Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g94 4/8 tsamba 6-10
  • Mfungulo za Kupulumuka

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mfungulo za Kupulumuka
  • Galamukani!—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kupeŵa ndi Kadyedwe
  • Kudziŵa Mwamsanga
  • Mankhwala
  • Kupsinjika Mtima ndi Kansa ya Maŵere
  • Zimene Akazi Ayenera Kudziŵa Ponena za Kansa ya Maŵere
    Galamukani!—1994
  • Zimene Mungachite Ngati Mwapezeka ndi Khansa ya M’mawere
    Galamukani!—2011
  • Zimene Makolo Angachite Ngati Mwana Wawo Ali ndi Khansa
    Galamukani!—2011
  • Malangizo Ofunika a Kuyamwitsa Bere
    Galamukani!—1994
Galamukani!—1994
g94 4/8 tsamba 6-10

Mfungulo za Kupulumuka

NGATI munamva mbiri ya nkhani yakuti wakupha akuyendayenda m’mudzi mwanu, kodi mukanapanga zoyesayesa kuti mudzitetezere inuyo ndi banja lanu? Mosakayikira mungatseke ndi kukhoma zitseko zanu kuti kusakhale kokhweka kuloŵamo. Mudzakhalanso tcheru ndi nkhope zachilendo zokayikiritsa ndipo mudzadziŵitsa apolisi mwamsanga.

Kodi akazi ayenera kuchita zochepa ndi nthenda yakupha, kansa ya maŵere? Kodi ndi njira zotani zimene angatenge kuti adzitetezere okha ndi kuwonjezera mwaŵi wawo wa kupulumuka?

Kupeŵa ndi Kadyedwe

Kwayerekezeredwa kuti kansa 1 mwa 3 mu United States imachititsidwa ndi zakudya. Kadyedwe kabwino kamene kadzathandiza kuchititsa thupi lanu kukhala ndi dongosolo labwino lolimbana ndi matenda kangakhale chinjirizo lanu lofunika koposa. Pamene kuli kwakuti palibe chakudya chodziŵika chimene chingachiritse kansa, kudya zakudya zina ndi kuchepetsa zina kungakhale njira zotetezera. “Kutsatira kadyedwe kabwino kungachepetse upandu wanu wa kukhala ndi kansa ya maŵere ndi maperesenti makumi asanu,” anatero Dr. Leonard Cohen wa bungwe la American Health Foundation mu Valhalla, New York.

Zakudya zokhala ndi fiber yambiri, monga ngati buledi wopangidwa ndi tirigu wosapuntha ndi dzinthu, zingathandize kuchepetsa unyinji wa prolactin ndi estrogen, mwinamwake mwa kuphatikana ndi mahomoni ameneŵa ndi kuwatulutsa m’thupi. Malinga ndi kunena kwa magazini a Nutrition and Cancer, “ziyambukiro zimenezi zingapondereze kupita patsogolo kwa kuyambika kwa kansa.”

Kuchepetsa mafuta a nyama kungachepetse upanduwo. Magazini a Prevention akupereka lingaliro lakuti kuleka kumwa mkaka wokhala ndi mafuta kumamwa mkaka wopanda mafuta, kuchepetsa kudya bata, kumadya nyama yopanda mafuta, ndi kuchotsa chikopa cha nkhuku kungachepetse kwambiri kudya mafuta a nyama.

Ndiwo zamasamba zokhala ndi vitamini A, monga ngati carrot, maungu, mbatata, ndi masamba obiriŵira modera, monga ngati spinach ndi chigwada, ndi mpiru, zingathandize. Kukulingaliridwa kuti vitamini A imaletsa kupangika kwa kusintha kochititsa kansa. Ndipo ndiwo zonga ngati broccoli, nkhwani, cauliflower, kabichi, ndi anyezi wosakhwima zimakhala ndi makemikolo amene amatulutsa maenzyme otetezera.

M’buku lakuti Breast Cancer—What Every Woman Should Know, Dr. Paul Rodriguez akunena kuti dongosolo lolimbana ndi matenda, limene limadziŵa ndi kuwononga maselo oipa, lingalimbitsidwe ndi kadyedwe. Iye akupereka lingaliro la kumadya chakudya chokhala ndi iron, monga ngati nyama yopanda mafuta, ndiwo zamasamba obiriŵira, nsomba zachikamba, ndi zipatso ndi ndiwo zamasamba zokhala ndi vitamini C. Zipatso ndi ndiwo zamasamba zokhala ndi vitamini C zimachepetsa upandu wa kansa ya maŵere, ikusimba motero Journal of the National Cancer Institute. Soybeans ndi zinthu zopangidwa ndi soy zosasasa zimakhala ndi genistein, yodziŵika kuti imapondereza kukula kwa chotupa m’kuyesa kwa mu laboratory, koma kugwira ntchito kwake pa anthu sikunatsimikiziridwe.

Kudziŵa Mwamsanga

“Kupeza mwamsanga kansa ya maŵere kudakali njira yofunika kwambiri yosinthira nthenda ya kansa ya maŵere,” chikutero chofalitsidwa cha Radiologic Clinics of North America. Pa nkhaniyi njira zitatu ndizo kupenda nokha nthaŵi zonse maŵere, kupimidwa chaka ndi chaka ndi dokotala, ndi X-ray ya maŵere yotchedwa mammography.

Kudzipenda maŵere kuyenera kuchitidwa mosalekeza mwezi uliwonse, popeza kuti mkazi ayenera kukhala maso kuyang’ana chilichonse chachilendo m’kaonekedwe kapena kamvekedwe ka maŵere ake, monga ngati kulimba kapena chotupa. Mosasamala kanthu kuti kaya wapeza kanthu kakang’ono bwanji, afunikira kupita kwa dokotala wake mwamsanga. Ngati chotupa chipimidwa mwamsanga, mkaziyo adzakhala ndi ulamuliro wokulira pa mtsogolo mwake. Lipoti lochokera ku Sweden linasonyeza kuti ngati kansa ya maŵere yosasintha malo inali ya ukulu woposa pang’ono pa mamilimita 15 kapena kucheperapo ndipo inachotsedwa mwa opaleshoni, chiyembekezo cha moyo wa zaka 12 chinali chothekera ndi 94 peresenti.

Dr. Patricia Kelly akunena kuti: “Ngati simunakhale ndi zizindikiro zobwerezanso za kansa m’zaka 12 1/2, ndiye kuti mwina sidzabweranso. . . . Ndipo akazi angaphunzitsidwe kupeza kansa ya maŵere ya ukulu wochepera pa sentimita imodzi mwa kungogwiritsira ntchito zala zawo.”

Kukuvomerezedwa kuti kupimidwa kuchitidwe mokhazikika ndi katswiri wa nthendayi kapena dokotala wamba chaka chilichonse, makamaka pambuyo pakuti mkazi wafika pa msinkhu wa zaka 40. Ngati mupeza chotupa, kungakhale bwino kumva lingaliro la katswiri wodziŵa za maŵere kapena dokotala wochita opaleshoni.

Bungwe la National Cancer Institute la ku United States likunena kuti chida chabwino cholimbana ndi kansa ya maŵere ndicho mammogram yosalekeza. Mtundu umenewu wa X-ray ungapeze chotupa zaka ziŵiri chisanayambe kugwirika. Njirayo imavomerezedwa kwa akazi a zaka zoposa 40. Komabe, Dr. Daniel Kopans akutidziŵitsa kuti: “Njirayo sili yangwiro konse.” Singapeze makansa onse a maŵere.

Dr. Wende Logan-Young wa pa kiliniki ya nthenda ya maŵere ku New York State anauza Galamukani! kuti ngati mkazi kapena dokotala wake apeza chachilendo koma mammogram sisonyeza kanthu, chikhoterero chingakhale cha kunyalanyaza zopezedwa ndi manjazo ndi kukhulupirira X-ray. Iye akuti chimenechi ndi “cholakwa chachikulu kopambana chimene timaona masiku ano.” Akulangiza akazi kuti sayenera kudalira kotheratu mphamvu ya mammography ya kuzindikira kansa ndipo ayeneranso kudalira mwamphamvu pa kupima maŵere.

Ngakhale kuti mammography ingapeze zotupa, singapime ngati chili cha benign (chopanda kansa) kapena cha malignant (cha kansa). Zimenezi zingachitidwe kokha ndi biopsy (opaleshoni yotenga minyewa ndi maselo ozungulira ndi kuwapima). Talingalirani nkhani ya Irene, amene anapita kukachita mammogram. Kudalira pa zotulukapo za X-ray, dokotala wake anapima chotupa chake kukhala nthenda ya maŵere yopanda kansa nati: “Ndili wotsimikizira kwenikweni kuti ulibe kansa.” Nesi amene anachita mammogram anada nkhaŵa, koma Irene anati: “Ndinaganiza kuti ngati dokotalayo anali wotsimikiza, mwinamwake ndimangochita mantha kwambiri.” Posakhalitsa chotupacho chinakula, chotero Irene anapita kwa dokotala wina. Anachita biopsy ndipo inasonyeza kuti anali ndi kansa yotupa ya m’minyewa yolumikiza, kansa yofalikira mofulumira. Kuti mudziŵe ngati chotupa chili chopanda kansa (monga momwe 8 mwa 10 zimakhalira) kapena cha kansa, minyewa ndi maselo ozungulira chotupacho ziyenera kuchotsedwa ndi kupimidwa. Ngati chotupacho chikuoneka kapena kumveka chokayikitsa kapena chikukula, biopsy iyenera kuchitidwa.

Mankhwala

Pakali pano, opaleshoni, radiation, ndi mankhwala ndizo njira zofala zochiritsira kansa ya maŵere. Chidziŵitso chonena za mtundu wa chotupacho, ukulu wake, kufalikira kwake, kaya chafika ku lymph nodes, ndi kaimidwe kanu pa nkhani ya kukhala kumwezi chingakuthandizeni inu ndi dokotala wanu kusankha mtundu wa mankhwala.

Opaleshoni. Kwa zaka makumi ambiri opaleshoni yochotsa bere, kuchotsa bere pamodzi ndi minofu ya pansi pake ndi malymph node, yagwiritsiridwa ntchito mofala. Koma m’zaka zaposachedwapa mankhwala osachotsa bere amene amaphatikizapo kuchotsa chotupa chokha ndi malymph node, kuphatikizapo radiation, agwiritsiridwa ntchito ndipo akhala ndi mlingo wa kupulumuka wolingana ndi wa mankhwala ochotsa bere lonse. Zimenezi zapatsa akazi ena mtendere wamaganizo wochuluka pamene alingalira zochotsa chotupa chaching’ono, zimene sizimasintha kaonekedwe kawo. Koma British Journal of Surgery ikunena kuti akazi achichepere, amene ali ndi kansa m’malo osiyanasiyana m’bere limodzimodzilo kapena amene ali ndi chotupa chaukulu woposa masentimita atatu, ali ndi upandu waukulu wakudwalanso nthendayo ngati agwiritsira ntchito mankhwala osachotsa bere.

Mfundo yofunika m’kupulumuka popanda kudwalanso yaonedwa ndi Cleveland Clinic Journal of Medicine: “Kuthira mwazi kuli ndi chiyambukiro choipa pa ukulu wa kupulumuka ndi kudwalanso . . . pambuyo pa opaleshoni yochotsa bere lokha.” Lipotilo linanena kuti mlingo wa kupulumuka wa zaka zisanu unali 53 peresenti kwa kagulu kamodzi kamene kanalandira mwazi, kuyerekezera ndi 93 peresenti ya kagulu komwe sikanalandire mwazi.

Chithandizo china cha kupulumuka chalembedwa mu The Lancet, mmene Dr. R. A. Badwe ananena kuti: “Kupenda nthaŵi yochita opaleshoni mogwirizana ndi nthaŵi ya kukhala kumwezi kuli ndi chiyambukiro chachikulu pa chotulukapo cha nthaŵi yaitali kwa odwala kansa ya bere omwe sanaleke kukhala kumwezi.” Lipotilo linasonyeza kuti akazi amene anachotsedwa chotupa mkati mwa kupangidwa kwa estrogen zinthu sizinawayendere bwino poyerekezera ndi awo amene anachitidwa opaleshoni panthaŵi ina ya kukhala kumwezi—54 peresenti anapulumuka kwa zaka khumi kuyerekezera ndi 84 peresenti ya gulu lomalizirali. Nyengo yoyenera kuchita opaleshoni akazi odwala kansa ya maŵere omwe sanaleke kukhala kumwezi inanenedwa kukhala masiku 12 pambuyo pa kukhala kumwezi komalizira.

Kuchiritsa kwa Radiation. Kuchiritsa kwa radiation kumapha maselo a kansa. M’mankhwala osachotsa bere, mbewu zazing’ono za kansa zingalephereke kuchotsedwa ndi dokotala wachita pa opaleshoni pamene akuyesayesa kusunga bere. Kuchiritsa kwa radiation kungachotse maselo otsalirawo. Koma radiation imabweretsa upandu woyambitsa kansa ya maŵere yachiŵiri m’bere la mbali ina. Dr. Benedick Fraass akuvomereza kuchepetsa kuvumbula bere la mbali inalo ku radiation. Iye akunena kuti: “Mwakuchita maluso okhweka ochepa kungakhale kotheka kuchepetsa mokulira unyinji wolandiridwa ndi bere la mbali inalo panthaŵi yochita radiation ku bere loyambalo.” Iye akupereka lingaliro lakuti chishango cha mtovu chochindikala ndi masentimita 2.5 chiikidwe pa bere la mbali inalo.

Kuchiritsa kwa Mankhwala. Mosasamala kanthu za zoyesayesa za kuthetsa kansa ya bere ndi opaleshoni, 25 kufika ku 30 peresenti ya akazi opimidwa chatsopano kukhala ndi kansa ya maŵere amakhala ndi kansa yosintha malo yobisika yosasonyeza zizindikiro poyamba. Chemotherapy ndi mankhwala amene amagwiritsira ntchito makemikolo kuyesa kupha maselo amenewo amene amaloŵa m’mbali zina za thupi.

Chemotherapy ili ndi polekezera m’chiyambukiro chake chifukwa chakuti zotupa za kansa zimapangidwa ndi maselo a mitundu yosiyanasiyana amene lililonse la iwo limakhala ndi chiyambukiro chakechake ku mankhwala. Maselo amene amapulumuka mankhwalawo angapange zotupa zatsopano zosamva mankhwala. Koma kope la January 1992 la The Lancet linapereka umboni wakuti chemotherapy inawonjezera ndi 5 mpaka 10 peresenti mwaŵi wa mkazi wa kupulumuka kwa zaka khumi zina, kudalira pa msinkhu wake.

Ziyambukiro zovulaza za chemotherapy zingaphatikizepo nseru, kusanza, kuyoyoka tsitsi, kukha mwazi, kuwonongeka kwa mtima, kupondereza dongosolo lolimbana ndi matenda, kusabala, ndi leukemia. John Cairns, ananena motere pamene analemba mu Scientific American: “Ameneŵa angaoneke ngati maupandu aang’ono kwa wodwala amene ali ndi kansa yofalikira yokula mofulumira, koma ayenera kulingaliridwa mwamphamvu ndi mkazi amene ali ndi chotupa chaching’ono cha [sentimita imodzi] chomwe mwachionekere chili kansa ya m’bere mokha. Kuthekera kwake kwa kufa ndi kansa yake mkati mwa zaka zisanu kuli chabe pafupifupi 10 peresenti ngakhale ngati salandira mankhwala owonjezereka pambuyo pa opaleshoni.”

Mankhwala a Mahomoni. Mankhwala oletsa estrogen amathetsa ziyambukiro zosonkhezera kukula za estrogen. Zimenezi zimachitika mwakuchepetsa unyinji wa estrogen mwa akazi amene sanaleke kukhala kumwezi kaya mwakuchita opaleshoni yochotsa mazira kapena ndi mankhwala. The Lancet inasimba mlingo wa kupulumuka kwa zaka khumi mwa akazi 8 mpaka 12 alionse pa okwanira 100 amene anachiritsidwa ndi mitundu yonse iŵiriyo.

Chisamaliro chotsatirapo kwa mkazi aliyense wodwala kansa ya bere chili choyesayesa cha moyo wonse. Kuyang’anira kosamalitsa kuyenera kuchitidwa, popeza kuti ngati dongosolo lochiritsa limodzi lilephereka, mitundu ina ya mankhwala ingapereke chithandizo.

Mtundu wina wa mankhwala a kansa umene umachita zinthu mosiyana umakhudza kagulu ka zizindikiro kotchedwa cachexia. Magazini a Cancer Research akulongosola kuti imfa ziŵiri mwa zitatu za kansa zonse zimachititsidwa ndi cachexia, liwu logwiritsiridwa ntchito kufotokoza kutha mphamvu kwa minofu ndi minyewa ina. Dr. Joseph Gold, wa ku Syracuse Cancer Research Institute mu United States, anauza Galamukani! kuti: “Tikuganiza kuti chotupa sichingadzifalitsire chokha m’thupi kusiyapo kokha ngati njira za biochemical za cachexia zili zotseguka.” Kupenda kwina kwa madokotala, kogwiritsira ntchito mankhwala opanda paizoni a hydrazine sulfate, kunasonyeza kuti zina za njira zimenezi zingatsekedwe. Kukhazikika kunafikiridwa mwa 50 peresenti ya odwala kansa ya maŵere oloŵetsedwamo.

Njira zoloŵa mmalo zotchedwa mankhwala othandizira zafunidwa ndi akazi ena kuti zipereke chithandizo cha kansa ya maŵere chosakhala opaleshoni kapena mankhwala opanda paizoni. Mankhwalawo amasiyanasiyana, ena amagwiritsira ntchito kadyedwe ndi zomera, monga ngati mankhwala opangidwa ndi Hoxsey. Koma zopenda zofalitsidwa zotheketsa munthu kupenda mphamvu ya mankhwala ameneŵa nzochepa.

Pamene kuli kwakuti nkhaniyi yalinganizidwa kupereka njira zopulumukira, si cholinga cha Galamukani! kuvomereza mankhwala alionse. Tikulimbikitsa onse kuyang’ana mwanzeru pa njira zosiyana zimenezi pochiritsa nthendayi.—Miyambo 14:15.

Kupsinjika Mtima ndi Kansa ya Maŵere

M’magazini a Acta neurologica, Dr. H. Baltrusch akulongosola kuti kupsinjika mtima kwakukulu kapena kokhalitsa kungachepetse mphamvu ya thupi yoletsa kutupa m’dongosolo lolimbana ndi matenda. Akazi amene ali otopa, opsinjika mtima, kapena osoŵa chichirikizo cha maganizo angakhale ndi dongosolo lolimbana ndi matenda lokhala paupandu ndi ukulu wa 50 peresenti.

Chifukwa chake, Dr. Basil Stoll, polemba mu Mind and Cancer Prognosis, anagogomezera kuti: “Kuyesayesa kulikonse kuyenera kuchitidwa kuchepetsa ululu wosapeŵeka wa kuthupi ndi maganizo umene odwala kansa amakhala nawo mkati ndi pambuyo pa mankhwala awo a nthendayo.”

Kodi mungayerekezere dziko lopanda kansa ya maŵere, kwenikweni, lopanda matenda alionse? Limeneli ndi lonjezo lopangidwa ndi Mulungu wa chitonthozo chonse, Yehova. Lemba la Yesaya 33:24 limalankhula za nthaŵi imene palibe munthu wokhala pa dziko lapansi adzanena konse kuti akudwala. Chiyembekezo chimenecho chidzakwaniritsidwa posachedwapa pamene Ufumu wa Mulungu m’manja mwa Mwana wake, Kristu Yesu, ubweretsa ulamuliro wake wonse ku dziko lapansi, kuchotsa zochititsa zonse za matenda, chisoni, ndi imfa! Kodi bwanji osaŵerenga za chiyembekezo chabwino koposa chimenechi pa Chivumbulutso 21:3 mpaka 5? Limbani mtima kuyang’anizana ndi mtsogolo ndi chichirikizo chimene chimapereka chitonthozo chenicheni.

[Mawu Otsindika patsamba 7]

Pamene kuli kwakuti palibe chakudya chodziŵika chimene chingachiritse kansa, kudya zakudya zina ndi kuchepetsa zina kungakhale njira zotetezera. ‘Kutsatira kadyedwe kabwino kumachepetsa upandu wanu wa kansa ndi maperesenti makumi asanu,’ anatero Dr. Leonard Cohen

[Mawu Otsindika patsamba 8]

“Kupeza mwamsanga kansa ya maŵere kudakali sitepe lofunika kwambiri m’kusintha njira ya kansa ya maŵere,” chikutero chofalitsidwa cha “Radiologic Clinics of North America.” Pankhaniyi njira zitatu zazikulu ndizo: kudzipima maŵere mokhazikika, kupimidwa kwa pachaka ndi dokotala, ndi “mammography”

[Bokosi patsamba 9]

Kudzipenda—Kufufuza kwa Mwezi ndi Mwezi

KUDZIPENDA maŵere kuyenera kuchitidwa patapita masiku anayi mpaka asanu ndi aŵiri pambuyo pa kukhala kumwezi. Akazi amene analeka kukhala kumwezi ayeneranso kufufuza mwezi uliwonse pa tsiku limodzimodzilo.

Zizindikiro Zofunika Kuona Mwezi Uliwonse pa Tsiku Limodzimodzilo

• Chotupa cha ukulu uliwonse (chaching’ono kapena chachikulu) kapena kulimba kwa bere.

• Kukwinyika, kufota, kapena kusintha mtundu kwa khungu la bere.

• Kukhwinyata kapena kupindika kwa nkhumbu.

• Tizilonda kapena kufundula kwa nkhumbu kapena kutuluka madzi.

• Kanjinji m’khwapa.

• Kusintha kwa mizera ya ku bere.

• Kusintha kwa mpangidwe kapena ukulu wa bere.

Kudzipenda

Mutaimirira, kwezani mkono wakumanzere. Mwakugwiritsira ntchito dzanja lakumanja ndi kuyambira kunja kwa bere, sindikizani mbali yophwatalala ya zala mozungulira, kuzungulira bere kumka cha ku nkhumbu. Perekaninso chisamaliro ku malo a pakati pa m’khwapa ndi bere.

Mutagona chagada, ikani mtsamiro pansi pa pheŵa la kumanzere, ndi kuika mkono wanu wakumanja pamwamba kapena kumbuyo kwa mutu. Gwiritsirani ntchito kachitidwe kozungulira komwe katchulidwa pamwambapo. Sinthani kuti muchite kulamanja.

Psinyani pang’ono nkhumbu kuona ngati mutuluka madzi. Bwerezani zimenezo ku bere lakumanja.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena