Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g16 No. 5 tsamba 7
  • Nkhani za ku North ndi South America

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Nkhani za ku North ndi South America
  • Galamukani!—2016
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mungachepetse Nkhawa Mukasiya Kumaona Maimelo Pafupipafupi
  • Nsomba Zayambanso Kuchuluka
  • Zachiwawa KU Brazil
  • Zimene Tingachite Kuti Tisamapanikizike Kwambiri
    Galamukani!—2010
  • Mungatani Kuti Muchepetse Nkhawa?
    Galamukani!—2020
  • Kupanikizika Maganizo Kwabwino ndi Koipa
    Galamukani!—1998
  • Kodi Ndingatani Ngati Ndimapanikizika Kwambiri Kusukulu?
    Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Loyamba
Onani Zambiri
Galamukani!—2016
g16 No. 5 tsamba 7
Nsomba ya m’nyanja yamchere

ZOCHITIKA PADZIKOLI

Nkhani za ku North ndi South America

Nkhani za kumayiko a ku North ndi South America zikusonyeza kuti mfundo za m’Baibulo n’zolondola komanso zothandiza.

Mungachepetse Nkhawa Mukasiya Kumaona Maimelo Pafupipafupi

Munthu wina amaona maimelo ake katatu kokha pa tsiku ndipo akuoneka wopanda nkhawa, pomwe munthu winayo amaona maimelo ake kambirimbiri ndipo akuoneka wankhawa

Pa kafukufuku wina yemwe anachitika mumzinda wa Vancouver, ku Canada, anapeza kuti anthu amene amaona maimelo katatu kokha patsiku sakhala ndi nkhawa kwambiri poyerekezera ndi anthu omwe amaona maimelo atsopano pafupipafupi. Munthu yemwe ankatsogolera pa kafukufukuyu, dzina lake Kostadin Kushlev, ananena kuti: “Zimavuta kuti anthu asiye kumaona maimelo pafupipafupi koma zingawathandize kuti achepetseko nkhawa.”

ZOTI MUGANIZIRE: Popeza tikukhala mu ‘nthawi yovuta,’ ndi bwino kuti tiziyesetsa kuchepetsa nkhawa.—2 Timoteyo 3:1.

Nsomba Zayambanso Kuchuluka

Bungwe lina loteteza nyama zakutchire linanena kuti: “Zikuoneka kuti nsomba komanso zamoyo zina zayamba kuchuluka m’madera amene boma likuletsa kuti anthu asamaphe nsomba” ku Belize ndi m’madera ena a ku Caribbean. Bungweli linanenanso kuti: “Pangatenge zaka zochepa kuti nsomba komanso zamoyo zina ziyambenso kuchuluka m’madera amene amaletsa kupha nsomba kusiyana ndi m’madera amene saletsa. Komabe pangatenge zaka zambiri . . . kuti nsombazi zichuluke ngati mmene zinalili poyamba.” Mtsogoleri wina wa m’bungweli dzina lake Janet Gibson ananena zokhudza dziko la Belize kuti: “Zikuoneka kuti kuletsa anthu kuti asamaphe nsomba m’madera ena kukhoza kuthandiza kuti nsomba komanso zamoyo zina ziyambenso kuchuluka m’maderawo.”

ZOTI MUGANIZIRE: Kodi mfundo yakuti zinthu zachilengedwe zikhoza kubwereranso mmene zinalili poyamba sikusonyeza kuti pali wina wanzeru amene anazilenga?—Salimo 104:24, 25.

Zachiwawa KU Brazil

Bungwe la boma lofalitsa nkhani ku Brazil linanena kuti zachiwawa zikuchuluka kwambiri m’dzikolo. Mwachitsanzo, mu 2012, unduna wa zaumoyo unapeza kuti anthu oposa 56,000 anaphedwa ndi anthu anzawo. Chiwerengerochi ndi chokwera kwambiri poyerekezera ndi cha zaka zam’mbuyo. Munthu wina woona za chitetezo m’dzikoli ananena kuti kuchuluka kwa anthu ophedwawa kukusonyeza kuti makhalidwe a anthu afika poipa kwambiri. Iye ananenanso kuti anthu akangosiya kulemekeza malamulo a dziko “amayamba kuchita zachiwawa nthawi iliyonse imene akufuna zinazake.”

KODI MUKUDZIWA? Baibulo linaneneratu kuti idzafika nthawi pamene anthu ambiri adzasiya kumvera malamulo komanso kuti chikondi cha anthu ambiri “chidzazirala.”—Mateyu 24:3, 12.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena