Kodi Dzina Liri ndi Tanthauzo Lanji?
KODI mukudziŵa chifukwa chimene makolo anu anakupatsirani dzina lanu? Kaŵirikaŵiri m’nthaŵi za Baibulo maina a anthu anasonyeza chikhulupiriro mwa Mulungu ndi malonjezo ake. Mwachitsanzo, dzina lakuti Abrahamu, limene Mulungu anampatsa, limatanthauza “Atate wa Khamu (Namtindi).” Dzina lakuti Isimayeli limatanthauza “Mulungu Amamva (Amamvetsera).” Ndipo dzina lakuti Yesu limatanthauza “Yehova Ndiye Chipulumutso.”
M’maiko a ku Afirika lerolino kupatsa maina kaŵirikaŵiri kumasonyeza zikhulupiriro ndi makhalidwe achipembedzo. Izi ziridi tero pakati pa Mboni za Yehova zambiri za ku Afirika.
Ku Nigeria mkazi wina wachichepere akusimba kuti: “Abambo anga anaphunzira chowonadi cha Baibulo kwa Mboni za Yehova chaka chimodzi ndisanabadwe. M’chaka chimodzimodzicho, bukhu la Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya linatulutsidwa m’Chingelezi. Pambuyo pake, pafupifupi nthaŵi ya kubadwa kwanga, bukhu la Coonadi linatuluka m’chinenero chathu cha Yoruba. Chifukwa cha chimenecho, bambo anga anachilingalira kukhala choyenera kundipatsa dzina lakuti Truth [Chowonadi].”
Mboni ina ya Yehova, mwamuna, akusimba kuti: “Atate anga anakhala Mboni chaka chimodzi ndisanabadwe. Iwo ankagwira ntchito pamalo olamulidwa ndi Akatolika okangalika, ndipo chifukwa cha zikhulupiriro zawo, anataya ntchito yawo. Pamene ndinabadwa, analibe ntchito ndipo anali ndi ndalama zochepa. Koma sanakhwethemulidwe. Iwo anati: ‘Ndikuvutika ndi ulova chifukwa cha kumamatira kwanga ku Ufumu wa Mulungu.’ Chotero ananditcha dzina lakuti Kingdom [Ufumu].”
“Makolo anga ananditcha Ifeanyichukwu, dzina la chinenero cha Igbo,” anatero mwamuna wina wachichepere. “Limenelo ndidzina lovuta kutchula kwa amene salankhula Chiigbo, choncho ndinafuna dzina lomwe linali losavuta. Ndinafuna kutumikira pa Beteli [ofesi yanthambi ya Watch Tower Society], ndipo ndinali ndi bwenzi lomwe dzina lake linali Bethel [Beteli]. Choncho ndinaŵapempha makolo anga ngati ndingatenge ‘Bethel’ kukhala dzina langa. Iwo anavomereza.”
“Makolo anga anali apainiya [aminisitala anthaŵi zonse],” akusimba motero mwamuna wina wa ku Nigeria. “Abambo anga anafuna kutcha mmodzi wa ana awo dzina la ntchito yawo. Ndimo mmene ndinapezera dzinalo Pioneer [Painiya]. Iwo analingalira kuti nanenso ndikakumana ndi madalitso olemera a utumiki wanthaŵi zonse.”
Pamene chiŵalo cha Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova chinali ku Côte d’Ivoire mu December 1978, anakumana ndi mlongo yemwe anali ndi mwana wotchedwa Victorious Faith [Chikhulupiriro Cholakika] chifukwa chakuti anabadwa pamene mayiyo anapezekapo pa Msonkhano wa “Chikhulupiriro Cholakika.”
Truth [Chowonadi], Kingdom [Ufumu], Bethel [Beteli], ndi Pioneer [Painiya], onse amagwira ntchito pa ofesi yanthambi ya Watch Tower Society mu Nigeria. Ndipo omwe akutumikira kumeneko ndi Mboni zokhala ndi maina onga Bible [Baibulo], Wisdom [Nzeru], Christian [Mkristu], Love, [Chikondi], Innocent [Wopanda Liŵongo], Genesis, ndi Blessing [Dalitso]. Aminisitala Achikristu onsewa akugwira ntchito zolimba kusunga mbiri yabwino, kapena dzina ndi Yehova Mulungu, amene anatcha dzina banja lirilonse kumwamba ndi pa dziko lapansi.—Yerekezerani ndi Aefeso 3:14, 15.