Tsamba 2
Mungathe Kulaka Kupsinjika Mtima 3-9
Kodi kupsinjika mtima kumayamba motani? Kodi kuli kotheka kukulaka kotero kuti kusalamulire kapena kuvulaza miyoyo yathu? Kodi ena achita nalo motani vutoli?
Mashantikompaundi—Nthaŵi Zovuta m’Chipwirikiti cha m’Tawuni 10
Anthu mamiliyoni mazanamazana kuzungulira dziko lonse akukhala m’malo ochulukitsitsa anthu ndi nyumba sosaukira kwambiri, chakudya, madzi, ndi mikhalidwe yoipa yotaira chimbudzi ndi zonyansa zina. Kodi pali chiyembekezo chotani kwa anthu oterowo?