Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g92 10/8 tsamba 32
  • Yankho la Pemphero

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Yankho la Pemphero
  • Galamukani!—1992
Galamukani!—1992
g92 10/8 tsamba 32

Yankho la Pemphero

MKAZI wa ku Christchurch, New Zealand, akunena kuti nkhani za mu Galamukani! zakuti ‘Kuchiritsa Mabala a Kuchitira Nkhanza Ana’ zinali yankho la pemphero lake. Iye akufotokoza kuti:

‘Mu August 1991 ambiri a ife tinali ndi chochitika chowopsa cha kuwona bwenzi likumavutika ndi kukumbukira kuipitsidwa. Ndinakhalabe wachisoni kwapafupifupi masiku atatu, koma tinapemphera ndi mtima wonse kwa Yehova kaamba ka magazini yochita ndi nkhani imeneyi. Tinafuna chithandizo. Tinayembekezera kwamilungu isanu yokha. Tikukuyamikani moimira mikhole yambirimbiri kaamba ka nkhani zabwino, zofunika koposa za mu Galamukani! ya October 8, 1991.’

Yapamwambapayi ndiimodzi yokha ya makalata mazana ambiri oyamikira Galamukani! pankhani ya kuchitira nkhanza ana. M’kalata ina yolandiridwa kuchiyambiyambi kwachaka chino, wolembayo ananena kuti anayesa kangapo kuŵerenga nkhanizo chifukwa chakuti sanali wokhoza kuleka kulira. Mkaziyo akuti:

“Ngakhale tsopano, ndimatukutira mkati mwanga pamene ndiyesa kufotokoza kuyamikira kwanga nthawi ndi nyonga zowonongedwera pa kuthandiza awo a ife amene ali ndi malingaliro a kululuzika ndi liwongo pambuyo pa kugwiriridwa chigololo ndi kuvulazidwa mwamaganizo ndi winawake amene anadzinenera kukhala ‘akutikonda’ pamene tinali achichepere kwambiri ndi osatetezereka. Sindinali kudziŵa kuti panali ena ambiri okhala ndi zochitika zonga zanga. Ndidakavutikirabe kulimbana ndi maganizo ovutawo, koma malingaliro a patsamba 10 ndi 11 ali othandiza kwambiri. Ndiri ndi zambirimbiri zoti ndilankhule, koma ndifunikira kokha kunena kuti mapemphero anga akumka kwa Yehova kaamba ka inu kaamba ka kudalira kwanu mwa Yehova kuti akupatseni kulimba mtima kwa kulemba nkhani zofunika zoterozo.”

Winabe anati: “Imeneyi inali imodzi ya nkhani zabwino kopambana zimene zinafalitsidwapo ndi inu pankhani za maunansi a anthu. Yavumbula chizoloŵezi chausatana chimenechi limodzi ndi ochichirikiza, yamveketsera osakhala mikholewo ululu wake wovulazawo; mikhole yake yatonthozedwa ndi kuphunzitsidwa. Khomo loyembekezera chifundo ndi chichirikizo cha anthu a Mulungu latsegulidwa phadagu.”

Mboni za Yehova ndizo gulu la m’mitundu yonse la ophunzira Baibulo oposa mamiliyoni anayi amene ali odzipereka kuthandiza anthu ndi mavuto awo ndi kuwathandiza kuphunzira zowonjezereka ponena za zifuno za Mulungu. Ngati mungakonde kudziŵa zowonjezereka kapena phunziro Labaibulo lapanyumba laulere, chonde lemberani Watch Tower, Box 33459, Lusaka 10101, kapena keyala yoyenerera pa ondandalitsidwa pa tsamba 5.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena