Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g93 8/8 tsamba 8-10
  • Chitsogozo Changwiro cha Makhalidwe Abwino

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chitsogozo Changwiro cha Makhalidwe Abwino
  • Galamukani!—1993
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Baibulo ndi Chisembwere
  • Baibulo ndi Nkhani ya Malonda
  • Kodi Ukatola Chinthu Nchako?
  • Chisonkhezero cha Anthu Onse!
  • Kodi Makhalidwe Akumka Kuti?
    Galamukani!—1993
  • Kutsogoleredwa ndi Nzeru Zapamwamba Kuposa Zachibadwa
    Galamukani!—2007
  • Magwero Apamwamba Kwambiri a Nzeru
    Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu?
  • Tizikhulupirira Zimene Baibulo Limanena pa Nkhani ya Zoyenera Ndi Zosayenera
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2024
Onani Zambiri
Galamukani!—1993
g93 8/8 tsamba 8-10

Chitsogozo Changwiro cha Makhalidwe Abwino

MMALINYERO wa ngalaŵa amafunikira mapu ndi ziwiya zodalirika kuti adziŵe mayendedwe oyenera. Mofananamo, anthu amafunikira chitsogozo chodalirika kuti apange zosankha m’makhalidwe zimene amayang’anizana nazo tsiku lililonse. Chitsogozo cha makhalidwe chimene chili cha kanthaŵi kapena chosinthasintha sichingamthandize, monga momwenso mmene sichingathandizire chitsogozo chimene chimagwira ntchito m’magulu ena kapena zitaganya za anthu. Chitsogozo changwiro cha makhalidwe abwino chiyenera kupyola pa fuko ndi miyambo.

Komatu nzodabwitsa kuti Baibulo—buku lenilenilo limene lakanidwa ndi anthu mamiliyoni ambiri, buku limene anthu ena alitcha la nthano zokondweretsa chabe, buku limene latsutsidwa kwambiri koposa buku lina lililonse m’mbiri—ndilo chitsogozo changwiro cha makhalidwe abwino. Baibulo limanena kuti lili chitsogozo cha makhalidwe abwino a Mlengi kaamba ka munthu, “nyali” imene ingaunikire njira yathu “m’mabande achilungano.”—Salmo 23:3; 119:105.

Kodi pali umboni wochilikizira mawu apadera amenewo? Kodi pali umboni wakuti kukhala ndi moyo mogwirizana ndi miyezo ya Baibulo kumaposa kwambiri kukhala ndi moyo mogwirizana ndi makhalidwe opangidwa ndi anthu?

Baibulo ndi Chisembwere

Lingalirani za nkhani ya chisembwere. Baibulo limaletsa kugonana ndi munthu wina amene simunakwatirane naye, likumati: “Thaŵani chisembwere.” (1 Akorinto 6:18, New International Version; Aefeso 5:5) Limalangiza anthu okwatirana kuti: “Ukwati uchitidwe ulemu ndi onse; ndi pogona pakhale posadetsedwa; pakuti adama ndi achigololo adzawaweruza Mulungu.” (Ahebri 13:4) Baibulo limasonyezanso kuti munthu amene amaswa lamulo limeneli amadziwononga yekha ndipo amawononga zoyenera za ena.—Miyambo 6:28-35; 1 Atesalonika 4:3-6.

Mavuto aakulu a kukhala ndi pakati kwa achichepere, chiwopsezo cha AIDS, matudza a kumpheto, chindoko, ndi nthenda zina zopatsirana mwa kugonana, ndipo kukwera kwa chiŵerengero cha chisudzulo kuli umboni wakuti uphungu umenewu udakali woyenerera moyo m’ma 1990 ano. Munthu amene amamamatira kumakhalidwe a Baibulo amapeŵa kuvutika mtima ndi mavuto ambiri. Chinthu chofunika kwambiri nchakuti, amakhala ndi chikumbumtima chabwino. (1 Petro 3:16) “Ndimadzilemekeza limodzi ndi chikhutiro cha kuchita chimene chili chabwino pamaso pa Mulungu,” akutero Jonathan wa zaka 24. Iyeyu ndimmodzi wa Mboni za Yehova. “Popeza kuti achichepere ambiri akufa ndi AIDS, kudzisungira mwamakhalidwe kungapulumutsedi moyo wanga.”

Mabanja owopa Mulungu apeza kuti kutsatira makhalidwe a Baibulo kwakhala ndi chiyambukiro chabwino paukwati wawo. Mkazi wina wa zaka 23 anati: “Ine ndi mwamuna wanga tinali anamwali pamene tinakwatirana. Ndimaona kuti tinali ndi kanthu kena kapadera koti tigaŵane, kanthu kena kamene ndiachichepere oŵerengeka okha amene angakhale nako ndi mnzawo masiku ano. Ndidziŵa kuti zimenezi zalimbitsa chomangira cha chikondi pakati pathu.”

Baibulo ndi Nkhani ya Malonda

Baibulo lili ndi mpambo wake wa malamulo a makhalidwe pankhani ya kuchita malonda. Pamene kuli kwakuti limavomereza kuti anthu osawona mtima amaonekera kukhala akulemerera, limatifulumizabe kukhala owona mtima. (Salmo 73:1-28) “Miyeso yosiyana [wolongosoka wogulira zinthu, ndi wosalongosoka ndi wosawona mtima wogulitsira zinthu], ndi malichero osiyana, zonse ziŵirizi zinyansa Yehova.” (Miyambo 20:10) Motero Mboni za Yehova zimapeŵa machenjera ameneŵa osawona mtima m’nkhani za malonda.

Zowonadi, Mkristu angakumane ndi zovuta m’kuchita motero. Kungakhale kovuta kwa iye kuchita malonda ndi amalonda osawona mtima. Ena angaganize za kuwona mtima kwakeko kukhala kwachilendo, ndipo mwinamwake kopusa, koma iye amakhalabe ndi chikumbumtima chabwino—kanthu kena kofunika kwambiri kuposa ndalama. Amakhala ndi mtendere wa maganizo ndipo akhoza kupeza tulo tabwino usiku. Samavutitsidwa ndi mantha osatha a kuwopa kugwidwa ndi kulangidwa chifukwa cha kusawona mtima.—Yerekezerani ndi Miyambo 3:21-26.

Ndiponso, Mboni zambiri zapeza kuti munthu akhoza kugwiritsira ntchito makhalidwe a Baibulo nachitanso bwino kumbali ya chuma. Kaŵirikaŵiri munthu wowona mtima amadaliridwa ndi antchito ake, makasitomala, opikulitsa katundu, ndi ogulitsa katundu pangongole. Zimenezi zingachititse phindu lake.

Kodi Ukatola Chinthu Nchako?

Monga momwe taonera poyambirirapo, lingaliro lakuti ukatola chinthu nchako lapangitsa anthu owona mtima kukhala mbala. Komabe, Baibulo linauza anthu a Mulungu a m’nthaŵi zakale kuti: “Pamene muona ng’ombe kapena nkhosa ya munthu mnzanu itasokera, musanyalanyaze koma ibwezereni kwa mwiniwake. Ngati mwiniwakeyo sali mnansi wanu wa pafupi ndipo simukudziŵa kuti iyeyo ndani, pitani ndi chifuyocho kwanu ndi kuchisunga kufikira pamene adzachifunafuna, ndipo mpatseni. Chitani mofananamo ndi bulu wake kapena chovala kapena chinthu chilichonse chimene munthu mnzanu wataya, mutachipeza.”—Deuteronomo 22:1-3, The New English Bible.

Mboni za Yehova zimapitiriza kutsatira lamulo la mkhalidwe limeneli lerolino. Mboni ina ku Brooklyn, New York, inapeza thumba la ndalama zokwanira $25,000 mumsewu. Ndalamazo zinagwa mosaonedwa m’galimoto lochingidwa lokhala ndi alonda pangozi yaing’ono imene inachitika. Ngakhale kuti ndalamazo zinali zitasinthidwa—ndipo motero zosakhoza kudziŵidwa—iye anapereka ndalamazo kupolisi. Anzake akuntchito anamdzudzula chifukwa cha zimene anachita. Modabwitsanso, ngakhale apolisi anamseka chifukwa cha kuwona mtima kwake. Koma mwamuna Wachikristu ameneyu akufotokoza kuti: “Ndimayesa kugwiritsira ntchito ziphunzitso za Baibulo m’moyo wanga wa tsiku ndi tsiku.” Pa Ahebri 13:18, Baibulo limati: “Mutipempherere ife; pakuti takopeka mtima kuti tili nacho chikumbumtima chokoma m’zonse, pofuna kukhala nawo makhalidwe abwino.”

Chisonkhezero cha Anthu Onse!

Baibulo limaperekanso zitsogozo zabwino pankhani zina za makhalidwe. Limalimbikitsa kukoma mtima, kupanda tsankho, kuweruza molungama, chowonadi, ulemu, kudekha, kukhala wathayo, ndi kudera nkhaŵa ena. Uphungu wake pamakhalidwe, wafotokozedwa mwachidule m’Lamulo la Makhalidwe Abwino lakuti: “Zinthu zilizonse mukafuna kuti anthu achitire inu, inunso muwachitire iwo zotero.”—Mateyu 7:12.

Pokhala zogwirizana ndi Magwero ake, zitsogozo za makhalidwe za Baibulo zimapambana m’dziko lililonse kapena chitaganya cha anthu. M’buku lakuti Christianity’s Contributions to Civilization, Charles D. Eldridge akunena kuti: “Mabuku olembedwa m’dziko lina samakhala okondedwa kumaiko ena; iwo amakhala ngati mitengo imene singathe kulimbana ndi zovuta za kuwokedwa panthaka ina . . . Sizili choncho ndi Baibulo: lawokedwa panthaka iliyonse padziko popanda kunyentchera.”

Pamenepo, mwapadera, Baibulo lakhala chisonkhezero cha anthu onse, mosasamala kanthu za chinenero, miyambo, ndi fuko. Wolemba Baibulo wina ananena motere: “Lemba lililonse nlouziridwa ndi Mulungu ndipo lipindulitsa pakuphunzitsa chikhulupiriro ndi kulungamitsa cholakwa, pakukonzanso njira ya moyo wa munthu ndi kumphunzitsa makhalidwe abwino.” (2 Timoteo 3:16, Phillips) Zowonadi, Baibulo nlovuta kulimva nthaŵi zina. M’nthaŵi zakale woŵerenga Baibulo wina wakhama anafunsidwa ngati anadziŵa zimene anali kuŵerenga. Iye anayankha kuti: “Ndingathe bwanji, popanda munthu wonditsogolera ine?”—Machitidwe 8:29-35.

Munthu ameneyo anapatsidwa chithandizo chachindunji kuti amvetsetse Baibulo. Lerolino, chithandizo chachindunji chotero nchopezeka mwa ntchito yophunzitsa Baibulo ya Mboni za Yehova. Izo zathandiza kale anthu mamiliyoni ambiri m’maiko oposa 200 kudziŵa Mawu a Mulungu. Ndipo zikupempha kuti inunso mudziŵe bwino Buku Lopatulika limenelo mwa kufika pa Nyumba Yaufumu yokhala chifupi nanu.

Mokondweretsa, kwanenedwa kuti makhalidwe abwino “akhoza kuphunziridwa mwa chitsanzo chabwino, . . . kapena ‘kungokhala ndi’ anthu a makhalidwe abwino.” Chimenechi chili chifukwa chinanso chokhalira ozoloŵerana ndi awo amene amafika pa Nyumba Yaufumu ya kwanuko. Kumeneku sikunena kuti Mboni za Yehova zimaposa anthu ena mwachibadwa, koma kupambana kwawo m’makhalidwe ndiko umboni wa mphamvu ya Mawu a Mulungu.—2 Akorinto 4:7.

Makhalidwe a dziko adzapitirizabe kunyonyosoka. Baibulo limaneneratu kuti: “Anthu oipa ndi onyenga, adzaipa chiipire.” (2 Timoteo 3:13) Komabe, inu simuyenera kutengedwera limodzi ndi funde la chiwonongeko limeneli. Mulungu wapereka mpimo wodalirika, chitsogozo chosalakwa. Kodi mudzachitsatira?

[Mawu Otsindika patsamba 8]

Baibulo limanena kuti lili chitsogozo cha makhalidwe abwino a Mlengi kaamba ka munthu, “nyali” imene ingaunikire njira yathu

[Mawu Otsindika patsamba 9]

Zitsogozo za makhalidwe za Baibulo zimapambana m’dziko lililonse kapena chitaganya cha anthu

[Mawu Otsindika patsamba 10]

“Zinthu zilizonse mukafuna kuti anthu achitire inu, inunso muwachitire iwo zotero.”—Mateyu 7:12

[Chithunzi patsamba 9]

Okwatirana owopa Mulungu apeza kuti kutsatira makhalidwe a Baibulo kuli ndi chiyambukiro chabwino paukwati wawo

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena