Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g91 9/8 tsamba 30-31
  • Limodzi la Maluso Apadera a Madagascar

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Limodzi la Maluso Apadera a Madagascar
  • Galamukani!—1991
  • Nkhani Yofanana
  • Muzilola Kuti Yehova Aziumba Maganizo ndi Makhalidwe Anu
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2017
  • Musalekerere Mtima wa Mwana Wanu!
    Nsanja ya Olonda—2003
  • Tiziyamikira Kuti Yehova Amatiumba
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2016
Galamukani!—1991
g91 9/8 tsamba 30-31

Limodzi la Maluso Apadera a Madagascar

CHIWONETSERO chokongola cha zotengera zadongo, miphika, ndi mapani zinatikopa pamene tinali kudutsa msika wa Antsirabe pachisumbu chathu cha Madagascar. Ngakhale kuti miphika yonse inali yofiirira, iyo inali ndi madontho aakulu akuda omwe anawonekera ngati kuti anawotchereredwa. Chidwi chinatikakamiza kufunsa mnyamata wachichepere yemwe anali kuigulitsa ngati zomwe tinaganizazo zinali zowona.

“Inde,” iye anatero, “izo zifunikira kuumikidwa m’ng’anjo kuti zikhale zotere. Koma tiribe mauvuni amakono, okongola onga omwe ali m’mizinda. Timagwiritsira ntchito njira zakale zimene makolo athu anatiphunzitsa.”

Ngakhale kuti mnyamatayo anayankha bwino mafunso athu owonjezereka, mawu ake anangodzutsabe chikhumbo chathu chakuwona mmene zoumba zadongo zoterozo zimapangidwira. Choncho tinapita pagalimoto kumalo akutali m’dzikolo komwe anthu am’mudzimo anali akatswiri oumba ndi dongo. Onse anali okoma mtima ndi ochereza. Posangalatsidwa kuti anthu amumzinda angakondweretsedwe ndi ntchito zawo, iwo anali ofunitsitsa kwenikweni kutisonyeza maluso awo.

Choyamba, tinadziŵa kuti dongo limene amagwiritsira ntchito siliri dongo wamba. Iwo anati dongo wamba limasweka pamene latenthedwa. Chotero amagwiritsira ntchito dongo lotchedwa tanimanga, (m’lingaliro lenileni, “dothi lobiriŵira”), lopezeka m’midzi mokha ndiponso m’magombe a mitsinje kapena mifuleni. Mnyamata wina anatiperekeza kugombe la mfuleni nakumba pansi. Pafupifupi masentimita 30 pansi, ndipo panawonekera dongo lachinyontho, lotuwira—tanimanga! Komabe, mosiyana ndi dzina lake, m’malo ena dongo la tanimanga limakhala lakuda kapena ngakhale lachikasu. Komabe, nthaŵi zonse limasiyana ndi dothi lakatondo la mbali yapakati imeneyi ya chisumbuchi.

Mwamuna wina anatiuzanso kuti pofuna kupanga zotengera zochulukirapo kapena miphika, amasakaniza thumba limodzi la tanimanga ndi mbali imodzi mwa zitatu ya thumba la mchenga wofeŵa, womwe umapezekanso m’magombe a mtsinje. Ndiyeno amaikako madzi kuti afeŵetse msanganizowo. Kodi madziwo amakhala ochuluka motani? Kwenikweni sipamakhala miyeso yakutiyakuti. Mwakuzoloŵera, woumbayo amaleka kuwonjezera madzi pamene awona kuti msanganizowo wafika pamlingo wabwino—osati wolimba kwambiri kapena wofeŵa kwambiri.

Ndiyeno, msanganizo umenewu wa dongo, mchenga, ndi madzi umaikidwa pamphasa yadothi lopanda miyala ndi udzu. Ndiyeno woumbayo amalipondaponda kwanthaŵi yaitali. Ichi chimatsimikizira kuti dongolo lasakanizika bwino ndi mchengawo, komwe kumapangitsa zotengera kapena miphika kukhala yolimba. Mawu angapo m’chinenero cha Malagasy amafotokoza mbali yofunika yakuumba imeneyi: hitsahina, disahina, tehafina, volavolaina, totoina. Komabe onse amasonya ku kachitidwe kofananako—kuponda msanganizo wa dongo. Pamene oumba atsimikiza kuti msanganizowo uli bwino, amakhala okonzeka kuyamba kuumba kwenikweniko.

Choyamba iwo amagawa msanganizowo kukhala mibulu ya ukulu wa nkhonya yanu. Amapanga mbulu umodzi wa pansi pa mphika naukanikiza pa chikombole—kaŵirikaŵiri mphika wadothi wakale—kuti apange mpangidwe wake. Atachotsa chikombolecho, amagwiritsira ntchito mbulu wina kupanga milomo, kapena kamwa ya mphikawo. Popanga zimenezi, oumbawo amasamala kuti sakulola msanganizowo kuuma kwambiri, popeza kuti ungasweke mosavuta.

Tsopano miphikayo imasiidwa kuti iume padzuŵa tsiku lonse. Pokhapo mpamene imakhala yokonzeka kaamba ka sitepe lomalizira: kuumika mwakuotcha. Koma ngakhale kuotchaku kumachitidwa sitepe ndi sitepe. Miphika yonse ndi zotengera zimadzazidwa ndi udzu ndi masamba ouma ndipo zimagonekedwa cha m’mbali. Zinthu zootchera zimenezi zimayatsidwa moto kuzilola kupsa kwa mphindi 10 kapena 15. Kutereku kumalimbitsa dongolo.

Pambuyo pa kuotcha koyamba kumeneko, miphikayo imaikidwa pamalo okutidwa ndi udzu ndi masamba ouma. Komabe, panthaŵiyi miphikayo imaikidwa moyang’anizana kukamwa. Oumbawo amaika udzu ndi masamba ouma pamwamba ndi m’mbali mwa miphikayo kufikira itabisika. Ndiyeno amaika zigulumwa za dothi m’mbali mwa malowo kuti motowo usafalikire mbali zina ndikuletsa miphikayo kuti isagubuduke. Zinthu zootcherazo zimayatsidwanso moto kwa nyengo yosachepera pa mphindi 30 kapena kufikira motowo utazima wokha. Miphikayo itazizira, imachotsedwa m’phulusa ndipo ikhoza kugwiritsiridwa ntchito.

Poyang’anitsitsa miphikayo, tsopano tinamvetsetsa madontho akuda omwe anali pamiphikayo. Anali mbali zomwe zinali mwachindunji pamoto. Mbali ina yonse ya mphikayo inali mtundu wanthaŵi zonse wa dongo lootchedwa—wofiirira mwachikasu.

Luso loumba miphika limeneli lapatsiridwa kuchokera ku mbadwo umodzi kumka ku mbadwo wina. Tinakumana ndi munthu amene amagwira ntchito pafakitale yaikulu yopanga nsalu m’tauni koma amapanga ndalama zowonjezereka mwakupanga ndi kugulitsanso zoumba. Iye anaphunzira lusoli kwa atate ake, omwe nawonso, anaphunzira kwa atate awo. Ndipo ndife otsimikiza kuti mwamuna wachichepereyo sadzaphonya mwaŵi wakuphunzitsa ana ake.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena