama zilizonse, zolengedwa zouluka zilizonse, zokwawa zilizonse za padziko lapansi, monga mwa magulu awo, zinatuluka m’chingalawamo.+ 20 Tsopano Nowa anamangira Yehova guwa lansembe.+ Atatero, anatenga zina mwa nyama zonse zoyera,+ ndi zina mwa zouluka zonse zoyera,+ n’kuzipereka nsembe yopsereza paguwapo.+ 21 Ndiyeno Yehova anamva fungo lokhazika mtima pansi,+ moti ananena mumtima+ mwake kuti: “Sindidzatembereranso nthaka+ chifukwa cha zochita za anthu, popeza maganizo+ a anthu amakhala oipa kuyambira pa ubwana wawo.+ Ndipo sindidzawononganso chilichonse monga ndachitiramu.+ 22 Masiku onse amene dziko lapansi lidzakhalapo, kubzala mbewu ndi kukolola sikudzatha. Ndiponso, nyengo yozizira ndi yotentha, chilimwe ndi chisanu, usana ndi usiku, zidzakhalapobe.”+

9 Kenako Mulungu anadalitsa Nowa ndi ana ake, kuti: “Muberekane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi.+ 2 Ndipo cholengedwa chilichonse chamoyo cha padziko lapansi, cholengedwa chilichonse chouluka m’mlengalenga, chilichonse chokwawa padziko lapansi, ndi nsomba zonse za m’nyanja, zizikuopani. Tsopano ndapereka zonsezi m’manja mwanu.+ 3 Nyama yamoyo iliyonse ikhale chakudya chanu.+ Komanso ndikukupatsani zamasamba zonse kuti zikhale chakudya chanu.+ 4 Koma musadye+ nyama pamodzi ndi magazi+ ake, amene ndiwo moyo+ wake. 5 Kuwonjezera pamenepo, ndidzafunsa za magazi anu. Ngati magazi anu akhetsedwa ndi chamoyo chilichonse, chamoyocho chiyenera kuphedwa, ndipo ngati moyo wa munthu wachotsedwa ndi munthu mnzake ndidzaufuna kuchokera kwa iye.+ 6 Aliyense wokhetsa magazi a munthu, nayenso magazi ake adzakhetsedwa ndi munthu,+ chifukwa Mulungu anapanga munthu m’chifaniziro chake. 7 Koma inuyo muberekane, muchuluke, mufalikire padziko lonse lapansi.”+

8 Ndipo Mulungu anauza Nowa ndi ana ake kuti: 9 “Tsopano ine ndikuchita pangano+ ndi inu, ndi ana obadwa pambuyo panu,+ 10 komanso ndi chamoyo chamtundu uliwonse chimene muli nacho limodzi, pakati pa mbalame ndi pakati pa nyama zonse zamoyo za padziko lapansi, kuyambira zonse zotuluka m’chingalawa, kufikira cholengedwa chamoyo chilichonse cha padziko lapansi.+ 11 Pangano limene ndikuchita nanu ndi ili: Zamoyo zonse sizidzawonongedwanso ndi madzi a chigumula, ndipo chigumula sichidzachitikanso n’kuwononga dziko lapansi.”+

12 Mulungu anawonjezera kuti: “Nachi chizindikiro+ cha pangano limene ndikuika pakati pa inu ndi ine, ndi pakati pa chamoyo chilichonse chimene muli nacho limodzi, ku mibadwomibadwo mpaka kalekale. 13 Ndiika utawaleza+ mumtambo, kuti ukhale chizindikiro cha pangano pakati pa ine ndi dziko lapansi. 14 Ndikabweretsa mtambo padziko lapansi, utawaleza udzaonekeranso mumtambowo. 15 Ndipo ndizikumbukira ndithu pangano+ la pakati pa ine ndi inu ndi chamoyo chilichonse.+ Komanso madzi sadzachitanso chigumula ndi kuwononga zamoyo zonse.+ 16 Utawalezawo uzionekera mumtambo.+ Ndipo ine ndiziuona ndithu, n’kukumbukira pangano limene lidzakhale mpaka kalekale,+ la pakati pa ine ndi chamoyo chilichonse chimene chili padziko lapansi.”+

17 Kenako Mulungu anabwereza kuuza Nowa kuti: “Ichi ndi chizindikiro cha pangano limene ndikukhazikitsa pakati pa ine ndi zamoyo zonse zimene zili padziko lapansi.”+

18 Ana a Nowa+ amene anatuluka m’chingalawa anali Semu, Hamu ndi Yafeti. Pambuyo pake, Hamu anakhala tate wake wa Kanani.+ 19 Atatuwa ndiwo anali ana a Nowa. Ndipo anthu onse amene ali padziko lapansi anachokera mwa iwowa.+

20 Tsopano Nowa anakhala mlimi,+ ndipo analima munda wa mpesa.+ 21 Pambuyo pake, iye anamwa vinyo ndi kuledzera naye.+ Kenako, ali m’hema wake, anavula zovala zake. 22 Ndiyeno Hamu,+ bambo wake wa Kanani, anaona maliseche a bambo ake.+ Atatero, anapita panja n’kukauza abale ake awiri aja zimenezo.+ 23 Atamva zimenezo, Semu ndi Yafeti anatenga chofunda+ atachigwirira pa mapewa pawo, n’kuyenda chafutambuyo. Atatero, anafunditsa bambo awo iwo akuyang’ana kumbali, kuwabisa maliseche, moti sanaone maliseche a bambo awo.+

24 Kenako, Nowa anagalamuka vinyo atamuthera m’mutu mwake, ndipo anamva zimene mwana wake wamng’ono anachita kwa iye. 25 Pamenepo iye anati:

“Ndikutemberera Kanani.+

Akhale kapolo wapansi kwambiri kwa abale ake.”+

26 Anawonjezera kuti:

“Adalitsike Yehova,+ Mulungu wa Semu,

Ndipo Kanani akhale kapolo kwa iye.+

27 Mulungu apereke malo aakulu kwa Yafeti,

Ndipo azikhala m’mahema a Semu.+

Koma Kanani akhalenso kapolo wa Yafeti.”

28 Pambuyo pa chigumula,+ Nowa anakhalabe ndi moyo zaka zina 350. 29 Chotero, masiku onse a Nowa anakwana zaka 950, kenako anamwalira.+

10 Tsopano nayi mbiri ya ana a Nowa,+ omwe ndi Semu, Hamu ndi Yafeti.

Pambuyo pa chigumula, iwowa anayamba kubereka ana.+ 2 Ana a Yafeti anali Gomeri,+ Magogi,+ Madai,+ Yavani,+ Tubala,+ Meseke+ ndi Tirasi.+

3 Ana a Gomeri anali Asikenazi,+ Rifati+ ndi Togarima.+

4 Ana a Yavani anali Elisaha,+ Tarisi,+ Kitimu+ ndi Dodanimu.+

5 Kuchokera mwa amenewa, anthu anafalikira m’zilumba* m’madera awo malinga ndi zilankhulo zawo, mabanja awo ndi mitundu yawo.

6 Ana a Hamu anali Kusi,+ Miziraimu,+ Puti+ ndi Kanani.+

7 Ana a Kusi anali Seba,+ Havila, Sabita, Raama+ ndi Sabiteka.

Ana a Raama anali Sheba ndi Dedani.+

8 Kusi anabereka Nimurodi,+ amene anali woyamba kukhala wamphamvu padziko lapansi. 9 Iye anakhala mlenje wamphamvu wotsutsana ndi Yehova. N’chifukwa chake pali mawu akuti: “Monga Nimurodi mlenje wamphamvu wotsutsana ndi Yehova.”+ 10 Ufumu wake unayambira ku Babele,+ Ereke,+ Akadi mpaka ku Kaline m’dziko la Sinara.+ 11 Kuchokera m’dzikoli analowera ku Asuri+ kumene anamanga Nineve,+ Rehoboti-iri, Kala, 12 komanso Resene wa pakati pa Nineve ndi Kala. Umenewu unali mzinda waukulu.

13 Miziraimu+ anabereka Ludimu,+ Anamimu, Lehabimu, Nafituhimu,+ 14 Patirusimu+ ndi Kasiluhimu+ (Afilisiti+ anachokera mwa iyeyu), ndiponso Kafitorimu.+

15 Kanani anabereka Sidoni+ mwana wake woyamba, kenako anabereka Heti.+ 16 Anaberekanso Ayebusi,+ Aamori,+ Agirigasi, 17 Ahivi,+ Aariki, Asini, 18 Aarivadi,+ Azemari ndi Ahamati,+ ndipo pambuyo pake, mabanja a Akanani anabalalikana. 19 Choncho malire a dziko la Akanani anachokera ku Sidoni mpaka ku Gerari+ kufupi ndi Gaza,+ n’kukafika ku Sodomu ndi Gomora+ mpakanso ku Adima+ ndi Zeboyimu,+ kufupi ndi Lasa. 20 Amenewa ndiwo anali ana a Hamu monga mwa mabanja awo, monga mwa zilankhulo zawo, m’mayiko awo, mwa mitundu yawo.

21 Nayenso Semu, kholo la ana onse a Ebere,+ anali ndi mbadwa zake. Semu anali mng’ono wake wa Yafeti, amene anali wamkulu pa onse. 22 Ana a Semu anali Elamu,+ Ashuri,+ Aripakisadi,+ Ludi ndi Aramu.

23 Ana a Aramu anali Uzi, Huli, Geteri ndi Masi.+

24 Aripakisadi anabereka Shela+ ndipo Shela anabereka Ebere.

25 Ebere anabereka ana awiri. Wina dzina lake anali Pelegi,*+ chifukwa m’masiku ake, dziko lapansi linagawikana.+ M’bale wakeyo dzina lake anali Yokitani.+

26 Yokitani anabereka Alamodadi, Selefi, Hazaramaveti, Yera,+ 27 Hadoramu, Uzali, Dikila,+ 28 Obali, Abimaele, Sheba,+ 29 Ofiri,+ Havila+ ndi Yobabi.+ Onsewa anali ana a Yokitani.

30 Dziko lawo limene anali kukhala linayambira ku Mesa mpaka ku Sefara, dera lamapiri la Kum’mawa.

31 Amenewa ndiwo ana a Semu monga mwa mabanja awo, zilankhulo zawo, m’mayiko awo, monga mwa mitundu yawo.+

32 Amenewa ndiwo mabanja a ana a Nowa monga mwa mibadwo yawo, monganso mwa mitundu yawo. Ndipo kuchokera mwa iwowa, mitundu inafalikira padziko lapansi pambuyo pa chigumula.+

11 Tsopano dziko lonse lapansi linali ndi chilankhulo chimodzi ndipo anthu anali kugwiritsa ntchito mawu ofanana. 2 Pamene anthuwo analowera chakum’mawa, anapeza chigwa m’dera la Sinara+ n’kukhazikika kumeneko. 3 Kenako anauzana kuti: “Tiyeni tiumbe njerwa tiziotche.” Atatero, anayamba kumanga ndi njerwa, n’kumagwiritsa ntchito phula ngati matope omangira.+ 4 Ndiyeno anati: “Tiyeni timange mzinda wathuwathu, ndipo nsanja yake ikafike m’mwamba mwenimweni.+ Tikatero tidzipangira dzina loti titchuke nalo,+ ndipo sitibalalikana padziko lonse lapansi.”+

5 Kenako, Yehova anatsikirako kukaona mzinda ndi nsanja imene ana a anthu anali kumanga.+ 6 Pamenepo Yehova anati: “Taonani! Izi n’zimene anthuwa ayamba kuchita popeza ndi amodzi ndipo onse ali ndi chilankhulo chimodzi.+ Mmene zililimu, angathe kuchita chilichonse chimene akuganiza.+ 7 Choncho, tiyeni+ tipiteko kuti tikasokoneze+ chilankhulo chawo, kuti asamamvane polankhula.”+ 8 Motero, Yehova anawabalalitsa pamalopo, kuti afalikire padziko lonse lapansi.+ Zitatero, iwo anasiya pang’onopang’ono kumanga mzindawo.+ 9 Mzindawo unatchedwa Babele,+ chifukwa kumeneko, Yehova anasokoneza chilankhulo cha anthu onse, ndipo Yehova anabalalitsira+ anthuwo padziko lonse lapansi.

10 Tsopano iyi ndi mbiri ya Semu.+

Semu anali ndi zaka 100 pamene anabereka Aripakisadi,+ patapita zaka ziwiri pambuyo pa chigumula. 11 Atabereka Aripakisadi, Semu anakhalabe ndi moyo zaka zina 500. Pa zaka zimenezi, anabereka ana aamuna ndi aakazi.+

12 Aripakisadi atakhala ndi moyo zaka 35, anabereka Shela.+ 13 Atabereka Shela, Aripakisadi anakhalabe ndi moyo zaka zina 403. Pa zaka zimenezi, anabereka ana aamuna ndi aakazi.

14 Shela atakhala ndi moyo zaka 30, anabereka Ebere.+ 15 Atabereka Ebere, Shela anakhalabe ndi moyo zaka zina 403. Pa zaka zimenezi, anabereka ana aamuna ndi aakazi.

16 Ebere atakhala ndi moyo zaka 34, anabereka Pelegi.+ 17 Atabereka Pelegi, Ebere anakhalabe ndi moyo zaka zina 430. Pa zaka zimenezi, anabereka ana aamuna ndi aakazi.

18 Pelegi atakhala ndi moyo zaka 30, anabereka Reu.+ 19 Atabereka Reu, Pelegi anakhalabe ndi moyo zaka zina 209. Pa zaka zimenezi, anabereka ana aamuna ndi aakazi.

20 Reu atakhala ndi moyo zaka 32, anabereka Serugi.+ 21 Atabereka Serugi, Reu anakhalabe ndi moyo zaka zina 207. Pa zaka zimenezi, anabereka ana aamuna ndi aakazi.

22 Serugi atakhala ndi moyo zaka 30, anabereka Nahori.+ 23 Atabereka Nahori, Serugi anakhalabe ndi moyo zaka zina 200. Pa zaka zimenezi, anabereka ana aamuna ndi aakazi.

24 Nahori atakhala ndi moyo zaka 29, anabereka Tera.+ 25 Atabereka Tera, Nahori anakhalabe ndi moyo zaka zina 119. Pa zaka zimenezi, anabereka ana aamuna ndi aakazi.

26 Tera anakhala ndi moyo zaka 70, kenako anabereka Abulamu,+ Nahori+ ndi Harana.

27 Tsopano iyi ndi mbiri ya Tera.

Tera anabereka Abulamu, Nahori ndi Harana. Harana anabereka Loti.+ 28 Pambuyo pake Harana anamwalira mumzinda wa Akasidi+ wa Uri,+ kumene anabadwira. Anamwalira bambo ake Tera adakali ndi moyo. 29 Abulamu ndi Nahori anakwatira. Mkazi wa Abulamu anali Sarai,+ pamene mkazi wa Nahori anali Milika,+ mwana wa Harana. Harana ameneyu analinso bambo ake a Yisika. 30 Koma Sarai anali wosabereka,+ choncho analibe mwana.

31 Pambuyo pake Tera anatenga mwana wake Abulamu, mdzukulu wake+ Loti mwana wa Harana, Sarai+ mpongozi wake, mkazi wa mwana wake Abulamu, ndi kunyamuka kuchoka mumzinda wa Akasidi wa Uri, kupita kudziko la Kanani.+ Kenako, anafika ku Harana+ ndipo anakhala kumeneko. 32 Choncho masiku a Tera anakwana zaka 205. Kenako, iye anamwalira ku Harana.

12 Tsopano Yehova anauza Abulamu kuti: “Tuluka m’dziko lako, pakati pa abale ako, ndi kusiya nyumba ya bambo ako. Upite kudziko limene ndidzakusonyeza.+ 2 Ine ndidzatulutsa mtundu waukulu mwa iwe. Ndidzakudalitsa ndi kukuza dzina lako, ndipo iwe ukhale dalitso+ kwa ena. 3 Odalitsa iwe ndidzawadalitsa, ndipo otemberera iwe ndidzawatemberera.+ Mabanja onse a padziko lapansi adzapeza madalitso* chifukwa cha iwe.”+

4 Pamenepo, Abulamu ananyamuka malinga ndi mmene Yehova anamuuzira, ndipo Loti ananyamuka naye limodzi. Pochoka ku Harana,+ Abulamu anali ndi zaka 75. 5 Iye anatenga mkazi wake Sarai,+ Loti mwana wa m’bale wake,+ ndi chuma chawo chonse,+ komanso akapolo awo onse amene anapeza kudziko la Harana. Iwo ananyamuka ulendo wopita kudziko la Kanani.+ Potsirizira pake anafika ku Kanani. 6 Tsopano Abulamu anayenda m’dzikomo mpaka kukafika ku Sekemu,+ pafupi ndi mitengo ikuluikulu ya More.+ Pa nthawiyo n’kuti m’dzikomo muli Akanani. 7 Ndiyeno Yehova anaonekera kwa Abulamu n’kumuuza kuti: “Ndidzapereka dziko ili+ kwa mbewu yako.”+ Pambuyo pake, iye anamanga pamalopo guwa lansembe la Yehova, yemwe anaonekera kwa iye. 8 M’kupita kwa nthawi, anasamuka pamalopo n’kupita kudera lamapiri, kum’mawa kwa Beteli.+ Kumeneko iye anamanga hema wake. Beteli anali kumadzulo kwake ndipo Ai+ anali kum’mawa kwake. Kenako anamangira Yehova guwa lansembe,+ n’kuyamba kuitana pa dzina la Yehova.+ 9 Pambuyo pake, Abulamu anasamutsa hema wake kumeneko. Kuyambira pa nthawi imeneyi, iye ankangokhalira kumanga ndi kusamutsa msasa, kulowera ku Negebu.+

10 Tsopano m’dzikomo munagwa njala, ndipo Abulamu ananyamuka kulowera ku Iguputo kukakhala kumeneko monga mlendo.+ Anatero chifukwa njalayo inafika poipa kwambiri m’dzikomo.+ 11 Ali pafupi kulowa mu Iguputo, anauza mkazi wake Sarai kuti: “Ndikudziwa ndithu kuti ndiwe mkazi wokongola m’maonekedwe ako.+ 12 Aiguputo akakuona, mosakayikira anena kuti, ‘Ameneyu ndi mkazi wake.’ Ndipo andipha ndithu, koma iweyo akusiya wamoyo. 13 Ndiye chonde, unene kuti ndiwe mlongo wanga+ kuti zindiyendere bwino. Ukatero upulumutsa moyo wanga.”+

14 Choncho zinachitikadi kuti, Abulamu atangolowa mu Iguputo, Aiguputo anaona kuti mkaziyo anali wokongola kwambiri. 15 Nawonso akalonga a Farao anamuona, ndipo anayamba kum’tamanda kwa Farao, moti anatenga mkaziyo n’kupita naye kunyumba kwa Farao. 16 Farao anamusamalira bwino Abulamu chifukwa cha mkazi wake, moti anamupatsa nkhosa, ng’ombe ndi abulu. Anamupatsanso antchito aamuna ndi aakazi, komanso abulu aakazi ndi ngamila.+ 17 Ndiyeno, Yehova anagwetsera Farao ndi banja lake miliri yoopsa+ chifukwa cha Sarai, mkazi wa Abulamu.+ 18 Farao ataona zimenezi anaitana Abulamu, n’kumufunsa kuti: “N’chiyani wandichitachi? N’chifukwa chiyani sunandiuze kuti ndi mkazi wako?+ 19 N’chifukwa chiyani unanena kuti, ‘Ndi mlongo wanga,’+ moti ndinatsala pang’ono kumutenga kukhala mkazi wanga? Nayu tsopano mkazi wako. Mutenge uzipita!” 20 Pamenepo Farao analamula anyamata ake kuti aperekeze Abulamu ndi mkazi wake, limodzi ndi zonse zimene anali nazo.+

13 Chotero Abulamu anachoka ku Iguputo, iye ndi mkazi wake ndi zonse zimene anali nazo, limodzinso ndi Loti, n’kulowera ku Negebu.+ 2 Abulamu anali ndi chuma chambiri. Anali ndi ziweto, siliva ndi golide.+ 3 Kenako Abulamu anachoka ku Negebu. Anali kumanga misasa ndi kusamuka mpaka kukafika ku Beteli, kumene kunali hema wake poyamba, pakati pa Beteli ndi Ai.+ 4 Kumeneko n’kumene anamangako guwa lansembe poyamba paja.+ Abulamu atafika kumeneko, anayamba kuitana pa dzina la Yehova.+

5 Loti, yemwe anali limodzi ndi Abulamu, nayenso anali ndi nkhosa, ng’ombe ndi mahema. 6 Choncho, chifukwa chokhala ndi katundu wambiri, malo anawachepera moti sakanatha kukhala limodzi.+ 7 Kenako panabuka mkangano pakati pa abusa a Abulamu ndi abusa a Loti. Pa nthawiyo, n’kuti Akanani ndi Aperizi akukhala m’dzikomo.+ 8 Chotero Abulamu anauza Loti+ kuti: “Chonde, pasakhale mkangano uliwonse pakati pa ine ndi iwe, ndi pakati pa abusa anga ndi abusa ako, pajatu ndife pachibale.+ 9 Tiye tipatukane. Ukhoza kutenga mbali iliyonse ya dzikoli. Iwe ukapita kumanzere, ine ndipita kumanja, koma iwe ukapita kumanja, ine ndipita kumanzere.”+ 10 Choncho, Loti anakweza maso ake n’kuona Chigawo* chonse cha Yorodano+ mpaka kukafika ku Zowari,+ ndipo anaona kuti chinali chigawo chobiriwira bwino. Chinali chobiriwira bwino kwambiri ngati mmene unalili munda wa Yehova+ komanso ngati mmene linalili dziko la Iguputo. Pa nthawiyi n’kuti Yehova asanawononge Sodomu ndi Gomora. 11 Pamenepo, Loti anasankha Chigawo chonse cha Yorodano, ndipo anasamutsira msasa wake kum’mawa. Motero iwo anapatukana. 12 Abulamu anakakhala kudziko la Kanani, koma Loti anakakhala pakati pa mizinda ya m’Chigawocho.+ Potsirizira pake, anakamanga hema wake pafupi ndi Sodomu. 13 Koma anthu a ku Sodomu anali oipa, ndipo anali ochimwa kwambiri pamaso pa Yehova.+

14 Abulamu atapatukana ndi Loti, Yehova anamuuza kuti: “Takweza maso ako kuchokera pamene ulipo. Uyang’ane kumpoto ndi kum’mwera, komanso kum’mawa ndi kumadzulo.+ 15 Dziko lonse limene ukulionali, ndidzalipereka kwa iwe ndi kwa mbewu yako, kuti likhale lanu mpaka kalekale.+ 16 Ndidzachulukitsa mbewu yako ngati mchenga wa padziko lapansi, kotero kuti ngati munthu angathe kuwerenga mchengawo, ndiye kuti mbewu yako idzatha kuwerengedwa.+ 17 Nyamuka, uyendere dziko lonselo, m’litali mwake ndi m’lifupi mwake, chifukwa ndidzalipereka kwa iwe.”+ 18 Choncho Abulamu anapitiriza kukhala m’mahema. M’kupita kwa nthawi, anakakhala pakati pa mitengo ikuluikulu ya ku Mamure,+ ku Heburoni.+ Kumeneko, anamangira Yehova guwa lansembe.+

14 Tsopano m’masiku a Amarafele mfumu ya ku Sinara,+ Arioki mfumu ya ku Elasara, Kedorelaomere+ mfumu ya ku Elamu,+ ndi Tidala mfumu ya ku Goimu,+ 2 mafumuwa anachita nkhondo ndi mafumu otsatirawa: Bera mfumu ya ku Sodomu,+ Birisa mfumu ya ku Gomora,+ Sinabi mfumu ya ku Adima,+ Semebere mfumu ya ku Zeboyimu,+ ndi mfumu ya ku Bela (kapena kuti ku Zowari).+ 3 Onsewa anagwirizana+ ndi kutsetserekera limodzi kuchigwa cha Sidimu,+ ku Nyanja Yamchere.+

4 Iwowa, anatumikira Kedorelaomere kwa zaka 12, koma m’chaka cha 13 anamupandukira. 5 M’chaka cha 14, Kedorelaomere anabwera limodzi ndi mafumu omwe anali naye. Iwo anagonjetsa Arefai ku Asiteroti-karanaimu,+ Azuzi ku Hamu, Aemi+ ku Save-kiriyataimu, 6 ndi Ahori+ kuphiri lawo la Seiri,+ mpaka kukafika ku Eli-parana,+ kuchipululu. 7 Kenako anatembenuka n’kulowera ku Eni-misipati, kumene ndi ku Kadesi,+ ndipo anagonjetsa dera lonse la Aamaleki,+ ndiponso Aamori+ omwe anali kukhala ku Hazazoni-tamara.+

8 Pa nthawi imeneyi, mfumu ya ku Sodomu, mfumu ya ku Gomora, mfumu ya ku Adima, mfumu ya ku Zeboyimu, ndi mfumu ya ku Bela (kapena kuti ku Zowari), ananyamuka n’kutsetserekera kuchigwa cha Sidimu.+ Kumeneko, iwo anafola mwa dongosolo lomenyera nkhondo kuti amenyane ndi 9 Kedorelaomere mfumu ya ku Elamu, Tidala mfumu ya ku Goimu, Amarafele mfumu ya ku Sinara, ndi Arioki mfumu ya ku Elasara.+ Panali mafumu anayi amene analimbana ndi mafumu asanu. 10 Kenako, mafumu a Sodomu ndi Gomora+ anayamba kuthawa. Koma chigwa cha Sidimu+ chinali ndi maenje aphula+ ambirimbiri, choncho iwo pothawa anali kugwera m’maenje amenewo. Amene anatsala anathawira kudera lamapiri.+ 11 Ndiyeno, ogonjetsawo anafunkha katundu yense wa ku Sodomu ndi Gomora, limodzi ndi chakudya chonse, n’kumapita.+ 12 Anatenganso Loti mwana wa m’bale wake wa Abulamu, ndi katundu wake, n’kupitiriza ulendo wawo. Pa nthawiyo n’kuti Loti akukhala ku Sodomu.+

13 Pambuyo pake, munthu wina amene anathawa anafika kwa Abulamu Mheberi.+ Pa nthawiyo n’kuti Abulamu akukhala m’hema wake pakati pa mitengo ikuluikulu. Mitengoyo mwiniwake anali Mamure, yemwe anali Muamori.+ Ameneyu anali m’bale wake wa Esikolo, ndipo analinso m’bale wake wa Aneri.+ Iwowa anapanga ubale ndi Abulamu. 14 Chotero Abulamu anamva kuti m’bale wake wagwidwa+ ndipo akupita naye kudziko lina. Atamva zimenezo iye anasonkhanitsa anyamata ake odziwa kumenya nkhondo.+ Anali akapolo ake okwanira 318, obadwira m’nyumba yake.+ Iwo analondola oukirawo mpaka ku Dani.+ 15 Usiku iye anagawa m’magulu asilikali akewo,+ omwe anali akapolo ake, kuti amenyane ndi adaniwo. Ndipo anawagonjetsa, moti anawapitikitsa mpaka ku Hoba, kumpoto kwa Damasiko. 16 Atatero anapulumutsa katundu wawo yense.+ Anapulumutsanso Loti m’bale wake, katundu wake, akazi, ndi anthu ena.+

17 Ndiyeno, mfumu ya ku Sodomu inapita kuchigwa cha Save, kapena kuti chigwa cha mfumu.+ Inapita kukakumana ndi Abulamu, pamene anali kubwera kuchokera kumene anakagonjetsa Kedorelaomere, limodzi ndi mafumu amene anali naye. 18 Ndipo Melekizedeki,+ mfumu ya ku Salemu,+ anabweretsa mkate ndi vinyo.+ Iyeyu anali wansembe wa Mulungu Wam’mwambamwamba.+ 19 Kenako anadalitsa Abulamu kuti:

“Mulungu Wam’mwambamwamba adalitse Abulamu,+

Iye amene anapanga kumwamba ndi dziko lapansi.+

20 Ndipo adalitsike Mulungu Wam’mwambamwamba,+

Amene wapereka okupondereza m’manja mwako!”+

Pamenepo, Abulamu anamupatsa iye chakhumi cha zilizonse.+

21 Kenako mfumu ya ku Sodomu inauza Abulamu kuti: “Mungondipatsako anthu okhawo,+ koma katunduyo mutenge.” 22 Koma Abulamu anauza mfumu ya ku Sodomuyo kuti: “Ndikukweza manja anga kulumbira+ kwa Yehova Mulungu Wam’mwambamwamba, Amene anapanga kumwamba ndi dziko lapansi. 23 Ndikulumbira kuti pa zinthu zako sinditengapo kanthu n’kamodzi komwe,+ kaya kakhale kaulusi kapena kachingwe komangira nsapato. Ayi sinditero, kuti usadzati, ‘Ndine ndinamulemeretsa Abulamu.’ 24 Ineyo sinditengapo chilichonse ayi,+ koma zokhazo zimene anyamata anadya, komanso zogawira anyamata amene anapita nane. Amenewo ndi Aneri, Esikolo ndi Mamure.+ Aliyense atenge gawo lake.”+

15 Ndiyeno zimenezi zitachitika, Yehova analankhula ndi Abulamu m’masomphenya,+ kuti: “Usaope+ Abulamu. Ine ndine chishango chako.+ Mphoto yako idzakhala yaikulu kwambiri.”+ 2 Abulamu atamva zimenezi anati: “Yehova Ambuye Wamkulu Koposa, mudzandipatsa chiyani ine? Taonani ndilibe mwana ndipo amene adzakhale wolowa nyumba yanga ndi munthu wa ku Damasiko, Eliezere.”+ 3 Ananenanso kuti: “Simunandipatse mbewu+ ndipo mtumiki wanga+ ndiye adzakhale wolowa nyumba yanga.” 4 Pamenepo Yehova anamuuza kuti: “Munthu ameneyu sadzakhala wolowa nyumba yako ayi, koma munthu amene adzatuluke mwa iwe ndi amene adzakhale wolowa nyumba yako.”+

5 Kenako anamutengera panja, n’kumuuza kuti: “Kweza maso ako kumwamba, uwerenge nyenyezizo ngati ungathe kuziwerenga.”+ Ndipo anamuuzanso kuti: “Umu ndi mmene mbewu yako idzakhalire.”+ 6 Pamenepo iye anakhulupirira mwa Yehova,+ ndipo Mulunguyo anamuona Abulamu ngati wolungama.+ 7 Anamuuzanso kuti: “Ine ndine Yehova, amene ndinakuchotsa ku Uri wa kwa Akasidi, kudzakupatsa dzikoli kuti likhale lako.”+ 8 Ndipo iye anayankha kuti: “Yehova Ambuye Wamkulu Koposa, nditsimikiza ndi chiyani kuti dzikoli ndidzalitengadi kukhala langa?”+ 9 Pamenepo iye anauza Abulamu kuti: “Unditengere ng’ombe ya zaka zitatu yomwe sinaberekepo, mbuzi yaikazi ya zaka zitatu, nkhosa yamphongo ya zaka zitatu, ndiponso njiwa yaing’ono ndi mwana wa nkhunda.”+ 10 Choncho iye anatenga zonsezi n’kuzidula pakati n’kuika mbali imodzi moyang’anana ndi inzake, koma mbalamezo sanazidule.+ 11 Ndipo mbalame zodya nyama zinayamba kutera pa nyama zophedwazo.+ Koma Abulamu anali kuziingitsa.

12 Patapita nthawi, dzuwa lili pafupi kulowa, Abulamu anagona tulo tofa nato.+ Pamenepo mdima woopsa wandiweyani unayamba kufika pa iye. 13 Kenako Mulungu anauza Abulamu kuti: “Udziwe ndithu kuti mbewu yako idzakhala mlendo m’dziko la eni,+ ndipo idzatumikira eni dzikolo. Iwo adzasautsa mbewu yako kwa zaka 400.+ 14 Koma mtundu umene adzautumikirewo ndidzauweruza.+ Pambuyo pake, iwo adzachokako ndi katundu wochuluka.+ 15 Kunena za iweyo, udzatsikira kwa makolo ako mu mtendere. Udzaikidwa m’manda uli wokalamba, utakhala ndi moyo wabwino ndi wautali.+ 16 Koma m’badwo wachinayi udzabwerera kuno,+ chifukwa nthawi yoti Aamori alangidwe sinakwane.”+

17 Tsopano dzuwa linali kulowa, ndipo kunayamba kugwa chimdima. Pamenepo, ng’anjo yofuka ndiponso muuni wamoto zinadutsa pakati pa nyama zodulidwazo.+ 18 Pa tsiku limeneli Yehova anachita pangano ndi Abulamu,+ kuti: “Dziko ili ndidzalipereka kwa mbewu yako,+ kuyambira kumtsinje wa ku Iguputo mpaka kumtsinje waukulu, mtsinje wa Firate.+ 19 Ndidzapereka kwa mbewu yako dziko la Akeni,+ Akenizi, Akadimoni, 20 Ahiti,+ Aperezi,+ Arefai,+ 21 Aamori, Akanani, Agirigasi ndi la Ayebusi.”+

16 Tsopano Sarai, mkazi wa Abulamu, sanamuberekere ana.+ Koma Saraiyo anali ndi kapolo wake Mwiguputo, dzina lake Hagara.+ 2 Choncho Sarai anauza Abulamu kuti: “Yehova ananditseka kuti ndisabereke ana.+ Tsopano gonani ndi kapolo wanga. Mwinatu ndingapeze ana kuchokera kwa iye.”+ Chotero Abulamu anamvera mawu a Sarai.+ 3 Pamenepo Sarai mkazi wa Abulamu anapereka Hagara, kapolo wake Mwiguputo, kwa mwamuna wake Abulamu kuti akhale mkazi wake.+ Zimenezi zinachitika Abulamu atakhala zaka 10 m’dziko la Kanani. 4 Chotero Abulamu anagona ndi Hagara ndipo Hagara anatenga pakati. Hagara atazindikira kuti ali ndi pakati, anayamba kuchitira chipongwe mbuye wake Sarai.+

5 Sarai ataona zimenezi anauza Abulamu kuti: “Mlandu wa chipongwe chikundichitikirachi ukhale pa inu. Ine ndinapereka kapolo wanga kwa inu kuti akhale mkazi wanu, koma iye poona kuti watenga pakati wayamba kundichitira chipongwe. Yehova aweruze pakati pa ine ndi inu.”+ 6 Poyankha, Abulamu anauza Sarai+ kuti: “Kapolo wakoyutu ali m’manja mwako. Chita chimene ukuchiona kuti n’chabwino.”+ Pamenepo Sarai anayamba kuzunza Hagara, mpaka Hagarayo anathawa kwa Sarai.+

7 Pambuyo pake, mngelo wa Yehova+ anakapeza Hagara m’chipululu ali pakasupe wamadzi wa panjira yopita ku Shura.+ 8 Ndiyeno mngeloyo anati: “Hagara kapolo wa Sarai, kodi ukuchokera kuti ndipo ukupita kuti?” Iye anayankha kuti: “Ndikuthawa kwa mbuye wanga Sarai.” 9 Mngelo wa Yehovayo anauza Hagara kuti: “Bwerera kwa mbuye wako ndipo ukadzichepetse kwa iye.”+ 10 Kenako mngelo wa Yehovayo anamuuzanso kuti: “Ndidzachulukitsa kwambiri mbewu yako,+ moti idzakhala yosawerengeka.”+ 11 Mngelo wa Yehovayo anapitiriza kulankhula ndi mkaziyo kuti: “Taona, panopo uli ndi pakati, ndipo udzabereka mwana wamwamuna. Mwanayo udzamutche Isimaeli,+ pakuti Yehova wamva kulira kwako.+ 12 Mwanayo adzakhala ngati mbidzi. Dzanja lake lidzalimbana ndi aliyense, ndipo dzanja la aliyense lidzalimbana naye.+ Iye adzamanga msasa pamaso pa abale ake onse.”+

13 Ndiyeno Hagara anayamba kutchula dzina la Yehova n’kunena kuti: “Inu ndinu Mulungu amene amaona chilichonse.”*+ Anatinso: “Kodi nanenso pano ndaona wotha kundionayo?” 14 Chimenechi ndicho chifukwa chake chitsimecho chinatchedwa Beere-lahai-roi,*+ ndipo chili pakati pa Kadesi ndi Beredi. 15 M’kupita kwa nthawi, Hagara anaberekera Abulamu mwana wamwamuna ndipo Abulamu anatcha mwanayo dzina lakuti Isimaeli.+ 16 Pamene Hagara anaberekera Abulamu Isimaeli, Abulamuyo n’kuti ali ndi zaka 86.

17 Pamene Abulamu anali ndi zaka 99, Yehova anaonekera kwa iye n’kumuuza kuti:+ “Ine ndine Mulungu Wamphamvuyonse.+ Yenda pamaso panga ndipo ukhale wolungama.+ 2 Ndidzakhazikitsa pangano langa pakati pa ine ndi iwe,+ pangano lakuti ndidzachulukitsa kwambiri mbadwa zako.”+

3 Abulamu atamva zimenezi anagwada n’kuwerama mpaka nkhope yake pansi.+ Kenako Mulungu anapitiriza kulankhula naye kuti: 4 “Ine ndinachita pangano ndi iwe,+ ndipo iwe udzakhaladi tate wa mitundu yambiri.+ 5 Tsopano dzina lako silikhalanso Abulamu, m’malo mwake likhala Abulahamu, chifukwa ndidzakupangitsa kukhala tate wa mitundu yambiri. 6 Ndidzakupatsa ana ambiri zedi, ndipo mwa iwe mudzatuluka mitundu ndi mafumu.+

7 “Ndidzakwaniritsa pangano langa la pakati pa ine ndi iwe,+ ndi mbewu yako yobwera pambuyo pa iwe ku mibadwomibadwo. Lidzakhala pangano mpaka kalekale,+ kusonyeza kuti ndine Mulungu wako ndi wa mbewu yako yobwera pambuyo pa iwe.+ 8 Dziko limene ukukhalamo ngati mlendoli,+ ndidzalipereka kwa iwe ndi mbewu yako yobwera pambuyo pako. Dziko lonse la Kanani lidzakhala lawo mpaka kalekale, ndipo ine ndidzakhala Mulungu wawo.”+

9 Mulungu anapitiriza kumuuza Abulahamu kuti: “Koma iwe usunge pangano langa, iwe ndi mbewu yobwera pambuyo pako ku mibadwo yawo yonse.+ 10 Ili ndi pangano limene anthu inu muyenera kulisunga, la pakati pa ine ndi inu, ngakhalenso mbewu yobwera pambuyo pa inu.+ Mwamuna aliyense pakati pa inu azidulidwa.+ 11 Muzichita mdulidwe kuti ukhale chizindikiro cha pangano la pakati pa ine ndi inu.+ 12 Mwana aliyense wamwamuna amene wakwanitsa masiku 8 azidulidwa+ m’mibadwo yanu yonse. Aliyense wobadwira m’nyumba yanu ndi aliyense wosakhala mbewu yanu koma wogulidwa ndi ndalama kwa mlendo azidulidwa. 13 Mwana aliyense wobadwa m’nyumba mwanu, ndi mwamuna aliyense amene mwamugula ndi ndalama zanu azidulidwa ndithu,+ ndipo pangano langa pathupi panu lidzakhala pangano mpaka kalekale.+ 14 Mwamuna aliyense wosadulidwa amene sadzadulidwa, ameneyo aphedwe kuti asakhalenso pakati pa anthu ake.+ Waphwanya pangano langa.”

15 Ndiyeno Mulungu anauza Abulahamu kuti: “Sarai mkazi wako usamutchulenso kuti Sarai, chifukwa tsopano dzina lake ndi Sara.+ 16 Iye ndidzamudalitsa ndipo iwe ndidzakupatsa mwana wamwamuna wochokera mwa iye.+ Ndidzamudalitsa ndipo adzakhala mayi wa mitundu yambiri ya anthu+ ndi wa mafumu a mitundu yambiri ya anthu.”+ 17 Abulahamu atamva zimenezi anagwada n’kuwerama mpaka nkhope yake pansi, n’kuyamba kuseka mumtima mwake+ kuti: “Kodi mwamuna wa zaka 100 angabereke mwana zoona? Komanso Sara mkazi wa zaka 90, zoona angakhale ndi mwana?”+

18 Kenako Abulahamu anapempha Mulungu woona kuti: “Mbuyanga! Isimaeli akhale ndi moyo pamaso panu.”+ 19 Pamenepo Mulungu anati: “Ndithu Sara mkazi wako adzakuberekera mwana wamwamuna ndipo dzina lake udzamutche Isaki.+ Ndidzakhazikitsa pangano ndi iye, limene lidzakhala mpaka kalekale kwa mbewu yake yobwera pambuyo pa iye.+ 20 Koma za Isimaeli ndamva pempho lako. Iye ndidzamudalitsa ndipo ndidzamupatsa ana ambiri, komanso ndidzachulukitsa kwambiri mbadwa zake.+ Atsogoleri 12 a mafuko adzatuluka mwa iye, ndipo ndidzamupangitsa kukhala mtundu waukulu.+ 21 Koma ndidzakhazikitsa pangano langa ndi Isaki,+ amene Sara adzakuberekera iwe nthawi ngati yomwe ino chaka chamawa.”+

22 Ndi mawu amenewa, Mulungu anamaliza kulankhula ndi Abulahamu, n’kuchoka.+ 23 Ndiyeno Abulahamu anatenga mwana wake Isimaeli ndi amuna onse obadwira m’nyumba yake, ndi aliyense amene anamugula ndi ndalama zake, komanso mwamuna aliyense wa m’nyumba ya Abulahamu. Anawadula khungu lawo la kunsonga tsiku lomwelo, monga mmene Mulungu anamuuzira.+ 24 Abulahamu anadulidwa khungu lake la kunsonga ali ndi zaka 99.+ 25 Ndipo Isimaeli anadulidwa khungu lake la kunsonga ali ndi zaka 13.+ 26 Choncho, Abulahamu ndi mwana wake Isimaeli anadulidwa tsiku lomwelo.+ 27 Komanso amuna onse a m’nyumba yake, aliyense wobadwira m’nyumba yake ndi aliyense wogulidwa ndi ndalama zake kwa mlendo anadulidwa limodzi naye.+

18 Kenako Yehova anaonekera+ kwa Abulahamu pakati pa mitengo ikuluikulu ya ku Mamure.+ Pa nthawiyi n’kuti Abulahamu atakhala pansi pakhomo la hema wake masana dzuwa likutentha.+ 2 Atakweza maso,+ anaona amuna atatu ataima chapatali ndi iye. Atawaona, ananyamuka pakhomo la hemayo n’kuthamanga kukakumana nawo. Atafika, anagwada n’kuwaweramira mpaka nkhope yake pansi.+ 3 Ndiyeno anati: “Yehova, ngati mungandikomere mtima, chonde, musangondipitirira ine kapolo wanu.+ 4 Mumweko madzi pang’ono, ndiponso tikusambitseni mapazi.+ Kenako, mupumeko pansi pa mtengo.+ 5 Popeza mwadzera njira yodutsa kwa kapolo wanu, mundilole ndikukonzereni kachakudya kuti mutsitsimutse mitima yanu.+ Mukatero mukhoza kupitiriza ulendo wanu.” Pamenepo iwo anati: “Chabwino, chita mmene waneneramo.”

6 Chotero Abulahamu anathamangira kwa Sara n’kumuuza kuti: “Fulumira! Tenga ufa wosalala wokwana miyezo itatu ya seya,* uukande, ndipo upange makeke ozungulira.”+ 7 Kenako, Abulahamu anathamangira kumene kunali ziweto, n’kutengako ng’ombe yaing’ono yamphongo yonona. Atatero, anaipereka kwa wantchito wake, ndipo iye anaikonza mwamsanga.+ 8 Ndiyeno Abulahamu anatenga mafuta a mkaka, mkaka, ndi ng’ombe yaing’ono yamphongo imene anakonza ija, n’kukaziika pamene panali alendowo.+ Pamene iwo anali kudya atakhala pansi pa mtengo, iye anaimirira chapafupi.+

9 Tsopano alendowo anati: “Kodi mkazi wako Sara ali kuti?”+ Iye anayankha kuti: “Ali m’hemamu!”+ 10 Ndiyeno mmodzi wa iwo anapitiriza kuti: “Ndidzabweranso kwa iwe ndithu chaka chamawa nthawi ngati yomwe ino, ndipo Sara mkazi wako adzakhala ndi mwana wamwamuna.”+ Pa nthawiyi n’kuti Sara akumvetsera, ali pakhomo la hemayo. Ndipo mlendoyo anali atafulatira hemayo. 11 Abulahamu ndi Sara anali okalamba ndipo anali ndi zaka zambiri.+ Sara anali atasiya kusamba.+ 12 Chotero Sara anayamba kuseka mumtima mwake+ kwinaku akunena kuti: “Kodi mmene ndatheramu, zoona ndingakhaledi ndi chisangalalo chimenechi, komanso ndi mmene mbuyanga wakalambiramu?”+ 13 Ndiyeno Yehova anafunsa Abulahamu kuti: “N’chifukwa chiyani Sara waseka, kuti, ‘Kodi n’zoona kuti ineyo, mmene ndakalambiramu, ndingaberekedi mwana?’+ 14 Kodi pali chosatheka ndi Yehova?+ Pa nthawi yoikidwiratu ndidzabweranso kwa iwe chaka chamawa. Ndidzabweranso nthawi ngati yomwe ino, ndipo Sara adzakhala ndi mwana wamwamuna.” 15 Koma Sara pochita mantha anakana kuti: “Sindinaseketu ine ayi!” Koma mlendoyo anati: “Ayi! Unaseka iwe.”+

16 Pambuyo pake amunawo anaimirira ndi kuyang’ana ku Sodomu,+ ndipo Abulahamu ananyamuka nawo n’kuwaperekeza.+ 17 Kenako Yehova anati: “Kodi ndingamubisire Abulahamu zimene ndikufuna kuchita?+ 18 Iyetu adzakhala mtundu waukulu ndi wamphamvu, ndipo mitundu yonse ya padziko lapansi idzapeza madalitso* kudzera mwa iye.+ 19 Ndapalana ubwenzi ndi Abulahamu kuti aphunzitse ana ake ndi mbadwa zake kuyenda m’njira ya Yehova ndi kuchita chilungamo.+ Awaphunzitse kutero, kuti Yehova adzakwaniritse kwa Abulahamu zimene ananena zokhudza iye.”+

20 Chotero Yehova anati: “Kudandaula kokhumudwa chifukwa cha Sodomu ndi Gomora+ kwamveka kwambiri, ndipo tchimo lawo n’lalikulu kwambiri.+ 21 Ndiye nditsikirako kuti ndikaone ngati akuchitadi monga mwa kudandaula kumene ndamva ndiponso ngati zochita zawo zilidi zoipa choncho. Ndikufuna ndidziwe zimenezi.”+

22 Pamenepo, amunawo anatembenuka kulowera ku Sodomu, koma Yehova+ anatsala ataima ndi Abulahamu.+ 23 Ndiyeno Abulahamu anamuyandikira n’kuyamba kumufunsa kuti: “Kodi zoona mungawononge olungama pamodzi ndi oipa?+ 24 Bwanji ngati mumzindamo mutapezeka anthu olungama 50, kodi muwawonongabe? Kodi simukhululukira mzindawo chifukwa cha olungama 50 amenewo?+ 25 Simungachite zimenezo, kupha munthu wolungama limodzi ndi woipa. Sizingatheke kuti wolungama aone zofanana ndi woipa.+ Simungachite zimenezo ayi.+ Kodi Woweruza wa dziko lonse lapansi sadzachita cholungama?”+ 26 Pamenepo Yehova anayankha kuti: “Ngati ndingapeze anthu olungama 50 mu Sodomu, ndikhululukira mzinda wonsewo chifukwa cha iwo.”+ 27 Koma Abulahamu anapitiriza kuti: “Pepanitu, musaone ngati ndatha mantha kulankhula kwa Yehova pamene ndine fumbi ndi phulusa.+ 28 Nanga ngati pa olungama 50 aja pataperewera asanu, kodi muwononga mzinda wonsewo chifukwa choti paperewera anthu asanu?” Pamenepo iye anayankha kuti: “Sindiwononga mzindawo ndikapezamo olungama 45.”+

29 Koma iye anafunsabe kuti: “Nanga mutapezeka 40?” Iye anayankha kuti: “Sindiwononga chifukwa cha 40 amenewo.” 30 Koma iye anapitiriza kuti: “Chonde Yehova, musandipsere mtima,+ koma ndiloleni ndilankhulebe.+ Nanga atapezeka 30?” Iye anayankha kuti: “Sindiwononga ndikapezamo 30.” 31 Iye anapitirizabe kuti: “Chonde, pepani musaone ngati ndatha mantha kulankhula kwa Yehova.+ Nanga mutapezeka 20?” Iye anayankha kuti: “Sindiwononga mzindawo chifukwa cha 20 amenewo.”+ 32 Potsirizira pake anati: “Chonde Yehova, pepani, musandipsere mtima,+ tandilolani ndilankhule komaliza kokhaka.+ Nanga mutapezeka 10?” Iye anayankha kuti: “Sindiwononga mzindawo chifukwa cha 10 amenewo.”+ 33 Ndiyeno Yehova+ atamaliza kulankhula ndi Abulahamu, ananyamuka n’kumapita, ndipo Abulahamu anabwerera kunyumba kwake.

19 Tsopano angelo awiri aja anafika ku Sodomu madzulo. Loti anali atakhala pachipata cha Sodomu.+ Atawaona ananyamuka kukakumana nawo, ndipo anawagwadira n’kuwerama mpaka nkhope yake pansi.+ 2 Ndiyeno anati: “Chonde ambuyanga, patukirani kunyumba ya kapolo wanu. Tikusambitseni mapazi ndiponso mukagone,+ kuti mawa mulawirire n’kupitiriza ulendo wanu.”+ Ndiyeno iwo anati: “Ayi, ife tigona m’bwalo la mzinda usiku wa lero.”+ 3 Koma Loti anawaumiriza kwambiri+ moti mpaka iwo anapita naye kunyumba kwake. Kumeneko anawakonzera phwando,+ n’kuwaphikira mikate yopanda chofufumitsa,+ ndipo anadya.

4 Koma iwo asanagone, amuna a mumzindamo, amuna a mu Sodomu, anafika n’kuzungulira nyumbayo.+ Anafika ali chigulu, kuyambira tianyamata mpaka nkhalamba.+ 5 Iwo anali kufuula kwa Loti kuti: “Kodi amuna amene abwera usiku uno aja, ali kuti? Atulutse kuti tigone nawo.”+

6 Pamenepo Loti anatuluka pakhomo kuti alankhule nawo, n’kutseka chitseko kumbuyo kwake. 7 Ndiyeno iye anati: “Chonde abale anga, musachite zoipazi.+ 8 Paja ine ndili ndi ana aakazi awiri amene sanagonepo ndi mwamuna.+ Bwanji ndikutulutsireni amenewo kuti muchite nawo zimene mukufuna.+ Koma amuna okhawa musawachite chilichonse ayi,+ chifukwa abwera m’nyumba* mwanga kuti adzatetezedwe.”+ 9 Pamenepo iwo anati: “Choka apa!” Ananenanso kuti: “Uyu ndi wobwera kwathu kuno, ndipo akukhala monga mlendo.+ Ndiye lero azitiuza zochita?+ Tsopano iweyo tikuchita zoopsa kuposa iwowo.” Atatero iwo anamukhamukira Lotiyo ndi kumupanikiza,+ moti anatsala pang’ono kuthyola chitseko.+ 10 Pamenepo alendo aja anatulutsa manja n’kukokera Loti m’nyumbamo, n’kutseka chitseko. 11 Koma anachititsa khungu amuna amene anali pakhomo la nyumbawo,+ kuyambira wamng’ono kwambiri mpaka wamkulu koposa,+ moti anthuwo anavutika kufufuza khomo.+

12 Ndiyeno alendowo anafunsa Loti kuti: “Kodi uli ndi achibale alionse kuno? Uwatulutse mumzinda uno,+ kaya ndi akamwini ako, ana ako aamuna, ana ako aakazi, kapena alionse amene ndi abale ako. 13 Malo ano tiwawononga chifukwa kudandaula kokhumudwa ndi anthuwa kwamveka kwambiri kwa Yehova,+ moti Yehova watituma kudzawononga mzindawu.”+ 14 Pamenepo Loti anatuluka n’kupita kukalankhula ndi akamwini ake omwe anali kudzakwatira ana ake. Iye anawauza mobwerezabwereza kuti: “Fulumirani! Tulukani mumzinda uno, chifukwa Yehova auwononga.”+ Koma akamwini akewo anangomuona ngati akunena zocheza.+

15 Komabe, m’kachizirezire ka m’bandakucha, angelowo anayamba kum’fulumiza Loti, kuti: “Fulumira! Tenga mkazi wako ndi ana ako aakazi awiriwa,+ kuti musawonongedwere limodzi ndi mzindawu chifukwa cha kulakwa kwake.”+ 16 Pamene iye anali kuzengereza,+ alendowo, mwa chifundo cha Yehova pa iye,+ anagwira dzanja iyeyo, mkazi wake, ndi ana ake aakazi awiriwo, n’kuwatulutsa kukawasiya kunja kwa mzinda.+ 17 Atafika nawo kunja kwa mzinda, mmodzi wa iwo anati: “Thawani mupulumutse moyo wanu!+ Musacheukire kumbuyo+ ndipo musaime chilili pamalo alionse m’Chigawochi.*+ Thawirani kudera la kumapiri kuti musawonongedwe!”+

18 Koma Loti anawauza kuti: “Chonde Yehova, kumeneko ayi! 19 Mwamukomera kale mtima mtumiki wanu,+ ndipo mwaonetsa kukoma mtima kwanu kosatha+ kuti mupulumutse moyo wanga.+ Koma chonde, sinditha kuthawira kudera la kumapiri chifukwa tsoka lingakandipeze kumeneko, ndipo ndingakafe ndithu.+ 20 Chonde taonani pali mzinda waung’ono+ pafupipa umene ndingathawireko. Zimene ndikukupemphanizi si nkhani yaing’ono kodi? Chonde ndiloleni ndithawire kumzinda umenewo. Ndikatero, moyo wanga upulumuka.”+ 21 Pamenepo iye anamuyankha Loti kuti: “Chabwino, ndavomera zimene wapempha.+ Sindiwononga mzinda umene wanenawo.+ 22 Tiye, fulumira! Thawira kumeneko, ndipo sindichita kanthu mpaka utafika kumeneko.”+ N’chifukwa chake iye anatcha mzindawo dzina lakuti Zowari.*+

23 Pamene Loti ankafika ku Zowari n’kuti dzuwa litakwera.+ 24 Ndiyeno Yehova anavumbitsa sulufule ndi moto kuchokera kwa Yehova kumwamba, kuvumbira pa Sodomu ndi Gomora.+ 25 Iye anawononga mizindayi, ngakhale Chigawo chonsecho ndi anthu onse a m’mizindayi, kuphatikizapo zomera za panthaka.+ 26 Kenako, mkazi wake amene anali kumbuyo kwake anacheukira kumbuyo, ndipo anasanduka chipilala chamchere.+

27 Tsopano Abulahamu ananyamuka m’mawa kwambiri kupita pamalo pamene anaimirira pamaso pa Yehova paja.+ 28 Ndiyeno anayang’ana kumunsi ku Sodomu ndi Gomora ndi kudera lonse la Chigawocho, ndipo anaona zoopsa. Kumeneko chiutsi chinali tolo! Chinali kufuka ngati chiutsi chochokera pa uvuni wa njerwa.+ 29 Choncho pamene Mulungu anawononga mizinda ya m’Chigawocho, anakumbukira Abulahamu. Anatero mwa kupulumutsa Loti ku chiwonongeko pamene ankawononga mizinda imene Loti anali kukhalako.+

30 Pambuyo pake Loti anachoka ku Zowari n’kukakhala kudera la kumapiri, iye limodzi ndi ana ake aakazi awiri aja,+ chifukwa anachita mantha kukhala ku Zowari.+ Kumeneko, iye ndi ana ake awiriwo anayamba kukhala m’phanga. 31 Ndiyeno mwana woyamba kubadwa anauza mng’ono wake kuti: “Bambo athuwa akalamba tsopano, ndipo kudziko kuno kulibe mwamuna woti angagone nafe monga mmene anthu amachitira padziko lonse lapansi.+ 32 Tiye tiwapatse vinyo bambo kuti amwe,+ ndipo tigone nawo kuti tisunge mbewu kuchokera kwa iwo.”+

33 Chotero usiku umenewo iwo anakhala akupatsa vinyo bambo awo kuti azimwa.+ Kenako, mwana woyamba kubadwayo anapita n’kukagona ndi bambo akewo. Koma kuyambira pamene mwanayo anabwera kudzagona nawo mpaka pamene anachoka, bambowo sanadziwe chilichonse. 34 Ndipo tsiku lotsatira, mwana woyambayo anauza mng’ono wake kuti: “Ndagona nawo bambo usiku. Usiku wa leronso tiwapatse vinyo kuti amwe. Ndiye iwenso upite ukagone nawo, kuti tisunge mbewu kuchokera kwa iwo.” 35 Chotero, usiku uwunso anakhala akuwapatsa vinyo bambo awo kuti azimwa. Kenako, mwana wamng’ono uja anapita n’kukagona nawo. Koma kuyambira pamene mwanayo anabwera kudzagona nawo mpaka pamene anachoka, bambowo sanadziwe chilichonse. 36 Ndipo ana a Loti awiri onsewo anatenga pakati pa bambo awo.+ 37 M’kupita kwa nthawi, mwana woyambayo anabereka mwana wamwamuna n’kumutcha dzina lakuti Mowabu.+ Iye ndiye tate wa Amowabu mpaka lero.+ 38 Nayenso mwana wamng’onoyo anabereka mwana wamwamuna, n’kumutcha dzina lakuti Beni-ami. Iye ndiye tate wa ana a Amoni+ mpaka lero.

20 Tsopano Abulahamu anasamutsa msasa wake+ n’kupita kudziko la Negebu. Kenako anakakhala monga mlendo ku Gerari+ pakati pa Kadesi+ ndi Shura.+ 2 Kumeneko Abulahamu anabwerezanso kunena za Sara mkazi wake kuti: “Ndi mlongo wanga.”+ Abimeleki* mfumu ya ku Gerariko atamva zimenezo, anaitanitsa Sara kuti abwere kwa iye.+ 3 Pambuyo pake Mulungu anafikira Abimeleki usiku m’maloto n’kumuuza kuti: “Ufatu iwe chifukwa cha mkazi amene watengayu,+ pakuti ndi mkazi wa mwini.”+ 4 Koma Abimeleki anali asanagone naye Sarayo.+ Chotero iye anati: “Yehova, kodi mudzapha mtundu wosalakwa?+ 5 Kodi mwamunayu sanandiuze yekha kuti, ‘Ndi mlongo wanga’? Ndipo mkaziyunso sananene yekha kuti, ‘Ndi mlongo wanga’? Zimenezitu ndachita popanda mtima wanga kunditsutsa, komanso mosadziwa kuti ndikulakwa.”+ 6 Pamenepo Mulungu woona anamuuza m’malotomo kuti: “Inenso ndinadziwa kuti mtima wako sunakutsutse pochita zimenezi,+ ndipo ndinakutchinga kuti usandichimwire.+ Ndiye chifukwa chake sindinakulole kuti umukhudze mkaziyu.+ 7 Tsopano bweza mkaziyo kwa mwamuna wake. Mwamunayo ndi mneneri,+ ndipo adzakupempherera.+ Ukatero udzakhala ndi moyo. Koma ukapanda kumubweza, udziwe kuti, iweyo ndi anthu ako onse mufa ndithu.”+

8 Kenako Abimeleki anadzuka m’mawa kwambiri n’kuitana antchito ake onse n’kuwauza zonsezi ndipo anthuwo anachita mantha kwambiri. 9 Tsopano Abimeleki anaitana Abulahamu, n’kumufunsa kuti: “N’chiyani wachita kwa ifechi? Ndakuchimwira chiyani ine, kuti ubweretse tchimo lalikulu+ chonchi pa ine ndi ufumu wanga? Wandichitira zinthu zosayenera kuchita.”+ 10 Abimeleki anapitiriza kufunsa Abulahamu kuti: “Cholinga chako chinali chiyani makamaka pochita zimenezi?”+ 11 Abulahamu anayankha kuti: “Ndachita zimenezi poganiza kuti, ‘Ndithu anthu a kuno saopa Mulungu,+ andipha ndithu chifukwa cha mkazi wangayu.’+ 12 Komabe, ndi mlongo wangadi ameneyu. Bambo athu ndi amodzi, tinangosiyana mayi, ndipo ndinam’kwatira.+ 13 Mulungu atandichotsa kunyumba kwa bambo anga+ kuti ndiyambe kuyendayenda, ndinauza mkazi wangayu kuti, ‘Undisonyeze kukoma mtima kosatha+ motere: Kumalo alionse kumene tizifika, uziuza anthu za ine kuti: “Ndi mlongo wanga.”’”+

14 Tsopano Abimeleki anatenga nkhosa, ng’ombe, ndiponso antchito aamuna ndi aakazi n’kumupatsa Abulahamu, ndi kumubwezeranso mkazi wake Sara.+ 15 Abimeleki ananenanso kuti: “Dziko lonseli ndi langa. Ungathe kukhala kulikonse kumene ungakonde.”+ 16 Kenako Abimeleki anauza Sara kuti: “Ndalama zasiliva 1,000 izi ndikuzipereka kwa mlongo wakoyu.+ Zikhale umboni wotsimikizira+ kwa onse amene muli nawo, ndi kwa wina aliyense, kuti sunaipitsidwe.” 17 Kenako Abulahamu anayamba kum’pempherera iye kwa Mulungu woona.+ Chotero Mulungu anachiritsa Abimeleki ndi mkazi wake, ndi akapolo ake aakazi, moti iwo anayamba kubereka ana. 18 Zinatero pakuti Yehova anachititsa kuti akazi onse a m’nyumba ya Abimeleki asabereke, chifukwa cha Sara mkazi wa Abulahamu.+

21 Tsopano Yehova anakumbukira Sara monga mwa mawu ake, ndipo Yehovayo anachitira Sara monga momwe ananenera.+ 2 Choncho Sara anakhala ndi pakati+ n’kuberekera Abulahamu mwana, Abulahamuyo atakalamba. Izi zinachitika pa nthawi yoikidwiratu imene Mulungu analonjeza Abulahamu.+ 3 Chotero Abulahamu anatcha mwana amene Sara anamuberekerayo dzina lakuti Isaki.+ 4 Isaki atakwanitsa masiku 8, Abulahamu anamudula mwana wakeyo, monga mmene Mulungu anamulamulira.+ 5 Abulahamu anali ndi zaka 100 pamene mwana wake Isaki anabadwa. 6 Ndiyeno Sara anati: “Mulungu wandipatsa chifukwa chosangalalira. Tsopano aliyense akamva zimenezi asangalala nane.”*+ 7 Anapitiriza kunena kuti: “Akanadziwa ndani kuti Sara adzayamwitsa mwana, moti n’kumuuza Abulahamu zimenezo? Koma taonani, ndamuberekera mwana Abulahamu atakalamba.”

8 Tsopano mwanayo anakula n’kumusiyitsa kuyamwa.+ Pa tsiku limene anamusiyitsa kuyamwalo, Abulahamu anakonza phwando lalikulu. 9 Kenako Sara anakhala akuona mwana amene Hagara Mwiguputo+ anaberekera Abulahamu akuseka Isaki.+ 10 Chotero Sara anayamba kuuza Abulahamu kuti: “Thamangitsani kapolo wamkaziyu pamodzi ndi mwana wakeyu pano, chifukwa mwana wa kapolo ameneyu sadzakhala wolandira cholowa pamodzi ndi mwana wanga Isaki.”+ 11 Abulahamu anaipidwa nazo kwambiri zimenezi chifukwa cha mwana wake.+ 12 Koma Mulungu anauza Abulahamu kuti: “Usaipidwe ndi chilichonse chimene Sara wakhala akunena kwa iwe chokhudza mnyamatayo ndiponso kapolo wakoyo. Mvera mawu ake, chifukwa amene adzatchedwa mbewu yako adzachokera mwa Isaki.+ 13 Kunena za mwana wa mdzakaziyo,+ nayenso ndidzamupangitsa kukhala mtundu, chifukwa iye ndi mbewu yako.”+

14 Choncho Abulahamu anadzuka m’mawa kwambiri n’kutenga mkate ndi thumba la madzi lachikopa, n’kuziika paphewa pa Hagara.+ Atatero anamuuza kuti azipita limodzi ndi mwana wakeyo.+ Chotero Hagarayo ananyamuka n’kumangoyendayenda m’chipululu cha Beere-seba.*+ 15 Potsirizira pake, madzi anamuthera+ m’thumba lachikopa lija, ndipo iye anangomusiya+ mwana uja pachitsamba. 16 Ndiyeno iye anapita chapatali n’kukakhala pansi payekhayekha pamtunda woti muvi woponya ndi uta ukhoza kufika. Anachita zimenezi chifukwa mumtima mwake anati: “Sindikufuna kuona mwana wanga akamafa.”+ Choncho anakakhala pansi pakatali n’kuyamba kulira mokweza.+

17 Pamenepo Mulungu anamva mawu a mnyamatayo,+ ndipo mngelo wa Mulungu analankhula ndi Hagara kuchokera kumwamba+ kuti: “Kodi watani Hagara? Usaope, Mulungu wamva mawu a mnyamatayo pomwe wagonapo. 18 Nyamuka! Dzutsa mnyamatayo, ndipo umugwirizize ndi dzanja lako, chifukwa ndidzamupangitsa kukhala mtundu waukulu.”+ 19 Ndiyeno Mulungu anamutsegula maso Hagara, moti anaona chitsime cha madzi.+ Chotero iye anapita pachitsimecho n’kutungira madziwo m’thumba lachikopa lija, n’kumupatsa mnyamatayo kuti amwe. 20 Mulungu anakhalabe ndi Isimaeli.+ Mnyamata ameneyu anali kukhala m’chipululu, ndipo anakula n’kukhala katswiri woponya muvi ndi uta.+ 21 Iye anakhalabe m’chipululu cha Parana,+ ndipo amayi ake anakamutengera mkazi kudziko la Iguputo.

22 Ndiyeno pa nthawi imeneyo, Abimeleki limodzi ndi Fikolo mkulu wa gulu lake lankhondo anauza Abulahamu kuti: “Mulungu ali ndi iwe pa zonse zomwe ukuchita.+ 23 Chotero lumbira panopo kuti, pali Mulungu+ udzakhala wokhulupirika kwa ine, kwa ana anga ndi kwa mbadwa zanga.+ Ndiponso kuti udzatero chifukwa cha chikondi chosatha+ chimene ine ndakusonyeza. Choncho udzandichitira ine motero, pamodzi ndi dziko limene ukukhalamo monga mlendoli.”+ 24 Abulahamu anayankha kuti: “Ndikulumbira.”+

25 Pamene Abulahamu anadzudzula kwambiri Abimeleki chifukwa cha chitsime cha madzi chimene antchito a Abimeleki analanda mwachiwawa,+ 26 Abimeleki anayankha kuti: “Sindikudziwa amene anachita zimenezi, ndipo ngakhale iwe sunandiuze. Inetu sindinamve za nkhani imeneyi, moti ndikuimvera pompano.”+ 27 Ndiyeno Abulahamu anatenga nkhosa ndi ng’ombe n’kuzipereka kwa Abimeleki.+ Kenako awiriwo anachita pangano.+ 28 Abulahamu atapatula ana a nkhosa aakazi 7 pa gululo n’kuwaika pa okha, 29 Abimeleki anafunsa Abulahamu kuti: “Kodi ana a nkhosa aakazi 7 amene wapatulawa, tanthauzo lake n’chiyani?” 30 Poyankha Abulahamu anati: “Landirani ana a nkhosa aakazi 7 amene ndikukupatsaniwa, kuti akhale umboni+ wakuti ndinakumba chitsimechi ndine.” 31 Ndiye chifukwa chake iye anatcha malowo Beere-seba,+ chifukwa chakuti onse awiri analumbirirana pamalopo. 32 Choncho iwo anachita panganolo+ pa Beere-sebapo, kenako Abimeleki limodzi ndi Fikolo mkulu wa asilikali ake, anabwerera kudziko la Afilisiti.+ 33 Zitatero, Abulahamu anabzala mtengo wa bwemba pa Beere-seba, n’kuitanirapo dzina la Yehova,+ Mulungu wanthawi zonse.+ 34 Ndipo Abulahamu anakhala masiku enanso ambiri monga mlendo m’dziko la Afilisiti.+

22 Tsopano zimenezi zitapita, Mulungu woona anamuyesa Abulahamu+ pomuuza kuti: “Abulahamu!” Iye anayankha kuti: “Ine mbuyanga!”+ 2 Mulungu anapitiriza kuti: “Tenga Isaki+ mwana wako mmodzi yekhayo, mwana wako amene umamukonda kwambiriyo,+ ndipo muyende ulendo wopita ku Moriya.+ Kumeneko ukamupereke nsembe yopsereza paphiri limene ndidzakuuza.”+

3 Choncho Abulahamu anadzuka m’mawa kwambiri, n’kumanga chishalo pabulu wake, ndi kutenga anyamata ake awiri limodzi ndi mwana wake Isaki.+ Anawazanso nkhuni zokawotchera nsembe. Atatero, ananyamuka ulendo wopita kumalo amene Mulungu woona anamuuza. 4 Pa tsiku lachitatu, Abulahamu anakweza maso ake n’kuyamba kuona malowo chapatali. 5 Tsopano Abulahamu anauza anyamata akewo+ kuti: “Inu tsalani pano ndi buluyu, ine ndi mwana wangayu tikupita uko kukalambira,+ tikupezani.”

6 Pamenepo Abulahamu anatenga nkhuni zokawotchera nsembe zija n’kumusenzetsa Isaki mwana wake.+ Iye ananyamula moto ndi mpeni wophera nyama, ndipo iwo anapitira limodzi.+ 7 Ndiyeno Isaki analankhula ndi Abulahamu bambo ake kuti: “Bambo!”+ Abulahamu anayankha kuti: “Lankhula mwana wanga.”+ Chotero iye anafunsa kuti: “Moto ndi nkhuni n’zimenezi, nanga nkhosa yokapereka nsembe yopsereza ili kuti?”+ 8 Abulahamu anayankha kuti: “Mwana wanga, Mulungu apeza yekha nkhosa yopereka nsembe yopsereza.”+ Choncho awiriwo anapitiriza ulendo wawo.

9 Kenako iwo anafika pamalo amene Mulungu woona anamuuza Abulahamu. Atafika pamalowo, iye anamanga guwa lansembe+ n’kuyala nkhuni zija paguwapo. Atatero, anamanga Isaki mwana wakeyo manja ndi miyendo, n’kumugoneka paguwapo, pamwamba pa nkhuni.+ 10 Tsopano Abulahamu anatenga mpeni uja kuti aphe mwana wakeyo.+ 11 Koma mngelo wa Yehova anamuitana kuchokera kumwamba kuti:+ “Abulahamu! Abulahamu!” Iye anayankha kuti: “Ine mbuyanga!” 12 Ndiyeno mngeloyo anapitiriza kulankhula kuti: “Usatambasulire dzanja lako mwanayo ndipo usam’chite kanthu kena kalikonse.+ Tsopano ndadziwa kuti ndiwe woopa Mulungu, pakuti sunakane kupereka kwa ine mwana wako mmodzi yekhayo.”+ 13 Pamenepo Abulahamu anakweza maso ake n’kuona nkhosa yamphongo chapotero, itakodwa ndi nyanga zake m’ziyangoyango. Ndiyeno Abulahamu anakaitenga n’kuipereka nsembe yopsereza m’malo mwa mwana wake.+ 14 Chotero Abulahamu anatcha malowo Yehova-yire.* Ndiye chifukwa chake lero pali mawu akuti: “M’phiri lake Yehova adzapereka zinthu zofunikira.”+

15 Mngelo wa Yehova anaitananso Abulahamu kachiwiri kuchokera kumwamba, 16 n’kumuuza kuti: “Yehova wati, ‘Ndikulumbira+ pali dzina langa, kuti chifukwa cha zimene wachitazi, posakana kupereka mwana wako yekhayo,+ 17 ndidzakudalitsa ndithu. Ndiponso ndidzachulukitsadi mbewu yako ngati nyenyezi zakumwamba, monganso mchenga wa m’mphepete mwa nyanja.+ Komanso mbewu yako idzalanda chipata* cha adani ake.+ 18 Kudzera mwa mbewu yako,+ mitundu yonse ya padziko lapansi idzapeza madalitso* ndithu chifukwa chakuti wamvera mawu anga.’”+

19 Kenako Abulahamu anabwerera kwa anyamata ake aja, n’kunyamukira nawo limodzi kubwerera ku Beere-seba.+ Abulahamu anapitirizabe kukhala ku Beere-seba.

20 Pambuyo pa zimenezi, uthenga unafika kwa Abulahamu wonena kuti: “Panopo Milika+ naye waberekera m’bale wako Nahori+ ana aamuna. 21 Mwana wake woyamba ndi Uza, ndi Buza+ m’bale wake, komanso Kemueli bambo ake a Aramu. 22 Palinso Kesede, Hazo, Pilidasi, Yidilafi ndi Betuele.”+ 23 Betuele anabereka Rabeka.+ Ana 8 amenewa ndi amene Milika anaberekera Nahori m’bale wake wa Abulahamu. 24 Panalinso mdzakazi* wake, dzina lake Reuma. M’kupita kwa nthawi iyenso anaberekera Nahori ana awa: Teba, Gahamu, Tahasi ndi Maaka.+

23 Sara anakhala ndi moyo zaka 127. Zimenezi ndizo zinali zaka za moyo wake.+ 2 Sara anamwalirira ku Kiriyati-ariba,+ kapena kuti ku Heburoni,+ m’dziko la Kanani.+ Pamenepo Abulahamu analowa muhema kukamulira Sara. 3 Ndiyeno Abulahamu anachoka pamene panali mtembo wa mkazi wake n’kupita kukalankhula ndi ana a Heti,+ kuti: 4 “Ine ndinadzakhala kwanu kuno ngati mlendo.+ Choncho ndigawireniko malo kuti ndikhale ndi manda angaanga, ndiikemo mkazi wanga.”*+ 5 Ana a Heti anayankha Abulahamu kuti: 6 “Timvereni mbuyathu.+ Inu ndinu mtsogoleri woikidwa ndi Mulungu.+ Sankhani manda abwino koposa pa manda amene tili nawo kuti muikemo malemuwo.+ Palibe aliyense wa ife amene angakanize manda ake kuti muikemo malemuwo.”+

7 Pamenepo Abulahamu anaimirira n’kugwada pansi pamaso pa eni dzikowo,+ ana a Heti.+ 8 Iye analankhula nawo kuti: “Ngati mukuvomera kuti ndiike m’manda malemu mkazi wanga, ndimvereni ndipo mundipemphere kwa Efuroni mwana wa Zohari.+ 9 Mundipemphere kuti andigulitse phanga lake la Makipela+ limene lili m’malire a malo ake. Andigulitse pa mtengo wake wonse inu mukuona, kuti ndiikemo malemu mkazi wanga.”+

10 Pa nthawiyi n’kuti Efuroni atakhala pansi pakati pa ana a Heti. Choncho Efuroni Mhiti+ anayankha Abulahamu, ana a Hetiwo akumva limodzi ndi onse amene analowa pachipata cha mzinda wake.+ Iye anati: 11 “Ayi mbuyanga! Ndimvereni. Malowo, pamodzi ndi phanga limene lili pamalopo, ndikupatsani pamaso pa anthu a mtundu wangawa.+ Kaikeni malemuwo.” 12 Pamenepo Abulahamu anagwada pamaso pa eni dzikowo. 13 Kenako iye analankhula kwa Efuroni pamaso pa eni dzikowo kuti: “Ndimvere chonde. Ine ndigulabe malowo. Landira silivayu+ kuti ndikaike mkazi wanga kumeneko.”

14 Ndiyeno Efuroni anayankha Abulahamu kuti: 15 “Ndimvereni mbuyanga. Malowo mtengo wake ndi siliva wolemera masekeli* 400. Koma zimenezo sindiyo nkhani yaikulu pakati pa ine ndi inu. Kaikeni malemuwo.”+ 16 Chotero Abulahamu anamveradi Efuroni, n’kumuyezera siliva wokwanira mtengo umene Efuroniyo ananena pamaso pa ana a Heti. Anamuyezera siliva wolemera masekeli 400, malinga ndi muyezo wovomerezeka ndi amalonda pa nthawiyo.+ 17 Chotero malo a Efuroni amene anali ku Makipela moyang’anizana ndi Mamure, ndiponso phanga limene linali mmenemo, komanso mitengo yonse imene inali mkati mwa malire onse a malowo,+ anatsimikizirika+ 18 pamaso pa ana a Heti ndi onse amene analowa pachipata cha mzinda, kuti Abulahamu ndiye wagula malowo ndipo ndi ake.+ 19 Zitatero, Abulahamu anaika Sara mkazi wake m’manda kuphanga la Makipela, moyang’anizana ndi Mamure, kapena kuti Heburoni, m’dziko la Kanani.+ 20 Chotero ana a Heti anagulitsa kwa Abulahamu malowo ndi phanga limene linali pamenepo, ndipo mkazi wake anamuika m’manda kumeneko.+

24 Tsopano Abulahamu anali atakalamba ndipo anali ndi zaka zambiri. Yehova anali atamudalitsa m’chilichonse.+ 2 Chotero Abulahamu anauza mtumiki wake yemwe anali wamkulu koposa m’nyumba yake, ndi woyang’anira zinthu zake zonse,+ kuti: “Chonde, ika dzanja lako pansi pa ntchafu yanga.+ 3 Ndikufuna ulumbire pali Yehova,+ Mulungu wakumwamba ndi Mulungu wa dziko lapansi, kuti sutengera mwana wanga mkazi pakati pa ana aakazi a Akanani, amene ndikukhala pakati pawo.+ 4 M’malomwake, upite kudziko lakwathu kwa abale anga,+ ndipo kumeneko, ndithu ukam’tengere mkazi Isaki mwana wanga.”

5 Koma mtumikiyo anamufunsa kuti: “Bwanji ngati mkaziyo atakana kubwera nane kuno? Kodi ndidzatenge mwana wanuyu ndi kum’bwezera kudziko lanu kumene munachokera?”+ 6 Pamenepo Abulahamu anayankha kuti: “Ayi, usadzabweze mwana wanga kudziko lakwathu.+ 7 Yehova Mulungu wakumwamba, amene ananditenga ine kunyumba kwa bambo anga ndi kudziko la abale anga,+ amenenso anandilankhula ndi kundilumbirira+ kuti, ‘Ndidzapereka dziko ili+ kwa mbewu yako,’+ ameneyo atumiza mngelo wake kuti akutsogolere,+ ndipo kumeneko, ndithu ukam’tengere mwana wanga mkazi.+ 8 Koma ngati mkaziyo angakakane kubwera nawe, iweyo udzamasuka pa lumbiro limeneli.+ Koma zoti ukabwezere mwana wanga kumeneko, zimenezo ayi.” 9 Atatero, mtumikiyo anaika dzanja lake pansi pa ntchafu ya Abulahamu mbuye wake, n’kulumbira kwa iye pa nkhani imeneyi.+

10 Pamenepo mtumikiyo anatenga ngamila 10 pa ngamila za mbuye wake, n’kutenganso zabwino za mtundu uliwonse kwa mbuye wake zoti akazigwiritse ntchito.+ Kenako ananyamuka ulendo wopita ku Mesopotamiya, kumzinda wa Nahori. 11 Atafika, anagwaditsa pansi ngamilazo kunja kwa mzindawo pachitsime cha madzi.+ Anafika chakumadzulo, pamene akazi mwachizolowezi anali kutuluka mumzindamo kukatunga madzi.+ 12 Ndiyeno mtumikiyo anati: “Yehova, Mulungu wa mbuyanga Abulahamu,+ chonde chititsani kuti lero zinthu zindiyendere bwino, ndipo sonyezani mbuyanga Abulahamu kukoma mtima kwanu kosatha.+ 13 Ndaima pano pakasupe wa madzi, ndipo ana aakazi a mumzindawu akubwera kudzatunga madzi.+ 14 Zichitike kuti, mtsikana amene ndimuuze kuti, ‘Chonde tula pansi mtsuko wako wa madzi kuti ndimweko,’ ndipo amenedi ati andiyankhe kuti, ‘Imwani, ndiponso nditungira madzi ngamila zanu kuti zimwe,’ ameneyo ndi amene mwasankhira mtumiki wanu+ Isaki. Mukachita zimenezo, ndidziwa kuti mwasonyeza mbuyanga chikondi chosatha.”+

15 Koma asanamalize kulankhula,+ anangoona Rabeka mwana wa Betuele+ akutuluka mumzindawo. Betuele anali mwana wa Milika,+ ndipo Milika anali mkazi wa Nahori,+ m’bale wake wa Abulahamu. Rabekayo anali atasenza mtsuko paphewa pake.+ 16 Mwana wa mkaziyo anali wokongola mochititsa kaso,+ ndipo anali namwali amene anali asanagonepo ndi mwamuna.+ Iye analowa m’chitsimemo n’kutunga madzi mumtsuko wake, kenako anatulukamo. 17 Nthawi yomweyo mtumiki wa Abulahamuyo anamuthamangira n’kumuuza kuti: “Chonde ndipatse madzi a mumtsuko wako ndimweko pang’ono.”+ 18 Rabekayo anayankha kuti: “Eni, imwani mbuyanga.” Atatero anatsitsa mtsuko wake mwamsanga n’kuupendeketsa kuti mtumikiyo amwe.+ 19 Atamaliza kupereka madzi akumwawo, anati: “Nditungiranso madzi ngamila zanu mpaka zitamwa mokwanira.”+ 20 Choncho, iye mwamsanga anakhuthulira madzi amene anali mumtsuko aja muchomweramo ziweto. Kenako anayamba kuthamanga mobwerezabwereza kukatunga madzi ena pachitsimepo+ mpaka ngamila zonse za mlendoyo zitamwa mokwanira. 21 Nthawi yonseyi n’kuti munthu uja akungomuyang’ana modabwa osanena kalikonse, kuti aone ngati Yehova wapangitsadi ulendo wake kukhala wopambana kapena ayi.+

22 Kenako, ngamila zija zitatha kumwa, mlendoyo anatenga ndolo yagolide yovala pamphuno+ yolemera hafu ya sekeli, ndi zibangili ziwiri+ zagolide zoti Rabeka azivala m’mikono, zolemera masekeli 10, 23 n’kumufunsa kuti: “Kodi ndiwe mwana wa ndani? Chonde ndiuze. Kodi kunyumba kwa bambo ako kuli malo oti tikhoza kugonako?”+ 24 Pamenepo iye anayankha kuti: “Ine ndine mwana wa Betuele.+ Bambo angawo mayi awo ndi Milika, bambo wawo ndi Nahori.”+ 25 Ananenanso kuti: “Chakudya cha ziweto tili nacho chambiri, komanso malo ogona alipo.”+ 26 Pamenepo mwamunayo anagwada pansi n’kuwerama pamaso pa Yehova+ 27 n’kunena kuti: “Atamandike Yehova,+ Mulungu wa mbuyanga Abulahamu, amene sanasiye kusonyeza mbuyanga kukoma mtima kosatha ndi kukhala wokhulupirika kwa iye. Pa ulendo wangawu, Yehova wanditsogolera kunyumba kwa abale a mbuyanga.”+

28 Ndiyeno mtsikanayo anathamangira kunyumba kwa mayi ake n’kufotokozera onse zimenezi. 29 Rabeka anali ndi mlongo wake dzina lake Labani.+ Ndipo Labani anathamanga kupita kwa munthu uja, yemwe anali kuchitsime, kunja kwa mzinda. 30 Tsopano Labani ataona ndolo ya pamphuno ndi zibangili+ pamikono ya mlongo wake, ndiponso atamva mawu a mlongo wake Rabeka akuti: “Munthuyo anandiuza zakutizakuti,” Labaniyo anapita kwa munthuyo ndipo anamupeza ataimirira ndi ngamila zake pachitsimepo. 31 Atangomuona anamuuza kuti: “Tabwerani, inu wodalitsika wa Yehova.+ Bwanji mwangoima kunja kuno? Inetu ndakonza kale malo kunyumbaku, a inu ndi a ngamilazi.” 32 Munthuyo atamva zimenezo, anapita n’kukalowa m’nyumbamo. Pamenepo Labani anamasula ngamila ndi kuzipatsa chakudya. Anatenganso madzi n’kusambitsa mapazi a mlendoyo ndi mapazi a anyamata omwe iye anali nawo.+ 33 Kenako anamuikira chakudya, koma iye anati: “Sindidya kufikira nditanena chimene ndabwerera.” Choncho Labani anati: “Ndiye lankhulanitu!”+

34 Iye anati: “Ine ndine mtumiki wa Abulahamu.+ 35 Yehova wamudalitsa kwambiri mbuyanga moti akum’lemeretsabe pomupatsa nkhosa, ng’ombe, siliva, golide, antchito aamuna ndi aakazi, ngamila ndi abulu.+ 36 Ndiponso Sara mkazi wake anamuberekera mbuyangayo mwana wamwamuna, mbuyangayo atakalamba.+ Mbuyangayo adzapatsa mwanayo zonse zimene ali nazo.+ 37 Choncho mbuyangayo anandilumbiritsa kuti, ‘Usatengere mwana wanga mkazi pakati pa ana aakazi achikananiwa amene ndikukhala m’dziko lawo.+ 38 Usachite zimenezo, koma upite kubanja la bambo anga, kwa abale anga,+ ukam’tengere mwana wanga mkazi.’+ 39 Koma ineyo ndinafunsa mbuyanga kuti, ‘Bwanji ngati mkaziyo sakabwera nane?’+ 40 Iye anandiyankha kuti, ‘Yehova, amene ndakhala ndikuyenda pamaso pake movomerezeka,+ atumiza mngelo+ wake kuti apite nawe limodzi, ndipo ameneyo akakuthandiza ndithu kuti ukapeze chimene uyendere.+ Kumeneko, ukam’tengere mkazi mwana wanga, kwa abale anga, kubanja la bambo anga.+ 41 Ukakafika kwa abale anga, udzamasuka ku lumbiro limene wachita, ndiponso ngati sakakupatsa mkaziyo, udzamasuka ku lumbiroli.’+

42 “Nditafika kuchitsime lero, ndinati, ‘Yehova, Mulungu wa mbuyanga Abulahamu, ngati mundithandizadi kuti ndipeze chimene ndayendera,+ 43 ndaima pano pakasupe wa madzi. Zichitike kuti, namwali+ wotuluka mumzindawu kudzatunga madzi amene ndimuuze kuti, “Chonde, ndimweko pang’ono madzi a mumtsuko wakowo,” 44 amenedi andiyankhe kuti, “Imwani, ndiponso nditungira ngamila zanu kuti zimwe,” ameneyo ndiye mkazi amene Yehova wasankhira mwana wa mbuyanga.’+

45 “Ndisanamalize kulankhula+ mumtima mwanga,+ ndinangoona Rabeka akutuluka mumzindawu, atanyamula mtsuko wake paphewa. Iye anatsikira kukasupe n’kuyamba kutunga madzi.+ Pamenepo ndinamupempha kuti, ‘Chonde ndigawireko madzi ndimwe.’+ 46 Mwamsanga iye anatula pansi mtsuko wake n’kundiuza kuti, ‘Imwani,+ ndipo nditungiranso ngamila zanu kuti zimwe.’ Choncho ndinamwa madziwo, ndipo iye anatungiranso ngamila kuti zimwe. 47 Atatero ndinamufunsa kuti, ‘Kodi ndiwe mwana wa ndani?’+ Iye anandiyankha kuti, ‘Ine bambo anga ndi a Betuele. Bambo awo ndi a Nahori, ndipo mayi awo ndi a Milika.’ Ndiyeno ndinamuveka ndolo ya pamphuno ndi zibangili m’mikono yake.+ 48 Kenako ndinagwada pansi n’kuwerama pamaso pa Yehova. Ndinatamanda Yehova, Mulungu wa mbuyanga Abulahamu,+ amene wanditsogolera panjira yolondola,+ kuti ndidzatengere mkazi mwana wa mbuyanga kwa m’bale wake. 49 Tsopano ngati mukusonyezadi mbuyanga kukoma mtima kosatha ndi kukhala okhulupirika kwa iye,+ ndiuzeni. Koma ngati ayi, mundiuzenso kuti ndikayang’ane kwina.”+

50 Ndiyeno Labani ndi Betuele anamuyankha kuti: “Zimenezi zachokera kwa Yehova.+ Ife sitingathe kuvomera kapena kukana kwa inu.+ 51 Nayu Rabeka. M’tengeni muzipita naye, ndipo akakhale mkazi wa mwana wa mbuye wanu monga Yehova wanenera.”+ 52 Mtumiki wa Abulahamu atamva zimenezi, nthawi yomweyo anagwada n’kuweramira pansi pamaso pa Yehova.+ 53 Kenako, mtumikiyo anayamba kutulutsa zinthu zasiliva, zagolide, ndi zovala n’kupatsa Rabeka. Anaperekanso zinthu zamtengo wapatali kwa mlongo wake wa Rabeka ndi kwa mayi ake.+ 54 Pambuyo pake, iye limodzi ndi anyamata ake anadya ndi kumwa, ndipo anagona komweko ndi kudzuka m’mawa.

Kenako mtumiki wa Abulahamu uja anati: “Ndiloleni ndizipita kwa mbuyanga.”+ 55 Koma mlongo wa mtsikanayo ndi mayi ake anati: “Bwanji mtsikanayu akhalebe nafe masiku 10 okha, pambuyo pake akhoza kupita.” 56 Iye anawauza kuti: “Musandichedwetse, chifukwa Yehova wandithandiza kukwaniritsa zimene ndayendera.+ Ndiloleni ndizipita kwa mbuyanga.”+ 57 Pamenepo iwo anati: “Tiyeni timuitane mtsikanayo kuti timve zimene iyeyo anene.”+ 58 Ndiyeno anamuitana Rabekayo ndi kumufunsa kuti: “Kodi upita naye limodzi munthuyu?” Iye anayankha kuti: “Inde ndipita.”+

59 Pamenepo, iwo analola kuti mlongo wawo Rabeka+ ndi mlezi wake,+ azipita limodzi ndi mtumiki wa Abulahamuyo ndi anyamata ake. 60 Ndiyeno iwo anayamba kudalitsa Rabeka kuti: “Iwe mlongo wathu, ukakhale mayi wa anthu masauzande kuchulukitsa ndi masauzande 10, ndipo mbewu yako ikalande mizinda ya adani awo.”+ 61 Atatha kum’dalitsa, Rabeka ndi adzakazi ake+ ananyamuka n’kukwera ngamila+ kumapita limodzi ndi mtumiki wa Abulahamu uja. Motero mtumikiyo anatenga Rabeka n’kupita naye.

62 Isaki anali kukhala m’dziko la Negebu.+ Tsiku lina, atapatuka panjira yopita ku Beere-lahai-roi,+ 63 anapita m’tchire madzulo kuti akasinkhesinkhe.+ Ataponya maso, anaona ngamila zikubwera poteropo! 64 Nayenso Rabeka atakweza maso anaona Isaki, ndipo mwamsanga anatsika pangamila. 65 Atatero, anafunsa mtumiki uja kuti: “Kodi munthu akubwera apoyo kuchokera m’tchire kudzakumana nafe ndani?” Mtumikiyo anayankha kuti: “Ameneyo ndi mbuyanga.” Pamenepo iye anatenga nsalu yophimba kumutu n’kudziphimba nayo.+ 66 Kenako, mtumikiyo anafotokozera Isaki zonse zimene anachita. 67 Zitatero, Isaki analowa ndi mkaziyo m’hema wa Sara, mayi ake.+ Umu ndi mmene Isaki anatengera Rabeka kukhala mkazi wake.+ Iye anam’konda kwambiri,+ ndipo anatonthozedwa pambuyo pa imfa ya mayi ake.+

25 Tsopano Abulahamu anatenganso mkazi wina, dzina lake Ketura.+ 2 M’kupita kwa nthawi, mkaziyo anamuberekera Zimirani, Yokesani, Medani, Midiyani,+ Isibaki ndi Shuwa.+

3 Yokesani anabereka Sheba+ ndi Dedani.+

Ana a Dedani anali Asurimu, Letusimu ndi Leumimu.

4 Ana a Midiyani anali Efa,+ Eferi, Hanoki, Abida ndi Elida.+

Onsewa anali ana aamuna a Ketura.

5 Pambuyo pake, Abulahamu anapatsa Isaki zonse zimene anali nazo.+ 6 Koma ana a adzakazi amene Abulahamu anali nawo, anawapatsa mphatso.+ Kenako, iye adakali ndi moyo, anatumiza anawo+ Kum’mawa,+ kutali ndi mwana wake Isaki. 7 Masiku onse a moyo wa Abulahamu anali zaka 175. 8 Kenako, Abulahamu anamwalira ali wokalamba, atakhala ndi moyo wabwino, wautali ndi wokhutira, ndipo anaikidwa m’manda n’kugona ndi makolo ake.+ 9 Chotero ana ake, Isaki ndi Isimaeli, anamuika iye m’manda. Anamuika m’phanga la Makipela, kumalo a Efuroni mwana wa Zohari Mheti, moyang’anana ndi Mamure.+ 10 Malo amenewa ndi omwe Abulahamu anagula kwa ana a Heti. Abulahamu anaikidwa kumeneko, komanso Sara mkazi wake.+ 11 Abulahamu atamwalira, Mulungu anapitiriza kudalitsa Isaki mwana wake.+ Isakiyo anali kukhala pafupi ndi Beere-lahai-roi.+

12 Tsopano nayi mbiri ya Isimaeli+ mwana wa Abulahamu, amene Hagara Mwiguputo, kapolo wa Sara anaberekera Abulahamu.+

13 Awa ndiwo mayina a ana a Isimaeli, amene kunachokera mabanja awo: Nebayoti,+ mwana woyamba wa Isimaeli, Kedara,+ Adibeele, Mibisamu,+ 14 Misima, Duma, Maasa, 15 Hadadi,+ Tema,+ Yeturi, Nafisi ndi Kedema.+ 16 Amenewa ndiwo ana a Isimaeli, potsata mayina awo, malinga ndi midzi yawo ndi misasa yawo yotchinga ndi mipanda.+ Anali atsogoleri okwanira 12 malinga ndi mafuko awo.+ 17 Zaka zonse zimene Isimaeli anakhala ndi moyo zinali 137. Kenako anamwalira, ndipo anaikidwa m’manda n’kugona ndi makolo ake.+ 18 Iwo anakhala m’mahema kuyambira ku Havila+ pafupi ndi Shura+ moyang’anana ndi Iguputo, mpaka ku Asuri. Anakhala pafupi ndi abale awo onse.+

19 Tsopano nayi mbiri ya Isaki mwana wa Abulahamu.+

Abulahamu anabereka Isaki. 20 Isaki anali ndi zaka 40 pamene anakwatira Rabeka, mwana wa Betuele,+ Msiriya+ wa ku Padana-ramu, mlongo wake wa Labani, Msiriya. 21 Isaki anali kupembedzera Yehova mosalekeza, makamaka chifukwa cha mkazi wake,+ popeza iye anali wosabereka.+ Yehova anamva kupembedzera kwake,+ ndipo Rabeka mkazi wakeyo anakhala ndi pakati. 22 Ndiyeno ana amene anali m’mimba mwake anayamba kulimbana,+ moti iye anati: “Ngati umu ndi mmene ndivutikire, ndiye ndi bwino ndingofa.” Atatero anapita kukafunsira kwa Yehova.+ 23 Yehova anamuyankha kuti: “M’mimba mwako+ muli mitundu iwiri ya anthu, ndipo mitundu iwiri imene idzatuluka m’mimba mwakoyo idzakhala yosiyana.+ Mtundu wina udzakhala wamphamvu kuposa mtundu winawo,+ ndipo wamkulu adzatumikira wamng’ono.”+

24 Potsirizira pake, masiku oti Rabeka abereke anakwana, ndipo m’mimba mwake munali mapasa.+ 25 Woyamba kubadwa anali wofiira, ndipo thupi lake lonse linali ngati wavala chovala chaubweya.+ Ndiye chifukwa chake anamutcha dzina lakuti Esau.*+ 26 Pambuyo pa iyeyu, panabadwa m’bale wake, dzanja lake litagwira chidendene cha Esau,+ choncho Isaki anapatsa mwanayo dzina lakuti Yakobo.+ Pamene Rabeka amabereka anawa n’kuti Isaki ali ndi zaka 60.

27 Anyamatawa anakula, ndipo Esau anakhala munthu wodziwa kusaka,+ munthu wokonda kuyenda m’tchire. Koma Yakobo anali kukhala nthawi yambiri m’mahema.+ Iye anali munthu wosalakwa.+ 28 Isaki anali kukonda kwambiri Esau chifukwa anali kum’phera nyama, koma Rabeka anali kukonda kwambiri Yakobo.+ 29 Tsiku lina Yakobo akuphika mphodza, Esau anafika kuchokera kutchire, ndipo anali atatopa. 30 Ndiyeno Esau anapempha Yakobo kuti: “Chonde, fulumira ndipatseko chakudya chofiiracho pang’ono, icho chofiiracho! Ndatopatu ine!” Ndiye chifukwa chake anatchedwa Edomu.*+ 31 Pamenepo Yakobo anayankha kuti: “Choyamba, undigulitse ukulu wako monga woyamba kubadwa.”+ 32 Esau anati: “Ine pano ndifa ndithu ndi njala, ndiye ukuluwo uli ndi phindu lanji kwa ine?” 33 Ndiyeno Yakobo anati: “Choyamba lumbira kwa ine!”+ Ndipo iye analumbiradi kwa Yakobo, n’kugulitsa kwa iye ukulu wake monga woyamba kubadwa.+ 34 Pamenepo Yakobo anapatsa Esau mkate ndi mphodza, ndipo iye anadya n’kumwa.+ Kenako, ananyamuka n’kumapita. Umu ndi mmene Esau ananyozera ukulu wake.+

26 Tsopano m’dzikomo munagwanso njala, kuwonjezera pa njala yoyamba ija imene inagwa m’masiku a Abulahamu.+ Choncho Isaki anapita kwa Abimeleki, mfumu ya Afilisiti, ku Gerari.+ 2 Ndiyeno Yehova anaonekera kwa iye,+ n’kumuuza kuti, “Usatsikire ku Iguputo. Umange mahema ako m’dziko limene ndikusonyeze.+ 3 Ukhale ngati mlendo m’dzikoli,+ ndipo ndidzapitiriza kukhala nawe ndi kukudalitsa, chifukwa mayiko onsewa ndidzawapereka kwa iwe ndi kwa mbewu yako.+ Ndidzakwaniritsa lumbiro limene ndinalumbirira Abulahamu bambo ako.+ 4 ‘Ndidzachulukitsa mbewu yako ngati nyenyezi zakumwamba, ndipo mayiko onsewa ndidzawapereka kwa mbewu yako.+ Mitundu yonse ya padziko lapansi idzapeza madalitso*+ ndithu kudzera mwa mbewu yako.’ 5 Zidzatero chifukwa Abulahamu anamvera mawu anga, ndipo anachita zofuna zanga ndi kusunga malamulo anga onse.”+ 6 Chotero Isaki anapita kukakhala ku Gerari.+

7 Anthu a kumeneko anali kufunsa za mkazi wake, ndipo iye anali kuwayankha kuti, “Ndi mlongo wanga.”+ Anali kuopa kunena kuti: “Ndi mkazi wanga,” chifukwa malinga ndi kunena kwake, anati: “Anthu a kuno andipha chifukwa cha Rabeka,” pakuti mkaziyo anali wokongola mochititsa kaso.+ 8 Patapita nthawi ali kumeneko, Abimeleki mfumu ya Afilisiti anali kuyang’ana pawindo, ndipo anaona Isaki akucheza mwachikondi ndi mkazi wake Rabeka.+ 9 Nthawi yomweyo Abimeleki anaitanitsa Isaki n’kumufunsa kuti: “Ameneyu ndi mkazi wako, eti? Nanga n’chifukwa chiyani unali kunena kuti, ‘Ndi mlongo wanga’?” Ndiyeno Isaki anayankha kuti: “Ndinali kunena choncho poopa kuti angandiphe chifukwa cha iye.”+ 10 Koma Abimeleki anapitiriza kuti: “N’chifukwa chiyani watichitira zoterezi?+ Pakanangopita kanthawi munthu wina akanagona naye mkazi wakoyu, ndipo ukanatipalamulitsa.”+ 11 Pamenepo Abimeleki analamula anthu ake onse kuti: “Aliyense amene akhudze munthuyu ndiponso mkazi wake, aphedwa.”

12 Zitatero, Isaki anayamba kubzala mbewu m’dzikomo.+ M’chaka chimenechi anakolola zochuluka moti pa mbewu zimene anabzala, anakolola zochuluka kuwirikiza nthawi 100,+ popeza Yehova anali kum’dalitsa.+ 13 Patapita nthawi, Isaki anakhala wolemera, ndipo chuma chake chinapitiriza kuchuluka mpaka anakhala wolemera kwambiri.+ 14 Iye anakhala ndi nkhosa ndi ng’ombe zankhaninkhani. Anakhalanso ndi antchito ochuluka kwambiri,+ moti Afilisitiwo anayamba kum’chitira kaduka.+

15 Zitsime zonse zimene antchito a Abulahamu bambo ake anakumba m’masiku a bambo akewo,+ Afilisiti anazifotsera ndi dothi.+ 16 Pamapeto pake, Abimeleki anauza Isaki kuti: “Utichokere kwathu kuno, chifukwa wakhala munthu wamphamvu kwambiri kuposa ifeyo.”+ 17 Choncho Isaki anachoka kumeneko n’kukamanga mahema ake m’chigwa* cha Gerari,+ n’kukhazikika kumeneko. 18 Kumeneko, Isaki anafukulanso zitsime za madzi zimene zinakumbidwa m’masiku a Abulahamu bambo ake. Afilisiti anafotsera zitsimezo Abulahamu atamwalira,+ ndipo iye anazitchanso mayina amene bambo ake anazipatsa.+

19 Antchito a Isaki anayamba kukumba m’chigwacho ndipo anapeza chitsime cha madzi abwino. 20 Koma abusa a ku Gerari anayamba kukangana ndi abusa a Isaki,+ kuti: “Ndi madzi athu amenewa!” Choncho iye anatcha chitsimecho Eseke,* chifukwa iwo anakangana naye. 21 Kenako iwo anakumbanso chitsime china, n’kukangananso za chitsimecho. Chitsimechi iye anachitcha Sitina. 22 Pambuyo pake, anasamukako kumeneko, n’kukakumbanso chitsime kwina.+ Koma pa chitsimechi, sanakanganepo. Chotero iye anachitcha Rehoboti,* n’kunena kuti: “Chifukwa chake n’chakuti, tsopano Yehova watipatsa malo okwanira,+ ndipo watichulukitsa m’dziko lino.”+

23 Kenako iye anachokanso kumeneko, n’kukwezeka mtunda kupita ku Beere-seba.+ 24 Usiku umenewo, Yehova anaonekera kwa iye ndipo anamuuza kuti: “Ine ndine Mulungu wa Abulahamu bambo ako.+ Usaope,+ chifukwa ndili nawe. Ndidzakudalitsa ndi kuchulukitsa mbewu yako chifukwa cha Abulahamu mtumiki wanga.”+ 25 Kumeneko Isaki anamanga guwa lansembe n’kuitana pa dzina la Yehova.+ Anamanganso mahema ake,+ ndipo antchito ake anakumba chitsime kumeneko.

26 Patapita nthawi, Abimeleki anafika kwa iye kuchokera ku Gerari. Anafika limodzi ndi Ahuzati bwenzi lake lapamtima, komanso Fikolo mkulu wa asilikali ake.+ 27 Pamenepo Isaki anawafunsa kuti: “Kodi n’chifukwa chiyani mwabwera kwa ine? Si paja inu munandida ine ndi kundipitikitsa kwanu kuja?”+ 28 Koma iwo anayankha kuti: “Ife taona kuti ndithu Yehova ali nawe.+ Choncho tinaganiza zokupempha kuti, ‘Chonde, tiye tilumbirirane,+ iwe ndi ife, ndipo tichite nawe pangano.+ 29 Tilumbirirane kuti sudzatichitira choipa chilichonse, pakuti ifenso sitinakukhudze. Tinakuchitira zabwino zokhazokha, mwa kukuchotsa kwathu mwamtendere.+ Tsopano Yehova wakudalitsa.’”+ 30 Pamenepo Isaki anawakonzera phwando, ndipo iwo anadya ndi kumwa.+ 31 M’mawa mwake, analawirira kudzuka n’kulumbiritsana.+ Kenako Isaki anatsanzikana nawo ndipo iwo anachoka kwa iye mwamtendere.+

32 Pa tsiku limenelo, antchito a Isaki anafika kwa iye n’kumuuza zokhudza chitsime chimene anakumba.+ Anamuuza kuti: “Madzi tawapeza.” 33 Chotero chitsimecho anachitcha Siba.* Ndiye chifukwa chake dzina la mzindawo ndi Beere-seba,+ mpaka lero.

34 Esau atakwanitsa zaka 40, anakwatira Yuditi mwana wa Beeri, Mhiti. Anakwatiranso Basemati mwana wa Eloni, Mhiti.+ 35 Akaziwo anabweretsa chisoni kwa Isaki ndi Rabeka.+

27 Tsopano Isaki anakalamba moti maso ake sanali kuonanso.+ Ndiyeno anaitanitsa mwana wake wamkulu Esau,+ n’kumuuza kuti: “Mwana wanga!” Iye anayankha kuti: “Ine bambo!” 2 Isaki anapitiriza kuti: “Taona, ine tsopano ndakalamba.+ Tsiku lililonse ndikhoza kufa.+ 3 Choncho tenga zida zako pompano. Utenge uta ndi kachikwama kako koikamo mivi ndipo upite kutchire ukandisakire nyama.+ 4 Udzaikonze kuti ikome mmene ndimaikondera muja n’kundibweretsera. Ndikufuna ndikhwasule, ndipo ndikudalitse ndisanafe.”+

5 Koma pamene Isaki anali kulankhula ndi mwana wake Esau, Rabeka anali kumvetsera. Chotero Esau anapita kutchire kuti akaphe nyama n’kubwera nayo.+ 6 Tsopano Rabeka anauza mwana wake Yakobo+ kuti: “Ndamva bambo ako akuuza mkulu wako Esau kuti, 7 ‘Ukandiphere nyama n’kuiphika bwino. Ndikufuna ndikhwasule, ndipo ndikudalitse pamaso pa Yehova ndisanafe.’+ 8 Tsopano mwana wanga, tamvera mawu anga, ndipo uchite zimene ndikuuze.+ 9 Pita kuli ziwetoko unditengereko ana a mbuzi awiri, onenepa bwino. Ndikufuna ndiwakonze mopatsa madyo mmene bambo ako amakondera muja. 10 Ndiye ukapereke kwa bambo ako akadye, kuti akudalitse asanamwalire.”

11 Pamenepo Yakobo anayankha Rabeka mayi ake kuti: “Koma m’bale wanga Esau ndi munthu wacheya,* pamene ine ndili ndi khungu losalala.+ 12 Nanga bambo akakandikhudza?+ Ndithu andiona ngati wachipongwe.+ Ndikatero, ndithu ndidzitengera ndekha temberero, osati madalitso.”+ 13 Koma mayi ake anamuyankha kuti: “Temberero limenelo libwere kwa ine m’malo mwa iwe mwana wanga.+ Ingomvera zimene ndanenazi. Pita ukanditengere ana a mbuziwo.”+ 14 Chotero iye anawatenga n’kubwera nawo kwa mayi ake. Mayiwo anaphika nyamayo mopatsa madyo mmene bambo ake ankaikondera. 15 Zitatero, Rabeka anatenga zovala zokongola koposa za mwana wake wamkulu Esau,+ zimene anali nazo m’nyumba.+ Zovalazo anaveka mwana wake wamng’ono, Yakobo.+ 16 Kenako, mayiwo anatenga zikopa za ana a mbuzi aja, n’kuveka Yakobo m’manja mwake ndi pakhosi pake popanda cheya.+ 17 Ndiyeno anapatsa mwana wake Yakobo chakudya chokoma chimene anakonzacho, limodzi ndi mkate umene anaphika.+

18 Tsopano Yakobo anapita kumene kunali bambo ake n’kunena kuti: “Bambo!” Ndipo Isaki anayankha kuti: “Ine pano! Ndiwe ndani kodi mwana wanga?” 19 Yakobo anapitiriza kunena kwa bambo ake kuti: “Ndine Esau, mwana wanu woyamba.+ Ndachita zonse zimene munandituma. Dzukani, khalani pansi mudye nyama imene ndakupherani, kuti mundidalitse.”+ 20 Pamenepo Isaki anafunsa mwana wake kuti: “Koma mwana wanga, waipeza bwanji mofulumira chonchi?” Iye anayankha kuti: “Yehova Mulungu wanu ndiye waikusira kwa ine kuti ndikumane nayo.” 21 Koma Isaki anauza Yakobo kuti: “Tayandikira ndikukhudze mwana wanga. Ndikufuna ndidziwe ngati ndiwedi mwana wanga Esau kapena ayi.”+ 22 Chotero Yakobo anafika pafupi ndi Isaki bambo ake. Atamukhudza ananena kuti: “Mawu, akumveka kuti ndi a Yakobo, koma manja, akumveka kuti ndi a Esau.”+ 23 Iye sanamuzindikire, chifukwa manja ake anali acheya ngati manja a Esau m’bale wake. Chotero anam’dalitsa.+

24 Kenako anamufunsanso kuti: “Koma ndiwedi mwana wanga Esau?” Iye anayankha kuti: “Ndine ndithu.”+ 25 Tsopano Isaki anati: “Mwana wanga, ndipatsire nyama imene wandiphera ndidye kuti ndikudalitse.”+ Choncho anamupatsira ndipo anayamba kudya. Anamupatsiranso vinyo iye n’kumwa. 26 Kenako bambo akewo anamuuza kuti: “Ndiyandikire mwana wanga, undipsompsone.”+ 27 Choncho anamuyandikira ndi kum’psompsona, ndipo anatha kumva kafungo ka zovala zake.+ Pamenepo anamudalitsa kuti:

“Eya, kafungo ka mwana wanga kakununkhira ngati fungo lokoma la munda umene Yehova waudalitsa. 28 Mulungu woona akupatse mame akumwamba,+ ndi nthaka yachonde ya dziko lapansi.+ Achulukitsenso zokolola zako ndi vinyo wako watsopano.+ 29 Mafuko akutumikire ndipo mitundu ya anthu ikugwadire.+ Ukhale mbuye wa abale ako, ndipo ana a mayi ako akugwadire.+ Aliyense wokutemberera atembereredwe, ndipo aliyense wokudalitsa adalitsidwe.”+

30 Tsopano Isaki atangomaliza kudalitsa Yakobo, ndipo Yakoboyo atangotuluka kumene kwa Isaki bambo ake, Esau m’bale wake anafika kuchokera kokasaka nyama.+ 31 Iyenso anakonzera bambo ake nyama ija mopatsa madyo. Kenako anapita nayo kwa bambo ake n’kuwauza kuti: “Bambo, dzukani mudye nyama imene ndakupherani ine mwana wanu, kuti mundidalitse.”+ 32 Ndiyeno Isaki, bambo ake, anati: “Nanga iwenso ndiwe ndani?” Ndipo iye anayankha kuti: “Ndine mwana wanu, mwana wanu woyamba Esau.”+ 33 Pamenepo Isaki anayamba kunjenjemera koopsa, ndipo anati: “Nanga ndani uja wandiphera nyama kutchire, imene wandibweretsera kuti ndidye? Ine ndadya yonse iwe usanabwere, moti ndamudalitsa iyeyo. Ndipo adzadalitsikadi!”+

34 Atamva mawu a bambo ake, Esau anayamba kulira ndi kukuwa mogonthetsa m’khutu, komanso mowawidwa mtima kwambiri.+ Iye anachonderera bambo ake kuti: “Bambo ndidalitseni, ndidalitseni inenso chonde!”+ 35 Pamenepo Isaki anapitiriza kunena kuti: “M’bale wako wabwera mwachinyengo, ndipo walandira madalitso omwe anali ako.”+ 36 Ndiyeno Esau anati: “Aka tsopano n’kachiwiri akundichenjerera amene uja!+ Kodi si chifukwa chake dzina lake ndi Yakobo?* Ukulu wanga anatenga kale,+ apa tsopano watenganso madalitso anga!”+ Iye anapitiriza kuti: “Kodi bambo, zoona palibiretu dalitso lililonse limene mwandisungirako?” 37 Koma Isaki anayankha Esau kuti: “Taona, iye uja ndamuika kukhala mbuye wako.+ Ndamupatsanso abale ake onse kuti akhale atumiki ake.+ Komanso ndam’dalitsira zokolola zake ndi vinyo wake watsopano.+ Nanga chatsalanso n’chiyani choti ndikuchitire mwana wanga?”

38 Pamenepo Esau anafunsa bambo ake kuti: “Bambo, ngakhale limodzi dalitso silinatsaleko? Bambo ndidalitseni, ndidalitseni inenso chonde!”+ Esau atatero analira mofuula kwambiri, misozi ili mbwembwembwe.+ 39 Koma Isaki bambo ake anamuuza kuti:

“Taona, udzakhala kutali ndi nthaka yachonde, kotalikirana ndi mame akumwamba.+ 40 Udzakhalira moyo lupanga+ ndipo udzatumikira m’bale wako.+ Koma ukadzatopa ndi goli lake, udzalithyola ndi kulichotsa m’khosi mwako.”+

41 Choncho, Esau anasunga chidani kwa Yakobo mumtima mwake.+ Anamuda chifukwa cha madalitso amene bambo ake anamupatsa. Iye anapitiriza kunena mumtima mwake+ kuti: “Masiku olira maliro a bambo anga ali pafupi.+ Pambuyo pake, ndidzamupha m’bale wanga Yakobo.”+ 42 Pamene Rabeka anauzidwa zimene mwana wake wamkulu Esau ananena, nthawi yomweyo anaitanitsa mwana wake wamng’ono Yakobo n’kumuuza kuti: “M’bale wako Esau akufuna akhazike mtima wake pansi pokubwezera. Iye akufuna kuti akuphe.+ 43 Tsopano, tamvera zimene ndikuuze mwana wanga.+ Nyamuka, thawira kwa Labani mlongo wanga, ku Harana.+ 44 Ukakhale naye kwa masiku ndithu, kufikira ukali wa m’bale wako utatha.+ 45 Ukakhaleko kufikira mkwiyo wa m’bale wako utaphwa, mpaka ataiwala zimene unamuchitira.+ Pamenepo ndidzatuma anthu kuti adzakutenge kumeneko. Kodi nditayirenji ana awiri pa tsiku limodzi?”

46 Zitatha izi, Rabeka anali kuuza Isaki nthawi ndi nthawi kuti: “Ndafika ponyansidwa nawo moyo wanga chifukwa cha ana aakazi achihetiwa.+ Ngati Yakobo atenga mkazi kuno pakati pa ana achiheti ngati amenewa, ndi bwino ndingofa!”+

28 Choncho, Isaki anaitana Yakobo ndipo anamudalitsa n’kumulamula kuti: “Usatenge mkazi pakati pa ana aakazi a ku Kanani.+ 2 Nyamuka, pita ku Padana-ramu kunyumba ya Betuele bambo a mayi ako. Kumeneko ukatenge mkazi pakati pa ana a Labani mlongo wa mayi ako.+ 3 Mulungu Wamphamvuyonse adzakudalitsa. Adzakupatsa ana ndipo adzawachulukitsa moti adzakhala mitundu yambiri ya anthu.+ 4 Adzakupatsa iwe ndi mbewu zako+ madalitso amene analonjeza Abulahamu,+ kuti udzakhale mwini dziko limene ukukhalamo ngati mlendo,+ limene Mulungu anapatsa Abulahamu.”+

5 Chotero Isaki anatumiza Yakobo, ndipo iye ananyamuka ulendo wopita ku Padana-ramu. Anapita kwa Labani mwana wa Betuele, Msiriya.+ Labaniyo anali mlongo wake wa Rabeka,+ mayi ake a Yakobo ndi Esau.+

6 Esau anaona kuti Isaki wadalitsa Yakobo, ndiponso kuti wam’tumiza ku Padana-ramu kukatenga mkazi kumeneko. Anaona kuti pomudalitsa anamulamula kuti: “Usatenge mkazi pakati pa ana aakazi a ku Kanani.”+ 7 Anaonanso kuti Yakobo wamvera bambo ake ndi mayi ake ndipo wapita ku Padana-ramu.+ 8 Pamenepo Esau anazindikira kuti, Isaki bambo ake, anali kuipidwa nawo ana aakazi a ku Kanani.+ 9 Chotero Esau anapita kwa Isimaeli* n’kukatengako mkazi kuwonjezera pa akazi amene anali nawo.+ Mkaziyo dzina lake anali Mahalati, ndipo anali mlongo wake wa Nebayoti. Mahalati anali mwana wa Isimaeli, mwana wa Abulahamu.

10 Yakobo anapitiriza ulendo wake wochokera ku Beere-seba kupita ku Harana.+ 11 Kenako anafika pamalo ena n’kuganiza zogona, popeza dzuwa linali litalowa. Chotero, anatenga mwala umodzi pamalopo n’kuuchita mtsamiro, n’kugona pamenepo.+ 12 Kenako anayamba kulota.+ M’malotowo anaona makwerero ochokera pansi mpaka kumwamba. Angelo a Mulungu anali kukwera ndi kutsika pamakwereropo.+ 13 Pamwamba pa makwererowo anaonapo Yehova, amene anamuuza kuti:+

“Ine ndine Yehova, Mulungu wa Abulahamu kholo lako, ndi Mulungu wa Isaki.+ Dziko limene wagonapoli ndidzalipereka kwa iwe ndi kwa mbewu yako.+ 14 Mbewu yako ndithu idzachuluka ngati mchenga wa padziko lapansi,+ ndipo ana ako adzafalikira kumadzulo, kum’mawa, kumpoto ndi kum’mwera.+ Komanso kudzera mwa iwe ndi mwa mbewu yako, mabanja onse a padziko lapansi adzapeza madalitso*+ ndithu. 15 Ine ndili nawe ndipo ndikuyang’anira pa ulendo wako wonse, kufikira ndidzakubwezera kumalo ano.+ Sindidzakusiya kufikira nditachitadi zimene ndanena kwa iwe.”+

16 Kenako Yakobo anagalamuka ku tulo take n’kunena kuti: “Ndithudi Yehova ali pamalo pano, koma ine sindinadziwe.” 17 Iye anachita mantha n’kunenanso kuti:+ “Malo ano ndi oopsa!+ Ndithu malo ano ndi nyumba ya Mulungu,+ ndiponso ndi khomo la kumwamba.” 18 Tsopano Yakobo anadzuka m’mawa kwambiri, n’kutenga mwala umene anautsamira uja, n’kuuimika monga mwala wachikumbutso. Atatero anauthira mafuta pamwamba.+ 19 Kenako, malowo anawatcha Beteli.+ Koma dzina lakale la mzindawo linali Luzi.+

20 Yakobo analonjeza+ kuti: “Ndithu ngati Mulungu adzakhalabe nane n’kundisungabe pa ulendo wangawu, ndiponso ngati adzandipatsadi chakudya ndi zovala,+ 21 komanso ngati ndidzabwereradi mwamtendere kunyumba ya bambo anga, pamenepo Yehova adzakhala atasonyezadi kuti ndi Mulungu wanga.+ 22 Mwala wachikumbutso umene ndauimika panowu, udzakhala nyumba ya Mulungu.+ Pa chilichonse chimene mudzandipatsa, sindidzalephera kukubwezerani chakhumi chake.”+

29 Kenako, Yakobo ananyamuka n’kupitiriza ulendo wake wopita Kum’mawa.+ 2 Atafika pamalo enaake anaona chitsime, ndipo panali magulu atatu a nkhosa zitagona pansi, chifukwa m’pamene anthu ankamwetsapo ziweto.+ Pachitsimepo+ panali potseka ndi mwala waukulu. 3 Nkhosa zonse zikafika pamalopo, abusa anali kugubuduza mwala kuuchotsa pachitsimepo n’kutungira nkhosazo madzi kuti zimwe. Akamaliza, anali kubwezeretsa mwalawo pachitsimepo.

4 Pamenepo Yakobo anawafunsa kuti: “Abale anga, kodi mwachokera kuti?” Iwo anayankha kuti: “Tachokera ku Harana.”+ 5 Iye anawafunsanso kuti: “Kodi Labani+ mdzukulu wa Nahori+ mumam’dziwa?” Iwo anati: “Inde timam’dziwa.” 6 Ndiyeno iye anawafunsa kuti: “Kodi iye ali bwino?”+ Iwo anayankha kuti: “Ali bwino. Komanso mwana wake Rakele,+ suyo akubwera apoyo ndi nkhosa?”+ 7 Kenako Yakobo anawauza kuti: “Inotu si nthawi yosonkhanitsa ziweto, ndi masanatu ano. Zimwetseni madzi, kenako mupite nazo kubusa.”+ 8 Iwo anayankha kuti: “Sitiloledwa kutero kufikira magulu onse a nkhosa atafika pano. Zikatero mwala wa pachitsimewu umachotsedwa, ndiyeno m’pamene timazimwetsa madzi nkhosazi.”

9 Akulankhula nawo choncho, Rakele+ anafika ndi nkhosa za bambo ake, popeza anali m’busa wamkazi.+ 10 Yakobo ataona Rakele mwana wa Labani, mlongo wa mayi ake, ndiponso nkhosa za Labaniyo, nthawi yomweyo anapita pachitsime paja, n’kugubuduza mwalawo kuuchotsa pachitsimepo. Atatero anatungira madzi nkhosa za Labani, mlongo wa mayi ake.+ 11 Ndiyeno Yakobo anapsompsona+ Rakele, n’kulira mofuula+ misozi ili mbwembwembwe. 12 Kenako anayamba kuuza Rakele kuti iye ndi wachibale+ wa bambo ake, ndiponso kuti ndi mwana wa Rabeka. Pamenepo Rakele anathamanga kukauza bambo ake.+

13 Tsopano Labani atangomva za Yakobo, mwana wa mlongo wake, anathamanga kukakumana naye.+ Atafika, anam’kumbatira ndi kum’psompsona, n’kupita naye kunyumba kwake.+ Kumeneko, Yakobo anafotokozera Labani zinthu zonse. 14 Ndiyeno Labani anamuuza kuti: “Ndithu, iwe ndiwe fupa langa ndi mnofu wanga.”+ Choncho anakhala naye mwezi wathunthu.

15 Kenako Labani anafunsa Yakobo kuti: “Kodi ukufuna undigwirire ntchito yaulere+ chifukwa chakuti ndiwe m’bale wanga?+ Ndiuze, kodi ndidzakulipire chiyani?”+ 16 Labani anali ndi ana aakazi awiri, wamkulu Leya,+ wamng’ono Rakele. 17 Leya anali ndi maso ofooka, pamene Rakele+ anali chiphadzuwa.+ 18 Koma Yakobo anakonda Rakele, ndiye anati: “Ndine wokonzeka kukugwirirani ntchito zaka 7, kuti mudzandipatse Rakele mwana wanu wamng’onoyu.”+ 19 Pamenepo Labani anati: “Kuli bwino Rakeleyu ndikupatse iweyo, kusiyana n’kuti ndipatse munthu wina.+ Uzikhalabe ndi ine.” 20 Yakobo anagwira ntchito zaka 7 kuti atenge Rakele.+ Koma iye anangoziona zakazo ngati masiku ochepa chabe, chifukwa anam’konda kwambiri mtsikanayo.+

21 Kenako Yakobo anauza Labani kuti: “Ndipatseni mkazi wanga, chifukwa masiku anga akwana, kuti ndim’kwatire.”*+ 22 Pamenepo Labani anasonkhanitsa anthu onse a kumeneko n’kuchita phwando.+ 23 Koma madzulo kutada, Labani anatenga Leya mwana wake n’kupita naye kwa Yakobo, ndipo iye anagona naye. 24 Labani anatenganso Zilipa+ kapolo wake, n’kumupereka kwa mwana wake Leya, kuti akhale kapolo wake. 25 Koma kutacha m’mawa, Yakobo anadabwa kuona kuti ali ndi Leya! Ataona zimenezi anakafunsa Labani kuti: “Ndiye chiyani mwachitachi? Kodi si Rakele amene ndakugwirirani ntchito? N’chifukwa chiyani mwandipusitsa chonchi?”+ 26 Labani anayankha kuti: “Kwathu kuno, mwambo sulola kukwatitsa wamng’ono mkulu wake asanakwatiwe. 27 Usangalale+ mokwanira ndi mkaziyu mlungu wonse wokondwerera ukwati wake. Kenako ndidzakupatsa mkazi winayu, komatu udzandigwirira ntchito zaka zina 7.”+ 28 Chotero Yakobo anasangalaladi mokwanira ndi Leya mlungu wonse wokondwerera ukwati wake. Kenako, Labani anam’patsa mwana wake Rakele ngati mkazi wake. 29 Anaperekanso kapolo wake Biliha+ kwa mwana wake Rakele kuti akhale kapolo wake.

30 Ndiyeno Yakobo anagonanso ndi Rakele, ndipo anam’konda kwambiri Rakele kuposa Leya.+ Motero anagwiriranso ntchito Labani zaka zina 7.+ 31 Yehova ataona kuti Leya sanali kukondedwa kwenikweni, anam’patsa mphamvu zobereka,+ koma Rakele anali wosabereka.+ 32 Kenako Leya anakhala ndi pakati n’kubereka mwana wamwamuna. Mwanayo anamutcha Rubeni,*+ popeza anati: “N’chifukwa chakuti Yehova waona kusautsika kwanga,+ ndipo tsopano mwamuna wanga ayamba kundikonda kwambiri.” 33 Leya anakhalanso ndi pakati n’kubereka mwana wamwamuna, ndipo anati: “Yehova wandipatsa mwana wina chifukwa wandimvera+ kuti sindikukondedwa kwenikweni.” Choncho mwanayo anamutcha Simiyoni.*+ 34 Anakhalanso ndi pakati pena n’kubereka mwana wamwamuna, ndipo anati: “Apa tsopano mwamuna wanga andikonda basi, chifukwa ndamuberekera ana aamuna atatu.” Choncho mwanayo anamutcha Levi.*+ 35 Anakhalanso ndi pakati pena n’kubereka mwana wamwamuna, ndipo anati: “Tsopano nditamanda Yehova.” Choncho Leya anatcha mwanayo, Yuda.*+ Atabereka mwana ameneyu, anayamba waleka kubereka.

30 Ndiyeno Rakele ataona kuti sanaberekere Yakobo mwana, anayamba kuchitira nsanje m’bale wake. Iye anauza Yakobo+ kuti: “Mundipatse ana, apo ayi kuli bwino ndingofa.”+ 2 Pamenepo Yakobo anamupsera mtima kwambiri Rakele n’kumuyankha kuti:+ “Kodi ine ndine Mulungu amene akukulepheretsa kuberekayo?”+ 3 Kenako Rakele anati: “Nayu kapolo wanga Biliha.+ Mugone naye kuti andiberekere mwana woti akhale wanga,* kuti ineyonso ndikhale ndi ana kuchokera kwa iye.”+ 4 Choncho Rakele anapereka Biliha kapolo wake kwa Yakobo, ndipo Yakobo anagona nayedi.+ 5 Chotero Biliha anakhala ndi pakati ndipo patapita nthawi anam’berekera Yakobo mwana wamwamuna.+ 6 Zitatero, Rakele anati: “Mulungu wakhala monga woweruza+ wanga ndipo wamvera mawu anga, choncho wandipatsa mwana wamwamuna.” N’chifukwa chake Rakele anatcha mwanayo dzina lakuti Dani.*+ 7 Biliha kapolo wa Rakele anakhalanso ndi pakati moti patapita nthawi anam’berekera Yakobo mwana wina wamwamuna. 8 Ndiyeno Rakele anati: “Ndalimbana mwamphamvu ndi m’bale wanga ndipo ndapambananso.” Chotero anatcha mwanayo dzina lakuti Nafitali.*+

9 Leya ataona kuti wasiya kubereka, anapereka kapolo wake Zilipa kwa Yakobo kuti akhale mkazi wake.+ 10 Patapita nthawi, Zilipa kapolo wa Leya anaberekera Yakobo mwana wamwamuna. 11 Pamenepo Leya anati: “Ndachita mwayi!” Chotero anatcha mwanayo dzina lakuti Gadi.*+ 12 Kenako, Zilipa kapolo wa Leya anaberekera Yakobo mwana wina wamwamuna. 13 Mwanayo atabadwa, Leya anati: “Ndasangalala kwambiri! Akazi adzanditcha wodala.”+ Chotero Leya anatcha mwanayo dzina lakuti Aseri.*+

14 Pa nthawi yokolola tirigu,+ Rubeni+ anapita kutchire kukayenda. Kumeneko anapezako zipatso za mandereki,* ndipo anawatenga n’kupita nawo kwa Leya mayi ake. Ndiyeno Rakele anapempha Leya kuti: “Chonde, ndigawireko mandereki+ a mwana wakowa.” 15 Pamenepo, Leya anayankha Rakele kuti: “Kodi ukuyesa ndi nkhani yaing’ono kuti iweyo unatenga mwamuna wanga?+ Tsopano ukufuna kutenganso mandereki a mwana wanga?” Ndipo Rakele anati: “Pa chifukwa chimenechi, usiku walero mwamunayu agona ndi iwe kuti tisinthane ndi mandereki a mwana wakowa.”

16 Pamene Yakobo anali kuchokera kumunda madzulo,+ Leya anakamuchingamira n’kumuuza kuti: “Lero mugona ndi ine, chifukwa ine ndakugulani ndithu ndi mandereki a mwana wanga.” Usiku umenewo Yakobo anagonadi ndi Leya.+ 17 Mulungu anamvera Leya n’kumuyankha, ndipo anakhala ndi pakati. Patapita nthawi, Leya anaberekera Yakobo mwana wamwamuna wachisanu.+ 18 Mwanayo atabadwa, Leya anati: “Mulungu wandipatsa mphoto chifukwa ndapereka kapolo wanga kwa mwamuna wanga.” Chotero Leya anatcha mwanayo dzina lakuti Isakara.*+ 19 Leya anakhalanso ndi pakati, moti patapita nthawi anaberekera Yakobo mwana wamwamuna wa 6.+ 20 Ndiyeno Leya anati: “Mulungu wandipatsadi mphoto yabwino. Tsopano mwamuna wanga ayamba kukondwera nane,+ chifukwa ndam’berekera ana aamuna 6.”+ Chotero Leya anatcha mwanayo dzina lakuti Zebuloni.*+ 21 Kenako, Leya anabereka mwana wamkazi ndipo anamutcha kuti Dina.+

22 Potsirizira pake, Mulungu anakumbukira Rakele ndipo anamumvera n’kumuyankha mwa kum’patsa mphamvu zobereka.+ 23 Rakele anakhala ndi pakati n’kubereka mwana wamwamuna. Ndiyeno iye anati: “Mulungu wandichotsera chitonzo.”+ 24 Chotero Rakele anatcha mwanayo dzina lakuti Yosefe,*+ ndipo anati: “Yehova wandiwonjezera mwana wina wamwamuna.”

25 Rakele atabereka Yosefe, nthawi yomweyo Yakobo anauza Labani kuti: “Ndiloleni ndizipita kwathu, kudziko lakwathu.+ 26 Ndipatseni akazi anga ndi ana anga amene ndakugwirirani ntchito kuti ndizipita, pakuti inuyo mukudziwa ntchito imene ndakugwirirani.”+ 27 Koma Labani anauza Yakobo kuti: “Ngati wandikomera mtima, ungokhala konkuno. Ndaombeza maula ndipo ndapeza kuti Yehova akundidalitsa chifukwa cha iwe.”+ 28 Anatinso: “Ndiuze malipiro ako ndipo ndikupatsa.” + 29 Yakobo anamuyankha Labani kuti: “Inuyo mukudziwa ntchito imene ndakugwirirani, ndiponso mmene ndasamalira ziweto zanu.+ 30 Mukudziwa kuti ine ndisanabwere munali ndi zochepa. Tsopano onani mmene Yehova wakudalitsirani ndi mmene zachulukira kuchokera pamene ndinabwera.+ Ndiye kodi ineyo ndidzayamba liti kugwirira ntchito banja langa?”+

31 Kenako Labani anati: “Ndikupatse chiyani?” Yakobo anayankha kuti: “Musandipatse kanthu.+ Koma mukachita zimene ndikupempheni pano, ndiyambiranso kuweta ziweto zanu,+ ndipo ndipitiriza kuziyang’anira.+ 32 Ine ndipita kukayenda pakati pa ziweto zanu zonse lero. Inuyo mukapatule nkhosa iliyonse yamathothomathotho kapena yamawangamawanga, ndi nkhosa iliyonse yaing’ono yamphongo yofiirira, ndi mbuzi iliyonse yaikazi yamawangamawanga kapena yamathothomathotho. Ngati ziweto zoterozo zidzabadwe pambuyo pake, ndizo zidzakhale malipiro anga.+ 33 Tsiku lililonse limene mudzabwere kudzaona malipiro+ anga, mudzaona chilungamo changa. Mukadzapeza mbuzi iliyonse yaikazi yopanda mathothomathotho kapena mawangamawanga, ndi nkhosa iliyonse yaing’ono yamphongo yomwe si yofiirira ili ndi ine, imeneyo ndiye kuti ndaba.”+

34 Pamenepo Labani anati: “Chabwino, zikhale monga waneneramo.”+ 35 Chotero tsiku lomwelo, Labani anapatula mbuzi zamphongo zamizeremizere ndi zamawangamawanga, ndiponso mbuzi zonse zazikazi zamathothomathotho ndi zamawangamawanga pakati pa ziweto zake. Anapatulanso nkhosa iliyonse imene inali ndi banga loyera ndi nkhosa iliyonse yamphongo yaing’ono yofiirira, n’kuzipereka kwa ana ake. 36 Atatero anapita ndi ziweto zakezo kumalo amene anali pamtunda woyenda masiku atatu kuchokera pamene panali ziweto za Yakobo. Yakobo anapitiriza kuweta ziweto zotsala za Labani.

37 Ndiyeno Yakobo anatenga timitengo+ tatiwisi ta mtengo wa mlanje,+ ta mtengo wa amondi+ ndi ta mtengo wa katungulume,+ n’kutisenda makungwa mwa apo ndi apo, mwakuti choyera chamkati mwake chinaonekera. 38 Potsirizira pake, anatenga timitengo timene anatisendasenda tija n’kutiika m’ngalande zimene ziweto zimamwera madzi.+ Anatiika mmenemo kuti ziweto zikabwera kudzamwa madzi, zazikazi zikaona timitengoto zizitentha thupi kukonzekera kutenga bere.

39 Motero ziweto zazikazi zikaona timitengoto zinali kutenthadi thupi kukonzekera kutenga bere. Zikatero, zinali kuswa ana amizeremizere ndi amawangamawanga.+ 40 Kenako, Yakobo anachotsapo nkhosa zamphongo zing’onozing’ono n’kuziika pazokha. Atatero, anapatula nkhosa zonse zamizeremizere ndi zofiirira zimene zinali pakati pa ziweto za Labani. Kenako anatembenuza nkhosa zotsalazo kuti ziyang’ane zamizeremizere ndi zofiirira zija. Iye anaika ziweto zake pazokha, ndipo sanaziphatikize ndi ziweto za Labani. 41 Nthawi zonse ziweto zazikazi zamphamvu+ zikatentha thupi, Yakobo anali kuika timitengo tija m’ngalande momwera madzi+ kuti nkhosazo zitiyang’ane pamene zili zotentha thupi. 42 Koma nkhosazo zikakhala zofooka, iye sanali kuika timitengo tija momwera madzimo. Chotero, nthawi zonse nkhosa zofooka zinali za Labani koma zamphamvu zinali za Yakobo.+

43 Chuma cha Yakobo chinapitirira kuwonjezeka. Iye anakhala ndi ziweto zambiri, antchito aakazi ndi aamuna, ngamila ndi abulu.+

31 Patapita nthawi, Yakobo anamva zimene ana aamuna a Labani anali kunena, kuti: “Yakobo watenga chilichonse cha bambo athu, ndipo chuma chonse chimene wasonkhanitsachi chachokera kwa bambo athu.”+ 2 Tsopano Yakobo anaona kuti Labani sanali kumuyang’ana ndi diso labwino ngati poyamba.+ 3 Potsirizira pake Yehova anauza Yakobo kuti: “Tsopano bwerera kudziko la makolo ako ndi kwa abale ako,+ ndipo ine ndidzakhalabe nawe.”+ 4 Ndiyeno Yakobo anaitanitsa Rakele ndi Leya, kuti abwere kubusa kumene iye anali ndi nkhosa zake. 5 Iye anawauza kuti:

“Ndikuona kuti bambo anu sakundiyang’ana ndi diso labwino ngati poyamba,+ koma Mulungu wa bambo anga sanandisiye.+ 6 Inunso mukudziwa ndithu, kuti ndagwirira ntchito bambo anu ndi mphamvu zanga zonse.+ 7 Koma bambo anu akhala akundipusitsa, ndipo asintha malipiro anga maulendo 10. Ngakhale ndi choncho, Mulungu sanawalole kuti andichite choipa.+ 8 Nthawi zonse Labani akanena kuti, ‘Zamawangamawanga ndizo zidzakhala malipiro ako,’ ziweto zonse zinali kubereka zamawangamawanga. Akanena kuti, ‘Zamizeremizere ndizo zidzakhala malipiro ako,’ ziweto zonse zinali kubereka zamizeremizere.+ 9 Mulungu anali kuchotsa ziweto kwa bambo anu n’kuzipereka kwa ine.+ 10 Pamene ziweto zinali m’nthawi yotentha thupi kukonzekera kutenga bere, ndinakweza maso anga n’kuona m’maloto+ mbuzi zamphongo zikukwera zazikazi. Mbuzi zamphongozo zinali zamizeremizere, zamawangamawanga ndi zamathothomathotho.+ 11 Kenako, mngelo wa Mulungu woona anandiitana m’malotowo kuti, ‘Yakobo!’ Ine ndinayankha kuti, ‘Ine pano.’+ 12 Iye anapitiriza kuti, ‘Kweza maso ako ndipo ona kuti mbuzi zonse zamphongo zimene zikukwerazi ndi zamizeremizere, zamawangamawanga ndiponso zamathothomathotho. Ndachita zimenezi chifukwa ndaona zonse zimene Labani akuchita kwa iwe.+ 13 Ndine Mulungu woona wa ku Beteli+ uja, kumene unadzoza mwala+ kuja, kumenenso unachita lonjezo kwa ine.+ Tsopano nyamuka, uchoke kudziko lino, ubwerere kudziko limene unabadwira.’”+

14 Pamenepo Rakele ndi Leya anamuyankha kuti: “Kodi ifeyo tatsala ndi cholowa chilichonse m’nyumba ya bambo athu ngati?+ 15 Kodi iwowa sakutiona ife ngati alendo? Bambowa anatigulitsa ndipo akupitiriza kudya ndalama zimene inu munatiperekera.+ 16 Pakuti chuma chonse chimene Mulungu watenga kwa bambo athuwa, ndi chathu ndi cha ana athu.+ Ndiye chilichonse chimene Mulungu wakuuzani, chitani.”+

17 Ndiyeno Yakobo ananyamuka n’kukweza ana ake ndi akazi ake pangamila.+ 18 Kenako, anayamba kukusa ziweto zake zonse, ndi kutenganso katundu wake yense amene anapeza+ ku Padana-ramu, n’kunyamuka ulendo wopita kudziko la Kanani kwa bambo ake Isaki.+

19 Pa nthawiyi n’kuti Labani atapita kukameta ubweya wa nkhosa zake. Akali kumeneko, Rakele anaba aterafi*+ a bambo ake. 20 Chotero Yakobo anachoka mozembera Labani Msiriya uja, chifukwa sanamuuze kuti akuchoka. 21 Yakobo anathawa n’kuwoloka Mtsinje*+ limodzi ndi zonse zimene anali nazo. Atatero, anayenda molunjika dera la kumapiri la Giliyadi.+ 22 Pa tsiku lachitatu, Labani anamva kuti Yakobo wathawa. 23 Atamva zimenezo, iye anatenga abale ake n’kuyamba kuthamangira+ Yakobo. Iwo anayenda ulendo wa masiku 7, ndipo anamupeza m’dera la kumapiri la Giliyadi. 24 Koma usiku m’maloto,+ Mulungu anafikira Labani Msiriyayo+ n’kumuuza kuti: “Samala kuti usanene chilichonse chosokoneza zochita za Yakobo.”+

25 Kenako Labani anapita kwa Yakobo. Pa nthawiyi n’kuti Yakobo atamanga hema wake m’dera la kumapiri la Giliyadi, ndipo Labani ndi abale ake anamanganso hema wawo m’dera lomwelo. 26 Ndiyeno Labani anafunsa Yakobo kuti: “Ndiye chiyani wachitachi, kuchoka mondizembera, n’kutenga ana anga aakazi ngati akapolo ogwidwa kunkhondo?+ 27 N’chifukwa chiyani wathawa mwamseri, kundizembera osandiuza? Bwenzi nditatsanzikana nawe mosangalala, nyimbo zikuimbidwa,+ ndiponso maseche ndi azeze akulira.+ 28 Sunandipatse mpata woti ndipsompsone adzukulu anga ndi ana anga.+ Zimene wachitazi n’zopusa. 29 Ndikanatha kukuchitani choipa anthu inu,+ koma Mulungu wa bambo anu analankhula nane usiku wapitawu kuti, ‘Samala kuti usanene chilichonse chosokoneza zochita za Yakobo.’+ 30 Ngati wachoka chifukwa cholakalaka kwambiri kunyumba kwa bambo ako, nanga n’chifukwa chiyani waba milungu yanga?”+

31 Poyankha, Yakobo anauza Labani kuti: “Ndinachoka chozemba chifukwa ndinachita mantha.+ Ndinaganiza kuti mungandilande ana anu. 32 Aliyense amene mum’peze ndi milungu yanu aphedwe.+ Pamaso pa abale athuwa, fufuzani milungu yanuyo pa katundu wathu. Mukaipeza muitenge.”+ Koma Yakobo sanadziwe kuti Rakele anali ataba milunguyo.+ 33 Pamenepo Labani anakalowa muhema wa Yakobo, ndi muhema wa Leya, ndiponso muhema wa akapolo aakazi awiri aja,+ koma sanaipeze. Potsirizira pake, anatuluka muhema wa Leya n’kukalowa muhema wa Rakele. 34 Rakele anali atatenga aterafi aja n’kuwabisa m’chishalo choika pangamila, n’kuchikhalira. Labani anafunafuna muhema monsemo, koma sanawapeze aterafiwo. 35 Kenako Rakele anauza bambo ake kuti: “Musakwiye nane mbuyanga+ poti sindikutha kunyamuka pano. Kungoti sindili bwino malinga ndi chikhalidwe chathu akazife.”+ Labani anapitiriza kufunafuna mosamala, koma sanawapeze aterafiwo.+

36 Ndiyeno Yakobo anapsa mtima+ n’kuyamba kukangana ndi Labani n’kumufunsa kuti: “Kodi ndakupandukirani motani,+ ndakuchimwirani chiyani kuti muchite kundilondola mwaukali chonchi?+ 37 Popeza tsopano mwafunafuna m’katundu wanga yense, kodi n’chiyani chimene mwapezapo pa katundu yense wa m’nyumba mwanu?+ Chiikeni apa pamaso pa abale anga ndi abale anu,+ kuti iwo atiweruze.+ 38 Pa zaka 20 zonsezi zimene ndakhala nanu, nkhosa zanu zazikazi ndi mbuzi zanu zazikazi sizinaberekepo mwana wakufa.+ Ndiponso, chikhalire sindinadyeko ndi imodzi yomwe ya nkhosa zanu zamphongo. 39 Nyama yanu iliyonse imene inakhadzulidwa ndi chilombo sindinaibweretse kwa inu.+ Ndinali kuitenga kukhala yanga. Kaya ina ibedwe usana kapena usiku, munali kundiuza kuti ndikulipireni.+ 40 Ndinkangokhalira kutenthedwa ndi dzuwa usana ndi kuzizidwa ndi mphepo usiku, ndipo tulo sindinkationa.+ 41 Zonse pamodzi ndakhala zaka 20 m’nyumba mwanu. Ndakugwirirani ntchito zaka 14, kugwirira ana anu aakazi awiriwa. Zaka zinanso 6, ndagwirira ntchito ziweto. Koma inu munapitiriza kusinthasintha malipiro anga mpaka maulendo 10.+ 42 Mulungu wa bambo anga,+ Mulungu wa Abulahamu, Mulungu amene Isaki anali kumuopa,+ akanapanda kukhala kumbali yanga, bwenzi mutandibweza kwathu chimanjamanja. Koma Mulungu waona kusautsika kwanga ndi ntchito zimene ndagwira molimbika, n’chifukwa chake anakudzudzulani usiku wapitawu.”+

43 Ndiyeno Labani anamuyankha Yakobo kuti: “Ana aakaziwa ndi ana anga, ana awo ndi ana anga, ziwetozi ndi ziweto zanga, ndipo chilichonse chimene ukuchiona ndi cha ine ndi ana anga aakaziwa. Kodi iwowa, kapena ana awo amene anabereka, ndingawachitire choipa lero chifukwa chiyani? 44 Tiye tichite pangano+ ine ndi iwe, kuti likhale mboni pakati pa ine ndi iwe.”+ 45 Pamenepo Yakobo anatenga mwala n’kuuimika ngati mwala wachikumbutso.+ 46 Kenako Yakobo anauza abale ake kuti: “Tengani miyala!” Iwo anatenga miyala n’kuiunjika mulu.+ Atatero, anadyera chakudya pamulu wa miyalapo. 47 Labani anatcha mulu wa miyalawo Yegara-sahaduta,* koma Yakobo anautcha Galeeda.*

48 Labani anapitiriza kulankhula kuti: “Mulu wa miyalawu ndi mboni yathu lero pakati pa ine ndi iwe.” N’chifukwa chake unatchedwa Galeeda,+ 49 ndiponso kuti Nsanja ya Mlonda, chifukwa Labani anati: “Yehova aziyang’anira iwe ndi ine tikasiyana pano.+ 50 Ukamakazunza ana angawa,+ ndipo ukakatenga akazi ena kuwonjezera pa ana anga, ngakhale palibe munthu pano, dziwa kuti Mulungu ndiye mboni pakati pa ine ndi iwe.”+ 51 Labani anauzanso Yakobo kuti: “Ona mulu wa miyala ndiponso mwala wachikumbutso umene ndaimika monga chizindikiro cha pangano la pakati pa ine ndi iwe. 52 Muluwu ndiponso mwala wachikumbutsowu ndi mboni.+ Zikuchitira umboni kuti, pakati pa ine ndi iwe, wina sadzadutsa muluwu ndi mwala wachikumbutsowu kukachitira mnzake choipa.+ 53 Atiweruze mulungu wa Abulahamu,+ mulungu wa Nahori,+ yemwe ali mulungu wa bambo awo.” Koma Yakobo analumbira pa Mulungu amene bambo ake Isaki anali kumuopa.+

54 Pambuyo pake, Yakobo anapereka nsembe m’phirimo n’kuitana abale ake kuti adye chakudya.+ Motero iwo anadya chakudya n’kugona m’phirimo usiku umenewo. 55 Ndiyeno Labani anadzuka m’mamawa n’kupsompsona+ adzukulu ake ndi ana ake aakazi ndipo anawadalitsa.+ Atatero, ananyamuka kubwerera kwawo.+

32 Nayenso Yakobo ananyamuka, koma ali m’njira, angelo a Mulungu anakumana naye.+ 2 Yakobo atangowaona, anati: “Ilitu ndi gulu la Mulungu!”+ Chotero malowo anawatcha kuti Mahanaimu.*+

3 Kenako Yakobo anatsogoza amithenga+ ake powatumiza kwa Esau m’bale wake, kudziko la Seiri,+ kudera la Edomu.+ 4 Anawalamula kuti: “Mukafika kwa mbuyanga+ Esau, mukanene kuti, ‘Kapolo wanu Yakobo wanena kuti: “Ndinali kukhala ndi Labani monga mlendo, ndipo ndakhala kumeneko nthawi yaitali mpaka leroli.+ 5 Tsopano ndili ndi ng’ombe, abulu, nkhosa, komanso antchito aamuna ndi aakazi.+ Ndatumiza amithenga kwa mbuyanga kukupemphani kuti mundikomere mtima.”’”+

6 Amithengawo atabwerako, anauza Yakobo kuti: “Tinakafika kwa m’bale wanu Esau, ndipo iyenso ali m’njira kudzakumana nanu. Akubwera limodzi ndi amuna 400.”+ 7 Atamva zimenezi, Yakobo anachita mantha ndi kuda nkhawa kwambiri.+ Chotero anagawa anthu amene anali nawo m’magulu awiri, kuphatikizapo nkhosa, mbuzi, ng’ombe ndi ngamila.+ 8 Kenako anati: “Ngati Esau angafikire gulu limodzi kuti alithire nkhondo, gulu linalo lingathe kuthawa.”+

9 Atatero, Yakobo anati: “Mulungu wa kholo langa Abulahamu, Mulungu wa bambo anga Isaki,+ inu Yehova munandiuza kuti, ‘Bwerera kudziko lakwanu, kwa abale ako, ndipo ndidzakusamalira.’+ 10 Ine ndine wosayenerera kukoma mtima kosatha ndi kukhulupirika konseku, kumene mwandionetsa ine mtumiki wanu.+ Ndinawoloka Yorodano ndilibe kanthu, koma ndodo yokha, ndipo tsopano ndili ndi magulu awiriwa.+ 11 Ndapota nanu, ndipulumutseni+ ku dzanja la m’bale wanga, dzanja la Esau. Ndikuchita naye mantha kuti akafika, ndithu angavulaze ineyo,+ akaziwa pamodzi ndi anawa. 12 Inuyotu munanena kuti, ‘Mosakayikira m’pang’ono pomwe ndidzakusamalira, ndipo ndidzachulukitsa mbewu yako ngati mchenga wa kunyanja, umene suwerengeka kuchuluka kwake.’”+

13 Tsiku limeneli Yakobo anagona pamalopo. Kenako pa chuma chake anapatulapo zinthu zoti akapatse m’bale wake Esau ngati mphatso.+ 14 Anapatula mbuzi zazikazi 200 ndi mbuzi zamphongo 20, nkhosa zazikazi 200 ndi zamphongo 20. 15 Anapatulanso ngamila zoyamwitsa 30 ndi ana ake, ng’ombe zazikazi 40 ndi nkhuzi 10, abulu aakazi 20 ndi amphongo 10.+

16 Atatero anapatsa anyamata ake magulu a ziwetozo, gulu lililonse palokha. Kenako anawalangiza mobwerezabwereza kuti: “Tsogolani muwoloke mtsinje, ndipo muzisiya mpata pakati pa gulu lililonse la ziweto.”+ 17 Ndiyeno analangiza mnyamata woyamba kuti: “Ngati angakumane nawe Esau m’bale wanga n’kukufunsa kuti, ‘Kodi mbuyako ndani? Ndipo ukupita kuti? Nanga ziweto zimene ukukusazi n’zandani?’ 18 Ukayankhe kuti, ‘Mbuyanga ndi Yakobo kapolo wanu. Ziwetozi ndi mphatso+ imene iye watumiza kwa inu mbuyanga+ Esau. Iyeyo ali m’mbuyo mwathumu.’” 19 Analamulanso mnyamata wachiwiri ndi wachitatu, komanso ena onse amene anawagawira ziwetozo kuti atsogole nazo, kuti: “Zimene ndanenazi mukalankhule kwa Esau pokumana naye.+ 20 Mukamuuzenso kuti, ‘Ndiponso kapolo wanu Yakobo ali m’mbuyo mwathumu.’”+ Popeza mumtima mwake anati: “Mwina ndingamusangalatse potsogoza mphatsoyi,+ ndipo pambuyo pake ndingathe kuonana naye pamasom’pamaso, kuti mwina angandilandire bwino.”+ 21 Choncho mphatsoyo inatsogola ndipo anawoloka nayo. Koma usikuwo, iye anagona pamsasapo.+

22 Usiku umenewo, iye anadzuka n’kutenga akazi ake awiri aja,+ akapolo ake awiri,+ ndi ana ake aamuna 11,+ n’kuwoloka powolokera mtsinje wa Yaboki.+ 23 Atawawolotsera kutsidya kwa chigwacho,*+ anawolotsanso zonse zimene anali nazo.

24 Potsirizira pake, Yakobo anatsala yekhayekha. Kenako, munthu winawake anayamba kulimbana naye usiku wonse mpaka m’bandakucha.+ 25 Munthuyo ataona kuti Yakobo sakugonja,+ anamugwira nsukunyu* yake, ndipo nsukunyuyo inaguluka polimbana naye.+ 26 Atatero anauza Yakobo kuti: “Ndileke ndizipita, chifukwa kukucha tsopano.” Koma Yakobo anayankha kuti: “Sindikuleka, kufikira utandidalitsa choyamba.”+ 27 Ndiyeno munthuyo anamufunsa kuti: “Dzina lako ndani?” Iye anayankha kuti, “Yakobo.” 28 Kenako munthuyo anati: “Dzina lako silikhalanso Yakobo, koma Isiraeli,*+ pakuti walimbana+ ndi Mulungu ndi anthu, ndipo potsirizira pake wapambana.” 29 Nayenso Yakobo anafunsa kuti: “Nawenso ndiuze dzina lako.” Koma iye anati: “Ukufunsiranji dzina langa?”+ Atatero, anamudalitsa pamalo amenewo. 30 Chotero Yakobo anatcha malowo Penieli,*+ chifukwa iye anati, “Ndaonana ndi Mulungu pamasom’pamaso, komabe ndapulumuka.”+

31 Dzuwa linali litatuluka pamene Yakobo anali kuchoka pa Penueli, koma anali kuyenda chotsimphina.+ 32 Pa chifukwa chimenechi, ana a Isiraeli sadya mnyewa wa pansukunyu kufikira lero, chifukwa ndi umene munthu uja anagwira pogulula nsukunyu ya Yakobo.+

33 Tsopano Yakobo anakweza maso ake n’kuona Esau akubwera limodzi ndi amuna 400.+ Ataona choncho, anagawa ana ake n’kuwapereka kwa Leya, kwa Rakele, ndi kwa akapolo ake awiri aja.+ 2 Akapolowo ndi ana awo anawaika patsogolo penipeni,+ Leya ndi ana ake anawaika pakati,+ ndipo Rakele ndi Yosefe anawaika pambuyo.+ 3 Koma iyeyo anapita patsogolo pawo, n’kuyamba kugwada, n’kumaweramitsa nkhope yake pansi mpaka nthawi 7. Anachita zimenezi mpaka kufika pafupi ndi m’bale wakeyo.+

4 Esau anathamanga kudzakumana naye,+ ndipo anamukumbatira+ ndi kum’psompsona. Atakumbatirana, onse awiri anagwetsa misozi kwambiri. 5 Kenako, Esau anakweza maso ake n’kuona akazi ndi ana. Ndiyeno anafunsa Yakobo kuti: “Nanga amene uli nawowa ndani?” Iye anayankha kuti: “Amenewa ndi ana amene Mulungu wapatsa ine kapolo wanu.”+ 6 Pamenepo akapolo aja anafika pafupi limodzi ndi ana awo n’kugwada pansi. 7 Nayenso Leya anafika pafupi limodzi ndi ana ake n’kugwada pansi. Potsirizira pake, Yosefe ndi Rakele anafika pafupi, nawonso n’kugwada pansi.+

8 Tsopano Esau anafunsa kuti: “Nanga n’chifukwa chiyani watumiza khamu lonse limene ndakumana nalo lija?”+ Poyankha iye anati: “Ndachita zimenezi kuti mundikomere mtima mbuyanga.”+ 9 Ndiyeno Esau anati: “Ziweto ndili nazo zambiri, m’bale wanga.+ Zako ndi zako, ukhale nazo.” 10 Koma Yakobo anati: “Ayi chonde, musatero. Ngati mwandikomeradi mtima,+ landirani mphatso yangayi, popeza cholinga chake chinali chakuti ndione nkhope yanu, ndipo ndaionadi. Zili ngati ndaona nkhope ya Mulungu, chifukwa mwandilandira ndi manja awiri.+ 11 Chonde, landirani mphatso yokufunirani mafuno abwinoyi kuchokera kwa ine,+ chifukwa Mulungu wandikomera mtima, ndipo wandipatsa chilichonse.”+ Anamuumirizabe mpaka analandira mphatsoyo.+

12 Pambuyo pake Esau anati: “Tiye tinyamuke tizipita, ine nditsogole.” 13 Koma Yakobo anati: “Monga mukudziwa mbuyanga, anawa ndi osakhwima, komanso ndili ndi nkhosa ndi ng’ombe zoyamwitsa.+ Tikaziyendetsa mofulumira kwambiri, ngakhale tsiku limodzi lokha, ndithu zifa zonse.+ 14 Chonde mbuyanga, tsogolani. Ine kapolo wanu ndizibwera m’mbuyo mwanu. Ndiziyenda pang’onopang’ono mogwirizana ndi mayendedwe a ziwetozi+ ndi kuyenda kwa anawa.+ Ndikakupezani ku Seiri, mbuyanga.”+ 15 Ndiyeno Esau anati: “Chabwino, ndiye ndikupatseko ena mwa anyamata angawa kuti akuthandize.” Koma iye anati: “Ayi musachite kutero. Musavutike mbuyanga,+ ndiyenda bwinobwino.” 16 Choncho, Esau anatembenuka kubwerera ku Seiri tsiku lomwelo.

17 Tsopano Yakobo ananyamuka ulendo wopita ku Sukoti.+ Kumeneko anamanga nyumba yake ndi makola a ziweto zake.+ N’chifukwa chake malowo anawatcha kuti Sukoti.*

18 Patapita nthawi, Yakobo anafika bwinobwino kumzinda wa Sekemu,+ m’dziko la Kanani,+ akuchokera ku Padana-ramu.+ Atafika, anamanga msasa pafupi ndi mzindawo. 19 Kenako anagula malo ndipo anamangapo msasa. Anawagula ndi ndalama zasiliva 100, kwa ana a Hamori, bambo wake wa Sekemu.+ 20 Atatero, anamangapo guwa lansembe n’kulitcha Mulungu, Mulungu wa Isiraeli.+

34 Dina, mwana wamkazi amene Leya+ anaberekera Yakobo, ankakonda kukacheza+ ndi ana aakazi a m’dzikolo.+ 2 Kenako Sekemu anaona mtsikanayu. Sekemuyu anali mwana wamwamuna wa Hamori, Mhivi,+ mmodzi wa atsogoleri a m’dzikolo. Atamuona, anamutenga n’kumugwiririra.+ 3 Atatero, nthawi zonse mtima wake unali kulakalaka Dina mwana wa Yakobo, ndipo anamukonda kwambiri m’tsikanayu, moti ankalankhula naye momunyengerera. 4 Potsirizira pake, Sekemu anauza bambo ake Hamori+ kuti: “Munditengere mtsikana ameneyu kuti akhale mkazi wanga.”+

5 Tsopano Yakobo anamva zakuti Sekemu wagwiririra mwana wake Dina. Pa nthawiyo n’kuti ana ake aamuna ali kubusa ndi ziweto zake.+ Choncho, Yakobo sananene kanthu kudikira kuti ana akewo abwere.+ 6 Pambuyo pake, Hamori bambo ake a Sekemu, anapita kwa Yakobo kukakambirana naye.+ 7 Koma ana a Yakobo anabwerako kubusa kuja atangomva za nkhaniyi. Nkhaniyi inawapweteketsa mtima kwambiri ndipo anakwiya koopsa,+ pakuti Sekemu anachitira Isiraeli chinthu chonyazitsa kwambiri pogona ndi mwana wa Yakobo.+ Zimenezi zinali zosayenera kuchitika m’pang’ono pomwe.+

8 Ndiyeno Hamori anawauza kuti: “Mwana wanga Sekemu wakonda mtsikana wanuyu ndi mtima wonse.+ Chonde, m’patseni kuti akhale mkazi wake.+ 9 Tiyeni tichite mgwirizano wakuti tizikwatirana.+ Muzitipatsa ana anu aakazi, inunso muzitenga ana athu aakazi.+ 10 Mukhale nafe kwathu kuno, dziko lino likhalanso lanu. Mukhazikike, ndipo muzichita malonda mwaufulu.”+ 11 Pamenepo Sekemu anauza bambo ake a Dina ndi alongo ake kuti: “Ndikomereni mtima, ndikupatsani zonse zimene munganene. 12 Kwezani kwambiri ndalama za ukwati ndi mphatso zoti ndipereke,+ ndipo ndine wokonzeka kupereka zilizonse zimene munganene, malinga mundipatse mtsikanayu kuti akhale mkazi wanga.”

13 Koma ana a Yakobo anayankha Sekemu ndi bambo ake Hamori mowapita pansi. Anatero chifukwa Sekemu anali atagwiririra Dina mlongo wawo.+ 14 Kuwayankha kwake anati: “Sitingachite zimenezo. Sitingapereke mlongo wathu kwa mwamuna wosadulidwa.+ Zimenezo n’zonyazitsa kwa ife. 15 Tikulolani pokhapokha mwamuna aliyense pakati panu atadulidwa, kuti mukhale ofanana ndi ife.+ 16 Mukatero, ndithu tidzakupatsani ana athu aakazi ndipo ifenso tidzatenga ana anu aakazi. Tidzakhaladi ndi inu, ndipo tidzakhala anthu amodzi.+ 17 Koma ngati simutsatira zimene tanena zakuti mudulidwe, mwana wathu wamkaziyo tikamutenga n’kubwera naye.”

18 Mawu awowa anakondweretsa Hamori ndi mwana wake Sekemu.+ 19 Chotero mnyamatayu sanachedwe kuchita zimene anauzidwazo+ chifukwa anamukonda kwambiri mwana wa Yakobo. Sekemuyo anali wolemekezeka kwambiri+ m’nyumba yonse ya bambo ake.+

20 Choncho Hamori ndi mwana wake Sekemu anapita kuchipata cha mzinda wawo, n’kuyamba kulankhula kwa anthu a mumzindawo+ kuti: 21 “Anthu awa n’ngofuna mtendere ndi ife.+ Ndiye aloleni akhale m’dzikoli ndi kuchitamo malonda, popeza dzikoli n’lalikulu moti atha kukhalamo.+ Tikhoza kukwatira ana awo aakazi, ndiponso tikhoza kuwapatsa ana athu aakazi.+ 22 Koma pakufunika chinthu chimodzi kuti anthuwa alole kukhala nafe limodzi n’kukhala anthu amodzi ndi ife. Akuti adzatero pokhapokha mwamuna aliyense pakati pathu atadulidwa+ ngati mmene iwonso alili. 23 Tikatero, katundu wawo, chuma chawo ndi ziweto zawo zonse sizidzakhala zathu kodi?+ Tiyeni tilolere zimene akufunazo kuti azikhala nafe.”+ 24 Chotero anthu onse otuluka pachipata cha mzindawo anamvera Hamori ndi mwana wake Sekemu, ndipo amuna onse a mumzinda wakewo anadulidwa.

25 Koma pa tsiku lachitatu, pamene anthuwo anali pa ululu,+ ana awiri a Yakobo, Simiyoni ndi Levi,+ alongo ake a Dina,+ aliyense anatenga lupanga lake n’kukalowa mumzindawo mosaonetsera cholinga chawo. Kenako anayamba kupha mwamuna aliyense.+ 26 Anaphanso Hamori ndi mwana wake Sekemu ndi lupanga.+ Kenako anatenga Dina m’nyumba ya Sekemu, n’kupita naye.+ 27 Ana ena a Yakobo anamalizitsa amuna omwe anali atapwetekedwa koopsa, n’kutenga katundu yense wa mumzindamo. Anatero chifukwa anthuwo anagwiririra mlongo wawo.+ 28 Anatenga nkhosa zawo, abulu awo ndi ziweto zina, ndi zonse zimene zinali mumzindawo, ndiponso zimene zinali kunja kwa mzindawo.+ 29 Anatenga chuma chawo chonse, ndipo ana awo onse ang’onoang’ono ndi akazi awo anawagwira ndi kupita nawo. Anatenga zonse zimene zinali m’nyumba zawo.+

30 Yakobo ataona zimenezi anauza Simiyoni ndi Levi+ kuti: “Mwandiputira chidani, ndipo mwandinunkhitsa kwa anthu a m’dziko lino,+ Akanani ndi Aperezi. Ine ndili ndi anthu ochepa,+ ndipo iwowa ndithu asonkhana pamodzi n’kutiukira. Atithira nkhondo n’kutitha tonse, ine ndi banja langa.” 31 Koma anawo anayankha kuti: “Kodi ndi bwino kuti munthu azitenga mlongo wathu ngati hule?”+

35 Zitatero, Mulungu anauza Yakobo kuti: “Nyamuka, pita ku Beteli ukakhale kumeneko.+ Ukamangire guwa lansembe Mulungu woona, amene anaonekera kwa iwe pamene unali kuthawa Esau m’bale wako.”+

2 Ndiyeno Yakobo anauza anthu a m’banja lake ndi onse amene anali naye kuti: “Chotsani milungu yachilendo imene ili pakati panu.+ Dziyeretseni ndipo sinthani zovala zanu.+ 3 Mukatero, tinyamuke tipite ku Beteli. Kumeneko ndikamangira guwa lansembe Mulungu woona, amene anandimvera m’tsiku la kusautsika kwanga,+ posonyeza kuti anali nane pa ulendo wanga.”+ 4 Choncho anthuwo anapereka kwa Yakobo milungu yachilendo+ yonse imene anali nayo, ndi ndolo* zimene anavala m’makutu. Kenako Yakobo anafotsera+ zinthuzo pansi pa mtengo waukulu pafupi ndi Sekemu.

5 Atatero anachoka, ndipo anthu a m’mizinda yowazungulira anagwidwa ndi mantha ochokera kwa Mulungu,+ moti sanatsatire ana a Yakobo kuti akawathire nkhondo. 6 Potsirizira pake Yakobo anafika ku Luzi+ komwe ndi ku Beteli, m’dziko la Kanani. Iye anafika kumeneko pamodzi ndi anthu onse amene anali naye. 7 Anamanga guwa lansembe kumeneko, n’kutchula malowo kuti Eli-beteli.* Malowo anawatcha dzinali chifukwa Mulungu woona anaonekera kwa iye kumeneko, pa nthawi imene anali kuthawa m’bale wake.+ 8 Pambuyo pake Debora+ mlezi wa Rabeka anamwalira, ndipo anamuika ku Beteli m’munsi mwa phiri, pansi pa mtengo waukulu. Choncho mtengowo anautcha kuti Aloni-bakuti.*

9 Tsopano Mulungu anaonekeranso kwa Yakobo pamene anali kubwerera kwawo kuchokera ku Padana-ramu,+ n’kumudalitsa.+ 10 Mulungu anamuuza kuti: “Iwe dzina lako ndi Yakobo.+ Koma kuyambira tsopano, dzina lako silikhalanso Yakobo, ukhala Isiraeli.” Choncho anayamba kumutchula kuti Isiraeli.+ 11 Mulungu anamuuzanso kuti: “Ine ndine Mulungu Wamphamvuyonse.+ Ubereke ndipo ukhale ndi ana ambiri. Mitundu ndi mafuko ambiri adzatuluka mwa iwe, ndipo mafumu adzatuluka m’chiuno mwako.+ 12 Dziko limene ndinalipereka kwa Abulahamu ndi Isaki, ndidzalipereka kwa iwe ndi kwa mbewu yako+ yobwera pambuyo pako.”+ 13 Kenako Mulungu anachoka pamwamba pamene anaima polankhula ndi Yakobo.+

14 Zitatero, Yakobo anaimika mwala wachikumbutso pamalo pamene anali kulankhula nayepo,+ kenako pamwalawo anathirapo nsembe yachakumwa ndi mafuta.+ 15 Ndiyeno Yakobo anapitiriza kutchula malo amene Mulungu analankhula nayewo kuti Beteli.+

16 Kenako ananyamuka kuchoka ku Beteliko. Padakali mtunda wautali ndithu kuti afike ku Efurata,+ inafika nthawi yoti Rakele abereke, koma poberekapo anali kuvutika kwambiri.+ 17 Pamene kubereka kunafika popweteka kwambiri, mzamba* anamuuza kuti: “Usaope, pakuti ubereka mwana wina wamwamuna.”+ 18 Pomalizira pake, pamene moyo wake+ unali kutayika (pakuti anamwalira),+ anatcha mwanayo dzina lakuti Beni-oni.* Koma bambo ake anamutcha Benjamini.*+ 19 Umu ndi mmene Rakele anamwalirira, ndipo anamuika m’manda ali m’njira popita ku Efurata, komwe ndi ku Betelehemu.+ 20 Yakobo anaika mwala pamandapo. Mwala umenewo ulipobe mpaka lero pamanda a Rakele.+

21 Pambuyo pake, Isiraeli ananyamuka n’kukamanga hema wake chapatsogolo ndithu kupitirira nsanja ya Ederi.+ 22 Isiraeli atamanga msasa+ m’dziko limenelo, Rubeni anagona ndi Biliha mkazi wamng’ono* wa bambo ake, ndipo Isiraeli anamva zimene zinachitikazo.+

Yakobo anali ndi ana aamuna 12. 23 Ana aamuna amene Leya anaberekera Yakobo anali Rubeni+ mwana wake woyamba, Simiyoni, Levi, Yuda, Isakara ndi Zebuloni. 24 Ana amene Rakele anaberekera Yakobo anali Yosefe ndi Benjamini. 25 Ana amene Biliha kapolo wa Rakele anaberekera Yakobo anali Dani ndi Nafitali. 26 Ana amene Zilipa kapolo wa Leya anaberekera Yakobo anali Gadi ndi Aseri. Amenewa ndiwo ana aamuna a Yakobo amene anabereka ku Padana-ramu.

27 Potsirizira pake Yakobo anafika kwa bambo ake Isaki ku Mamure,+ m’dera la Kiriyati-ariba,+ komwe ndi ku Heburoni. Uku n’kumenenso Abulahamu ndi Isaki anakhalako monga alendo.+ 28 Masiku onse a Isaki anakwana zaka 180.+ 29 Kenako Isaki anamwalira, ndipo anaikidwa m’manda n’kugona ndi makolo ake. Anamwalira ali wokalamba, wokhutira ndi masiku ake.+ Ana ake, Esau ndi Yakobo, anamuika m’manda.+

36 Mbiri ya Esau, kapena kuti Edomu,+ ili motere:

2 Esau anatenga akazi pakati pa ana aakazi a ku Kanani.+ Anatenga Ada,+ mwana wamkazi wa Eloni, Mhiti.+ Anatenganso Oholibama,+ yemwe anali mwana wamkazi wa Ana, komanso anali mdzukulu wa Zibeoni, Mhivi. 3 Anatenganso Basemati,+ yemwe anali mwana wamkazi wa Isimaeli, komanso anali mlongo wake wa Nebayoti.+

4 Ada anaberekera Esau mwana dzina lake Elifazi, ndipo Basemati anam’berekera Reueli.

5 Ana amene Oholibama anaberekera Esau ndiwo Yeusi, Yalamu ndi Kora.+

Amenewa anali ana a Esau amene anabereka m’dziko la Kanani. 6 Pambuyo pake, Esau anatenga akazi ake, ana ake aamuna ndi aakazi, ndi ena onse a m’nyumba yake, ziweto zake zonse ndi chuma chake+ chonse chimene anachipeza m’dziko la Kanani, n’kupita kudziko lina kutali ndi Yakobo m’bale wake.+ 7 Iye anachoka chifukwa chuma chawo chinali chitawachulukira kwambiri, moti sakanathanso kukhala limodzi. Dziko lachilendo limene anali kukhalalo linali litawachepera chifukwa cha kuchuluka kwa ziweto zawo.+ 8 Chotero Esau anakakhazikika kudera lamapiri ku Seiri.+ Esau analinso kutchedwa Edomu.+

9 Tsopano nayi mibadwo ya Esau, kholo la Aedomu, amene anali kukhala kudera lamapiri la Seiri.+

10 Mayina a ana a Esau ndi awa: Elifazi, mwana wamwamuna wobadwa kwa Ada mkazi wake wa Esau, komanso Reueli, mwana wamwamuna wobadwa kwa Basemati mkazi wake wa Esau.+

11 Ana a Elifazi anali Temani,+ Omari, Zefo, Gatamu ndi Kenazi.+ 12 Elifazi mwana wa Esau anali ndi mdzakazi dzina lake Timina.+ Patapita nthawi, mdzakaziyu anaberekera Elifazi mwana wamwamuna dzina lake Amaleki.+ Amenewa ndiwo anali ana a Ada mkazi wa Esau.

13 Ana a Reueli anali awa: Nahati, Zera, Shama ndi Miza.+ Amenewa ndiwo anali ana a Basemati+ mkazi wa Esau.

14 Oholibama, mkazi wake wa Esau, anaberekera Esau ana aamuna awa: Yeusi, Yalamu ndi Kora.+ Oholibamayu anali mwana wa Ana, komanso mdzukulu wa Zibeoni.

15 Nawa mafumu+ a mafuko a ana a Esau: Ana a Elifazi, mwana woyamba wa Esau, anali: Mfumu Temani,+ mfumu Omari, mfumu Zefo, mfumu Kenazi, 16 mfumu Kora, mfumu Gatamu ndi mfumu Amaleki. Amenewa ndiwo anali mafumu a kubanja la Elifazi+ m’dziko la Edomu. Iwowa anali ana obadwa kwa Ada.

17 Nawa ana a Reueli, mwana wamwamuna wa Esau: Mfumu Nahati, mfumu Zera, mfumu Shama ndi mfumu Miza. Amenewa ndiwo anali mafumu a kubanja la Reueli m’dziko la Edomu.+ Iwowa anali ana obadwa kwa Basemati mkazi wa Esau.

18 Potsiriza, nawa ana a Oholibama mkazi wa Esau: Mfumu Yeusi, mfumu Yalamu ndi mfumu Kora. Amenewa ndiwo anali mafumu a kubanja la Oholibama mkazi wa Esau, mwana wa Ana.

19 Amenewa ndiwo anali ana a Esau kapena kuti Edomu,+ ndi mafumu awo.

20 Nawa ana a Seiri Mhori, eni dzikolo:+ Lotani, Sobala, Zibeoni, Ana,+ 21 Disoni, Ezeri ndi Disani.+ Amenewa anali ana a Seiri, mafumu a fuko la Ahori, m’dziko la Edomu.

22 Ana a Lotani anali Hori ndi Hemamu, ndipo Lotani anali ndi mlongo wake dzina lake Timina.+

23 Ana a Sobala anali Alivani, Manahati, Ebala, Sefo ndi Onamu.

24 Ana a Zibeoni anali Aya ndi Ana. Uyu ndi Ana amene anapeza akasupe a madzi otentha m’chipululu, pamene anali kudyetsa abulu a Zibeoni bambo ake.+

25 Ana anabereka Disoni ndi Oholibama mwana wamkazi wa Ana.

26 Ana a Disoni anali Hemadani, Esibani, Itirani ndi Kerana.+

27 Ana a Ezeri anali Bilihani, Zavani ndi Ekani.

28 Ana a Disani anali Uzi ndi Arani.+

29 Nawa mafumu a fuko la Ahori: Mfumu Lotani, mfumu Sobala, mfumu Zibeoni, mfumu Ana, 30 mfumu Disoni, mfumu Ezeri ndi mfumu Disani.+ Amenewa ndiwo anali mafumu a fuko la Ahori monga mwa ufumu wawo m’dziko la Seiri.

31 Nawa tsopano mafumu aakulu amene analamulira dziko la Edomu,+ ana a Isiraeli asanayambe kulamulidwa ndi mfumu ina iliyonse:+ 32 Bela mwana wa Beori analamulira Edomu,+ ndipo dzina la mzinda wake linali Dinihaba. 33 Bela atamwalira, Yobabi mwana wa Zera wa ku Bozira,+ anayamba kulamulira m’malo mwake.+ 34 Yobabi atamwalira, Husamu wa kudziko la Atemani,+ anayamba kulamulira m’malo mwake.+ 35 Husamu atamwalira, Hadadi mwana wa Bedadi amene anagonjetsa Amidiyani+ m’dziko la Mowabu,+ anayamba kulamulira m’malo mwake, ndipo dzina la mzinda wake linali Aviti.+ 36 Hadadi atamwalira, Samila wa ku Masereka anayamba kulamulira m’malo mwake.+ 37 Samila atamwalira, Shauli wa ku Rehoboti mzinda wa m’mphepete mwa Mtsinje,* anayamba kulamulira m’malo mwake.+ 38 Shauli atamwalira, Baala-hanani mwana wa Akibori, anayamba kulamulira m’malo mwake.+ 39 Baala-hanani mwana wa Akibori atamwalira, Hadari anayamba kulamulira m’malo mwake, ndipo dzina la mzinda wake linali Pau. Mkazi wake dzina lake anali Mehetabele, mwana wa Matiredi. Matiredi anali mwana wamkazi wa Mezahabu.+

40 Mayina a mafumu a Esau monga mwa mabanja awo, mwa madera awo, ndi monga mwa mayina awo, ndi awa: Mfumu Timina, mfumu Aliva, mfumu Yeteti,+ 41 mfumu Oholibama, mfumu Ela, mfumu Pinoni,+ 42 mfumu Kenazi, mfumu Temani, mfumu Mibezari,+ 43 mfumu Magidieli ndi mfumu Iramu. Amenewa ndiwo anali mafumu a Edomu+ monga mwa madera awo m’dziko lawo.+ Iyi ndiyo mibadwo ya Esau, kholo la Aedomu.+

37 Yakobo anakhalabe m’dziko la Kanani,+ kumene bambo ake anakhalako ngati mlendo.+

2 Nayi mbiri ya Yakobo.

Pamene Yosefe+ anali ndi zaka 17, tsiku lina anapita kokadyetsa nkhosa limodzi ndi abale ake.+ Pokhala wamng’ono, anali limodzi ndi ana a Biliha+ ndi ana a Zilipa,+ omwe anali akazi a bambo ake. Tsopano Yosefe anakauza bambo ake zoipa zimene abale ake anali kuchita.+ 3 Isiraeli anali kum’konda kwambiri Yosefe kuposa ana ake ena onse,+ chifukwa anali mwana amene anam’bereka atakalamba. Chotero anam’soketsera mkanjo wamizeremizere wamanja aatali.+ 4 Abale ake ataona kuti bambo awo anali kum’konda kwambiri Yosefe kuposa iwo onse, anayamba kudana naye,+ moti sankatha kulankhula naye mwamtendere.+

5 Pambuyo pake, Yosefe analota maloto ndi kuuza abale ake.+ Kwa iwo chinakhala chifukwa china chomudera. 6 Iye anawauza kuti: “Tamverani maloto amene ine ndinalota.+ 7 Ndinalota tikumanga mitolo ya tirigu pakati pa munda. Mtolo wanga unadzuka n’kuima chilili. Mitolo yanunso inadzuka, ndipo inazungulira mtolo wanga n’kuyamba kuuweramira.”+ 8 Pamenepo abale akewo anamufunsa kuti: “Kodi iweyo ndithu ukuganiza kuti ungadzakhale mfumu yathu?+ Moti ukuona kuti ungadzatilamulire ife?”+ Kwa iwo, maloto amenewa ndi mawu akewa anakhala chifukwa chinanso chomudera.

9 Tsiku linanso analota maloto ena, ndipo anakauza abale akewo kuti: “Leronso ndinalota maloto ena. Ndinalota dzuwa ndi mwezi ndiponso nyenyezi zokwanira 11 zikundigwadira.”+ 10 Kenako anafotokozeranso malotowo bambo ake ndi abale akewo. Koma bambo ake anam’dzudzula kuti:+ “Kodi maloto walotawa akutanthauza chiyani? Kodi ineyo ndithu ndi mayi akowa, komanso abale akowa tidzagwada pansi pamaso pa iwe?” 11 Abale akewo anachita naye kaduka,+ koma bambo ake anasunga mawuwo.+

12 Tsopano abale ake aja anapita kokadyetsa nkhosa za bambo awo kufupi ndi ku Sekemu.+ 13 Pambuyo pake, Isiraeli anauza Yosefe kuti: “Kodi abale ako sakudyetsa nkhosa cha ku Sekemu? Tabwera ndikutume kwa iwo.” Iye anati: “Chabwino bambo.”+ 14 Ndiye Isiraeli anati: “Pita ukaone ngati abale ako ali bwino limodzi ndi nkhosa. Kenako ubwere udzandiuze.”+ Chotero, anamuuza kuti anyamuke kuchigwa cha Heburoni+ ndipo iye analowera ku Sekemu. 15 Ali pa ulendowo, munthu wina anakumana ndi Yosefe akungoyenda uku ndi uku kutchireko. Ndiyeno munthuyo anamufunsa kuti: “Kodi ukufunafuna chiyani?” 16 Iye anayankha kuti: “Ndikufunafuna abale anga. Tandiuzani chonde, Kodi iwo akudyetsera kuti nkhosa?” 17 Munthuyo anati: “Amenewo achoka. Ndinawamva akunena kuti, ‘Tiyeni tipite ku Dotana.’” Pamenepo Yosefe anawalondolabe abale akewo mpaka anakawapeza ku Dotanako.

18 Iwo anamuonera patali akubwera, ndipo asanafike pafupi anayamba kupangana chiwembu choti amuphe.+ 19 Chotero anauzana kuti: “Tamuonani wolota uja.+ Uyo akubwera apoyo! 20 Tiyeni timuphe, timuponye m’chitsime chopanda madzi,+ ndipo tikanene kuti chilombo cholusa chamudya.+ Tidzaone kuti chidzachitike n’chiyani ndi maloto ake aja.” 21 Rubeni atamva zimenezo anayesa kum’landitsa kwa iwo.+ Iye anati: “Ayi, tisachite kuwononga moyo wake.”+ 22 Ndipo anapitiriza kuwauza kuti: “Musakhetse magazi ayi.+ Muponyeni m’chitsime chopanda madzichi kutchire kuno, musamuvulaze.”+ Cholinga chake chinali chakuti amupulumutse kwa iwo ndi kum’bwezera kwa bambo ake.

23 Choncho Yosefe atangofika kwa abale akewo, anamuvula mkanjo wake wamizeremizere uja, womwe anavala.+ 24 Atatero, anamutenga n’kukamuponya m’chitsimecho.+ Pa nthawiyo chitsimecho chinali chopanda madzi.

25 Ndiyeno anakhala pansi kuti adye chakudya.+ Koma pamene anakweza maso, anaona gulu la apaulendo la Aisimaeli.+ Anali kuchokera ku Giliyadi, ndipo ngamila zawo zinali zitanyamula mafuta onunkhira a labidanamu ndi a basamu, komanso makungwa a utomoni wonunkhira.+ Apaulendowo anali kupita ku Iguputo. 26 Yuda atawaona, anauza abale ake kuti: “Tipindulapo chiyani tikapha m’bale wathu ndi kubisa imfa yake?+ 27 Tiyeni timugulitse kwa Aisimaeliwa,+ tisam’pweteke ayi.+ Ndipotu ndi m’bale wathu ameneyu, magazi* athu enieni.” Atamva mawuwa, iwo anamvera m’bale wawoyo.+ 28 Tsopano amuna amalonda achimidiyani+ aja anali kudutsa mumsewu. Pamenepo abale a Yosefe anamutulutsa m’chitsimemo+ n’kumugulitsa kwa Aisimaeliwo. Anamugulitsa ndalama zasiliva 20,+ ndipo iwo anapita naye ku Iguputo.

29 Pambuyo pake, Rubeni anabwerera kuchitsime kuja, koma anakapeza kuti Yosefe mulibe m’chitsimemo. Ataona choncho, anang’amba zovala zake.+ 30 Atabwerera kwa abale ake aja, anafuula kuti: “Mwana ujatu kulibe! Kalanga ine, ndilowera kuti ine?”+

31 Tsopano iwo anatenga mkanjo wa Yosefe uja, n’kupha mbuzi yamphongo, n’kuviika mkanjowo mobwerezabwereza m’magazi a mbuziyo.+ 32 Kenako, iwo anatumiza mkanjo wamizeremizere uja kwa bambo awo. Atafika nawo anati: “Tapeza mkanjo uwu. Chonde, uonetsetseni+ kuti muone ngati uli mkanjo wa mwana wanu kapena ayi.”+ 33 Bambo awo anauyang’anitsitsa mkanjowo. Ndiyeno anafuula kuti: “Kalanga ine! Mkanjowu ndi wa mwana wanga! Chilombo cholusa chamudya basi mwana wanga.+ Wakhadzulidwa+ ndithu mwana wanga Yosefe!” 34 Pamenepo Yakobo anang’amba zovala zake, n’kuvala chiguduli* m’chiuno mwake, ndipo anamulira mwana wake masiku ambiri.+ 35 Ana ake onse aamuna ndi aakazi anali kupita kukam’tonthoza,+ koma iye anali kukana kutonthozedwa. Anali kunena kuti:+ “Ayi! Ndidzalira mpaka kutsikira ku Manda* kumene kuli mwana wanga.” Ndipo bambo akewo anapitiriza kumulira.

36 Amidiyani aja anakagulitsa Yosefe ku Iguputo kwa Potifara. Potifara anali nduna ya panyumba ya Farao,+ ndiponso anali mkulu wa asilikali olondera mfumu.+

38 Tsopano Yuda anachoka pakati pa abale ake, ndipo anakamanga hema wake pafupi ndi munthu wina wachiadulamu,+ dzina lake Hira. 2 Kumeneko Yuda anaona mwana wamkazi wa Mkanani+ winawake, ndipo anam’kwatira mtsikanayo. Mkananiyo dzina lake anali Sua. 3 Mkaziyo anatenga pakati. Kenako, anabereka mwana wamwamuna, ndipo Yuda anamutcha dzina lakuti Ere.+ 4 Anatenganso pakati pena n’kubereka mwana wamwamuna ndipo anamutcha dzina lakuti Onani. 5 Anaberekanso mwana wina wamwamuna n’kumutcha dzina lakuti Shela. Mwana ameneyu anam’bereka ali ku Akizibu. +

6 Patapita nthawi, Yuda anatengera mkazi Ere, mwana wake woyamba. Mkaziyo dzina lake anali Tamara.+ 7 Koma Ere, mwana woyamba wa Yuda, anakhala munthu woipa pamaso pa Yehova.+ Chotero Yehova anamupha.+ 8 Yuda ataona zimenezi anauza Onani kuti: “Gona ndi mkazi wa m’bale wako ndipo uchite chokolo, kuti um’berekere ana m’bale wako.”+ 9 Koma Onani anadziwa kuti anawo sadzakhala ake.+ Choncho, nthawi zonse akagona ndi mkazi wa m’bale wakeyo, anali kutaya pansi umuna wake kuti asam’berekere ana m’bale wakeyo.+ 10 Zimene anachitazo zinamuipira Yehova,+ chotero nayenso anamupha.+ 11 Zitatero, Yuda anauza Tamara mpongozi wake kuti: “Pita kunyumba kwa bambo ako, ukakhale kumeneko monga mkazi wamasiye kufikira Shela mwana wanga wamwamuna atakula.”+ Anatero chifukwa mumtima mwake anati: “Nayenso Shela angamwalire ngati abale ake aja.”+ Choncho, Tamara anapita kukakhala kunyumba kwa bambo ake.+

12 Patapita nthawi, mkazi wa Yuda, yemwe anali mwana wa Sua,+ anamwalira. Nthawi yolira maliro+ itatha Yuda anapita ku Timuna,+ kumene anyamata ake anali kumeta ubweya nkhosa zake. Anapita kumeneko limodzi ndi bwenzi lake Hira wachiadulamu+ uja. 13 Tsopano munthu wina anauza Tamara kuti: “Apongozi ako akupita ku Timuna kukameta nkhosa zawo.”+ 14 Tamara atamva zimenezo, anavula zovala zake zaumasiye n’kufunda nsalu. Kenako anaphimba nkhope yake ndi nsalu ina. Atatero anakakhala pansi pachipata cha Enaimu m’mbali mwa msewu wopita ku Timuna. Tamara anachita zimenezi poona kuti Shela wakula, koma apongozi ake sakudzam’tenga kuti akakhale mkazi wa Shelayo.+

15 Yuda ataona mkaziyo, anaganiza kuti ndi hule+ chifukwa anali ataphimba nkhope yake.+ 16 Choncho Yuda anapatukira kwa mkaziyo pambali pa msewu n’kumuuza kuti: “Ndikufuna ndigone nawe.”+ Anatero posadziwa kuti anali mpongozi wake.+ Koma mkaziyo anayankha kuti: “Mundipatsa chiyani kuti mugone nane?”+ 17 Iye anayankha kuti: “Ndidzakutumizira mwana wa mbuzi.” Koma mkaziyo anati: “Mundipatse chikole choti ndisunge kufikira pamene mudzaitumize.”+ 18 Iye anati: “Ukufuna ndikupatse chikole chotani?” Mkaziyo anapitiriza kuti: “Mundipatse mphete yanu ya udindo+ wanuyo ndi chingwe chake, ndiponso ndodo yanuyo.” Pamenepo iye anapereka zinthuzo kwa mkaziyo, n’kugona naye ndipo mkaziyo anakhala ndi pakati. 19 Atagona naye, mkaziyo ananyamuka n’kubwerera kwawo. Atafika anavula nsalu imene anadziphimba nayo ija n’kuvala chovala chake chaumasiye.+

20 Yuda anatumiza mwana wa mbuzi uja. Anapempha mnzake wachiadulamu+ uja kuti akam’perekere mbuziyo, ndi cholinga chakuti akamutengere chikole chake kwa mkazi uja, koma sanakam’peze. 21 Kenako anayamba kufunsira kwa amuna akumaloko, kuti: “Kodi hule lapakachisi+ lija lili kuti, lija limene limaima pambali pa msewu kuno ku Enaimu?” Koma amunawo ankayankha kuti: “Kunotu sitinakhalepo ndi hule lapakachisi.” 22 Potsirizira pake, mnzakeyo anabwerera kwa Yuda n’kumuuza kuti: “Mkazi ujatu sindinam’peze. Ndiponso amuna akumeneko anena kuti, ‘Kunotu sitinakhalepo ndi hule lapakachisi.’” 23 Pamenepo Yuda anati: “Mulekeni atenge zinthuzo zikhale zake, kuopera kuti anthu angatiseke.+ Ndipotu kutumiza ndinatumiza ndithu mwana wa mbuziyo, koma sunakam’peze mkaziyo.”

24 Patapita miyezi itatu, Yuda anauzidwa kuti: “Tamara mpongozi wako anachita chiwerewere,+ ndipo ali ndi pakati.”+ Yuda atamva zimenezo, anati: “M’tulutseni kuti aphedwe ndi kuotchedwa.”+ 25 Pamene anali kum’tulutsa, Tamarayo anatumiza mawu kwa apongozi ake kuti: “Mwiniwake zinthu izi ndiye anandipatsa pakatipa.”+ Ananenanso kuti: “Chonde ziyang’anitsitseni,+ muone kuti mpheteyo ndi chingwe chake, komanso ndodoyo n’zandani.”+ 26 Ndiyeno Yuda ataziyang’anitsitsa, ananena kuti:+ “Mkaziyu ndi wolungama koposa ine,+ chifukwa sindinam’pereke kwa mwana wanga Shela.”+ Zitatero, Yuda sanagone nayenso.+

27 Itakwana nthawi yoti Tamara abereke, anapezeka kuti ali ndi mapasa m’mimba mwake. 28 Ndipo mmene anali kubereka, mwana mmodzi anatulutsa dzanja lake. Nthawi yomweyo mzamba anatenga kachingwe kofiira kwambiri n’kumanga dzanjalo, n’kunena kuti: “Uyu ndiye wayamba kubadwa.” 29 Koma mwanayo anabweza dzanja lake. Nthawi yomweyo m’bale wake anatuluka, moti mzambayo anafuula kuti: “Ndiye chiyani wachitachi? Bwanji ukuchita kung’amba wekha njira?” N’chifukwa chake anamutcha dzina lakuti Perezi.*+ 30 Pambuyo pake, m’bale wake yemwe anali ndi kachingwe kofiira kwambiri padzanja lake uja anatuluka, ndipo anamutcha dzina lakuti Zera.+

39 Tsopano Yosefe uja, Aisimaeli+ anapita naye ku Iguputo,+ ndipo kumeneko anakam’gulitsa kwa Potifara.+ Potifara anali Mwiguputo, yemwe anali nduna ya panyumba ya Farao, komanso mkulu wa asilikali olondera mfumu. 2 Koma Yehova anakhalabe ndi Yosefe, ndipo iye anakhala wopambana m’zochita zake zonse.+ Anakhalanso munthu waudindo m’nyumba ya mbuye wake, Mwiguputoyo. 3 Mbuye wakeyo anaona kuti Yehova anali ndi mnyamatayo, ndi kuti chilichonse chimene anali kuchita, Yehova anali kuchidalitsa.

4 Potifara anapitiriza kumukonda Yosefe pamene anali kum’tumikira, moti anamusankha kukhala woyang’anira nyumba yake.+ Zonse zimene Potifara anali nazo anazipereka m’manja mwa Yosefe. 5 Kuyambira pamene Potifara anasankha Yosefe kukhala woyang’anira nyumba yake ndi zinthu zake zonse, Yehova anapitiriza kudalitsa nyumba ya Mwiguputoyo chifukwa cha Yosefe. Yehova anadalitsa zonse za m’nyumba ya Potifara ndi zakumunda zomwe.+ 6 Potsirizira pake, Potifara anasiya zinthu zake zonse m’manja mwa Yosefe,+ moti sanali kudera nkhawa chilichonse kupatulapo chakudya chimene ankadya. Komanso, Yosefe anali wokongola m’maonekedwe ndi wa thupi loumbika bwino.

7 Kenako, mkazi wa mbuyake anayamba kuyang’ana Yosefe momusirira,+ moti anali kumuuza kuti: “Ugone nane.”+ 8 Koma Yosefe anali kukana+ ndi kuuza mkazi wa mbuye wakeyo kuti: “Chifukwa cha ine, mbuye wanga sadera nkhawa za chilichonse m’nyumba muno, ndipo chilichonse chimene iye ali nacho wachipereka m’manja mwanga.+ 9 M’nyumba muno mulibe woyang’anira woposa ine, ndipo mbuye wanga anaika chilichonse m’manja mwanga kupatulapo inuyo, chifukwa ndinu mkazi wake.+ Ndiye ndingachitirenji choipa chachikulu chonchi n’kuchimwira Mulungu?”+

10 Mkaziyo anali kulankhula ndi Yosefe tsiku ndi tsiku, koma iye sanamvere zoti agone pambali pake, kuti agone naye.+ 11 Monga mwa masiku onse, tsiku lina Yosefe analowa m’nyumba kukagwira ntchito yake, ndipo m’nyumbamo munalibe antchito ena.+ 12 Pamenepo mkaziyo anam’gwira malaya+ mnyamatayo n’kumuuza kuti: “Ugone nane basi!”+ Koma mnyamatayo anangovula malayawo n’kuwasiya m’manja mwa mkaziyo n’kuthawira panja.+ 13 Mkaziyo ataona kuti mnyamatayo wasiya malaya ake m’manja mwake n’kuthawira panja, 14 anayamba kufuulira antchito ena a m’nyumbamo, kuti: “Taonani! Anatibweretsera mwamuna uyu, Mheberi, kuti adzatichite chipongwe kuti anthu atiseke. Anabwera kwa ine kuti adzandigwiririre, koma ndinakuwa mwamphamvu.+ 15 Ndiye ataona kuti ndayamba kukuwa, anasiya malaya ake pambali pangapa n’kuthawira panja.” 16 Atatero, anasunga malaya a mnyamatayo pambali pake kufikira mwamuna wake atabwera kunyumbako.+

17 Mwamuna wake atafika, mkaziyo anamuuza kuti: “Wantchito wachiheberi amene munam’bweretsa kwa ife uja, anabwera kwa ine kuti andichite zachipongwe. 18 Koma ataona kuti ndayamba kukuwa, anasiya malaya ake pambali pangapa n’kuthawira panja.”+ 19 Mbuye wa mnyamatayo atamva zimene mkazi wake anamuuza zakuti: “Wantchito wanu anachita zakutizakuti,” mkwiyo wake unayaka.+ 20 Pamenepo, mbuye wake wa Yosefe anatenga Yosefeyo n’kumupereka kundende ya akaidi a mfumu, ndipo anakhala kumeneko.+

21 Koma Yehova anapitirizabe kukhala ndi Yosefe ndi kumusonyeza kukoma mtima kosatha. Ndipo anachititsa mkulu wa ndende kum’konda Yosefe.+ 22 Choncho, mkulu wa ndendeyo anaika Yosefe kukhala woyang’anira akaidi onse m’ndendemo, ndi chilichonse chimene chinali kuchitika mmenemo.+ 23 Mkulu wa ndendeyo sanali kuyang’aniranso chilichonse chimene chinali m’manja mwake. Zinali choncho chifukwa Yehova anali ndi Yosefe, ndipo chilichonse chimene iye anali kuchita Yehova anali kuchidalitsa.+

40 Pambuyo pake, woperekera chikho+ wa Farao mfumu ya ku Iguputo+ ndi womuphikira mkate, anachimwira mbuye wawo. 2 Farao anawakwiyira kwambiri atumiki ake awiriwo,+ mkulu wa operekera chikho ndi mkulu wa ophika mkate.+ 3 Choncho, anawaika m’ndende+ ya m’nyumba mwa mkulu wa asilikali olondera mfumu,+ mmene Yosefe anali mkaidi. 4 Mmenemo, mkulu wa asilikali olondera mfumu anaika Yosefe kuti azikhala nawo n’kumawalondera,+ ndipo iwo anakhala m’ndendemo kwa masiku ndithu.

5 Usiku wina,+ woperekera chikho ndi wophika mkate, atumiki a mfumu ya Iguputo omwe anali m’ndende+ aja, analota maloto.+ Aliyense analota maloto ake okhala ndi tanthauzo lakelake.+ 6 Yosefe atabwera kudzawaona m’mawa, anadabwa poona kuti nkhope zawo zinali zakugwa.+ 7 Choncho anafunsa atumiki a Farao aja, omwe anali naye m’ndende ya kunyumba kwa mbuye wakeyo, kuti: “N’chifukwa chiyani nkhope zanu zili zachisoni lero?”+ 8 Iwo anamuyankha kuti: “Talota maloto, koma palibe wotimasulira malotowo.” Pamenepo Yosefe anawauza kuti: “Kodi Mulungu sindiye amamasulira?+ Tandifotokozerani malotowo.”

9 Choncho mkulu wa operekera chikho anafotokozera Yosefe maloto ake kuti: “M’maloto anga, ndinaona mtengo wa mpesa uli pamaso panga. 10 Mtengo wa mpesawo unali ndi nthambi zitatu, ndipo unatulutsa mphukira.+ Kenako unamasula maluwa n’kubereka mphesa ndipo zinapsa. 11 M’manja mwanga ndinali ndi chikho cha Farao, ndipo ndinatenga mphesazo n’kuzifinyira m’chikho cha Faraocho.+ Nditatero, ndinapereka chikhocho kwa Farao.”+ 12 Pamenepo Yosefe anamuuza kuti: “Kumasulira kwake ndi uku:+ Nthambi zitatuzo zikuimira masiku atatu. 13 Pakapita masiku atatu, Farao akutulutsa. Adzakubwezera ndithu pa ntchito yako yakale,+ yoperekera chikho kwa mfumuyo.+ 14 Komabe, zonse zikadzakhala bwino kwa iwe usadzandiiwale.+ Chonde, udzandikomere mtima ponditchula kwa Farao,+ ndipo ukayesetse kuti ndidzatuluke m’ndende muno. 15 Kuti ndipezeke kuno anachita chondiba kudziko la Aheberi,+ ndiponso kuno palibe chilichonse chimene ndinalakwa choti andiikire m’ndende muno.”+

16 Mkulu wa ophika mkate ataona kuti Yosefe wamasulira zabwino, nayenso anati: “Inenso ndinalota maloto. Ndinalota nditasenza pamutu pangapa nsengwa zitatu za mikate yoyera. 17 Munsengwa yapamwambayo munali mikate yosiyanasiyana ya Farao,+ ndipo mbalame+ zinali kudya mikateyo munsengwayo pamutu panga.” 18 Ndiyeno Yosefe anati: “Kumasulira kwake ndi uku:+ Nsengwa zitatuzo zikuimira masiku atatu. 19 Pakapita masiku atatu, Farao akutulutsa n’kukudula mutu. Adzakupachika pamtengo,+ ndipo mbalame zidzadya nyama yako ndithu.”+

20 Tsiku lachitatulo linafika, ndipo linali tsiku lokumbukira kubadwa kwa Farao.+ Mfumuyo inakonzera phwando antchito ake onse. Pa tsikuli, Farao anatulutsa m’ndende mkulu wa operekera chikho ndi mkulu wa ophika mkate, n’kuwaimika pamaso pa antchito ake onse.+ 21 Farao anabwezeradi pa ntchito mkulu wa operekera chikho uja,+ moti anapitiriza ntchito yake yoperekera chikho kwa Farao. 22 Koma mkulu wa ophika mkate anam’pachika,+ monga mmene Yosefe anawauzira pomasulira maloto+ aja. 23 Komabe, mkulu wa operekera chikho uja anamuiwala Yosefe osam’kumbukira.+

41 Patapita zaka ziwiri zathunthu, Farao analota maloto.+ Analota kuti waimirira m’mbali mwa mtsinje wa Nailo. 2 Kenako iye anaona ng’ombe 7 zikutuluka mumtsinje wa Nailo. Ng’ombezo zinali zokongola m’maonekedwe ndi zonenepa, ndipo zinali kudya udzu wa m’mbali mwa mtsinjewo.+ 3 Anaonanso ng’ombe zina 7 zikutuluka mumtsinje wa Nailowo pambuyo pa zoyambazo. Zimenezi zinali zonyansa ndi zowonda,+ ndipo zinaima pambali pa zinazo m’mbali mwa mtsinjemo. 4 Tsopano ng’ombe zonyansa ndi zowondazo zinayamba kudya ng’ombe 7 zooneka bwino ndi zonenepa zija.+ Kenako Farao anagalamuka.+

5 Koma Farao anagonanso n’kulota maloto ena. M’malotowa anaona ngala za tirigu 7 zikutuluka paphesi limodzi. Ngalazo zinali zokhwima ndi zazikulu bwino.+ 6 Anaonanso ngala zina 7 zikutuluka pambuyo pa zoyambazo.+ Ngalazo zinali zonyala ndi zowauka ndi mphepo yakum’mawa.+ 7 Ngala zonyalazo zinayamba kumeza ngala 7 zokhwima ndi zazikulu bwinozo.+ Kenako Farao anagalamuka, n’kuona kuti anali maloto.

8 Kutacha m’mawa, Farao anavutika kwambiri ndi maganizo.+ Chotero anaitanitsa ansembe onse amatsenga+ ndi amuna anzeru+ onse a mu Iguputo, n’kuwafotokozera maloto akewo.+ Koma palibe amene anatha kum’masulira Farao malotowo.

9 Kenako mkulu wa operekera chikho uja anauza Farao+ kuti: “Lero ndinene zolakwa zanga.+ 10 Inuyo a Farao munatikwiyira kwambiri ife atumiki anu.+ Ineyo ndi mkulu wa ophika mkate munatitsekera m’ndende ya kunyumba kwa mkulu wa asilikali olondera mfumu.+ 11 Kundendeko tonse awiri tinalota maloto usiku umodzi. Aliyense analota maloto ake okhala ndi tanthauzo lakelake.+ 12 Tinalinso ndi mnyamata wina wachiheberi+ kumeneko. Iyeyo anali wantchito wa mkulu wa asilikali olondera mfumu.+ Titamufotokozera maloto athu,+ anatimasulira matanthauzo ake. Aliyense anam’masulira malinga ndi maloto amene analota. 13 Zimene anamasulirazo n’zimene zinachitikadi. Ineyo ndinabwezeretsedwa pa ntchito,+ koma mnzangayo anapachikidwa.”+

14 Tsopano Farao anatuma anthu kukatenga Yosefe+ kundendeko,+ kuti abwere naye mofulumira. Choncho Yosefeyo anameta bwinobwino,+ kenako anasintha zovala+ n’kukaonekera pamaso pa Farao. 15 Ndiyeno Farao anauza Yosefe kuti: “Ine ndalota maloto, ndipo palibe munthu amene wakwanitsa kuwamasulira. Koma ndamva kuti iweyo ukamva maloto umatha kumasulira.”+ 16 Pamenepo Yosefe anayankha Farao kuti: “Yemwe anene uthenga wokhudza moyo wa inu Farao ndi Mulungu osati ine.”+

17 Farao anafotokozera Yosefe kuti: “Ndinalota nditaimirira m’mbali mwa mtsinje wa Nailo. 18 Ndiyeno ndinaona ng’ombe 7 zikutuluka mumtsinje wa Nailo. Ng’ombezo zinali zonenepa ndi zooneka bwino, ndipo zinayamba kudya udzu wa m’mbali mwa mtsinjewo.+ 19 Kenako ndinaonanso ng’ombe zina 7 zikutuluka mumtsinjewo pambuyo pa zoyamba zija. Ng’ombe zimenezi zinali zamaonekedwe onyansa ndi zowonda.+ Sindinaonepo ng’ombe zonyansa ngati zimenezo m’dziko lonse la Iguputo. 20 Ng’ombe zowonda ndi zonyansazo zinayamba kudya ng’ombe 7 zonenepa zija.+ 21 Koma zitadya zinzakezo, mimba za ng’ombe zowondazo sizinaoneke kuti mwalowa kanthu, popeza ng’ombezo zinaonekabe zowonda ngati poyamba.+ Pamenepo ndinagalamuka.

22 “Kenako, ndinalotanso maloto ena. Ndinalota ngala 7 za tirigu, zokhwima ndi zooneka bwino, zikutuluka paphesi limodzi.+ 23 Ndinaonanso ngala zina 7 zikutuluka pambuyo pa zoyamba zija. Zimenezi zinali zonyala ndi zowauka ndi mphepo yakum’mawa.+ 24 Ndiyeno ngala zonyalazo zinayamba kumeza ngala 7 zooneka bwinozo.+ Malotowo ndinawafotokoza kwa ansembe amatsenga,+ koma palibe ndi mmodzi yemwe amene anatha kundimasulira.”+

25 Pamenepo Yosefe anauza Farao kuti: “Maloto anu awiriwo tanthauzo lake n’limodzi. Mulungu woona wakudziwitsani zimene adzachite.+ 26 Ng’ombe 7 zonenepazo zikuimira zaka 7. Chimodzimodzinso, ngala 7 zooneka bwinozo zikuimira zaka 7. Malotowa ndi amodzi. 27 Ng’ombe 7 zowonda ndi zonyansazo, zimene zinatuluka pambuyo pa zoyamba zija, zikuimira zaka 7. Koma ngala 7 zimenezo, zopanda kanthu ndi zowauka ndi mphepo yakum’mawa,+ zidzakhala zaka 7 za njala.+ 28 Choncho, monga ndinakuuzirani inu Farao, Mulungu woona wakuonetsani zimene adzachita.+

29 “Kukubwera zaka 7 zimene kudzakhala chakudya chambiri m’dziko lonse la Iguputo. 30 Koma pambuyo pa zaka zimenezo, ndithudi padzabwera zaka 7 za njala. Chakudya chonse chochuluka chija m’dziko la Iguputo sichidzakumbukika m’pang’ono pomwe, ndipo njalayo idzawononga dziko lonse.+ 31 Chifukwa cha njalayo, sikudzadziwika kuti m’dzikoli pa nthawi ina munali chakudya chambiri, pakuti njalayo idzakhaladi yoopsa kwambiri. 32 Popeza kuti inu mwalota kawiri malotowa, ndiye kuti Mulungu woona watsimikiza mtima kuchitadi zimenezi,+ ndipo azichita posachedwapa.+

33 “Tsopano mufunefune munthu wozindikira ndi wanzeru, ndipo mumuike kukhala woyang’anira dziko la Iguputo.+ 34 Muike akapitawo m’dziko lino,+ ndipo iye azitenga gawo limodzi mwa magawo asanu a chakudya cha dziko la Iguputo pa zaka 7 za zokolola zambiri.+ 35 Mwa lamulo lanu, m’zaka zimene kudzakhale chakudya chambiri, akapitawo amenewo azidzasonkhanitsira tirigu yense m’mizinda+ ndi kum’sunga bwino. 36 Chakudya chimenecho chidzakhala chakudya cha dzikoli pa zaka 7 za njala imene idzagwe m’dziko la Iguputo,+ kuti anthu ndi ziweto asadzawonongeke ndi njalayo.”+

37 Zimene Yosefe ananena zinakomera Farao ndi antchito ake onse.+ 38 Pamenepo Farao anafunsa antchito ake kuti: “Kodi pangapezekenso munthu wina wonga uyu, wokhala ndi mzimu wa Mulungu?”+ 39 Kenako Farao anauza Yosefe kuti: “Popeza kuti Mulungu wakudziwitsa zonsezi,+ palibenso munthu wina wozindikira ndi wanzeru ngati iwe.+ 40 Iweyo ukhala woyang’anira nyumba yanga,+ ndipo anthu anga onse azimvera iweyo.+ Ine ndikhala wokuposa pa ufumu wokha.”+ 41 Farao anauzanso Yosefe kuti: “Tsopano ndikukuika kukhala woyang’anira dziko lonse la Iguputo.”+ 42 Atatero, Farao anavula mphete yake yachifumu+ kudzanja lake, n’kuiveka kudzanja la Yosefe. Anamuvekanso malaya amtengo wapatali, ndi tcheni chagolide m’khosi mwake.+ 43 Ndiponso, anamukweza pagaleta* lachiwiri laulemu limene anali nalo,+ ndipo anthu anali kufuula patsogolo pake kuti, “A·vrékh!”* posonyeza kuti ndi wamkulu m’dziko lonse la Iguputo.

44 Farao anauzanso Yosefe kuti: “Farao ndine, koma popanda chilolezo chako, palibe wina aliyense angachite* kanthu m’dziko lonse la Iguputo.”+ 45 Farao atatero, anapatsa Yosefe dzina lakuti, Zafenati-panea.* Anam’patsanso mkazi dzina lake Asenati.+ Mtsikanayu anali mwana wa Potifera, yemwe anali wansembe wa mzinda wa Oni.+ Pamenepo Yosefe anayamba kuyendera dziko la Iguputo.+ 46 Yosefe anali ndi zaka 30+ pamene anayamba kutumikira Farao, mfumu ya Iguputo.

Kenako anachoka pamaso pa Farao n’kuyamba kuyendera dziko lonse la Iguputo. 47 Pa zaka zonse 7 za chakudya chamwanaalirenji, dzikolo linabereka chakudya chambiri.+ 48 Pa zaka 7 zimenezo, Yosefe anasonkhanitsa chakudya chonse chimene anakolola m’dziko lonse la Iguputo, n’kuchisunga m’mizinda.+ Chakudya chonse chochokera m’minda yonse yozungulira mzinda uliwonse, anachisunga pakati pa mzindawo.+ 49 Yosefe anapitiriza kusunga tirigu, mpaka anachuluka kwambiri+ ngati mchenga wa kunyanja. Tiriguyo anachuluka kwadzaoneni, moti sanathenso kumamuyeza chifukwa cha kuchuluka kwake.+

50 Chaka cha njala chisanafike, Yosefe anakhala ndi ana aamuna awiri,+ amene anam’berekera mkazi wake Asenati, mwana wa Potifera, wansembe wa mzinda wa Oni. 51 Mwana woyambayo Yosefe anamutcha dzina lakuti Manase,*+ chifukwa anati, “Mulungu wandiiwalitsa mavuto anga onse, ndi nyumba yonse ya bambo anga.”+ 52 Wachiwiriyo anamutcha Efuraimu,*+ chifukwa anati, “Mulungu wandipatsa ana m’dziko la masautso anga.”+

53 Kenako zaka 7 zosunga chakudya m’dziko la Iguputo zinatha.+ 54 Tsopano zaka 7 za njala zinayamba, monga Yosefe ananenera.+ Njalayo inafalikira m’mayiko onse, koma dziko lonse la Iguputo linali ndi chakudya.+ 55 Potsirizira pake, njala ija inafalikira mpaka m’dziko lonse la Iguputo, ndipo anthu anayamba kulirira Farao kuti awapatse chakudya.+ Koma Farao anauza Aiguputo onse kuti: “Pitani kwa Yosefe! Zilizonse zimene akuuzeni, chitani zomwezo.”+ 56 Njala ija inafalikira padziko lonse lapansi.+ Zitatero, Yosefe anayamba kutsegula nkhokwe zonse zimene zinali pakati pawo n’kuyamba kugulitsa chakudyacho kwa Aiguputo,+ chifukwa njalayo inali itakula kwambiri m’dziko la Iguputo. 57 Komanso, anthu a padziko lonse lapansi anayamba kubwera ku Iguputo kudzagula chakudya kwa Yosefe, pakuti njalayo inali itafika poipa kwambiri padziko lonse lapansi.+

42 Tsopano Yakobo anamva kuti ku Iguputo kuli tirigu,+ ndipo anafunsa ana ake kuti: “Kodi muzingoyang’anana?” 2 Anapitiriza kuti: “Ine ndamva kuti ku Iguputo kuli tirigu.+ Pitani kumeneko mukatigulire tirigu kuti tikhalebe ndi moyo, tingafe ndi njala.” 3 Choncho abale ake a Yosefe 10+ ananyamuka kuti akagule tirigu ku Iguputo. 4 Koma Yakobo sanalole kuti Benjamini,+ m’bale wake wa Yosefe, apite limodzi ndi abale akewo, chifukwa anati: “Mwina angakumane ndi tsoka n’kufa.”+

5 Ndiyeno ana a Isiraeliyo anafika ku Iguputo limodzi ndi anthu ena okagula tirigu, chifukwa m’dziko la Kanani munali njala.+ 6 Tsopano Yosefe ndiye anali wolamulira m’dzikomo.+ Iye ndiye anali kugulitsa tirigu kwa anthu onse ochokera kumayiko ena onse.+ Choncho abale a Yosefe anafika kwa iye. Anamugwadira n’kumuweramira mpaka nkhope zawo pansi.+ 7 Yosefe atawaona abale akewo, anawazindikira nthawi yomweyo, koma anadzisintha kuti asam’dziwe.+ Chotero analankhula nawo mwaukali n’kuwafunsa kuti: “Mwachokera kuti?” Iwo anayankha kuti: “Tachokera kudziko la Kanani, ndipo tabwera kuno kudzagula chakudya.”+

8 Ngakhale kuti Yosefe anawazindikira abale akewo, iwo sanam’zindikire. 9 Nthawi yomweyo Yosefe anakumbukira maloto ake aja onena za abale akewo.+ Pamenepo anawauza kuti: “Inu ndinu akazitape! Ndithu mwabwera kuno kudzafufuza malo amene dziko lathu lili lofooka!”+ 10 Koma iwo anakana kuti: “Ayi mbuyathu,+ akapolo anufe+ tabwera kudzagula chakudya. 11 Tonsefe ndife ana a munthu mmodzi, ndipo ndife anthu achilungamo. Akapolo anufe sitichita zaukazitape ayi.”+ 12 Koma iye anawauza kuti: “Mukunama! Mwabwera kuno kudzafufuza malo ofooka a dziko lathu.”+ 13 Pamenepo iwo anati: “Akapolo anufe tilipo 12 pa ubale wathu.+ Ndife ana a munthu mmodzi amene akukhala ku Kanani.+ Wamng’ono kwambiri watsala ndi bambo athu,+ koma winayo kulibenso.”+

14 Komabe Yosefe anawauza kuti: “Pajatu ndanena kale kuti, ‘Anthu inu ndinu akazitape!’ 15 Chabwino, ndikuyesani motere kuti ndione ngati mukunena zoona: Simuchoka kuno mpaka mng’ono wanuyo atabwera,+ ndithu pali Farao wamoyo! 16 Tumani mmodzi pakati panu apite akatenge mng’ono wanuyo. Enanu ndikutsekerani m’ndende. Ndikufuna ndione ngati zimene mukunena zili zoona.+ Ndipo ngati si zoona, pali Farao wamoyo, ndiye kuti ndinu akazitape basi.” 17 Atatero, anawatsekera pamodzi m’ndende masiku atatu.

18 Pa tsiku lachitatu, Yosefe anawauza kuti: “Popeza ine ndimaopa+ Mulungu woona, chitani izi kuti mukhale ndi moyo: 19 Ngati mulidi achilungamo, mmodzi wa inu atsale m’ndendemu.+ Ena nonsenu pitani, mukapereke tirigu kunyumba zanu chifukwa kuli njala.+ 20 Ndiyeno mukabweretse mng’ono wanuyo kwa ine. Mukatero, ndidzatsimikiza kuti mukunena zoona, ndipo simudzaphedwa.”+ Iwo anavomereza kuchita zimenezo.

21 Kenako iwo anayamba kulankhulana kuti: “Ndithudi, izi zikuchitika chifukwa cha zimene tinachitira m’bale wathu uja.+ Pajatu tinaona kusautsika kwake pamene anatichonderera kuti timumvere chisoni, koma ife sitinalabadire. N’chifukwa chake tsokali latigwera.”+ 22 Ndiyeno Rubeni anayankhira kuti: “Kodi ine sindinanene kuti, ‘Mwanayu musam’chite choipa’? Koma inu simunamve.+ Si izi nanga, magazi ake akufunidwatu kwa ife.”+ 23 Iwo sanadziwe kuti Yosefe anali kumva zimene amanena, chifukwa anali kulankhula nawo kudzera mwa womasulira. 24 Ndiyeno Yosefe anapita payekha kukalira.+ Kenako anabwerako n’kuyambiranso kulankhula nawo, ndipo anatenga Simiyoni+ n’kumumanga iwo akuona.+ 25 Yosefe atatero, analamula anyamata ake kuti awadzazire tirigu m’matumba awo. Anawalamulanso kuti aliyense am’bwezere ndalama zake pomuikira m’thumba lake.+ Anatinso awapatse kamba wa pa ulendo wawo.+ Anyamatawo anawachitiradi zimenezo.

26 Chotero, iwo anasenzetsa abulu awo tiriguyo n’kuyamba ulendo wawo. 27 Atafika pamalo ogona, mmodzi wa iwo anamasula thumba lake kuti atengemo chakudya chopatsa bulu wake.+ Atamasula, anangoona kuti ndalama zake zili pakamwa pa thumbalo.+ 28 Ameneyo anauza abale ake kuti: “Taonani! Ndalama zanga andibwezera, izi zili m’thumbazi!” Pamenepo mitima yawo inangoti myuu! ndipo anayamba kunthunthumira+ n’kuyamba kufunsana kuti: “Kodi Mulungu akutichita chiyani ife?”+

29 Potsirizira pake, anafika kwa bambo awo Yakobo kudziko la Kanani. Iwo anafotokozera bambo awo zonse zimene zinawagwera kuti: 30 “Nduna yaikulu ya dzikolo inalankhula nafe mwaukali,+ chifukwa inatiyesa akazitape okafufuza dzikolo.+ 31 Koma tinaiuza kuti, ‘Ndife anthu achilungamo,+ sitichita zaukazitape ayi. 32 Ndife ana a bambo mmodzi,+ ndipo tilipo 12 pa ubale wathu.+ Mmodzi kulibenso,+ koma wamng’ono ali ndi bambo athu kudziko la Kanani.’+ 33 Koma munthuyo, yemwe ndi nduna yaikulu ya dzikolo, anatiuza kuti,+ ‘Ngati mulidi achilungamo+ muchite izi: Mmodzi wa inu atsale ndi ine kuno.+ Koma enanu tengani chakudya, mupite nacho kunyumba zanu chifukwa kuli njala.+ 34 Mukabweretse m’bale wanu wamng’onoyo kwa ine kuti ndidzatsimikize kuti si inu akazitape koma anthu achilungamo. Mukadzatero, ndidzakubwezerani m’bale wanuyu, ndipo mudzatha kuchita malonda m’dziko lino.’”+

35 Tsopano pamene anali kukhuthula matumba awo, aliyense anapeza mpukutu wa ndalama zake m’thumba lake. Ataziona ndalamazo limodzi ndi bambo awo, onse anachita mantha. 36 Pamenepo Yakobo bambo wawo anadandaula kuti: “Inetu mwandisandutsa namfedwa!+ Yosefe anapita, Simiyoni kulibenso.+ Tsopano mukufuna kutenga Benjamini! Masoka onsewa akugwera ine!” 37 Koma Rubeni anauza bambo ake kuti: “Ndikapanda kudzam’bwezera kwa inu Benjamini, mudzaphe ana anga awiri.+ Mum’pereke m’manja mwanga, ndipo ineyo ndi amene ndidzam’bwezere kwa inu.”+ 38 Komabe bambo awo anati: “Zoti mwana wanga apite nanu, izo ndakana, chifukwa m’bale wake anafa, ndipo iye anatsala yekha.+ Ngati angakumane ndi tsoka n’kufa panjira, ndithu mudzatsitsira ku Manda+ imvi zanga ndi chisoni.”

43 Tsopano njala ija inakula kwambiri m’dzikomo.+ 2 Tirigu amene anachokera naye ku Iguputo uja atatha,+ bambo awo anawauza kuti: “Pitaninso mukatigulireko chakudya pang’ono.”+ 3 Koma Yuda anauza bambo ake kuti:+ “Munthu ujatu anatichenjeza mwamphamvu kuti, ‘Musadzayese n’komwe kuonekeranso pamaso panga mukadzalephera kubwera naye m’bale wanuyo.’+ 4 Ngati mutilola kutenga m’bale wathuyu,+ ndife okonzeka kutsikira ku Iguputo kuti tikagule chakudya. 5 Koma ngati simutilola kupita naye, sititsikirako, chifukwa munthu uja ananenetsa kuti, ‘Musadzayese n’komwe kuonekeranso pamaso panga mukadzalephera kubwera naye m’bale wanuyo.’”+ 6 Pamenepo Isiraeliyo anadandaula+ kuti: “N’chifukwa chiyani munandipweteka chotero, pomuuza munthuyo kuti muli ndi m’bale wanu wina?” 7 Koma iwo anayankha kuti: “Munthuyo anachita kufunsa za ife ndi banja lathu kuti, ‘Kodi bambo anu akali ndi moyo?+ Kodi muli ndi m’bale wanu wina?’ Ndipo ife tinayankha mogwirizana ndi zimene anafunsa.+ Nanga tikanadziwa bwanji zoti anena kuti, ‘Mukam’bweretse kuno m’bale wanuyo’?”+

8 Potsirizira pake, Yuda anauza Isiraeli bambo ake kuti: “M’perekeni kwa ine mnyamatayu+ kuti tinyamuke tizipita. Tipite kuti tikhalebe ndi moyo tisafe,+ inuyo ndi ife, limodzi ndi ana athu aang’onowa.+ 9 Ineyo ndikhala chikole cha moyo wa mnyamatayu.+ Chilangocho chikabwere pa ine.+ Ndikadzalephera kubwera naye ndi kum’pereka kwa inu, ndidzakhale wochimwa kwa inu moyo wanga wonse. 10 Ndipotu tikanapanda kuzengereza, bwenzi pano titapita n’kubwerako maulendo awiri.”+

11 Ndiyeno bambo awo Isiraeli anawauza kuti: “Chabwino, ngati ndi choncho,+ chitani izi: Tengani zinthu zamtengo wapatali za dziko lino m’matumba anu, mukam’patse munthuyo monga mphatso.+ Tengani mafuta a basamu+ pang’ono, uchi+ pang’ono, mafuta onunkhira a labidanamu, khungwa la utomoni wonunkhira,+ mtedza wa pisitasho, ndi zipatso za amondi.+ 12 Mutengenso ndalama kuwirikiza kawiri zoyamba zija. Komanso mutenge ndalama anakubwezerani zija, zimene munazipeza pamwamba pa matumba anu, mukazibweze.+ Mwina anangosokoneza.+ 13 Mukatero, mutenge m’bale wanuyu mubwerere kwa munthuyo. 14 Mulungu Wamphamvuyonse apangitse munthuyo kukuchitirani chifundo,+ kuti akamasule m’bale wanu uja, ndipo mukabwere naye limodzi ndi Benjamini. Koma ngati ndingatayikidwe ana anga, chabwino, zikhale choncho!”+

15 Ndiyeno amunawo anatenga mphatso zija, ndalama zowirikiza kawiri zija, ndiponso Benjamini, n’kunyamuka kupita ku Iguputo. Kumeneko anakaonekera pamaso pa Yosefe.+ 16 Yosefe atangoona Benjamini ali ndi amunawo, anauza mwamuna woyang’anira nyumba yake kuti: “Atengere kunyumba anthuwa. Uphe nyama ndi kukonza chakudya,+ chifukwa anthuwa adya ndi ine masana ano.” 17 Nthawi yomweyo mwamuna uja anachita zimene Yosefe ananena.+ Anatengera anthu aja kunyumba kwa Yosefe. 18 Koma amunawo anachita mantha poona kuti awatengera kunyumba kwa Yosefe.+ Ndipo iwo anati: “Atibweretsa kuno chifukwa cha ndalama zimene tinabwerera nazo m’matumba athu pa ulendo woyamba uja. Ndithu amenewa akufuna atiukire, kuti atigwire tikhale akapolo, ndiponso kuti atilande abulu athu!”+

19 Pamenepo iwo anapita kwa munthu woyang’anira nyumba ya Yosefe uja, n’kulankhula naye pakhomo lolowera kunyumbako, 20 kuti: “Pepani mbuyathu! Ifetu tinabwera kuno kudzagula chakudya ulendo woyamba.+ 21 Pobwerera, zinachitika n’zakuti, titafika pamalo ogona+ n’kumasula matumba athu, tinangoona kuti ndalama za aliyense zili pakamwa pa thumba lake, zonse malinga ndi kulemera kwake. Choncho tabwera nazo kuti tizibweze tokha.+ 22 Tabweranso ndi ndalama zina zogulira chakudya. Koma ndithu sitikudziwa kuti ndani anatibwezera ndalama zathu poziika m’matumba athu.”+ 23 Pamenepo mwamunayo anati: “Musachite mantha,+ simunalakwe kanthu. Mulungu wanu, Mulungu wa bambo anu ndiye anakupatsani chumacho m’matumba mwanu.+ Ndalama zanu zinafikira kwa ine.” Atatero mwamunayo anamasula Simiyoni n’kumubweretsa kwa iwo.+

24 Tsopano munthuyo analowetsa amunawo m’nyumba ya Yosefe. Anawapatsa madzi kuti asambe mapazi awo,+ n’kuwapatsanso chakudya choti adyetse abulu awo.+ 25 Amunawo anakonzeratu mphatso+ zimene anabwera nazo zija kuti apatse Yosefe masanawo, popeza anali atamva kuti adyera nawo limodzi chakudya kumeneko.+ 26 Ndiyeno Yosefe atafika n’kulowa m’nyumbamo, iwo anapereka mphatsozo kwa iye. Anamugwadira n’kumuweramira mpaka nkhope zawo pansi.+ 27 Kenako Yosefe anawafunsa ngati ali bwino.+ Anawafunsanso kuti: “Kodi bambo anu okalamba amene munkanena aja ali bwino? Kodi adakali ndi moyo?”+ 28 Iwo anayankha kuti: “Kapolo wanu bambo athu ali bwino. Adakali ndi moyo.” Atatero anagwada n’kuwerama mpaka nkhope zawo pansi.+

29 Yosefe atakweza maso ake n’kuona mng’ono wake Benjamini, m’bale wake wa mimba imodzi,+ anati: “Kodi uyu ndiye mng’ono wanu amene munali kunena uja?”+ Ananenanso kuti: “Mulungu akukomere mtima+ mwana wanga.” 30 Tsopano Yosefe anachokapo mofulumira chifukwa anagwidwa chifundo mumtima poona m’bale wakeyo.+ Anafunafuna malo oti akalirire, ndipo analowa m’chipinda chamkati n’kukagwetsa misozi.+ 31 Kenako, anasamba kumaso, n’kutuluka panja. Anadzilimbitsa+ n’kunena kuti: “Ikani chakudya.”+ 32 Iwo anaikira Yosefe chakudya payekha. Abale akewo anawaikiranso paokha. Nawonso Aiguputo amene ankadya m’nyumba mwake anawaikira paokha. Aiguputo sankadya limodzi ndi Aheberi, chifukwa chinali chinthu chonyansa kwa iwo.+

33 Abale akewo anakhala pansi pamaso pake, kuyambira woyamba kubadwa malinga ndi ukulu wake,+ mpaka wamng’ono malinga ndi msinkhu wake. Iwo anali kuyang’anana modabwa. 34 Yosefe ankatapa chakudya patebulo pake n’kumapatsa operekera chakudya kuti aziwonjezera pachakudya cha abale akewo. Koma chakudya chowonjezera pa Benjamini anali kuchiwirikiza kasanu kuposa cha enawo.+ Choncho iwo anapitiriza kudya ndi kumwa naye limodzi pamadyererowo mosangalala.+

44 Kenako Yosefe analamula woyang’anira nyumba yake+ uja kuti: “Udzaze chakudya m’matumba a anthuwa mpaka mlingo woti akhoza kunyamula. Aliyense umubwezere ndalama zake poziika pamwamba pa thumba lake.+ 2 Koma uike kapu yanga yasiliva ija pamwamba pa thumba la wamng’onoyo limodzi ndi ndalama zake zogulira tirigu.” Choncho woyang’anira nyumba yakeyo anachita monga mmene Yosefe ananenera.+

3 M’mawa kutacha, abale ake a Yosefe aja analoledwa kupita+ pamodzi ndi abulu awo. 4 Iwo anatuluka mumzindawo koma asanapite patali, Yosefe anauza woyang’anira nyumba yake kuti: “Nyamuka, athamangire anthu aja. Ukawapeza uwafunse kuti, ‘N’chifukwa chiyani mwabwezera zoipa pa zabwino?+ 5 N’chifukwa chiyani mwaba kapu yomwera mbuye wanga, imenenso amaombezera pofuna kudziwa zinthu?+ Mwachita chinthu choipa kwambiri.’”

6 Munthu uja atawapeza, anawafunsa zimenezo. 7 Koma iwo anamuyankha kuti: “N’chifukwa chiyani mukulankhula choncho mbuyathu? N’zosatheka kuti akapolo anufe tichite chinthu chotero. 8 Pajatu ndalama zimene tinazipeza pamwamba pa matumba athu kudziko la Kanani tinazibweza kwa inu.+ Ndiye zingatheke bwanji kuti tibe siliva ndi golide m’nyumba ya mbuye wanu?+ 9 Amene apezeke ndi kapuyo mwa akapolo anufe aphedwe, ndipo enafe tikhale akapolo anu mbuyathu.”+ 10 Ndiyeno iye anati: “Chabwino, zichitike mmene mwaneneramo.+ Amene ati apezeke nacho akhala kapolo wanga,+ koma enanu mukhala opanda mlandu.” 11 Pamenepo, aliyense anatsitsa pansi thumba lake mwamsanga n’kulimasula. 12 Munthu uja anayamba kufufuza mosamala m’matumba awo, kuyambira la wamkulu kumalizira ndi la wamng’ono. Potsirizira pake, kapuyo inapezeka m’thumba la Benjamini.+

13 Zitatero, iwo anang’amba zovala zawo.+ Kenako aliyense anakwezanso thumba lake pabulu wake n’kubwerera kumzinda kuja. 14 Atafika, Yuda+ ndi abale ake analowa m’nyumba ya Yosefe. Anamupeza akanali m’nyumbamo, ndipo anagwada n’kumuweramira mpaka nkhope zawo pansi.+ 15 Tsopano Yosefe anati: “Ndiye chiyani mwachitachi? Kodi inu simukudziwa kuti munthu ngati ine ndimatha kudziwa zinthu poombeza maula?”+ 16 Ndiyeno Yuda anadandaula kuti: “Kodi tinganene chiyani kwa inu mbuyathu? Tilankhule kuti chiyani? Titani kuti muone kuti sitinalakwe?+ Pamenepa Mulungu woona ndiye wapeza cholakwa mwa ife akapolo anu.+ Basi, titengeni ndife akapolo anu mbuyathu,+ ifeyo limodzi ndi amene mwam’peza ndi kapuyo.” 17 Koma Yosefe anati: “Sindingachite zimenezo!+ Amene wapezeka ndi kapu yangayo ndiye akhale kapolo wanga.+ Enanu mupite kwa bambo anu mwamtendere.”+

18 Tsopano Yuda anayandikira kwa Yosefe n’kunena kuti: “Chonde mbuyanga, ndapota nanu. Lolani kuti kapolo wanune ndinene mawu amodzi okha.+ Chonde musandipsere mtima,+ pakuti inu muli ngati Farao+ yemwe. 19 Pajatu inu mbuyanga munatifunsa ife akapolo anu kuti: ‘Kodi muli ndi bambo kapena m’bale wanu wina?’ 20 Ife tinakuyankhani mbuyanga kuti, ‘Bambo tili nawo koma ndi okalamba. Ali ndi mwana amene anabereka atakalamba, amene ndiye wamng’ono pa ife tonse.+ M’bale wake wa mimba imodzi anamwalira, moti anatsala yekha,+ ndipo bambo amam’konda kwambiri.’ 21 Titatero, inu munatiuza ife akapolo anu kuti, ‘Mukabwere naye kuno kuti ndidzamuone.’+ 22 Koma ife tinakuuzani inu mbuyanga kuti, ‘Mwanayo sangachoke kwa bambo. Atati achoke, ndithu bambo adzafa.’+ 23 Ndiyeno munatiuza ife akapolo anu kuti, ‘Musadzayese n’komwe kuonekeranso pamaso panga mukadzalephera kubwera naye m’bale wanuyo.’+

24 “Ife tinapita kwa kapolo wanu, bambo athu, ndipo tinakawauza zimene munanena mbuyanga. 25 Patapita nthawi bambo athu anatiuza kuti, ‘Mubwerere, mukatigulire chakudya pang’ono.’+ 26 Koma ife tinati, ‘Sitingathe kutsikira kumeneko. Ngati tikhala naye limodzi mng’ono wathuyu tipitako, chifukwa sitingathe kukaonekeranso pamaso pa munthuyo tikapanda kupita naye.’+ 27 Ndiyeno kapolo wanu bambo athuwo anatiuza kuti, ‘Inuyo mukudziwa bwino ndithu kuti mkazi wanga anandiberekera ana awiri okha.+ 28 Koma mmodzi wa awiriwo anandisiya, ndipo ndinafuula kuti: “Kalanga ine! Ndithu wakhadzulidwa mwana wanga!”+ Mpaka lero sindinamuonenso. 29 Ndiye ngati uyunso mungapite naye, iye n’kukakumana ndi tsoka n’kufa, ndithu mudzatsitsira ku Manda+ imvi zangazi ndi chisoni.’

30 “Choncho, ndikakangofika kwa kapolo wanu bambo anga, ndilibe mwanayu, amene bambo amam’konda kwambiri ngati mmene amakondera moyo wawo,+ 31 akakangoona kuti mwanayu palibe, basi akafa. Ndithu, akapolo anufe tidzakhala titatsitsira ku Manda imvi za kapolo wanu bambo athu ndi chisoni. 32 Ine kapolo wanu ndinadzipereka kukhala chikole+ cha moyo wa mwanayu pamene ali kutali ndi bambo ake. Ndinalonjeza kuti, ‘Ndikadzalephera kubwera naye kwa inu, ndidzakhale wochimwa kwa inu bambo anga moyo wanga wonse.’+ 33 Ndiye chonde mbuyanga, tengani ineyo ndikhale kapolo wanu m’malo mwa mwanayu, kuti iye apite ndi abale akewa.+ 34 Ndingathe bwanji kupita kwa bambo anga ndilibe mwanayu? Ayi, sindikufuna kukaona bambo anga akuzunzika ndi chisoni.”+

45 Pamenepo Yosefe analephera kudzigwira pamaso pa anthu onse amene anaima pafupi naye.+ Choncho anafuula kuti: “Tulutsani aliyense muno!” Motero, panalibe aliyense amene anali naye pa nthawi imene Yosefe ankadziulula kwa abale ake.+

2 Atatero, anayamba kulira mokweza mawu+ mpaka Aiguputo anamva, ndiponso a kunyumba ya Farao anamva zakuti Yosefe akulira. 3 Kenako Yosefe anauza abale akewo kuti: “Ndine Yosefe! Kodi bambo anga ali moyobe?” Koma abale akewo sanathe kumuyankha chifukwa anali atawasokoneza maganizo.+ 4 Pamenepo Yosefe anauza abale akewo kuti: “Senderani pafupi ndi ine.” Ndipo anasenderadi pafupi naye.

Ndiyeno Yosefe anati: “Ndine m’bale wanu uja Yosefe, amene munamugulitsa ku Iguputo.+ 5 Koma musadzimvere chisoni+ kapena kudzipsera mtima kuti munandigulitsa kuno. Mulungu ndiye ananditumiza patsogolo panu kuti ndidzapulumutse miyoyo yanu.+ 6 Chino ndi chaka chachiwiri cha njala padziko pano.+ Kutsogoloku kukubwera zaka zina zisanu zimene anthu sadzalima kapena kukolola.+ 7 Choncho Mulungu ananditumiza kuno patsogolo panu, kuti pakhale otsalira a anthu inu padziko lapansi,+ ndi kuti mukhalebe ndi moyo mwa chipulumutso chachikulu. 8 Chotero si inu amene munanditumiza kuno,+ koma Mulungu woona. Anachita zimenezi kuti andiike kukhala tate+ kwa Farao, ndi mbuye wa nyumba yake yonse, ndiponso woyang’anira wa dziko lonse la Iguputo.

9 “Pitani kwa bambo anga msanga, ndipo mukawauze kuti, ‘Mwana wanu Yosefe wati: “Mulungu wandiika ine kukhala mbuye wa dziko lonse la Iguputo.+ Bwerani kuno kwa ine, musachedwe. 10 Inuyo, ana anu, adzukulu anu, nkhosa ndi ng’ombe zanu, ndi zonse zimene muli nazo mudzakhale m’dziko la Goseni+ pafupi ndi ine. 11 Kumeneko ndizidzakupatsani chakudya. Kwatsala zaka zisanu za njala,+ ndipo sindikufuna kuti inuyo ndi a m’nyumba yanu, ndi zonse zimene muli nazo muvutike ndi njala.”’ 12 Inuyo ndi m’bale wangayu Benjamini, mukuona ndi maso anu kuti ndine amene ndikulankhula kwa inu ndi pakamwa pangapa.+ 13 Choncho, mukauze bambo anga za ulemerero wanga wonse kuno ku Iguputo, ndi zonse zimene mwaona. Ndipo fulumirani mukatenge bambo anga n’kubwera nawo kuno.”

14 Yosefe atatero, anakumbatira Benjamini m’bale wake n’kuyamba kulira. Nayenso Benjamini analira atakumbatira m’bale wakeyo.+ 15 Pamenepo Yosefe anayamba kupsompsona abale ake onsewo n’kumalira akuwakumbatira.+ Pambuyo pake, abale akewo analankhula naye.

16 Nkhani inamveka kunyumba kwa Farao kuti: “Abale ake a Yosefe abwera!” Farao ndi atumiki ake anasangalala atamva zimenezo.+ 17 Ndiyeno Farao anauza Yosefe kuti: “Uza abale ako kuti, ‘Chitani izi: Kwezani katundu panyama zanu, mupite kudziko la Kanani.+ 18 Mukatenge bambo anu ndi mabanja anu n’kubwera nawo kuno kwa ine. Ndidzakupatsani zabwino za dziko la Iguputo, ndipo mudzadya zonona za dzikoli.+ 19 Uwauzenso kuti:+ “Chitani izi: Mutenge ngolo+ kuno ku Iguputo zokatengera ana anu aang’ono ndi akazi anu. Ngolo ina mukatengere bambo anu n’kubwera kuno.+ 20 Musakadandaule za katundu wanu,+ chifukwa zabwino za dziko lonse la Iguputo ndi zanu.”’”+

21 Ana a Isiraeli aja anachitadi zimenezo. Yosefe anawapatsa ngolo monga momwe Farao analamulira. Anawapatsanso kamba+ wa pa ulendo. 22 Aliyense wa iwo anam’patsa chovala choti asinthire,+ koma Benjamini anam’patsa zovala zosinthira zisanu, ndi ndalama zasiliva 300.+ 23 Kwa bambo ake anatumizako abulu 10 onyamula zinthu zokoma zochokera ku Iguputo, ndi abulu aakazi 10 onyamula tirigu ndi chakudya chawo cha pa ulendo. 24 Atatero, anauza abale akewo kuti anyamuke, ndipo iwo ananyamuka. Koma anawachenjeza kuti: “Musakanganetu m’njira.”+

25 Iwo ananyamuka ku Iguputo kuja n’kuyenda ulendo wawo mpaka kukafika kudziko la Kanani, kwa Yakobo bambo awo. 26 Atafika, anauza bambo awo kuti: “Yosefe uja ali moyo! Ndiye woyang’anira dziko lonse la Iguputo!”+ Yakobo atamva zimenezo sizinam’khudze chifukwa sanazikhulupirire.+ 27 Koma atamufotokozera mawu onse amene Yosefe ananena, ndiponso ataona ngolo zimene Yosefe anatumiza kuti zidzam’tenge, mtima wa Yakobo bambo awo unayamba kubwereramo.+ 28 Pamenepo Isiraeli anafuula kuti: “Basi, tsopano ndakhulupirira! Yosefe mwana wanga akadali ndi moyo! Ndipita ndikamuone ndisanafe!”+

46 Choncho Isiraeli ndi onse a m’nyumba yake ananyamuka kupita ku Beere-seba.+ Kumeneko iye anapereka nsembe kwa Mulungu wa bambo ake Isaki.+ 2 Ndiyeno Mulungu analankhula ndi Isiraeli m’masomphenya usiku,+ kuti: “Yakobo, Yakobo!” Ndipo Yakobo anayankha kuti: “Ine pano!”+ 3 Mulungu anapitiriza kuti: “Ine ndine Mulungu woona,+ Mulungu wa bambo ako.+ Usaope kupita ku Iguputo, chifukwa kumeneko ndidzakukuza kukhala mtundu waukulu.+ 4 Ineyo ndipita nawe ku Iguputo, ndiponso ine ndi amene ndidzabwere nawe kuchokera kumeneko.+ Ndipo Yosefe ndi amene adzakutseke maso pa imfa yako.”+

5 Kenako, Yakobo ananyamuka ku Beere-sebako. Ana a Isiraeliwo anatenga bambo awo, Yakobo, limodzi ndi ana awo aang’ono, ndi akazi awo. Anawatengera m’ngolo zimene Farao anatumiza.+ 6 Anatenganso ziweto zawo zonse ndi katundu wawo yense amene anapeza m’dziko la Kanani.+ Potsirizira pake, Yakobo ndi ana ake onse anafika ku Iguputo. 7 Anafika limodzi ndi ana ake aamuna ndi aakazi, limodzinso ndi adzukulu ake aamuna ndi aakazi obadwa kwa ana ake aamuna, mbadwa zake zonse.+

8 Tsopano nawa mayina a ana a Isiraeli, kapena kuti ana a Yakobo, omwe anabwera nawo ku Iguputo:+ Mwana woyamba wa Yakobo anali Rubeni.+

9 Ndipo ana a Rubeni anali Hanoki, Palu, Hezironi ndi Karami.+

10 Ana a Simiyoni+ anali Yemueli, Yamini, Ohadi, Yakini,+ Zohari ndi Shauli+ mwana wa mkazi wachikanani.

11 Ana a Levi+ anali Gerisoni,+ Kohati+ ndi Merari.+

12 Ana a Yuda+ anali Ere,+ Onani,+ Shela,+ Perezi,+ ndi Zera.+ Komabe, Ere ndi Onani anafera kudziko la Kanani.+

Ana a Perezi anali Hezironi+ ndi Hamuli.+

13 Ana a Isakara+ anali Tola,+ Puva,+ Yabi ndi Simironi.+

14 Ana a Zebuloni+ anali Seredi, Eloni ndi Yahaleeli.+

15 Amenewa ndiwo anali ana a Leya,+ amene anaberekera Yakobo ku Padana-ramu, kuphatikizapo Dina+ mwana wamkazi wa Yakobo. Ana ake onse aamuna ndi aakazi ndi adzukulu ake analipo 33.

16 Ana a Gadi+ anali Zifioni, Hagi, Suni, Eziboni, Eri, Arodi ndi Areli.+

17 Ana a Aseri+ anali Imuna, Isiva, Isivi ndi Beriya.+ Panalinso mlongo wawo Sera.

Ana a Beriya anali Hiberi ndi Malikieli.+

18 Amenewa ndiwo anali ana a Zilipa,+ yemwe Labani anam’pereka kwa mwana wake wamkazi Leya. Ndiwo ana amene Zilipa anaberekera Yakobo m’kupita kwa nthawi. Onse pamodzi analipo 16.

19 Ana a Rakele,+ mkazi wa Yakobo, anali Yosefe+ ndi Benjamini.+

20 Yosefe anabereka Manase+ ndi Efuraimu*+ ku Iguputo. Anabereka anawa kwa mkazi wake Asenati+ mwana wa Potifera, yemwe anali wansembe wa mzinda wa Oni.

21 Ana a Benjamini anali Bela,+ Bekeri,+ Asibeli, Gera,+ Namani,+ Ehi, Rosi, Mupimu,+ Hupimu+ ndi Aridi.

22 Amenewa ndiwo ana amene Rakele anaberekera Yakobo. Onse pamodzi analipo 14.

23 Ana a Dani+ anali Husimu.*+

24 Ana a Nafitali+ anali Yahazeeli, Guni,+ Yezera ndi Silemu.+

25 Amenewa ndiwo anali ana a Biliha,+ yemwe Labani anam’pereka kwa mwana wake wamkazi Rakele. Awa ndiwo ana amene Biliha anaberekera Yakobo m’kupita kwa nthawi. Onse pamodzi analipo 7.

26 Ana onse a Yakobo otuluka m’chiuno mwake,+ amene anali nawo ku Iguputo, analipo 66 onse pamodzi, osawerengera akazi a ana ake. 27 Ana amene Yosefe anabereka ku Iguputo analipo awiri. Onse a m’nyumba ya Yakobo amene anali nawo ku Iguputo analipo 70.+

28 Yakobo anatumiza Yuda+ kuti atsogole kupita kwa Yosefe kukam’dziwitsa za kubwera kwa bambo ake ku Goseni. Pambuyo pake iwo anafika ku Goseni.+ 29 Pamenepo Yosefe anakonza galeta lake n’kunyamuka kupita kukakumana ndi Isiraeli bambo ake ku Goseni.+ Atangofika kwa bambo akewo, nthawi yomweyo anawakumbatira n’kulira ndi kugwetsa misozi. Anachita zimenezi mobwerezabwereza.+ 30 Pamapeto pake Isiraeli anauza Yosefe kuti: “Ndingathe kufa+ tsopano chifukwa ndaona nkhope yako, popeza ukadali ndi moyo.”

31 Ndiyeno Yosefe anauza abale ake ndi a m’nyumba ya bambo ake kuti: “Ndipite kwa Farao ndikam’dziwitse.+ Ndikanene kuti, ‘Abale anga ndi a m’nyumba ya bambo anga, amene anali m’dziko la Kanani, abwera kuno kwa ine.+ 32 Anthuwa ndi abusa,+ pakuti amaweta ziweto.+ Abwera ndi nkhosa zawo, ng’ombe, ndi zinthu zawo zonse.’+ 33 Farao akakuitanani n’kukufunsani kuti, ‘Kodi mumagwira ntchito yanji?’ 34 Inu mukayankhe kuti: ‘Akapolo anufe takhala tikuweta ziweto kuyambira tili ana kufikira lero, ifeyo ndi makolo athu omwe.’+ Mukayankhe choncho kuti mukhale ku Goseni,+ chifukwa aliyense woweta nkhosa Aiguputo amanyansidwa naye.”+

47 Yosefe anafikadi kwa Farao n’kumuuza kuti:+ “Bambo anga ndi abale anga abwera kuchokera ku Kanani. Abwera ndi nkhosa zawo, ng’ombe zawo ndi zonse zimene ali nazo, ndipo afikira ku Goseni.”+ 2 Pa abale ake onsewo, Yosefe anatengapo asanu kuti akawasonyeze kwa Farao.+

3 Ndiyeno Farao anafunsa abale ake a Yosefe aja kuti: “Kodi mumagwira ntchito yanji?”+ Iwo anayankha Farao kuti: “Akapolo anufe timaweta nkhosa+ monga ankachitira makolo athu.”+ 4 Kenako anauza Farao kuti: “Tabwera kuno kudzakhala monga alendo,+ chifukwa akapolo anufe tilibe chakudya chopatsa ziwetozi,+ popeza njala yafika poipa kwambiri ku Kanani.+ Ndiye chonde, tiloleni ife akapolo anu tikhale ku Goseni.”+ 5 Pamenepo Farao anauza Yosefe kuti: “Bambo ako ndi abale akowa abwera kuno kwa iwe. 6 Dziko la Iguputo lili m’manja mwako,+ chotero uwapatse malo abwino koposa.+ Auze akhale ku Goseni,+ ndipo ngati ukudziwapo amuna olimbikira ntchito pakati pawo,+ uwaike kukhala akapitawo oyang’anira ng’ombe zanga.”+

7 Kenako Yosefe anabweretsa bambo ake Yakobo n’kuwasonyeza kwa Farao. Ndipo Yakobo anadalitsa Farao.+ 8 Ndiyeno Farao anafunsa Yakobo kuti: “Kodi muli ndi zaka zingati?” 9 Yakobo anayankha Farao kuti: “Zaka za moyo wanga monga mlendo m’malo osiyanasiyana zikukwana 130.+ Zaka zimenezi zakhala zowerengeka ndi zosautsa,+ ndipo sizinafike pa zaka za moyo wa makolo anga monga alendo m’malo osiyanasiyana.”+ 10 Atatero, Yakobo anadalitsa Farao n’kuchoka pamaso pake.+

11 Chotero Yosefe anakhazika bambo ake ndi abale akewo ku Iguputo. Anawapatsa malo abwino koposa a dzikolo ku Ramese,+ monga mmene Farao analamulira. 12 Kumeneko, Yosefe anali kugawira chakudya bambo ake, abale ake ndi banja lonse la bambo ake,+ malinga ndi kuchuluka kwa ana.+

13 Njala itafika poipa kwambiri,+ chakudya chinatheratu m’dziko lonselo. Anthu onse a ku Iguputo ndi a ku Kanani anali ofooka chifukwa cha njalayo.+ 14 Yosefe anasonkhanitsa ndalama zonse zimene zinali m’dziko la Iguputo ndi la Kanani, zomwe anthu anali kugulira chakudya.+ Iye anali kutenga ndalamazo kuzipititsa kunyumba kwa Farao. 15 Potsirizira pake, ndalama zonse za m’dziko la Iguputo ndi dziko la Kanani zinatha. Pamenepo anthu onse a ku Iguputo anayamba kufika kwa Yosefe n’kunena kuti: “Tipatseni chakudya!+ Kodi tikufereni mukuona chifukwa choti ndalama zatithera?”+ 16 Ndiye Yosefe anati: “Ngati ndalama zakutherani, bweretsani ziweto zanu tidzasinthane ndi chakudya.” 17 Pamenepo anthuwo anayamba kubweretsa ziweto zawo kwa Yosefe. Yosefeyo anali kuwapatsa chakudya mosinthana ndi mahatchi* awo, nkhosa, ng’ombe ndi abulu.+ M’chaka chonsecho, Yosefe anali kuwagawira chakudya mosinthana ndi ziweto zawo.

18 Kenako, chakacho chinafika kumapeto, ndipo anthu anayamba kufika kwa iye chaka chotsatira. Iwo ankanena kuti: “Sitikubisirani mbuyathu, ndalama zathu ndi ziweto zonse zathera kwa inu.+ Zimene tangotsala nazo ndi matupi athuwa ndi nthaka yathuyi basi.+ 19 Tiferenji ife inu mukuona,+ ndipo minda yathu ikhalirenji yogonera? Mutigule limodzi ndi minda yathu potipatsa chakudya+ kuti tikhale akapolo a Farao. Mutipatse tirigu kuti tikhale ndi moyo tisafe, kutinso minda yathu isagonere.”+ 20 Choncho, Yosefe anagulira Farao nthaka yonse ya Aiguputo,+ chifukwa Mwiguputo aliyense anagulitsa munda wake. Anatero chifukwa njala inali itawapanikiza koopsa, moti nthaka yonse inakhala ya Farao.

21 Yosefe anasamutsira anthuwo m’mizinda, kuchokera kumalire a dziko la Iguputo mpaka kumalire ena.+ 22 Nthaka ya ansembe+ yokha ndi imene sanaigule, chifukwa chakudya chimene ansembe anali kudya chinali kuchokera kwa Farao.+ N’chifukwa chake ansembewo sanagulitse nthaka yawo.+ 23 Tsopano Yosefe anauza anthuwo kuti: “Onani, ndakugulani inu lero limodzi ndi nthaka yanu, kugulira Farao. Nayi mbewu, mubzale m’minda yanu.+ 24 Pa nthawi yokolola,+ muzipereka kwa Farao gawo limodzi mwa magawo asanu a zokololazo.+ Magawo anayi otsalawo muzigwiritsa ntchito monga mbewu yobzala m’minda yanu, chakudya chanu ndi cha a m’nyumba zanu, komanso cha ana anu.”+ 25 Iwo anayankha kuti: “Mwapulumutsa miyoyo yathu.+ Mwatikomera mtima mbuyathu, ndipo tidzakhala akapolo a Farao.”+ 26 Chotero Yosefe anakhazikitsa lamulo limene lilipobe mpaka lero lakuti, Farao azilandira gawo limodzi mwa magawo asanu a zokolola za minda yonse ya mu Iguputo. Koma ansembe, monga gulu lapadera, minda yawo sinakhale ya Farao.+

27 Aisiraeliwo anakhazikika m’dziko la Iguputo, m’chigawo cha Goseni.+ Kumeneko anaberekana n’kuchulukana kwambiri.+ 28 Ndipo Yakobo anakhalabe ndi moyo m’dziko la Iguputo kwa zaka 17. Choncho masiku onse a moyo wa Yakobo anakwana zaka 147.+

29 Tsopano nthawi inayandikira yakuti Isiraeli amwalire.+ Ndiye anaitana mwana wake Yosefe n’kumuuza kuti: “Ngati ungandikomere mtima, ika dzanja lako pansi pa ntchafu yanga.+ Ulumbire kuti udzandisonyeza kukoma mtima kosatha ndipo udzakhala wokhulupirika kwa ine.+ Chonde, usadzandiike m’manda ku Iguputo kuno.+ 30 Ndikufuna ndikagone limodzi ndi makolo anga.+ Choncho udzandinyamule ku Iguputo kuno, ukandiike m’manda a makolo anga.”+ Yosefe anayankha kuti: “Ndidzachitadi monga mwa mawu anu.” 31 Ndiyeno Yakobo anati: “Lumbira kwa ine.” Yosefe analumbira kwa iye.+ Pamenepo Isiraeli anawerama n’kutsamira kumutu kwa bedi lake.+

48 Ndiyeno patapita nthawi Yosefe anauzidwa kuti: “Bambo anutu afooka.” Pamenepo, Yosefe anatenga ana ake awiri, Manase ndi Efuraimu,+ n’kupita kwa bambo akewo. 2 Ndiyeno Yakobo anauzidwa kuti: “Mwana wanu Yosefe wabwera.” Choncho Isiraeli anadzuka modzilimbitsa n’kukhala tsonga pabedi. 3 Tsopano Yakobo anauza Yosefe kuti:

“Mulungu Wamphamvuyonse anaonekera kwa ine ku Luzi+ m’dziko la Kanani kuti andidalitse.+ 4 Ndipo anandiuza kuti, ‘Ndidzakupatsa ana,+ ndipo mwa iwe mudzatuluka mitundu yambiri ya anthu.+ Dziko ili ndidzalipereka kwa mbewu yako kuti lidzakhale dziko lawo mpaka kalekale.’+ 5 Tsopano ana awiri amene unabereka ku Iguputo kuno ine ndisanabwere, ndi ana anga.+ Efuraimu ndi Manase akhala ana anga monga alili Rubeni ndi Simiyoni.+ 6 Koma ana amene udzabereke pambuyo pa anawa, amenewo adzakhala ako. Iwo adzalandira mbali ya malo amene abale awo adzalandire ngati cholowa.+ 7 Kunena za ine, pamene ndinali kuchokera ku Padani,+ mayi ako Rakele anandifera+ panjira m’dziko la Kanani, patatsala mtunda ndithu kuti tifike ku Efurata. Zitatero, ndinawaika m’manda panjira yopita ku Efurata,+ kapena kuti Betelehemu.”+

8 Tsopano Isiraeli anaona ana a Yosefe, ndipo anafunsa kuti: “Kodi awa ndani?”+ 9 Yosefe anayankha bambo akewo kuti: “Ndi ana anga amene Mulungu wandipatsa kunoko.”+ Ndiyeno bambo akewo anati: “Chonde, tawabweretsa kuno ndiwadalitse.”+ 10 Maso a Isiraeli anali atafooka chifukwa chokalamba,+ moti sankatha kuona. Yosefe anabweretsa anawo pafupi ndi bambo ake, ndipo bambo akewo anawapsompsona anawo n’kuwakumbatira.+ 11 Ndiyeno Isiraeli anauza Yosefe kuti: “Ndinalibiretu chiyembekezo choti ndidzaonanso nkhope yako,+ koma tsopano Mulungu wandilola kuona iwe limodzi ndi ana ako omwe.” 12 Atatero, Yosefe anachotsa anawo pambali pa mawondo a bambo ake. Kenako, anagwada n’kuwerama mpaka nkhope yake pansi.+

13 Tsopano Yosefe anatenga ana ake awiriwo. Efuraimu anamuika kudzanja lake lamanja, kumanzere kwa Isiraeli.+ Ndipo Manase anamuika kudzanja lake lamanzere, kudzanja lamanja la Isiraeli.+ Atatero, anawabweretsa pafupi ndi bambo ake. 14 Koma Isiraeli anatambasula dzanja lake lamanja n’kuliika pamutu pa Efuraimu,+ ngakhale kuti ndiye anali wamng’ono.+ Anatambasulanso dzanja lake lamanzere n’kuliika pamutu pa Manase.+ Anasemphanitsa dala choncho manja ake chifukwa Manase ndiye anali mwana woyamba.+ 15 Pamenepo anadalitsa Yosefe,+ kuti:

“Mulungu woona amene makolo anga Abulahamu ndi Isaki anayenda pamaso pake,+

Mulungu woona amene wakhala m’busa wanga moyo wanga wonse mpaka lero,+

16 Mngelo amene wakhala akundiwombola ku masoka anga onse,+ adalitse anyamatawa.+

Dzina langa ndi mayina a makolo anga, Abulahamu ndi Isaki, apitirize kutchulidwa kudzela mwa anawa,+

Komanso, anawa adzachulukane, adzakhale khamu la anthu padziko lapansi.”+

17 Yosefe ataona kuti bambo ake aika dzanja lawo lamanja pamutu pa Efuraimu, sizinamusangalatse.+ Choncho, anagwira dzanja la bambo ake kuti alichotse pamutu pa Efuraimu, n’kuliika pamutu pa Manase.+ 18 Yosefe anauza bambo ake kuti: “Ayi bambo, musatero ayi. Mwana woyamba ndi uyu.+ Ikani dzanja lanu lamanja pamutu pake.” 19 Koma bambo akewo anakanabe, kuti: “Ndikudziwa mwana wanga, ndikudziwa zimenezo. Uyunso adzakhala mtundu wa anthu, ndipo adzakhala wamkulu.+ Koma mng’ono wakeyu adzakhala wamkulu kuposa iyeyu,+ ndipo mbadwa zake zidzachuluka kwambiri n’kupanga mitundu ya anthu.”+ 20 Iye anapitiriza kuwadalitsa pa tsikulo.+ Anati:

“Pogwiritsa ntchito dzina lako, Aisiraeli azidzadalitsana kuti,

‘Mulungu akudalitse monga anadalitsira Efuraimu ndi Manase.’”+

Choncho Isiraeli anaikabe Efuraimu patsogolo pa Manase.+

21 Isiraeli atatero, anauza Yosefe kuti: “Taona, inetu ndikufa.+ Koma Mulungu adzakhalabe nanu ndithu anthu inu, ndipo adzakubwezerani kudziko la makolo anu.+ 22 Koma ine ndikukuwonjezera gawo limodzi la dziko kuposa abale ako,+ limene ndinalanda Aamori ndi lupanga langa ndi uta wanga.”

49 Pambuyo pake, Yakobo anaitana ana ake n’kuwauza kuti: “Sonkhanani pamodzi kuti ndikuuzeni zimene zidzachitika kwa inu m’masiku am’tsogolo. 2 Bwerani pamodzi nonse kuti mumvetsere, inu ana a Yakobo. Bwerani mumvetsere kwa Isiraeli bambo anu.+

3 “Rubeni, iwe ndiwe mwana wanga woyamba kubadwa,+ nyonga yanga ndi poyambira mphamvu zanga zobereka.+ Unayenera kukhala ndi ulemu wopambana ndi mphamvu zopambana. 4 Usakhale wopambana, chifukwa ndi khalidwe lako lotayirira ngati madzi osefukira,+ unakwera pogona bambo ako.+ Unaipitsa bedi langa pa nthawiyo.+ Anagonapo ndithu ameneyu!

5 “Simiyoni ndi Levi m’pachibale pawo.+ Malupanga awo ndiwo zida zochitira zachiwawa.+ 6 Pagulu lawo, moyo wanga usakhale nawo.+ Maganizo anga asagwirizane ndi mpingo wawo,+ chifukwa atakwiya anapha anthu,+ ndipo mwankhanza zawo, anapundula* ng’ombe zamphongo. 7 Utembereredwe mkwiyo wawo+ chifukwa ndi wankhanza,+ ndi ukali wawo chifukwa umachita mwachiwawa.+ Ndidzawamwaza mwa Yakobo, ndipo ndidzawabalalitsa mwa Isiraeli.+

8 “Koma iwe Yuda,+ abale ako adzakutamanda.+ Dzanja lako lidzakhala pambuyo pa khosi la adani ako.+ Ana a bambo ako adzakugwadira.+ 9 Yuda ndi mwana wa mkango.+ Umapha nyama n’kubwerako ndithu, mwana wanga. Iye amapinda mawondo ake n’kudziwongola ngati mkango utagona pansi. Ndipo monga mkango, ndani angamudzutse?+ 10 Ndodo yachifumu sidzachoka kwa Yuda,+ ndiponso chibonga cha wolamulira sichidzachoka pakati pa mapazi ake, kufikira Silo*+ atabwera. Ndipo mitundu ya anthu idzamumvera.+ 11 Atamanga bulu wake wamphongo pamtengo wa mpesa, ndi kamwana ka bulu wake wamkazi pamtengo wa mpesa wabwino, ndithu, adzachapa zovala zake m’vinyo, ndi malaya ake m’madzi ofiira a mphesa.+ 12 Maso ake ndi ofiira ndi vinyo, ndipo mano ake ndi oyera ndi mkaka.

13 “Zebuloni adzakhala kugombe la nyanja,+ pafupi ndi gombe lokochezapo zombo.+ Malire ake akutali adzakhala cha ku Sidoni.+

14 “Isakara+ ndi bulu wa mafupa olimba, amagona pansi atasenza matumba a katundu uku ndi uku. 15 Adzaona kuti malo opumirawo ndi abwino, ndi kuti dzikolo n’losangalatsa. Adzaweramitsa phewa lake kuti anyamule akatundu, ndipo adzakakamizidwa kugwira ntchito yakalavulagaga ngati kapolo.

16 “Dani adzaweruza anthu a mtundu wake monga mmodzi wa mafuko a Isiraeli.+ 17 Dani adzakhala njoka yobisala m’mbali mwa msewu, njoka yokhala ndi tinyanga yobisala m’mphepete mwa njira, imene imaluma chidendene cha hatchi ndipo wokwerapo amagwa chagada.+ 18 Ndithu ndidzayembekezera chipulumutso kwa inu, Yehova.+

19 “Kunena za Gadi, gulu la achifwamba lidzamuukira, koma iye adzawathira nkhondo, ndipo achifwambawo pothawa iye adzawakantha koopsa.+

20 “Chakudya chochokera kwa Aseri chidzakhala chonona,+ ndipo chakudya chokoma cha mfumu chidzachokera kwa iye.+

21 “Nafitali+ ndi mbawala yaikazi yopepuka miyendo, ndipo amanena mawu okoma.+

22 “Yosefe ndi mphukira yamtengo wobala zipatso.+ Ndithu iye ndi mphukira yamtengo wobala zipatso pakasupe.+ Iye ndi mtengo woponya nthambi zake pamwamba pa khoma* la mpanda.+ 23 Oponya mivi ndi uta sanaleke kumuzunza, kumulasa ndi kumusungira chidani.+ 24 Koma uta wake unakhalabe pamalo ake achikhalire,+ ndipo manja ake anali amphamvu ndi ochenjera.+ M’busayo, Mwala wa Isiraeli,+ akuchokera m’manja mwa Wamphamvu wa Yakobo.+ M’busayo akuchokera kumeneko ndithu. 25 Iye ndi wochokera kwa Mulungu wa bambo ako,+ ndipo adzakuthandiza.+ Iye ali ndi Wamphamvuyonse,+ ndipo Mulunguyo adzakudalitsa ndi madalitso ochokera kumwamba,+ ndi madalitso a pansi pa madzi akuya,+ ndi madalitso a mabere a mkaka wambiri, ndi a mimba yobereka.+ 26 Madalitso a bambo ako adzapambana madalitso a mapiri amene adzakhalapo mpaka kalekale.+ Adzapambananso ulemerero wa zitunda zosatha.+ Madalitsowo adzakhalabe pamutu pa Yosefe, paliwombo pa wosankhidwa pakati pa abale ake.+

27 “Benjamini adzapitiriza kukhadzula ngati mmbulu.+ M’mawa adzadya nyama imene wagwira, ndipo madzulo adzagawa zimene wafunkha.”+

28 Onsewa ndiwo mafuko 12 a Isiraeli, ndipo izi n’zimene bambo awo analankhula kwa iwo powadalitsa. Anapatsa aliyense wa iwo madalitso ake omuyenerera.+

29 Atatero anawalamula kuti: “Ine uno ndi ulendo wopita kumene kunapita makolo anga.+ Mukandiike limodzi ndi makolo anga, m’phanga limene lili m’munda wa Efuroni, Mhiti.+ 30 Ndithu mukandiike m’phanga limene lili m’munda wa Makipela, umene uli moyang’anana ndi munda wa Mamure, m’dziko la Kanani. Mundawo ndi umene Abulahamu anagula kwa Efuroni, Mhiti, kuti akhale ndi manda.+ 31 Kumeneko n’kumene anaika Abulahamu ndi mkazi wake Sara.+ N’kumene anaika Isaki ndi Rabeka mkazi wake,+ ndipo n’kumene ndinaika Leya. 32 Munda umene anaugulawo, ndiponso phanga limene lili mmenemo, zinali za ana a Heti.”+

33 Yakobo atamaliza kulangiza ana akewo, anabwezeranso miyendo yake pabedi, n’kumwalira. Kenako anaikidwa m’manda n’kugona limodzi ndi makolo ake.+

50 Pamenepo Yosefe anakumbatira mtembo wa bambo ake+ ndipo analira kwambiri n’kuupsompsona.+ 2 Kenako Yosefe analamula atumiki ake omwe anali madokotala, kuti akonze mtembo wa bambo ake ndi mankhwala kuti usawonongeke.+ Choncho madokotalawo anakonza mtembo wa Isiraeli. 3 Anatenga masiku 40 kukonza thupi lake, pakuti kukonza mtembo kunali kutenga masiku ochuluka choncho. Aiguputowo anamulirabe Isiraeli kwa masiku 70.+

4 Masiku olira maliro a Yakobo atatha, Yosefe anauza a m’nyumba ya Farao kuti: “Ngati mungandikomere mtima,+ chonde ndilankhulireni kwa Farao kuti, 5 ‘Bambo anga anandilumbiritsa+ kuti: “Inetu ndikufa.+ Ukandiike m’manda+ amene ndinadzikonzera m’phanga kudziko la Kanani.”+ Ndiye chonde, ndiloleni ndipite ndikaike bambo anga, pambuyo pake ndikabweranso.’” 6 Pamenepo Farao anayankha kuti: “Pita ukaike bambo ako monga anakulumbiritsira.”+

7 Choncho Yosefe anapita kukaika bambo ake. Atumiki onse a Farao, akuluakulu+ a m’nyumba yake, ndi akuluakulu onse a m’dziko la Iguputo anam’perekeza. 8 Onse a m’nyumba ya Yosefe, abale ake, ndi a m’nyumba ya bambo ake,+ anapita naye limodzi. Ku Goseni kunangotsala ana awo aang’ono, nkhosa, mbuzi ndi ng’ombe zawo. 9 Anatenganso magaleta+ ndi a pamahatchi, moti gululo linakhala lalikulu kwambiri. 10 Kenako anafika pamalo opunthira mbewu+ a Atadi m’chigawo cha Yorodano.+ Kumeneko, anthuwo analira ndi kubuma kwakukulu, ndipo Yosefe anachita nawo miyambo yolirira maliro a bambo ake kwa masiku 7.+ 11 Akanani amene anali kukhala m’dzikolo anaona miyambo yolirira maliro imene inali kuchitikira pamalo opunthira mbewu a Atadi. Ataona choncho, iwo anati: “Maliro amene agwera Aiguputowa ndi aakulu!” N’chifukwa chake malowo anawatcha Abele-miziraimu,* ndipo ali m’chigawo cha Yorodano.+

12 Ana a Yakoboyo anam’chitira zonse monga mmene iye anawalamulira.+ 13 Anamunyamula n’kupita naye kudziko la Kanani. Kumeneko anakamuika m’phanga m’munda wa Makipela, woyang’anana ndi munda wa Mamure.+ Mundawo ndi umene Abulahamu anagula kwa Efuroni Mhiti, kuti akhale ndi manda. 14 Yosefe ataika bambo ake m’manda, anabwerera ku Iguputo limodzi ndi abale ake ndi onse amene anam’perekeza pokaika bambo ake.

15 Bambo awo atamwalira, abale ake a Yosefe anayamba kunena kuti: “Mwina Yosefe anatisungira chidani,+ ndipo ndithu atibwezera pa zoipa zonse zimene tinam’chitira.”+ 16 Choncho iwo anauza Yosefe kuti: “Bambo anu asanamwalire anatisiyira mawu. Anatiuza kuti, 17 ‘Mukamuuze Yosefe kuti: “Chonde ndikukupempha, ukhululuke+ chiwembu cha abale ako, ndi kuchimwa kwawo pa zoipa zimene anakuchitira.”’+ Ndiye chonde, tikhululukireni ife akapolo a Mulungu wa bambo anu.”+ Atamuuza zimenezi, Yosefe analira kwambiri. 18 Kenako abale akewonso anafika, n’kudzigwetsa pansi pamaso pake, n’kunena kuti: “Tikudzipereka kwa inu ngati akapolo anu.”+ 19 Pamenepo Yosefe anawauza kuti: “Musaope ayi. Kodi ine ndatenga malo a Mulungu?+ 20 Inu munali ndi cholinga chondichitira zoipa. Koma Mulungu anali ndi cholinga chabwino, kuti apulumutse miyoyo ya anthu ambiri ngati mmene akuchitira panomu.+ 21 Choncho musachite mantha. Ine ndipitiriza kukugawirani chakudya limodzi ndi ana anu.”+ Anawalimbikitsa n’kuwatsimikizira motero.

22 Yosefe anakhalabe ku Iguputoko limodzi ndi a m’nyumba ya bambo ake. Zaka za moyo wa Yosefe zinali 110 zonse pamodzi. 23 Yosefe anakhalabe ndi moyo mpaka kuona ana a Efuraimu a m’badwo wachitatu.+ Anaonanso ana a Makiri+ mwana wa Manase. Onsewo anabadwira pamiyendo pa Yosefe.+ 24 Potsirizira pake, Yosefe anauza abale ake kuti: “Ine ndikufa, koma Mulungu adzakucheukirani,+ ndipo adzakutulutsani ndithu m’dziko lino. Adzakupititsani kudziko limene analonjeza polumbira kwa Abulahamu, kwa Isaki ndi kwa Yakobo.”+ 25 Tsopano Yosefe analumbiritsa ana a Isiraeliwo, kuti: “Ndithu Mulungu adzakucheukirani. Akadzatero mudzanyamule mafupa anga pochoka kuno.”+ 26 Patapita nthawi, Yosefe anamwalira ali ndi zaka 110. Thupi lake analikonza ndi mankhwala kuti lisawonongeke,+ ndipo analiika m’bokosi ku Iguputoko.

Kapena kuti “mzimu wa Mulungu.”

Mawu achiheberi amene tawamasulira kuti “nyama zokwawa” amatanthauza zamoyo zimene zimayenda chokwawa monga nyama zing’onozing’ono, mbewa, abuluzi, njoka, ndi tizilombo tina ting’onoting’ono.

Ena amati “zolasa.”

Dzina limeneli limatanthauza “Wamoyo.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Dzina limeneli limatanthauza “Woberekedwa.”

Dzina lachiheberi lakuti “Seti” limatanthauza “Kusankhidwa; Kuika; Kukhazikitsa,” m’lingaliro la kulowa m’malo.

Kapena “wandisankhira.”

Mawu akuti “Anefili” amatanthauza “ogwetsa anzawo.”

“Mkono umodzi” ndi wofanana ndi masentimita 44 ndi hafu.

Mawu achiheberi ndi “tsoʹhar,” ndipo angatanthauze “windo” kapenanso “denga.”

Kapena kuti “tsindwi.”

Onani Zakumapeto 4.

“Mwezi wachiwiri” umene ukutchulidwa m’vesili unadzakhala mwezi wa 8 pakalendala yopatulika imene Yehova anapatsa Aisiraeli atatuluka m’dziko la Iguputo. Mwezi umenewu, wotchedwa Buli, unkayambira chapakati pa October n’kutha chapakati pa November. Onani Zakumapeto 13.

Mawu akuti “madzi akuya” m’vesili akutanthauza madzi akuthambo omwe analipo kuzungulira dziko lapansi. Madzi amenewa akutchulidwanso pa Ge 1:6, 7 kuti, ‘madzi . . . a pamwamba pa mlengalenga.’

Onani mawu a m’munsi pa Ge 1:24.

Onani Zakumapeto 4.

“Mwezi wa 7” umene ukutchulidwa m’vesili unali kuyenderana ndi mwezi wa Abibu pakalendala yopatulika ya Ayuda. Pakalendala ya Ayuda imeneyi, mwezi wa Abibu kapena kuti Nisani, unali mwezi woyamba.

Mawu omasuliridwa kuti “zilumba” pano kwenikweni amatanthauza madera a m’mphepete mwa nyanja.

Dzina lakuti “Pelegi” limatanthauza “Kugawika” ndiponso “Mfuleni.”

Kapena kuti “adzadzidalitsa okha,” kusonyeza kuti akufunika kuchitapo kanthu kuti apeze madalitsowo.

Kapena kuti “kumunsi kwa chigwa cha Yorodano.”

Kapena kuti “amene akundiona,” kapena “amene amalola kuonedwa.”

Dzina lakuti “Beere-lahai-roi” limatanthauza “Chitsime cha Wamoyo Amene Amandionayo.”

Muyezo umodzi wa seya unali wokwana malita pafupifupi 8.

Onani mawu a m’munsi pa Ge 12:3.

Mawu ake enieni, “pansi pa mthunzi wa denga langa.”

Onani mawu a m’munsi pa Ge 13:10.

Dzina lakuti “Zowari” limatanthauza “Kuchepa.”

Mwina limeneli linali dzina laudindo.

Mawu achiheberi amene m’vesili tawamasulira kuti “chisangalalo” ndiponso kuti “asangalala,” amatanthauza “kuseka.”

Dzina lakuti “Beere-seba” limatanthauza “Chitsime cha Lumbiro” kapena, “Chitsime cha 7.”

Dzina lakuti “Yehova-yire” limatanthauza kuti, “Yehova Adziwa Chochita,” ndiponso kuti, “Yehova Adzapereka Zinthu Zofunikira.”

“Chipata” ichi ndi chipata cha mzinda.

Onani mawu a m’munsi pa Ge 12:3.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Mawu ake enieni, “ndiike malemu anga kuti ndisawaonenso.”

“Sekeli” unali muyezo wachiheberi wa kulemera kwa chinthu ndi wotchulira ndalama. Sekeli imodzi inali yofanana ndi magalamu 11.4, ndipo mtengo wake unali wofanana ndi madola 2.20 a ku America.

Dzina lakuti “Esau” limatanthauza “Wacheya.”

Dzina lakuti “Edomu” limatanthauza “Chofiira” kapena “Wofiira.”

Onani mawu a m’munsi pa Ge 12:3.

Mawu achiheberi amene tawamasulira kuti “chigwa” angatanthauze chigwa chimene mumadutsa mtsinje, ndipo angatanthauzenso mtsinje weniweniwo. Chigwa choterocho nthawi zambiri chimakhala chouma koma nthawi zina mumadutsa madzi ambiri.

Dzina lakuti “Eseke” limatanthauza “Mkangano.”

Dzina lakuti “Rehoboti” limatanthauza “Malo Aakulu.”

Dzina lakuti “Siba” limatanthauza “Lumbiro” kapena “7.”

“Cheya” ndi ubweya wa pathupi la munthu.

Dzina lakuti “Yakobo” limatanthauza “Kugwira Chidendene” ndiponso kuti “Wochenjerera Mnzake.”

“Isimaeli” pano amatanthauza “Aisimaeli.” Pa nthawiyi Isimaeli anali atamwalira kale, ndipo Esau anali ndi zaka pafupifupi 77. Onani Ge 25:17, 26.

Onani mawu a m’munsi pa Ge 12:3.

Kapena kuti “kuti ndigone naye.”

Dzina lakuti “Rubeni” limatanthauza “Onani, ndi Mwana Wamwamuna!”

Dzina lakuti “Simiyoni” limatanthauza “Kumvedwa.”

Dzina lakuti “Levi” limatanthauza “Kuphatika,” “Kulumikiza,” kapenanso “Kukonda.”

Dzina lakuti “Yuda” limatanthauza “Tamandika,” ndiponso “Wotamandika.”

Mawu ake enieni, “aberekere pamawondo anga.”

Dzina lakuti “Dani” limatanthauza “Woweruza.”

Dzina lakuti “Nafitali” limatanthauza “Ndalimbana Nazo.”

Dzina lakuti “Gadi” limatanthauza “Mwayi.”

Dzina lakuti “Aseri” limatanthauza “Kusangalala” ndiponso “Chisangalalo.”

“Mandereki” ndi chitsamba cha m’gulu la mbatata, chimene chimabereka zipatso.

Dzina lakuti “Isakara” limatanthauza “Iye Ndi Malipiro” ndiponso kuti, “Amabweretsa Malipiro.”

Dzina lakuti “Zebuloni” limatanthauza “Malo Okhala,” kapenanso “Kulolera.”

Dzina lakuti “Yosefe” limatanthauza “Woonjezera.”

“Aterafi” ndi milungu kapena mafano a banja.

Umenewu ndi mtsinje wa Firate.

“Yegara-sahaduta” ndi dzina lachiaramu lotanthauza kuti “Mulu wa Umboni.”

“Galeeda” ndi dzina lachiheberi lotanthauza kuti “Mulu wa Umboni.”

Dzina lakuti “Mahanaimu” limatanthauza “Magulu Awiri.”

Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.

“Nsukunyu” ndi mfundo ya chiuno, pamene fupa la ntchafu limalumikizana ndi chiuno.

Dzina lakuti “Isiraeli” limatanthauza kuti “Mulungu Walimbana Naye,” ndiponso kuti “Walimbana ndi Mulungu.”

Dzina lakuti “Penieli” limatanthauza “Nkhope ya Mulungu.”

Dzina lakuti “Sukoti” limatanthauza “Makola” ndiponso “Makola Adenga.”

Ena amati, “masikiyo.”

Dzina lakuti “Eli-beteli” limatanthauza kuti “Mulungu wa Beteli.”

Dzina lakuti “Aloni-bakuti” limatanthauza “Chimtengo Chachikulu Cholirirapo.”

“Mzamba” ndi munthu amene amathandiza amayi pobereka. Ena amamutcha “namwino.”

Dzina lakuti “Beni-oni” limatanthauza “Mwana wa Chisoni Changa.”

Dzina lakuti “Benjamini” limatanthauza “Mwana wa Dzanja Langa Lamanja.”

“Mkazi wamng’ono” ameneyu anali mdzakazi wa Rakele.

Umenewu ndi mtsinje wa Firate.

Mawu ake enieni, “thupi.”

Kapena kuti “saka.”

Onani Zakumapeto 5.

Dzina lakuti “Perezi” limatanthauza kung’amba njira yotulukira mwana pobadwa.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Mawu olembedwa m’Chiheberi kuti “A·vrékh!” anatengedwa ku Chiiguputo, koma tanthauzo lenileni silinadziwikebe bwinobwino.

Mawu ake enieni, “palibe aliyense amene anganyamule dzanja lake kapena phazi lake.”

Kwa Aheberi, dzina lakuti “Zafenati-panea” linali kutanthauza “Wovumbula Zinthu Zobisika.”

Dzina lakuti “Manase” limatanthauza “Wochititsa Kuiwala,” ndiponso “Woiwalitsa.”

Dzina lakuti “Efuraimu” limatanthauza “Wobereka Mowirikiza,” ndiponso “Dziko Lachonde.”

Pambuyo potchula “Efuraimu,” Baibulo la Septuagint limawonjezera mayina ena asanu, pamene limati: “Koma Manase anali ndi ana ndipo wina anali Makiri, amene mdzakazi wake wa ku Siriya anam’berekera. Ndipo Makiri anabereka Galaadi. Koma ana a Efuraimu, m’bale wake wa Manase, anali Sutalaamu ndi Taamu. Sutalaamu anali ndi ana ndipo wina anali Edemu.” Ichi chingakhale chifukwa chake Baibulo la Septuagint limatchula anthu 75 m’malo mwa 70 pa Ge 46:27 ndi pa Eks 1:5, komanso Sitefano anatchula zomwezi pa Mac 7:14.

Mwina mayina a ana ena sanatchulidwe.

Ena amati “mahosi” kapena “akavalo.”

Anali kuzipundula mwa kudula mtsempha wakuseri kwa mwendo wam’mbuyo.

Dzina lakuti “Silo” limatanthauza “Mwini Wake.”

Ena amati “chipupa” kapena “chikupa.”

Dzina lakuti “Abele-miziraimu” limatanthuza kuti, “Kulira Maliro kwa Aiguputo.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena