Chiyembekezo Chomwe Chipembedzo Choona Chimapereka
MWACHIBADWA timakonda kukamba zinthu zimene zimatikhudza kapena kutisangalatsa. Ichi ndicho chifukwa chimodzi chimene chimapangitsa Mboni za Yehova kukonda kuuza ena uthenga wodabwitsa wa m’Baibulo. Uthenga umenewo umene umanena za Ufumu wa Mulungu, uli ndi mayankho a mafunso a zinthu zimene zimakhudzadi anthu masiku ano, monga ngati tsogolo la anthu, chitetezo, thanzi, ndi chimwemwe.—Luka 4:43.
Koma choyamba, kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?
Chiyembekezo Chosangalatsa
Ufumu wa Mulungu ndi boma lolamulidwa ndi Mwana wake, “Kalonga Wamtendere.” Baibulo ponena za Iye limati: “Kwa ife mwana wakhanda wabadwa, kwa ife mwana wamwamuna wapatsidwa; ndipo ulamuliro udzakhala pa phewa lake, ndipo adzamutcha dzina lake . . . Kalonga wamtendere. Za kuenjezera ulamuliro wake, ndi za mtendere sizidzatha.”—Yesaya 9:6, 7.
Tikayang’ana m’tsogolo, inde, m’nthaŵi yathu yomwe ino ndi olamulira omwewa, ulosi wina wa m’Baibulo unati: “Ndipo masiku a mafumu aja Mulungu wa Kumwamba adzaika ufumu woti sudzawonongeka ku nthaŵi zonse . . . udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse. Nudzakhala chikhalire.—Daniel 2:44.
Ufumu wa Mulungu umenewu, wolamulidwa ndi Kristu, Kalonga Wamtendere, udzakwaniritsa pemphero lomwe Yesu anaphunzitsa omutsatira, lakuti: “Atate wathu wa Kumwamba . . . , Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga Kumwamba chomwecho pansi pano.” (Mateyu 6:9, 10) Kodi Ufumu wa Mulungu ukadzabwera udzachitanji padzikoli. Lingalirani zimene Yehova Mulungu mwiniyo analonjeza. Zina mwa izo zithunzi zake zasonyezedwa pa masambawa.
Uthenga Wochokera kwa Mulungu
Malonjezo odabwitsa a m’Mawu a Mulungu sayenera kubisidwa, ndipo zimenezi zitibwezeranso ku mfundo yakukambirana za chipembedzo. Yesu ananeneratu kuti mapeto a dongosolo lino la zinthu asanafike, omutsatira adzagwira ntchito yolalikira Ufumu wa Mulungu: “Ndipo uthenga uwu wabwino wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro.”—Mateyu 24:14; 28:19, 20; Machitidwe 1:8.
Ndi uthenga umenewu wonena za Ufumu wa Mulungu umene Mboni za Yehova zimalengeza padziko lonse. Nsanja ya Olonda, inzake ya magazini inoyi, imafalitsidwa m’zinenero 130, ndipo pachikuto cha magazini iliyonse mwa magazini 22 miliyoni amene amasindikizidwa pamalembedwa mawu akuti “Yolengeza Ufumu wa Yehova.”
Monga munthu wanzeru, mungafune kuyamba mwakhutira ndi zimene mwamva ndiye pambuyo pake n’kusankha zochita zokhudza moyo wanu. (Miyambo 18:13) Choncho ife tikukupemphani kuti muphunzire zambiri zokhudza Ufumu wa Mulungu waulemerero ndi zimene ungatanthauze kwa inu. Chifukwa cha chimenecho, musadzipatule nokha kukana kukambirana za m’Baibulo. Palibe makambitsirano ena amene angakhale omveka bwino, okondweretsa, ndi ofunika kuposa ameneŵa.—Yohane 17:3.
[Bokosi/Zithunzi pamasamba 8, 9]
Malonjezo a Paradaiso pa Dziko Lapansi
Padzakhala mtendere weniweni padziko lonse. “Masiku ake wolungama adzakhazikika; ndi mtendere wochuluka, kufikira sipadzakhala mwezi.”—Salmo 72:7, 8.
Ngakhale akufa adzautsidwa. “kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama.”—Machitidwe 24:15.
Anthu adzakhala ndi thanzi lenileni kosatha. “[Mulungu] adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa.”—Chivumbulutso 21:3, 4.
Anthu adzamanga nyumba zawo ndi kukhalamo. “Iwo adzamanga nyumba ndi kukhalamo; ndipo iwo adzawoka minda yamphesa, ndi kudya zipatso zake.”—Yesaya 65:21.
Padzakhala chakudya chambiri. “M’dzikomo mudzakhala dzinthu dzochuluka pamwamba pa mapiri; Zipatso zake zidzati waa.”—Salmo 72:16.