Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g94 4/8 tsamba 32
  • Anazizwa ndi Unyinji wa Kusindikizidwa kwa Galamukani!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Anazizwa ndi Unyinji wa Kusindikizidwa kwa Galamukani!
  • Galamukani!—1994
Galamukani!—1994
g94 4/8 tsamba 32

Anazizwa ndi Unyinji wa Kusindikizidwa kwa Galamukani!

MUŴERENGI WA GALAMUKANI! KU MINNESOTA, U.S.A., amagwira ntchito pa koleji pamene katswiri wa zamoyo za m’nyanja Sam LaBudde anaikidwa pa ndandanda kuti akakambe nkhani yakuti “Kodi ma Dolphin Anapita Kuti?” Atakumbukira kuti iyeyo anagwidwa mawu m’nkhani ya mu Awake! yakuti “Kodi Kusodza ndi Makoka Kudzachotsedwa?” (May 22, 1992), iye anapita ndi magazini ku nkhaniyo.

“Pamagazinipo ndinalembapo mawu kwa a LaBudde. Ndinanena kuti ndinaganiza kuti akasangalala kudziŵa kuti nkhani yabwino imeneyi inali kukafalitsidwa padziko lonse m’zinenero zambiri ndi kuti magaziniwo anali kusindikizidwa oposa 13,000,000. Ndiyeno ndinalembapo dzina langa ndi kusiya Awake! ili yotseguka pa sitandi yokambira nkhani ndi kubwerera kumpando wanga.

“Posapita nthaŵi ndinaona mwamuna akupita ku sitandi yokambira nkhaniyo, ananyamula magaziniyo, nayamba kuŵerenga. Pambuyo pa mphindi zoŵerengeka, anakweza maso nafunsa mofuula ngati munthu amene anasiya magaziniyo analipo. Pamene ndinatukula dzanja langa ndikuti, ‘Ndine,’ anabwera kudzakhala kumbali kwanga. Anandithokoza kaamba ka magaziniyo nati amayamikira pamene munthu ampatsa mawu amene amafotokoza ntchito kapena zipambano za m’ntchito yake. Komabe, analingalira kuti ndinaphonya ponena kuti anasindikizidwa 13,000,000. Analingalira kuti ndiyenera kuti ndinatanthauza 13,000. Ndinamsonyeza kuchiyambi kwa magaziniyo kuti inali 13,000,000. Iye anazizwa. Anachitanso chidwi kwambiri ndi chiŵerengero cha zinenero zimene magaziniyo inafalitsidwamo [tsopano zinenero 74]. Analingalira kuti magaziniyo inafalitsidwa mu United States mokha, koma ndinamfotokozera mmene imafalitsidwira padziko lonse.”

Ngati mungakonde kuti kope la Galamukani! litumizidwe kunyumba kwanu, chonde lemberani ku Watch Tower, Box 33459, Lusaka 10101, kapena ku keyala yoyenera patsamba 5.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena