Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • bi12 Zephaniah 1:1-3:20
  • Zefaniya

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zefaniya
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Zefaniya

Zefaniya

1 M’masiku a Yosiya+ mwana wa Amoni+ mfumu ya Yuda, Yehova analankhula kudzera mwa Zefaniya mwana wa Kusa, mwana wa Gedaliya, mwana wa Amariya, mwana wa Hezekiya. Iye anati:

2 “Ine ndidzafafaniza chilichonse chimene chili panthaka,” watero Yehova.+

3 “Ndidzafafaniza anthu ndi nyama.+ Ndidzafafaniza zolengedwa zouluka m’mlengalenga, nsomba za m’nyanja,+ zokhumudwitsa pamodzi ndi anthu oipa,+ ndipo ndidzawononga anthu onse ndi kuwachotsa panthaka,”+ watero Yehova. 4 “Ndidzatambasula dzanja langa ndi kuwononga Yuda pamodzi ndi anthu onse okhala mu Yerusalemu.+ Ndidzawononga anthu onse otsala amene amapembedza Baala+ ndi kuwachotsa pamalo ano. Ndidzafafanizanso dzina la ansembe a mulungu wachilendo pamodzi ndi ansembe ena.+ 5 Ndidzafafaniza anthu amene akugwadira khamu la zinthu zakuthambo pamadenga* a nyumba zawo,+ ndiponso amene akugwada ndi kulumbira+ kuti adzakhala okhulupirika kwa Yehova+ koma amakhalanso akulumbira m’dzina la Malikamu.+ 6 Ndidzafafaniza amene akusiya kutsatira Yehova,+ amene sanayesetse kuyandikira Yehova ndi amene sanafunsire kwa iye.”+

7 Khalani chete pamaso pa Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa,+ pakuti tsiku la Yehova lili pafupi,+ ndipo Yehova wakonza nsembe+ moti wakonzekeretsa*+ anthu amene wawaitana.

8 “Ndiyeno pa tsiku limene Yehova adzapereka nsembe, ine ndidzalanga akalonga, ana a mfumu+ ndi onse ovala zovala zachilendo.+ 9 Pa tsiku limenelo, ndidzalanga aliyense amene ali pafupi ndi mpando wachifumu, anthu amene adzaza nyumba za ambuye awo ndi chiwawa ndiponso chinyengo.+ 10 Pa tsiku limenelo,” watero Yehova, “ku Chipata cha Nsomba+ kudzamveka phokoso la kulira ndipo kuchigawo chatsopano cha mzinda+ kudzamveka phokoso la kulira mokweza. Kumapiri+ kudzamveka phokoso la chiwonongeko chachikulu. 11 Lirani mofuula+ anthu inu okhala ku Makitesi, pakuti amalonda onse awonongedwa+ ndipo onse amene amayeza siliva pasikelo aphedwa.

12 “Pa nthawi imeneyo ndidzafufuza ndi nyale mu Yerusalemu mosamala kwambiri,+ ndipo ndidzalanga anthu amene akukhala mosatekeseka ngati vinyo amene nsenga zake zakhazikika pansi.+ M’mitima yawo, anthu amenewa akunena kuti, ‘Yehova sadzachita zabwino kapena kuchita zoipa.’+ 13 Chuma chawo chidzafunkhidwa ndipo nyumba zawo zidzakhala bwinja.+ Iwo adzamanga nyumba, koma sadzakhalamo.+ Iwo adzalima minda ya mpesa koma sadzamwa vinyo wochokera mmenemo.+

14 “Tsiku lalikulu+ la Yehova lili pafupi.+ Lili pafupi ndipo likubwera mofulumira kwambiri.+ Mkokomo wa tsiku la Yehova ukubwera ndi zowawa.+ Pa tsiku limenelo mwamuna wamphamvu adzalira.+ 15 Tsiku limenelo ndi tsiku lamkwiyo, tsiku lansautso ndi zowawa,+ tsiku la mphepo yamkuntho ndi losakaza, tsiku lamdima wochititsa mantha,+ tsiku lamitambo yakuda ndi lamdima wandiweyani. 16 Pa tsiku limenelo, lipenga la nyanga ya nkhosa ndiponso chizindikiro chochenjeza zidzalira+ pochenjeza mizinda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri, komanso nsanja zazitali kwambiri za m’makona.+ 17 Pamenepo ndidzasautsa mtundu wa anthu moti adzayenda ngati anthu akhungu+ chifukwa chakuti iwo achimwira Yehova.+ Magazi awo adzakhuthulidwa pansi ngati fumbi,+ ndipo matumbo awo adzakhuthulidwa pansi ngati ndowe.+ 18 Siliva kapena golide wawo sadzawapulumutsa pa tsiku la mkwiyo wa Yehova.+ Moto wa mkwiyo wake udzanyeketsa dziko lonse lapansi,+ chifukwa iye adzafafaniza anthu onse okhala padziko lapansi.”+

2 Sonkhanani pamodzi, sonkhanani pamodzi,+ inu anthu a mtundu wopanda manyazi.+ 2 Lamulo lisanayambe kugwira ntchito,+ tsiku lisanadutse ngati mankhusu,* mkwiyo woyaka moto wa Yehova usanakugwereni anthu inu,+ tsiku la mkwiyo wa Yehova lisanakufikireni,+ 3 bwerani kwa Yehova,+ inu nonse ofatsa a padziko lapansi,+ amene mwakhala mukutsatira zigamulo zake. Yesetsani kukhala olungama,+ yesetsani kukhala ofatsa.+ Mwina+ mungadzabisike pa tsiku la mkwiyo wa Yehova.+ 4 Gaza adzakhala mzinda wosiyidwa,+ ndipo Asikeloni adzakhala bwinja.+ Kunena za Asidodi,+ anthu ake adzawathamangitsa dzuwa lili paliwombo,+ ndipo Ekironi adzazulidwa.+

5 “Tsoka kwa anthu okhala m’chigawo cha m’mphepete mwa nyanja, mtundu wa Akereti.+ Yehova wakudzudzulani anthu inu. Iwe Kanani, dziko la Afilisiti, nawenso ndidzakuwononga, kotero kuti m’dziko lako simudzatsala munthu aliyense.+ 6 Chigawo cha m’mphepete mwa nyanja chidzakhala malo odyetserako ziweto,+ malo okhala ndi zitsime za abusa ndiponso malo a makola amiyala a nkhosa. 7 Chigawo chimenecho chidzakhala cha otsala a m’nyumba ya Yuda+ ndipo adzapezamo msipu. Madzulo iwo adzagona momasuka m’nyumba za mu Asikeloni. Zidzatero chifukwa chakuti Yehova Mulungu wawo adzawakumbukira+ ndipo adzasonkhanitsa ndi kubwezeretsa anthu awo omwe anagwidwa n’kutengedwa kupita ku ukapolo.”+

8 “Ndamva chitonzo cha Mowabu+ ndi mawu onyoza a ana a Amoni+ amene anali kunena kwa anthu anga. Iwo anali kuopseza anthu anga modzitukumula kuti awalanda dziko lawo.” 9 Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli wanena kuti: “Pali ine Mulungu wamoyo,+ Mowabu adzakhala ndendende ngati Sodomu,+ ndipo ana a Amoni+ adzakhala ngati Gomora, malo odzaza zomera zoyabwa ndiponso mchere ndiponso malo abwinja mpaka kalekale.*+ Otsala mwa anthu anga adzafunkha zinthu zawo, ndipo otsala a mtundu wa anthu anga adzawagwira ukapolo.+ 10 Anthu amenewo adzaona zimenezi chifukwa cha kunyada kwawo,+ komanso chifukwa chakuti anali kunyoza ndi kudzikweza pamaso pa anthu a Yehova wa makamu.+ 11 Yehova adzawachititsa mantha,+ pakuti adzawondetsa milungu yonse ya padziko lapansi.+ Pamenepo anthu adzamugwadira,+ aliyense pamalo pake, zilumba zonse za mitundu ya anthu zidzamugwadira.+

12 “Inunso Aitiyopiya+ mudzaphedwa ndi lupanga langa.+

13 “Iye adzatambasulira dzanja lake kumpoto ndipo adzawononga Asuri.+ Adzachititsa Nineve kukhala bwinja,+ kukhala dziko lopanda madzi ngati chipululu. 14 Magulu a nyama, nyama zakutchire za m’deralo zidzagona momasuka pakati pa mzindawo.+ Nungu ndiponso mbalame ya vuwo+ zidzagona usiku wonse pakati pa zipilala zakugwa za mzindawo.+ Pawindo padzamveka mawu a nyimbo. Pamakomo a nyumba padzakhala zibuma za nyumba zakugwa, pakuti iye adzakanganula matabwa oyalidwa kukhoma.*+ 15 Mzinda uwu unali wosangalala ndipo unkakhala mosaopa chilichonse.+ Mumtima mwake unali kunena kuti, ‘Ndilipo ndekha, ndipo palibe wondiposa.’+ Mzindawu wakhala chinthu chodabwitsa, malo amene nyama zakutchire zimagonamo momasuka. Aliyense wodutsa pafupi ndi mzindawu adzaimba mluzu ndipo adzapukusa mutu.”+

3 Tsoka kwa iye amene akuchita zinthu zopanduka, amene akudziipitsa, mzinda wopondereza anthu ake.+ 2 Mzindawo sunafune kumvera,+ sunalole kulangizidwa,*+ sunakhulupirire Yehova+ ndipo sunayandikire Mulungu wake.+ 3 Akalonga ake anali mikango imene inali kubangula.+ Oweruza ake anali mimbulu yoyenda usiku imene sinatafune mafupa mpaka m’mawa.+ 4 Aneneri ake anali amwano ndi achinyengo.+ Ansembe ake anaipitsa zinthu zopatulika ndipo anaphwanya chilamulo.+ 5 Yehova anali wolungama mkati mwa mzindawo+ ndipo sanali kuchita zosalungama.+ M’mawa uliwonse iye anali kuchita chilungamo chake+ moti sichinali kusowa mpaka m’bandakucha,+ koma wosalungamayo sanali kuchita manyazi.+

6 “Ine ndinafafaniza mitundu ya anthu ndi kusakaza nsanja zawo za m’makona. Ndinawononga misewu yawo moti simunali kuyendanso munthu. Mizinda yawo inakhala mabwinja ndipo simunatsale munthu aliyense.+ 7 Ndiyeno ndinati, ‘Mosakayikira udzandiopa ndipo udzalola kulangizidwa’+ kuti malo ake okhala asawonongedwe,+ pakuti ndidzamuimba mlandu wa zonsezi.+ Koma zinthu zawo zonse zimene anali kuchita zinali zowawonongetsa ndipo anazichitadi mofulumira.+

8 “‘Choncho pitirizani kundiyembekezera,’+ watero Yehova, ‘mpaka tsiku limene ndidzanyamuka kuti ndikaukire ndi kulanda zinthu zofunkhidwa.+ Chigamulo changa ndicho kusonkhanitsa mitundu ya anthu+ ndi kusonkhanitsa pamodzi maufumu kuti ndiwadzudzule mwamphamvu+ ndi kuwatsanulira mkwiyo wanga wonse woyaka moto, pakuti moto wa mkwiyo wanga udzanyeketsa dziko lonse lapansi.+ 9 Pamenepo ndidzapatsa mitundu ya anthu chilankhulo choyera+ kuti onse aziitanira pa dzina la Yehova+ ndi kumutumikira mogwirizana.’*+

10 “Anthu amene akundichonderera, anthu anga obalalitsidwa, adzandibweretsera mphatso kuchokera kuchigawo cha mitsinje ya ku Itiyopiya.+ 11 Pa tsiku limenelo, sudzachita manyazi chifukwa cha zochita zako zimene unandilakwira nazo,+ pakuti ndidzachotsa pamaso pako anthu odzikweza amene amakhala mosangalala+ ndipo sudzakhalanso wodzikweza m’phiri langa lopatulika.+ 12 Mwa iwe ndidzasiyamo anthu ena, odzichepetsa ndi ofatsa,+ ndipo amenewa adzapeza chitetezo m’dzina la Yehova.+ 13 Otsala mwa Isiraeli+ sadzachita zinthu zosalungama+ kapena kunena bodza.+ Sadzakhala ndi lilime lachinyengo+ koma iwo adzadya ndi kugona pansi momasuka+ ndipo sipadzakhala wowaopsa.”+

14 Fuula mosangalala iwe mwana wamkazi wa Ziyoni! Fuula mokondwera+ iwe Isiraeli! Sangalala ndi kukondwera ndi mtima wonse, iwe mwana wamkazi wa Yerusalemu!+ 15 Yehova wachotsa zigamulo zake pa iwe.+ Watembenuza ndi kubweza mdani wako.+ Mfumu ya Isiraeli, Yehova, ali pakati pa anthu ako+ ndipo sudzaopanso kuti tsoka likugwera.+ 16 Tsiku limenelo Yerusalemu adzauzidwa kuti: “Usaope iwe Ziyoni+ ndipo usalefuke.+ 17 Yehova Mulungu wako ali pakati pa anthu ako ndipo adzakupulumutsa chifukwa ndi wamphamvu.+ Iye adzakondwera nawe.+ Adzakhala phee chifukwa chokhutira ndi chikondi chimene akukusonyeza, ndipo adzafuula mosangalala chifukwa chokondwera nawe.

18 “Anthu ogwidwa ndi chisoni+ amene sanapezeke pa zikondwerero zako ndidzawasonkhanitsa pamodzi.+ Iwo sanali ndi iwe chifukwa anali kudziko lachilendo kumene anali kutonzedwa.+ 19 Pa nthawi imeneyo ndidzaukira onse amene akukuzunza+ ndipo ndidzapulumutsa otsimphina.+ Anthu obalalitsidwa ndidzawasonkhanitsa pamodzi+ ndipo ndidzawachititsa kukhala otamandidwa komanso otchuka m’dziko lonse limene anachititsidwa manyazi. 20 Pa nthawi imeneyo ndidzakubwezaninso kunyumba anthu inu. Ndithu, pa nthawi imeneyo ndidzakusonkhanitsani pamodzi. Ndidzakuchititsani kukhala otchuka komanso otamandidwa pakati pa mitundu yosiyanasiyana padziko lapansi. Zimenezi zidzachitika ndikadzabwezeretsa pamaso pako anthu ako amene anagwidwa ndi kutengedwa kupita ku ukapolo,” watero Yehova.+

Kapena kuti “patsindwi.”

Mawu ake enieni, “wayeretsa.”

“Mankhusu” ndi makoko amene amachotsa ku mbewu ngati mpunga popuntha, ndipo amatha kuwauluza ndi mphepo.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Ena amati “chipupa” kapena “chikupa.”

Onani mawu a m’munsi pa Miy 1:2.

Mawu ake enieni, “azimutumikira phewa ndi phewa.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena