Tsamba 2
Kodi Maiko Olemera Adzadyerera Osauka Nthaŵi Zonse? 3-11
Ngalaŵa, malole, ndi sitima zapamtunda zodzala zinyalala zakupha zikuyenda uku ndi uku papulaneti lino kufunafuna malo otayirako zinyalalazo. Kumene amawapeza ndi kumaiko omwe ali kale osakazidwa ndi umphaŵi, njala, ndi matenda. Koma kodi zotulukapo zake zidzakhala zotani potsirizira pake pa pulaneti lathuli, Dziko Lapansi?
Kodi Kukhala Bwenzi la Mulungu Kudzandithandiza? 12
Achichepere ambiri apeza kuti ubwenzi ndi Mulungu umawathandizadi m’nthaŵi zovuta kwambiri.
Kumene Ziombankhanga Zimaulukira Kukadya Nsomba 15
Chozizwitsa chachichibadwa chimachititsa mtsinje kuyenda ndiponso nsomba kupezeka kokha pamalo aang’ono aŵa.
[Mawu a Chithunzi patsamba 2]
Alaska Division of Tourism