Habakuku
1 Uwu ndi uthenga umene ine, mneneri Habakuku, ndinauzidwa m’masomphenya. Ndinati: 2 “Inu Yehova, kodi ndidzalirira thandizo koma inu osandimva kufikira liti?+ Kodi ndidzapempha thandizo kuti mundipulumutse ku chiwawa koma inu osandimva kufikira liti?+ 3 N’chifukwa chiyani mukundichititsa kuona zinthu zopweteka? N’chifukwa chiyani mukupitiriza kuyang’ana khalidwe loipa? N’chifukwa chiyani kufunkha ndi chiwawa zikuchitika pamaso panga? Ndipo n’chifukwa chiyani pali mikangano ndi kumenyana?+
4 “Choncho lamulo latha mphamvu ndipo anthu sakuchitanso chilungamo.+ Chilungamo chapotozedwa chifukwa anthu oipa akupondereza anthu olungama.+
5 “Yang’anani pakati pa mitundu ya anthu ena anthu inu, ndipo muyang’anitsitse, kenako muyang’anane modabwa.+ Dabwani pakuti pali ntchito imene winawake akuichita m’masiku anu imene anthu inu simungakhulupirire ngakhale wina atakufotokozerani.+ 6 Ine ndikuutsa Akasidi,+ mtundu waukali ndi waphuma umene ukupita kumalo otakasuka a padziko lapansi kukatenga malo amene si awo.+ 7 Mtundu umenewu ndi woopsa ndipo anthu amachita nawo mantha. Mtunduwo umapanga malamulo akeake ndipo umadzipezera wokha ulemu.+ 8 Mahatchi* ake ndi aliwiro kuposa akambuku* ndiponso ndi oopsa kuposa mimbulu yoyenda usiku.+ Mahatchi ake ankhondo amachita mgugu ndipo amachokera kutali. Mahatchiwo amauluka ngati chiwombankhanga chimene chikuthamangira chakudya chake.+ 9 Mtunduwo umabwera wonse wathunthu kuti udzachite chiwawa.+ Ukakumana wonse pamodzi umayenda ngati mphepo yamkuntho yochokera kum’mawa,+ ndipo umasonkhanitsa anthu ogwidwa, ochuluka ngati mchenga. 10 Mtunduwu umaseka mafumu monyodola ndipo umaona nduna zapamwamba ngati choseketsa.+ Umasekanso malo alionse okhala ndi mpanda wolimba kwambiri+ ndipo umaunjika dothi kenako n’kulanda malowo. 11 Pa nthawi imeneyo mtunduwo udzayendabe ngati mphepo ndipo udzadutsa m’dzikoli ndi kupalamula.+ Mphamvu zake ndizo mulungu wake.”+
12 Inu Yehova, inutu mwakhalapo kuyambira kalekale.+ Inu Mulungu wanga, Mulungu wanga Woyera, inu simufa.+ Inu Yehova, mwaika Akasidi pamalo oti muwaweruze. Inu Thanthwe,+ mwasankha kuti mutidzudzule.+
13 Inu ndinu woyera kwambiri moti simungaonerere zinthu zoipa ndipo simungathe kuonerera khalidwe loipa.+ N’chifukwa chiyani mumayang’ana anthu amene amachita zachinyengo,+ ndipo n’chifukwa chiyani mukupitiriza kukhala chete pamene munthu woipa akumeza munthu amene ndi wolungama kuposa iyeyo?+ 14 N’chifukwa chiyani mukuchititsa munthu kukhala ngati nsomba zam’nyanja ndiponso ngati zokwawa zam’nyanja zimene zilibe mtsogoleri woziteteza?+ 15 Mdani amagwira zonsezi ndi mbedza+ ndipo amazikokolola ndi khoka lake n’kuzisonkhanitsa muukonde wake wophera nsomba.+ N’chifukwa chake iye amasangalala ndipo amakhala wokondwa.+ 16 N’chifukwa chake mdaniyo amaperekera nsembe khoka lake ndipo amafukizira nsembe yautsi ukonde wake wophera nsomba. Iye amatero chifukwa chakuti amapeza chakudya chonona ndiponso chakudya chopatsa thanzi chifukwa cha khoka ndi ukonde wakewo.+ 17 Kodi ndicho chifukwa chake adzapitirizabe kudzaza ndi kukhuthula nsomba za m’khoka lake? Kodi iye adzapitirizabe kupha mitundu ya anthu mopanda chifundo?+
2 Ine ndidzaimabe+ pamalo a mlonda ndiponso pakhoma lachitetezo. Ndidzakhala tcheru+ kuti ndione uthenga umene iye adzalankhula kudzera mwa ine+ ndi zimene ndidzayankha pamene iye akundidzudzula.+
2 Pamenepo Yehova anandiyankha kuti: “Lemba masomphenyawa moonekera bwino pamiyala yosema,+ kuti wowerenga mokweza awerenge mosadodoma.+ 3 Uchite zimenezi pakuti masomphenyawa akuyembekezera nthawi yake yoikidwiratu+ ndipo akuthamangira kumapeto kwake. Zimene zili m’masomphenyazi si zonama. Ngakhale masomphenyawa atazengereza, uziwayembekezerabe* chifukwa adzakwaniritsidwa ndithu.+ Iwo sadzachedwa.
4 “Taona! Iye wadzitukumula+ ndipo si wowongoka mtima. Koma wolungama adzakhalabe ndi moyo mwa chikhulupiriro chake.+ 5 Ndiye pakuti vinyo ndi wachinyengo,+ mwamuna wamphamvu amadzimva,+ koma sadzakwaniritsa cholinga chake.+ Iye wakulitsa chilakolako chake ngati Manda* ndipo sangakhutire ngati imfa.+ Iye akupitiriza kudzisonkhanitsira mitundu yonse ya anthu ndi anthu onse pamodzi.+ 6 Kodi anthu onsewa sadzamunenera mwambi,+ chining’a ndi mawu okuluwika? Wina adzanena kuti,
“‘Kodi iye adzapitiriza kuchulukitsa zinthu zimene si zake+ kwa nthawi yaitali bwanji?+ Tsoka kwa iye pakuti akungochulukitsa ngongole yake. 7 Kodi amene uli nawo ngongole sadzanyamuka ndi kubwera modzidzimutsa kuti uwabwezere ngongole yawo? Kodi okugwedeza mwachiwawa sadzanyamuka ndi kubwera kudzafunkha zinthu zako zonse?+ 8 Chifukwa chakuti iwe unafunkha mitundu yambiri ya anthu, anthu onse otsala a m’mitunduyo adzafunkha zinthu zako.+ Iwo adzateronso chifukwa unakhetsa magazi a mtundu wa anthu komanso unachitira chiwawa dziko lapansi, tauni ndi anthu onse okhala mmenemo.+
9 “‘Tsoka kwa munthu amene akupezera nyumba yake phindu mwachinyengo.+ Iye akuchita zimenezi kuti amange chisa chake pamalo okwezeka ndi cholinga choti tsoka lisamupeze.+ 10 Wapereka malangizo ochititsa manyazi kunyumba yako, kumene ndi kuphetsa mitundu yambiri ya anthu+ ndipo wachimwa.+ 11 Mwala wa pakhoma* udzalira mwachisoni ndipo kuchokera padenga* mtanda wa denga udzayankha.+
12 “‘Tsoka kwa munthu amene akumanga mzinda mwa kukhetsa magazi, amenenso wakhazikitsa tauni mwa kuchita zosalungama.+ 13 Taona! Kodi si Yehova wa makamu amene adzachititsa anthu kugwira ntchito yakalavulagaga kuti moto uwononge ntchitoyo? Kodi sindiye amene wachititsa kuti mitundu ya anthu idzitopetse pachabe?+ 14 Pakuti dziko lapansi lidzadzaza ndi anthu odziwa ulemerero wa Yehova ngati mmene madzi amadzazira nyanja.+
15 “‘Tsoka kwa amene akupatsa anzake chakumwa kuti amwe, koma atachisakaniza ndi mkwiyo ndiponso kupsa mtima kuti anzakewo aledzere+ ndipo iye aone maliseche awo.+ 16 Iwenso adzakumwetsa+ ndipo udzaonekera kuti ndiwe wosadulidwa.+ Udzakhuta zinthu zamanyazi m’malo mwa ulemerero.+ Chikho chochokera m’dzanja lamanja la Yehova chidzakupeza+ ndipo ulemerero wako udzasanduka manyazi. 17 Zidzakhala choncho chifukwa chiwawa chimene unachitira Lebanoni+ chidzafika pa iwe ndiponso chifukwa cha kuwononga kwako kwakukulu kumene unaopseza nako zilombo zakutchire, kukhetsa magazi a anthu ndi chiwawa chimene unachitira dziko lapansi,+ tauni ndi onse okhala mmenemo.+ 18 Kodi chifaniziro chosema, chifaniziro chopangidwa ndi chitsulo chosungunula ndiponso mphunzitsi wonama,+ zili ndi phindu lanji+ kuti wozipanga azizikhulupirira+ ndipo azipanga milungu yopanda pake yosalankhula?+
19 “‘Tsoka kwa munthu amene akuuza chidutswa cha mtengo kuti: “Dzuka!” Amene amauzanso mwala wosalankhula kuti: “Dzuka! Tipatse malangizo”!+ Taona! Fanolo ndi lokutidwa ndi golide ndi siliva+ ndipo mulibe mpweya* mkati mwake.+ 20 Koma Yehova ali m’kachisi wake wopatulika.+ Inu anthu onse a padziko lapansi, khalani chete pamaso pake!’”+
3 Ili ndi pemphero la mneneri Habakuku limene anaimba ngati nyimbo yoimba polira:* 2 “Inu Yehova, ndamva uthenga wonena za inu.+ Ndachita mantha ndi ntchito zanu, Inu Yehova.+
M’zaka zimenezi sonyezani ntchito zanu! m’zaka zimenezi chititsani ntchito zanu kuti zidziwike. Pa nthawi ya mkwiyo wanu kumbukirani kusonyeza chifundo.+
3 Mulungu anabwera kuchokera ku Temani, Woyerayo anabwera kuchokera kuphiri la Parana.+ [Seʹlah.]+
Ulemerero wake unaphimba kumwamba+ ndipo dziko lonse linamutamanda.+
4 Kuwala kwake kunali ngati kuwala kwa masana.+ Kuwala kwa mitundu iwiri kunali kutuluka m’dzanja lake ndipo m’dzanja lakemo ndi mmene munali kubisala mphamvu zake.+
5 Mliri unali kuyenda patsogolo pake+ ndipo matenda otenthetsa thupi anali kuyenda patsogolo pa mapazi ake.+
6 Iye anaima chilili kuti agwedeze dziko lapansi.+ Anayang’ana mitundu ya anthu ndipo mitunduyo inadumpha.+
Mapiri amuyaya anaphwanyidwa.+ Zitunda zimene zidzakhalapo mpaka kalekale* zinawerama.+ Zimenezi ndi njira zake zakalekale.
7 Ndinaona mahema a Kusani ali ndi nkhawa. Nsalu za mahema a m’dziko la Midiyani+ zinayamba kunjenjemera.+
8 Inu Yehova, kodi mwapsera mtima mitsinje?+ Kodi mkwiyo wanu wayakira nyanja+ pamene inu munakwera pamahatchi anu?+ Magaleta anu anabweretsa chipulumutso.+
9 Munachotsa uta moikamo mwake.+ Zimene mafuko a anthu ananena ndiwo malumbiro awo.+ [Seʹlah.] Munagawa dziko lapansi pogwiritsa ntchito mitsinje.+
10 Mapiri anakuonani ndipo anamva ululu waukulu.+ Mvula yamphamvu yamabingu inadutsa. Madzi akuya anachita mkokomo+ ndipo anathuvuka m’malere.
11 Kumwamba,+ dzuwa ndi mwezi zinaima.+ Mivi yanu inapitiriza kuyenda ngati kuwala.+ Kunyezimira kwa mkondo wanu kunakhala ngati kuwala kounikira.+
12 Munadutsa m’dziko lapansi ndi kulidzudzula mwamphamvu. Inu mutakwiya munapuntha mitundu ya anthu ngati mbewu.+
13 Munapita kuti mukapulumutse anthu anu,+ kuti mukapulumutse wodzozedwa wanu. Munaphwanyaphwanya mtsogoleri wa nyumba ya wochimwa.+ Nyumbayo inafafanizidwa mpaka kudenga moti maziko a nyumbayo anaonekera.+ [Seʹlah.]
14 Munabaya*+ mitu ya asilikali ake ndi zida zake zomwe, pamene iwo anali kubwera ngati mphepo yamkuntho kuti adzandimwaze.+ Kukondwera kwawo chifukwa cha tsoka langa kunali ngati kwa anthu amene akonzeka kuti ameze munthu wosautsidwa m’malo obisalamo.+
15 Munadutsa panyanja ndi mahatchi anu, munadutsa pamadzi ambiri.+
16 Nditamva mawu ake, m’mimba mwanga munayamba kubwadamuka ndipo milomo yanga inanjenjemera. Mafupa anga anayamba kuwola+ ndipo ndinanthunthumira chifukwa cha mmene zinthu zinalili. Choncho ndidzayembekezera mofatsa tsiku la nsautso.+ Tsiku limeneli lidzabwera kwa anthu+ ngati mmene munthu amabwerera kwa adani ake kuti awaukire.
17 Ngakhale mkuyu usaphukire maluwa,+ mtengo wa mpesa usabale zipatso, mtengo wa maolivi ulephere kubala zipatso, munda wa m’mphepete mwa phiri usatulutse chakudya,+ nkhosa ndi ng’ombe zithemo m’khola,+
18 Ine ndidzakondwerabe mwa Yehova+ ndipo ndidzasangalala mwa Mulungu wachipulumutso changa.+
19 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, ndiye mphamvu yanga.+ Iye adzachititsa miyendo yanga kukhala ngati ya mbawala,+ moti adzandiyendetsa pamalo anga okwezeka.”+
Kwa wotsogolera nyimbo zoimbidwa ndi zipangizo zanga za zingwe.
Ena amati “mahosi” kapena “akavalo.”
Ena amati “nyalugwe.”
Kapena kuti, “Ngakhale masomphenyawa ataoneka ngati akuchedwa, uziwayembekezerabe.”
Onani Zakumapeto 5.
Ena amati “chipupa” kapena “chikupa.”
Kapena kuti “patsindwi.”
Onani Zakumapeto 4.
Tanthauzo la mawu achiheberi amene tawamasulira kuti “nyimbo yoimba polira” silikudziwika, koma mwina angatanthauze nyimbo yoimba mokhudzika mtima kwambiri. Kaimbidwe kake kangasonyeze kuti moyo wa munthu woimbayo uli pangozi, akufuula kupempha thandizo, kapena akukondwera ndiponso kutamanda winawake.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Ena amati “kugwaza.”