Amampatsa Chidziŵitso
Muŵerengi wina wamkazi ku Ohio, U.S.A., analemba kuti: “Ndingofuna kukudziŵitsani za mmene ndimayamikirira magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Alidi ngale.” Iye anafotokoza mmene kuwaŵerenga kumampatsira chidziŵitso.
“Ndinalephera sukulu yasekondale zaka 13 zapitazo,” iye analemba motero. “Posachedwapa, boma linafuna kuti ndilembe mayeso ofanana ndi a sukulu ya sekondale, odziŵika bwino lomwe monga mayeso a GED (General Educational Development). Kuti ndikonzekere mayeso amenewa, ndinafunikira kumapita ku kalasi. Kaŵirikaŵiri, ngati munthu akuchita bwino m’makalasi ameneŵa, m’miyezi isanu ndi umodzi chabe, akhoza kulemba mayeso a GED. Komabe, ine ndinali wokonzekera kuwalemba m’milungu inayi yokha, ndipo ndinapambana kwambiri.
“Chifukwa ninji? Pafupifupi chinthu chilichonse pamayesopo—sayansi, social studies, ndi zina zotero—zinali zitalongosoledwapo kale mwa njira ina yake m’makope akumbuyo a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Mwa kungoŵerenga magaziniwo, maluso anga a kuŵerenga, kulemba mawu, ndi zizindikiro polemba anakhala akuthwa. Kwenikweni, sindinaphunzire ndi komwe alionse a maphunziro ameneŵa. Makalasi amene ndinkapitako anangondithandiza kukumbukira luso langa la masamu.”
Ngati mungafune kukhala ndi kope la Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! kapena ngati mufuna kukhala ndi phunziro la Baibulo lapanyumba laulere, chonde lemberani ku Watch Tower, Box 33459, Lusaka 10101, kapena ku keyala yoyenera yondandalikidwa patsamba 2.