Kodi Zipembedzo za Dziko Zili Pafupi Kutha?
YOLEMBEDWA NDI MTOLANKHANI WA GALAMUKANI! KU SWEDEN
KODI mutu umenewu ukukuchititsani kuganiza kuti: ‘Kodi zimenezo zingachitike bwanji? Kodi zipembedzo za dzikoli sizili zamphamvu ndi zosonkhezera kwambiri padziko lonse lapansi lerolino?’
Inde, ngakhale kuti zapyola m’mavuto ochuluka, izo zikuonekadi zotero. M’zaka za zana la 20 lino, chipembedzo chakayikidwa ndi kuvumbulidwa kuposa ndi kale lonse m’mbiri ya munthu. Openda zakuthambo ayang’ana thambo ndi matelesikopo awo aakulu, ndipo opita kumlengalenga ayendayenda mumlengalenga; ndipo malinga ndi kunena kwa wopita kumlengalenga wa ku Soviet Union, iwo “sanaone Mulungu kapena angelo.” Akatswiri a physics agaŵa zinthu kukhala tinthu tochepetsetsa popanda kupeza mphamvu yaumulungu yoziyambitsa. Akatswiri a zamoyo ndi a paleontology akuti akonzanso tsatanetsatane wamtali wa moyo wa m’chisinthiko, kuyambira pa amoeba kufikira kwa munthu, popanda kupeza umboni ngakhale umodzi m’tsatanetsatane wamtali ameneyo wakuti kuli mlengi.
Komabe, nzeru ya dziko ndi kukonda chuma kwalephera kufafaniza mzimu wa chipembedzo papulanetili, ndipo maulamuliro andale ndi mafilosofi okana Mulungu sanakhoze kuchita zimenezo. Kwa zaka zoposa 70, Chikomyunizimu chokana Mulungu chotsendereza chinati chipembedzo ndi mwambo ndipo ndi “namgoneka wa anthu,” chinalanda udindo atsogoleri achipembedzo ndi kuletsa zochita zawo, kuwononga kapena kufunkha matchalitchi ndi akachisi, ndi kusokoneza maganizo olambira ndi kuwapha. Komabe, machitidwe amenewo sanathetse mzimu wa chipembedzo. Maboma amenewo atangogwa, chipembedzo chinabukanso ndi mphamvu yooneka ngati yatsopano. M’maiko omwe kale anali achikomyunizimu, anthu akusonkhananso muunyinji wawo ku akachisi awo akale, kugwada polambira modzipereka monga makolo awo akale.
Mzimu wa chipembedzo udakali wamphamvu kumadera ena a dziko. Chaka chilichonse mzinda wa Mecca, ku Saudi Arabia, umalandira alendo achisilamu mamiliyoni ambiri kuchokera padziko lonse lapansi. St. Peter’s Square ku Vatican nthaŵi zambiri imadzala ndi makamu ochulukitsa a okhulupirira achikatolika ofuna kuona papa ndiponso ofuna kulandira dalitso lake. Ahindu odzipereka mamiliyoni ambiri amapitabe kumalo opatulika mazana ambiri kumagombe a mitsinje “yoyera” mu India. Ayuda opembedza amapita ku khoma lotchedwa Wailing Wall ku Jerusalem kukapemphera ndi kusiya m’ming’alu ya khomalo mapemphero awo olembedwa.
Inde, zikuoneka kukhala zosatheka kufafaniza chipembedzo pakati pa anthu. “Munthu mwachibadwa ndi cholengedwa chopembedza,” inatero nduna yachiairishi Edmund Burke. Malinga ndi ziŵerengero, 5 mwa anthu 6 alionse padziko lapansi mwanjira ina ali ndi chipembedzo chawo. Malinga ndi ziŵerengero zaposachedwa, pali anthu ngati 4,700,000,000 otsata zipembedzo zodziŵika padziko lonse, pamene kuli kwakuti pali anthu osapembedza ndi okana Mulungu oposa pangono 1,000,000,000.a
Polingalira zimenezi, kodi nkwanzeru kukhulupirira kuti zipembedzo za dzikoli zili pafupi kutha? Ndipo ngati zilidi tero, kodi zidzatha liti ndipo motani? Kodi padzakhala chipembedzo chilichonse chotsala? Tiyeni tipende mafunso ameneŵa m’nkhani ziŵiri zotsatira.
[Mawu a M’munsi]
a “Osapembedza” amaphatikizapo: “Anthu omwe amati alibe chipembedzo, osakhulupirira, omwe amati Mulungu ngwosadziŵika, okana zikhulupiriro za chipembedzo, anthu a dziko okana zipembedzo zonse.”
[Chithunzi patsamba 3]
St. Peter’s Square, Vatican City