Pamene Agogo Ake Anamwalira
Nakubala wa ku Virginia Beach, Virginia, U.S.A., analemba kuti: “Mwezi watha atate wanga anamwalira. Iwo ndi mwana wanga wamwamuna wamng’ono kwambiri ankakondana kwambiri, mosasamala kanthu za mtunda womwe unali pakati pawo. Pamene ndinamudziŵitsa kuti agogo ake amwalira, anayamba kulira momvetsa chisoni.
“Ndinafunafuna mofulumira trakiti yakuti Kodi Pali Chiyembekezo Chotani Kaamba ka Okondedwa Akufa? Mwamsanga nditaipeza, pamene nkhope yake inali idakali ndi misozi, ndinayamba kumuŵerengera. Pamene ndinamaliza, iye anatontholako. Ndikuthokozani kaamba ka chidziŵitso chamtengo wake choterocho, chomwe chinali chothandiza kwambiri panthaŵi yowawitsa imeneyi.”
Mukhoza kulandira trakiti yotonthoza imeneyi, limodzi ndi ena, mwakungodzaza ndi kutumiza kapepala kotsatiraka.
Ndingakonde kulandira trakiti uakuti Kodi Pali Chiyembekezo Chotani Kaamba ka Okondedwa Akufa? limodzi ndi matrakiti ena. (Kunja kwa Zambia, lemberani ku nthambi ya Watch Tower yakwanuko kaamba ka chidziŵitso. Onani tsamba 5.)