“Lingaliro Langa la Ntchito ya Dokotala Lasintha”
AKANE, mtsikana wa zaka zinayi wa ku Osaka, Japan, anali ndi mavuto a mtima ocholoŵana—kutsekeka kwa valuvu ya mtima yotchedwa tricuspid ndi kusagwira bwino ntchito kwa mbali ya mtima yotchedwa atrial septal—zimene zinafuna kuti achitidwe opaleshoni yaikulu ya mtima. Makolo ake anachonderera madokotala kuchita opaleshoniyo popanda mwazi.a
Opaleshoni yotsegula mtima yosagwiritsira ntchito mwazi njovuta kuchita pa ana chifukwa cha mlingo wawo wochepa wa mwazi. M’chochitika cha Akane, madokotala anavomereza kuchita opaleshoni popanda mwazi. Opaleshoni ya Akane inachitika bwino lomwe, ikumasonyeza maluso awo opambana m’zamankhwala. Iye anachira mofulumira ndipo tsopano akusangalala ndi thanzi labwino.
Amake a Akane analemba kalata kwa madokotala amene anali ndi mbali mu opaleshoni imeneyo, natsekeramo chithunzithunzi chaposachedwa cha Akane. Dokotala wochititsa dzanzi analemba kalata yoyankha amake Akane. Mbali yake ya kalatayo ikuti:
“Kuchira kozizwitsa kwa Akane kumatisangalatsa kwambiri. Zinali zovuta kwambiri kwa ine kugwira misozi yanga pamene ndinaona chithunzithunzi chokongola chimene munatsekera m’kalata yanu. Chimene chinandivutitsa maganizo kwambiri sindicho kuvuta kwa opaleshoniyo koma kusiyana kwa zikhulupiriro zanu ndi zanga. Tsopano, chifukwa cha chokumana nacho chimenechi, lingaliro langa la ntchito ya dokotala lasintha. Madokotala ayenera kugwiritsira ntchito luntha lawo lamphamvu la chidziŵitso cha mankhwala kuti apulumutse moyo, koma ayeneranso kusunga ulemu wa wodwalayo ndi kulemekeza zifuno zake.”
[Mawu a M’munsi]
a Mogwirizana ndi Machitidwe 15:29, Mboni za Yehova zimasala mwazi, kuphatikizapo kuthiridwa mwazi. Komabe, izo zimavomereza njira zochiritsira zopanda mwazi.