Achichepere Akufunsa Kuti . . .
Kuba—Kulekeranji?
“Ndili ndi zaka 16 ndipo ndili ndi vuto lalikulu kwambiri. Posachedwapa, ndakhala ndikuba kwambiri. Ndinangopita kusitolo lina ndi kuba mapeya asanu ndi aŵiri a ndolo. Ndikuwopa kuuza aliyense za vuto langa. Ndithandizeni chonde!”
ANALEMBA motero mtsikana wina wovutika maganizo m’danga la kupempha thandizo la m’magazini. Mlembi wina anasimba kuti: “Katundu wogulitsa kwa anthu wa ndalama pafupifupi madola mamiliyoni zikwi khumi . . . amabedwa, kufunkhidwa, kulandidwa, kapena kubedwa mwanjira ina m’sitolo chaka chilichonse [mu United States]. Pafupifupi theka la ogwidwa chifukwa cha kuba ali achinyamata.”
Malinga ndi kufunsa kwina kwaposachedwapa, mwana wa sukulu ya sekondale (high school) mmodzi mwa atatu alionse anavomera kuti anabapo m’sitolo. Ndipo malinga ndi kufunsa kwina, kochitidwa ndi ofufuza otchedwa Jane Norman ndi Myron Harris, “pafupifupi [achichepere] onse akuvomereza kuti panthaŵi ina anatengapo kanthu kena popanda kulipira.”
Chifukwa Chake Amaba
Mbala ndi munthu yemwe mwadala amatenga kanthu ka wina popanda chilolezo. Nthaŵi zina kuba kungaoneke kukhala koyenera malinga ndi kusoŵa kwa munthu. “Ndinali mumkhalidwe wovuta kwambiri,” akukumbukira motero wachichepere wina mmphaŵi. “Ndinali kupita kuseri kwa [lesitilanti yophika zakudya zamwamsanga] ndi kutsegula chitseko mwa kuchiponda ndi kutengamo nkhuku. Koma ndi zokhazo basi. Ndinangozichita chifukwa chakuti ndinali ndi njala.”
Mwambi wa m’Baibulo umati: “Anthu sanyoza mbala ikaba, kuti ikhutitse mtima wake pomva njala.” Ngakhale zili choncho, kuba nkoipa. Chifukwa chake vesi lotsatira la Baibulo limasonyeza kuti ngakhale mbala yanjala inafunikira ‘kubwezera’ mwa kulangidwa kwakukulu.—Miyambo 6:30, 31.
Komabe, nzodabwitsa kuti ndi mbala zachinyamata zochepa chabe zimene zimaba chifukwa cha kusoŵa kwenikweni. Chitsanzo chabwino ndi Mary Jane wachichepere amene anavomereza kuti: “Inde, ndinaba m’sitolo ndipo zinali zachilendo kwenikweni, chifukwa chakuti sindidziŵa chimene ndinachitira zimenezo. Makolo anga amandipatsa ndalama zogulira chilichonse. Sindinasoŵe kalikonse.”a Momwemonso magazini akuti Seventeen anasimba kuti: “Pakufufuza kumene kunachitidwa ndi National Crime Prevention Council, chifukwa chofala chimene amaliwongowo anapereka chinali chakuti anafuna kanthu kena kaulere.” Achichepere ena analungamitsa ngakhale kadzanja kawo mwa kunenetsa kuti sitolozo ‘zinalipiritsa ndalama zambiri’!
Kwa achichepere ambiri, kuba kwangokhala njira yochepetsera kunyong’onyeka. “Kanali kanthu kena chabe kokachita nditachoka kusukulu,” anafotokoza motero Jeremy yemwe anali mbala. Ndiponso zikuchita monga ngati kuti kuba kumakhala mtundu wina wa maseŵero obweretsa nthumanzi; ena amachita ngati amakonda kugunda kwa mtima kumene kumachitika poika bulauzi yakuba m’chola kapena poika compact disc m’chola cha kumsana.
Kodi Kumabisa Kupsinjika Mtima?
Zoona, pali njira zachisungiko kwambiri zolimbanirana ndi kusungulumwa kuposa kudziika pangozi ya kuponyedwa m’ndende. Pamenepo, kodi kungakhale kwakuti pali zinthu zina kumbuyo kwa nthumanziyo m’malo mwa kungofuna kukondwera pang’ono? Akatswiri ambiri amakhulupirira kuti zilipo. Ladies’ Home Journal inanena kuti achichepere ena “amaona kukhala kovuta kulimbana ndi zitsenderezo za kukula. Ndewu ndi makolo awo, kutha kwa ubwenzi, kulephera mayeso, zingawachititse kumva kuti sakulamulira moyo wawo; kuswa malamulo kumawapatsanso mphamvu.”
Inde, kusimbwa kwa mbalako kumabisa kupweteka ndi kuŵaŵa kwenikweni kwa mtima. Monga momwe Baibulo limanenera, “ngakhale m’kuseka mtima uŵaŵa.” (Miyambo 14:13) Umboni umasonyeza kuti kuba m’sitolo kobwerezabwereza kungakhale chizindikiro cha tondovi. Mbala zina zachichepere zapezeka ndi mbiri yakuti zinachitidwapo nkhanza paubwana. Mosasamala kanthu za choŵaŵitsa mtimacho, nthumanzi ya kuba ingaoneke monga ngati imachithetsa—kwakanthaŵi chabe.b Mwachitsanzo, tatengani mnyamata wina Wachimereka amene anasangalala ndi kuba galimoto ndi kuziyendetsa mothamanga kwambiri. “Kumasangalatsa,” iye akutero. “Umamva ngati kuti uli ndi mantha, ngati kuti waledzera.”
Mabwenzi ndi Kukakamiza Kwawo
Baibulo limati: “Mayanjano oipa aipsa makhalidwe okoma.” (1 Akorinto 15:33) Choonadi chimenechi ochuluka amachidziŵa. Mlembi Denise V. Lang anati: “Sizimachitikachitika kuti wachichepere angoloŵa m’mavuto mwa iye yekha.” Nthaŵi zambiri, mabwenzi amalimbikitsana kuba kuti aone kuti wolimba mtima ndani. Nzachisoni kunena kuti achichepere ambiri amagonja pokakamizidwa.
“Ndinayamba kuyanjana ndi kagulu ka atsikana pasukulu ya sekondale ya achichepere,” akutero Kathy wachichepere. Kodi mtengo wolipirira kuloŵa m’kagulu kawo kapaderako unali wotani? Kuba juzi yokwera mtengo. “Ndinafuna kukhalabe m’kaguluko, chotero ndinaloŵa m’sitolo ndi kudzitengera juzi yanga,” akuulula motero.
Kukhala ndi Lingaliro la Mulungu
Chiyembekezo cha kukhala ndi zinthu zimene simungapeze, cha kusangalala ndi maseŵero odzetsa nthumanzi, kapena cha kuyanjidwa ndi anzanu chingachititse kuba kuoneka ngati kokopa. Komabe, limodzi la Malamulo Khumi m’Baibulo nlakuti: “Usabe.” (Eksodo 20:15) Mtumwi Paulo analemba kuti ‘ambala sadzaloŵa ufumu wa Mulungu.’ (1 Akorinto 6:10) Lingaliro la Mulungu liyenera kukhala lofunika kwambiri kwa achichepere omwe analeredwa kukhala Akristu. Kungakhale chinyengo chotani nanga kupereka chithunzi cha chilungamo ndi kumaba mwamseri! Mtumwi Paulo ananena motere: “Ndiwe tsono wakuphunzitsa wina, kodi ulibe kudziphunzitsa mwini? Iwe wakulalikira kuti munthu asabe, kodi ulikuba mwini wekha?”—Aroma 2:21.
Kugwidwa kochititsa manyazi kumene kungachitike kuli chifukwa chokwanira chopeŵera chizoloŵezi cha kubacho. Atagwidwa, wakuba wina wachichepere anati: “Ndinakhumba kufa.” Kudziŵa kuti Yehova ‘amada achifwamba’ ndiko chifukwa champhamvu koposa chopeŵera kugonja pa chikhumbo—kapena chikakamizo—chakuti mube. (Yesaya 61:8) Ngakhale ngati wina angabise umbala wake kwa akulu a m’sitolo, apolisi, ndi makolo, iye sakhoza kuubisa kwa Yehova. Mpaka adzadziŵika tsiku lina.—Yesaya 29:15.
Kumbukiraninso kuti munthu amapimbidzala ndi uchimo. (Ahebri 3:13) Kuba tinthu tating’ono kumakula kukhala kuba zazikulu ndi kuchita machitachita aukandifere. Mwachitsanzo, Roger wachichepere anayamba moyo wake waupandu mwa kuba ndalama m’chikwama cha amake. M’kupita kwa nthaŵi anayamba kugwetsera akazi achikulire pansi ndi kuba zikwama zawo!
Kulimbana ndi Kukopeka Mtima
Zoona, ngati wina wayamba kuba mwa mseri, kuleka kungakhale kovuta. “Kunali ngati kumwerekera,” anavomereza motero wachichepere wina. Kodi chingathandize wachichepere kusintha njira zake nchiyani?
Ululani tchimo lanu kwa Mulungu. Iye “adzakhululukira koposa” aja amene amalapa pa zolakwa zawo ndi kumuululira machimo poyera.—Yesaya 55:7.
Pezani chithandizo. Oŵerenga magazini ano ambiri amadziŵa bwino mipingo Yachikristu ya Mboni za Yehova imene ili kumadera awo. Amenewo angapite kwa oyang’anira Achikristu akumaloko napempha chithandizo chauzimu ndi kuwongoleredwa. (Yakobo 5:14, 15) Makolo amene ali ndi miyezo yabwino ya makhalidwe angakhalenso magwero a chithandizo ndi chichirikizo. Ngati kupwetekedwa mtima, kuŵaŵidwa mtima, kapena kusungulumwa kuli chochititsa kupulupudzako, kukambitsirana nkhaniyo ndi womvetsera wachifundo kungakhale kothandiza kwambiri.—Miyambo 12:25.
Bwezani. Pansi pa Chilamulo cha Mose, mbala zinafunikira kulipirira katundu wobedwa ndi chiwongola dzanja. (Levitiko 6:4, 5) Kuchita mofananamo sikumangothandiza kumasula chikumbumtima cha munthu komanso kumamthandiza kuzindikira mavuto omwe kuba kumadzetsa pa ena. Baibulo limalonjeza kuti munthu “akabweza icho anachilanda mwachifwamba, nakayenda m’malemba a moyo . . . , adzakhala ndi moyo ndithu, sadzafa.”—Ezekieli 33:15.
Letsani malingaliro akusirira ndi umbombo. Lomaliza pa Malamulo Khumi nlakuti, “Usasirire . . . kanthu kalikonse ka mnzako.” (Eksodo 20:17) Ngati pali kanthu kena kamene mukukafunadi koma simukhoza kukagula, mwinamwake mungapeze njira yopezera ndalama yokagulira. Mtumwi Paulo analangiza kuti: “Wakubayo asabenso; koma makamaka agwiritse ntchito, nagwire ntchito yokoma ndi manja ake.”—Aefeso 4:28.
Samalani mayanjano anu. “Ngati muli ndi bwenzi kapena kagulu ka mabwenzi kamene kamachita cholakwa kapena upandu,” akukumbutsa motero mlembiyo Denise Lang, “inunso mudzayesedwa waliwongo chifukwa chabe cha kukhalapo kwanu pamodzi nawo.” Khalani wokhoza kukana ngati mabwenzi akukuuzani kuchita chinthu chosaloleka.—Miyambo 1:10-19.
Lingalirani za mmene kuba kumavulazira ena. Mbala imangoganiza za iyo yokha. Koma Yesu akutilangiza kuti: “Zinthu zilizonse mukafuna kuti anthu achitire inu, inunso muwachitire iwo zotero.” (Mateyu 7:12) Pamene munthu aphunzira kusamala za anthu ena, iye samakonda kwambiri kuchita kanthu kena kamene kangavulaze ena.
Lingalirani za zotulukapo kwa inu. (Agalatiya 6:7) M’malo moganiza mmene kungakhalire kwabwino kukhala ndi kachiŵiya kapena kachipangizo kokongolako kamene simutha kugula, lingalirani za manyazi amene kugwidwa ndi kulangidwa kungabweretse; lingalirani za chitonzo chimene mungadzetse pa makolo anu ndi Mulungu mwiniyo! Kunena zoona mudzafika ponena kuti kuba si lingaliro labwino nkomwe.
Ngati mungakhale ndi mafunso alionse okhudza Baibulo pambuyo poŵerenga magazini ano, chonde khalani aufulu kufikira Mboni za Yehova pa Nyumba Yaufumu yakwanuko, kapena kulembera ofalitsa magazini ano. (Onani patsamba 5.)
[Mawu a M’munsi]
a Maina ena asinthidwa.
b Sitikukambitsirana za kleptomania—nthenda ya maganizo yosonyezedwa ndi chikhumbo champhamvu cha kuba. Madokotala amanena kuti kleptomania si yofala, ikumapezeka kwa akuba m’sitolo odziŵika ochepera 5 peresenti. Kaŵirikaŵiri nthendayo imachira ndi mankhwala.
[Chithunzi patsamba 31]
Akuba m’sitolo kaŵirikaŵiri amayang’anizana ndi manyazi akugwidwa